بسم الله الرحمن الرحيم
من كتاب/ الكلمات النافعة في الأخطاء الشائعة صـ330
75 خطأ في صلاة الجمعة
Zolakwika 75 za Tsiku la Jum’ah
No. 8
Kusiya kuswali Tahiyyatal Masjid
•••••••
Tahiyyatul Masjid ndi ma rakaat awiri omwe munthu amayenera kuswali akangolowa munzikiti asanakhale pansi kapena kuchita chirichonse. Ngakhale atakhala kuti sakupita kukaswali, kapena akungodutsa kuti atulukire khomo lina, koma ngati walowa akuyenera kuswali ma rakaat amenewa.
Tahiyyatul Masjid ndi “Kulonjera mzikiti” mmene timanenera kuti “Assalam Alaikum” tikakumana ndi munthu, malonje a munzikiti ndi kuswali ma rakaat awiri.
Choncho Tsiku la Jum’ah timamva zambiri; ena amanena kuti ngati walowa nkupeza imaam ali pa minbar basi usaswali kalikonse ungofikira kukhala nkumamvera khutbah.
Tikawafunsa komwe anadzitenga izi, amanena kuti Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
“Khatweeb akakwera pa minbar, palibenso kuswali kapena kuyankhula kulikonse”
Chabwino…
Nanga poti Mtumiki wathu Muhammad salla Allah alaih wasallam yemweyonso anatiphunzitsa kuti:
“Mmodzi wa inu akalowa munzikiti, asakhale mpaka ataswali ma rakaat awiri”
Hadith yopanda chigamba, yomwe ikupezeka mu Sahih Al Bukhari (1167) ndi Sahih Muslim (714)
Zikakhala choncho, timayenera kufufuza hadith yomwe ikuonetsa kuti ikuletsa zochitayo.
Tamva kale kuti yomwe ikulamula kuti tiswaliyo ndi ya saheeh (yopanda chigamba, yosakaikitsa komanso ikupezeka mu mabuku awiri akuluakulu a Sahih (opanda chikaikitso). Choncho tiyeni tiyione hadith yomwe ikuletsayo kuti ikupezeka kuti.
Hadith imeneyi ndi yofooka kwambiri ndipo sitikuyenera kuigwiritsa ntchito ngati umboni pankhaniyi.
Tsopanotu ambiri amakonda kufunsa kuti kodi tingadziwe bwanji kuti hadith ndi yofooka?
Njira ndi zambiri komanso ‘ilm yodziwira njira zimenezi ikufunika kuyambira pansipansi, kulowa mkalasi ndikuphunzira phunziro lapadera la Hadith..  koma apa ndingolongosola zokhunza hadith imeneyi…
Al Tabarani anaibweretsa mu buku lake “Al Kabeer” mu chain chomwe akupezekamo Ayyub bun Nuhaik yemwe anali okaikitsa potulutsa nkhani, (choncho nkhani zake kuphatikiza ma hadith sizimafunika kudzitenga chifukwa za Mtumiki sizimafunika kukhala zokaikira pokamba).
Choncho hadithiyi anatsimikiza ma ulamaa ambiri kuti ndi yofooka, monga Al Haithami mu buku la “Al Majma’ (vol.2/184)”, Al Haafidh bun Hajar mu “Fat’hul Baari (vol.2/409)”. Komanso Sheikh Al Albaani mu “Al Dhwaeefah (78)” anati ndi hadith yabodza.
Choncho zomwe zili zotsimikizika ndi zoti yemwe walowa pamene Imam akupanga khutbah, aswali ma rakaat awiri.
Umboni winanso ndi hadith yaoona yochokera kwa Jabir bun Abdillah radhia Allah anhu, anati: anafika munthu pamene Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kupanga khutbah Lachisanu (ndipo anafikira kukhala). Mtumiki anamufunsa kuti: “waswali?” anayankha kuti ayi..Mtumiki anati: “imilira ndipo uwerame ma rakat awiri (uswali ma rakaat awiri)”
Hadith ikupezeka mu Sahih Al Bukhari (930) komanso Sahih Muslim (875).
Mu report la Muslim, hadith yomweyo ya Jabir bun Abdillah radhia Allah anhu aipitiriza motere: anati: Anafika Sulaykun Al Ghatafaaniyy tsiku la Jum’ah pamene Mtumiki anali kupanga khutbah, ndipo anakhala. Mtumiki anati: “Ee iwe Sulaiku, ima uswali ma rakat awiri ndipo ufupikitse” kenako anati: “Mmodzi wa inu akabwera tsiku la Jum’ah pamene imaam akupanga khutbah, aswali ma rtakaat awiri ndipo afupikitse”
Sahih Muslim (875)
Choncho palibe umboni woletsa kuswali pamene mwampeza imaam ali pa minbar. Komanso tidziwe kuti imeneyi si sunnah ya Jum’ah koma kulonjera mzikiti