Jamaatun Tablighi ndi gulu lomwe limagwira ntchito yofalitsa uthenga wa Allah kudzera mu liwu la Tawhid,  kalimah Laa ilaaha illa Allah
“Tableegh تبليغ Kufalitsa”
Ntchitoyi ndi yotamandika ndipo ndi ya malipiro aakulu. Msilamu aliyense ndi udindo wake kufalitsa uthenga wa deen.
Umboni wa tableegh yomwe tikukambayi ukupezeka mu Qur’an Surah Al Maaidah Aayah 67:
يَا أَيُّهَا الرَّسُولُ بَلِّغْ مَا أُنزِلَ إِلَيْكَ مِن رَّبِّكَ وَإِن لَّمْ تَفْعَلْ فَمَا بَلَّغْتَ رِسَالَتَهُ وَاللّهُ يَعْصِمُكَ مِنَ النَّاسِ إِنَّ اللّهَ لاَ يَهْدِي الْقَوْمَ الْكَافِرِينَ
“Ee iwe Mtumiki, falitsa zomwe zinabvumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako,  ndipo ulapanda kutero ndiye kuti sunafalitse uthenga wake,  ndipo Allah akuteteza kwa anthu,  Allah samaongola anthu okanira”
Apa Allah akumulamula Mtumiki wake za kufalitsa uthenga,  ndipo ife ndi ntchito yathu kupitiriza ntchito yomwe anatisiyira Mtumiki. Iye ananena kuti:
بَلِّغُوا عَنِّي وَلَوْ آيَةً…
“Falitsani uthenga wanga ngakhale liwu limodzi/ngakhale aayah”
Choncho apa tikupeza kuti Mtumiki akutilamula za kufalitsa uthenga,  ntchito yomwe iye ankachita. Pofuna kugwira ntchito ya Mtumiki timayenera kupanga monga momwe iye ankapangira,  osaonjezera kapena kupungula.
Monga mmene akunenera pankhani ya swalaat,
صلوا كما رأيتموني أصلي
“Pempherani monga mmene mwandionera ine ndikupemphelera”
Apatu sizikutanthauza kuti aliyense anamuona Mtumiki mmene ankaswalira, koma akutanthauza kuti tiswali malinga ndi mmene anatiphunzitsira kuti tidziswali … timatha kudziwa mmene ankaswalira kudzera mma hadith ndi nkhani zina.
Choncho izi nchimodzimodzi ntchito ina iliyonse ya deen, tikuyenera kuigwira monga mom we ankagwilira mwini wake.
Ndipo analetsa kuonjezera zinthu muntchito kapena ibaadah za mu deen. Mu hafith yoyambayo, anthu amaimira poti
بَلِّغُوا عَنِّي وَلَوْ آيَةً
“Falitsani uthenga wanga ngakhale aayah imodzi”
basi, komatu ikupitilira kutsogoloko akuletsa zoonjezera zabodza popanga tabligh:
بَلِّغُوا عَنِّي وَلَوْ آيَةً, وَحَدِّثُوا عَنْ بَنِي إِسْرَائِيلَ وَلَا حَرَجَ, وَمَنْ كَذَبَ عَلَيَّ مُتَعَمِّدًا فَلْيَتَبَوَّأْ مَقْعَدَهُ مِنَ النَّارِ*
“Falitsani uthenga wanga ngakhale aatah imodzi,  ndipo kambani za ana a Israel palibe vuto, _koma yemwe angandinamizire ine, ndithu akudzikhonzera malo okhala ku moto”.
Tikuona kuti pambuyo potilamula kuti tifalitse uthenga wake, watiloleza kukamba za ma Bani Israeel, ndipo watichenjedza kuti tisamunamizire … tisatenge zabodza za ma Bani Israel nkumati ananena Mtumiki. Tisaonjezere mu uthenga wake nkumati ananena Mtumiki. Tisapungule mzichitochito za Mtumiki nkumati anapanga Mtumiki.
Ndipo amene angapange zimenezo, adziwe kuti akudzikhonzera yekha malo okhala ku moto wa Jahannam.
Tatiyeni tibwelere ku Aayah ija,
يَا أَيُّهَا الرَّسُولُ بَلِّغْ مَا أُنزِلَ إِلَيْكَ مِن رَّبِّكَ وَإِن لَّمْ تَفْعَلْ فَمَا بَلَّغْتَ رِسَالَتَهُ وَاللّهُ يَعْصِمُكَ مِنَ النَّاسِ إِنَّ اللّهَ لاَ يَهْدِي الْقَوْمَ الْكَافِرِينَ
“Ee iwe Mtumiki, falitsa zomwe zinabvumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako,  ndipo ukapanda kutero ndiye kuti sunafalitse uthenga wake, ndipo Allah akuteteza kwa anthu,  Allah samaongola anthu okanira”
Kumapetoko kuli mau oti
“…ndipo Allah akuteteza kwa anthu. Allah samaongola anthu okanira.” mau amenewa akugwirizananso ndi muy a Mtumiki aja onena kuti
وَمَنْ كَذَبَ عَلَيَّ مُتَعَمِّدًا فَلْيَتَبَوَّأْ مَقْعَدَهُ مِنَ النَّارِ
“yemwe angandinamizire one akudzikhonzera mall ku moto”
Chifukwa Allah akumulimbikitsa Mtumiki kuti amuteteza kwa adani, apa Mtumiki akutichenjedza ife kuti tisakhale gulu la adani (omwe Allah akumutetezera Mtumiki) pomunamizira muzokamba ndi muzochita zake
Ndipo ambiri tikangomva kuti tableegh, timabwera ndi maganizo olakwika kuti tableegh ndi yoipa,  ndi gulu la anthu oipa,  ndi bid’ah,  ndi zolakwika mChisilamu.
Zili ngati sadaqa…
Anthu anapotodza sadaqa yomwe inalamulidwa Mchisilamu,  ndikulowetsapo sadaqa za chikunja, za makolo,  ndipo tikangomva liwu loti sadaqa,  timabwera ndi maganizo oti ndi zoioa chifukwa choti sadaqa yomwe inalamulidwa mu Quran sitikuidziwa, timangodziwa za makolo zija zomwe anadzilowetsa mu deen nkudzioezera malamulo awo ndikuldziliwetsa mmalo mwa sadaqa yokakamizidwa ija.
Jamaat Tabligh جماعة التبليغ Gulu Lofalitsa Uthenga
Inu ndi ine kukhonza gulu la tableegh ndikumayendera malamulo komanso njira zomwe Qur’an ndi Sunnah zalamula,  sipangakhale vuto lirilonse. Komatu vuto Lori pa kapangidwe, kake. Kuonjezera zomwe Chisilamu sichinaphunzitse kudzera mu Qur’an ndi Hadith.
Tatiyeni tione limodzi magulu omwe amagwira ntchitoyi padziko lino lapansi,  ndipo amatchuka ndi dzina limeneli la Jamaat Tableegh, dzinali limangosiyana kumapetoko,  amaonjezera malinga ndi madera omwe akuchokera,  mwachitsanzo:
جماعة التبليغ الديوباندية
Jamaatu Tableegh Deoband ndi gulu la tableegh kuchokera ku Deoband, India. Awa amatchuka ndi zichitochito zachilendo monga
kuika chiwelengero cha masiku monga 40 oyendera pofalitsa uthenga
kugwiritsa ntchito buku lomwe Mtumiki sanasiye,  nkumalombikitsa anthu kuwerenga ndikimawaiwalitsa Qur’an ndi zina zotero
Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena mmau ake omaliza kuti
تَرَكْتُ فِيكُمْ أَمْرَيْنِ لَنْ تَضِلُّوا مَا تَمَسَّكْتُمْ بِهِمَا: كِتَابَ اللهِ وَسُنَّةَ نَبِيِّهِ
Ndakusiirani zinthu ziwiri ndipo simudzasochera ngati mutadzigwiritsa, Buku la Allah ndi Sunnah za Mtumiki wake
Munthu ofuna kuyenda munjira ya Mtumiki akuyenera kugwiritsa zintju ziwirizi ndipo akangophonyana nazo,  asocheretsa anthu.  Asapange buku lakelake nkimagwiritsa ntchito yomwe Qur’an ndi Hadith ikanagwira.
Monga mmene tanenera,  tikupeza kuti Jamaat Tabligh ndi magulu a Asilamu ndithu, komanso kulimbikira kwawo pa ntchito za Da’wah ndiye zofunikirazo ndithu. Koma gulu limene tikulidziwa ambirifeli, nchimodzimodzi magulu ena ambiri omwe amachita zolakwika zomwe zimafunika kudzikhonza.
Ndafotokoza zabwinozomwe tableegh yeniyeni imayenera kumachita, choncho apa ndilongosolanso zolakwika zomwe gulu la Jamaat Tabligh lomwe tikulidziwali limachita, komanso limayenera kukhonza chifukwa ndi zolakwika mu deen zomwe zimapangitsa kuti ntchito yawo yomwe anali ndi cholinga chotukula Deen ikhale yoonongeka. Komanso tidziwe kuti zolakwikazi zimasiyana malinga ndikutinso maguluwa alipo mmalo osiyanasiyana, zikhalidwe zosiyanasiyana komanso zikhulupiliro zosiyanasiyana. Mwa ma Jamaat amenewa, omwe mumapezekamo ilm komanso ma ulamaa omwe amagwiritsa Sunnah pakufalitsa uthenga ndikumapewa bid’ah, amakhala ndi zolakwika zochepa komanso ndi ochepa kwambiri. Pomwe ma jamaat ena, muli zolakwika zochuluka kwambiri zoti zimapereka picture yoti ntchito yomwe amagwirayo yonse ndi yolakwika.
Tatiyeni tionere limodzi zolakwika izi, zomwe ambiri amaganiza kuti ndiye deeniyo;
Chomwe chili choopsa kambiri nchoti samatenga aqeeda ya Ahlu Sunnah wal Jamaah (Sunnah ya Mtumiki ndi ma Sahaba ake), zimenezi zingamveke tikaonesetsa zambiri mwa zikhulupiliro zawo komanso zochita za atsogoleri awo.
Samakhala ndi chidwi pa maphunziro a deen kuti adziwe chilungamo. (kungodziwa kalma laa ilaah illah Allah basi ntchito yayambika).
Amatanthauzira ma aayah a mu Qur’an ndikumabweretsa maphunziro osemphana ndi zomwe zikufunikira mu aayahyo….mwachitsanzo ma aayah a Jihaad, amatanthauzira kuti “kutuluka kukapanga da’wah”, ma aayah omwe ali ndi liwu loti الخروج – kutuluka, kwa iwo likutanthauza kutuluka kukapanga da’wah.
Masiku omwe amawaika kuti ndi otuluka kukapanga da’wah amawapanga kuti ndi a ibaadah, ndipo izi amapereka ma umboni amu Qur’an, monga aaya yoti
فَسِيحُواْ فِي الأَرْضِ أَرْبَعَةَ أَشْهُرٍ
“Yendani padziko miyezi inayi basi”
amatanthauzira kuti kutuluka komwe amatuluka iwoko umboni wake ndi umenewu, ndipo osatulukayo akunyozera aayah.
Kodi aayah imeneyi tanthauzo lake ndi loti chani?
Aayah imeneyi ikukamba za ma Mushrik, anthu opembedza mafano, amene awatchula mu aayah ya mbuyo mwakeyo, ndipo ili chonchi:
بَرَاءةٌ مِّنَ اللّهِ وَرَسُولِهِ إِلَى الَّذِينَ عَاهَدتُّم مِّنَ الْمُشْرِكِينَ
فَسِيحُواْ فِي الأَرْضِ أَرْبَعَةَ أَشْهُرٍ وَاعْلَمُواْ أَنَّكُمْ غَيْرُ مُعْجِزِي اللّهِ وَأَنَّ اللّهَ مُخْزِي الْكَافِرِين
“Uku ndikudzipatula kochokera kwa Mulungu ndi Mtumiki wake ku mapanganowa amene mudapangana nawo (Kenako nkuswa mapangano awowo) am’gulu la opembedza mafano.”
(Auze opembedza mafano): Yendani padziko miyezi inayi basi. (pambuyo pake sipadzakhala chitetezo pakati pawo ndi ife). Ndipo dziwani kuti inu simungathe kumpambana Mulungu. Ndipo Mulungu ngosambula osakhulupirira.
Mau awa amawauza ma Mushrik osati Asilamu.
Anthu tikukamba apa,  ndi aja omwe amakhala ndi chikhulupiliro choti amamupanga munthu mmodzi kuti adzikhala oyankhula pochita da’wah akatuluka, ndipo kulephera kapena kupambana kwa gulu lonse pa da’wah kumakhala malinga ndi munthu ameneyo.
Ma hadith ambiri ofooka komanso opeka amapezeka ndi anthu amenewa ndipo amawagwiritsa ntchito, komanso amagwiritsa ntchito tinkhani topeka ngati ma umboni pa zoyankhula zawo. Tinkhani monga ta ma Sahaba
Mistake ina yoopsa kwambiri ndi yoti samayankhula kapena kuletsa ma munkaraat (zoipa), chifukwa choganiza kuti kulamula zabwino kokha kukukwanira ngakhale osaletsa zoipa. Choncho muwapeza kuti mma da’wah awo samaletsa zoipa zomwe zafalikira pakati pa anthu, kumachita slogan ya Ummah uno yagona pa kulamulana kuchita zabwino komanso kuletsana kuchita zoipa. Ndipo uwapeza akubwerezabwereza aayah iyi:
وَلْتَكُنْ مِنْكُمْ أُمَّةٌ يَدْعُونَ إِلَى الْخَيْرِ وَيَأْمُرُونَ بِالْمَعْرُوفِ وَيَنْهَوْنَ عَنِ الْمُنْكَر وَأُولَئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ
“Ndipo mwa inu lipezeke gulu la anthu oitanira kuzabwino (Chisilamu) ndipo alamule (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa. Iwo ndiwo opambana. Surah Aali Imran 104
Omwe ali okhulupirika pamaso pa Allah ndi amene amalamulana zabwino ndikuletsana zoipa, koma osati kumangolamulana zabwino zokhazokha.
Ena mwa iwo amayamba kudzikonda komanso kudzitukumula ndikumanyoza ena kumawaona ngati apansi, komanso kumapezeka kunyoza ma ulamaa ena chifukwa choti samatuluka kuma jamaat ndipo amawapanga kuti ndi ongokhala nkumangogona, komanso zambiri zimachitika podzionetsera kwa anthu kuti akuchita, monga kulembana maina…yomwe ndi riyaa (shirk yaing’ono). Da’wah munthu ukamachita udzichita zoti akuone Allah osati akuone Sheikh aakulu kapena mtsogoleri wa Da’wah, pamenepo ndiye kuti udzichita pofuna kukhutitsa maso a munthu osati cholinga cha da’wah.
Amanena kuti kutuluka kumeneku ndi kwabwino kwambiri kuposa kupanga ibada monga jihaad kapena kufunafuna ilm, kumachita kuti zomwe akudzipanga kuti nzosafunikirazo ndiye zomwe ziri ntchito zofunikira komanso ndi ibaada yaikulu.
Ena mwa iwo amalowa mkatikati ndikumatanthauzira ma Aayah (tafsir) komanso ma Hadith moononga komanso mopanda kuzindikira kulikonse.
Ambiri mwa iwo samasamala ufulu wa ana ndi akazi awo akamachoka pakhomo, ndipo amachoka ngakhale pakhomo palibe chakudya, akuti awadyetsa Allah. Mapeto ake ana amagona ndi njala.
Choncho ma Ulamaa sanaloleze kutuluka munjira imeneyo nkumakachita nawo chimodzimodzi, kupatula kuti Ngati ungafune kutuluka, utuluke ncholinga chokawathandiza kukhonza zolakwika zimene amachitazi kuti da’wah ikhale yolandiridwa kwa Allah.
Chonchonso sizololedwa kuti tidziletsa anthu kuti asamapange da’wah, kuti asamayendere anthu nkumawauza za deen, koma zoyenera kwa ife nkuyesetsa kukhonza zolakwika komanso kuwalangiza mmene da’wah ikuyenera kukhalira malinga ndi Qur’an ndi Sunnah.
Sheikh Abdul Aziz bun Baaz anati:
Sizololedwa kukhala nawo pa kutuluka kumeneku kupatula amene ali ndi ilm (ozindikira) pa aqeedah yolondola imene Ahlu Sunnah wal Jamaah amayendera, kuti awaongolere ndikuwalangiza komanso kuthandizana nawo pa zabwino chifukwa iwowo ali very active koma vuto ndi loti akufunika ilm (maphunziro) oonjezera komanso akufunikira omwe angawaongolere ku tauhid yolondola. Allah atipatse tonse kuzindikira za deen komanso kugwiritsa ntchito. Majmu’ Fataawa Al Sheikh Ibn Baaz vol.8/331
Kutuluka mu njira ya Allah si kutanthauza kutuluka kumene amachita anthu a Tabligh … Kutuluka munjira ya Allah ndi kutuluka polimbana ndi kuteteza Deen mu njira zomwe Mtumiki ndi ma Sahaba ake ankagwiritsa ntchito. Koma zomwe zimatchedwa masiku ano kuti kutuluka – tabligh, ndi bid’ah komanso sizinachitike ndi ma Sahaba.
Ndipo kutuluka kwa munthu kukapanga da’wah munjira ya Allah sikukuyenera kukhala ndi chiwelengero cha masiku chokhanzikika, koma ayenera kuitanira kwa Allah malinga ndi mmene angathere, popanda kukhala pa jamat kapena kuika masiku 40 kapena ochepera pamenepo.
Ma umboni omwe amagwiritsa ntchito ndi olakwika komanso amatanthauzira ma hadith ndi ma aayah molakwika kuti zifanane.
Munthu oitanira munjira ya Allah akuyenera kukhala ozindikira osati mbuli pa deen ndi malamulo ake. Allah akunena mu Surah Yusuf 108:
قل هذه سبيلي أدعو إلى الله على بصيرة
Nena: “Iyi ndi njira yanga. Ndikuitanira Kwa Mulungu mwanzeru zokwanira,
Kutanthauza kuti zimafunika kumapanga da’wah ndi nzeru chifukwa wa Da’wa akuyenera kudziwa komanso kuzindikira zomwe akuitanirazo, monga ma waajib, ma mustahab, haram, makrooh, komanso adziwe zomwe zili shirk, zomwe zili za machimo, zopangitsa kufr, kapena kukhala oipa mu deen.
Popanda kudziwa izi munthu ameneyo asocheretsa anthu.
Kutuluka kukapanga da’wah munjira yopanda nayo ilm ya deen nkumene kumatchinga njira yofunira maphunziro kwa amene akupanga da’wayo, chifukwa iwo amaona kuti basi ilm ali nayo pomwe ilm yomwe ilipoyo ndi yosokonekera. Choncho kutuluka kumeneko kumakhala kosayenera chifukwa akusiya faradh ya kufunafuna maphunziro, nkumanka nafalitsa bodza mu deen.
Ntchito yopanda ilm ndiyoonongeka
Kuchokera mu buku la
ثلاث محاضرات في العلم والدعوة
Allah ndamene Adziwa Zonse