Tiyeni titsegule page103 ya chitabu cha أحكام الجنائز وبدعها cha Allaamatu Sheikh Muhammad Naasirul-Deen Al Albaaniy, ndipo tiyambire pa mutu wa number 13 kumapita kutsogolo mmapage otsatira mu chitabuchi

Zoyenera kuchita pa Janaaza

Janaaza ndi mwambo wa maliro womwe umachitika munthu akamwalira, ndipo pemphero kapena kuti swalaat yomwe imayenera kuchitika pa mwambowu imatchedwa swalaatul Janaaza (pemphero la maliro kapena kuti swalaat ya maliro).

Msilamu aliyense akamwalira, otsala amayenera kumuchitira zinthu zinayi:

  • Kumusambitsa (Ghusl)
  • Kumuveka (Kafn)
  • Kumuswalira (Swalaat)
  • Kumuika mmanda (Dafn)

Kuswalira Maliro

Swalaat ya maliro a Msilamu ndi Faradh Kifaaya (Faradh Kifaaya ndi ntchito yokakamizidwa yokwanira anthu onse ndi omwe sanachite; ochepa omwe angachite ntchito imeneyo, imakwanira kwa omwe sanachite omwe ali pamalopo. Choncho ngati gulu la anthu lasonkhana pamaliro ndipo ochepa apemphelera maliro, zimakwanira kwa omwe sanapempherewo ngati ali ndi niyyah yofanana ndi omwe apempherawo. Zili chonchi pa swalaat ya Maliro malinga ndi lamulo la Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Jamaah ya Swalaatul Janaaza

Swalaatul Janaaza ndi Sunnah kumpheredwa pa jamaah, ndipo atsogolere Imam, monga mmene swalaat zina zimapempheredwera. Apa tisasokonezeke ndi mmene swalaat janaaza ya Mtumiki inachitikira, poti anthu anaswali magulumagulu popanda imam. Imeneyo inali special swalaat ya Mtumiki, koma ngakhale Mtumikiyo pamene anali moyo swalaat Janaza zomwe anali kutsogolera anali kuchita momwe tilongosolere kutsogoloku.

Imaam wa Swalaatul Janaza: Oyenera kutsogolera swalaat ya Jeneza. Sheikh akutilongosolera izi pa page 128 mu cvhitabu chawochi:

Oyambilira weniweni akhale yemwe omwalirayo anamusankha (waswiyyah) pamene anali moyo (ngati anaterodi), ndipo akhale wabwino osati wodzadza ndi machimo. Tafsir Ibn Uthaymin (Al Fatiha & Al Baqarah 2/311), Kasshaaful Qannaa’-Al Bahwati (2/88).

Wachiwiri, ngati palibe waswiyyah, imaam akhale mtsogoleri, malinga ndi maumboni ochokera mwa ma imam onse anayi, kuphatikizapo ma Salaf Swaalih ndi ma ulamaa ochuluka. Ndipotu iwowa anadzitenga kuchokera mma hadith ambiri monga yochokera kwa ‘Uqbah bun ‘Amru ndi Tha’laba, anati: Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “asatsogolere munthu pa mtsogoleri wake” . Akunenanso Al Bahwatiy mu Kasshaaful Qannaa’- (2/110) kuti, chifukwa choti ndi Sunnah kusonkhana pa swalaat, choncho ngati angapezekepo mtsogoleri kapena mfumu (ozindikira), akuyenera kutsogozedwa.

Wachitatu, ngati palibe mtsogoleri, imam akhale yemwe ali odziwa kuwerenga, monga mmene ndondomeko iliri mu Hadith iyi polongosola za utsogoleri wa swalaat: Atsogolere gulu mwa inu yemwe ali odziwa kuwerenga Qur’an, koma ngati ali ofanana kuwerenga, atsogolere yemwe akudziwa Sunnah, ngati ali ofana kudziwa Sunnah, atsogolere yemwe anayambilira pa msamuko … ndipo asakhale imam munthu pa mtsogoleri….. Sahih Muslim 2/133 ndi ena ambiri, ndipo Hadithiyi inachokera kwa Abi Mas’ud Al Badriy Al Answaariy radhia Allah anhu.

Yemwe ali odziwa Qur’an ngakhale atakhala mwana, atsogolere, malinga ndi Hadith yochokera kwa Amru bun Salamah, pamene anasowa otsogolera ndipo iye analolezedwa kutsogolera, koma nthawi imeneyo anali mwana wamng’ono kwambiri. Ikupezeka mu Sunan Abi Dawud ndi Al Bayhaqiy (599, 500, 602).

Pamene maliro angapo achitika mosakanikirana amuna ndi akazi, ndizololedwa kuswali swalaat imodzi, komanso ndizololedwa kuswalira pamodzi malinga ndi mmene anali kuchitira Mtumiki ndi ma Swahaba ake.

Ndizololedwa kuswalira jeneza munzikiti, malinga ndi hadith ya Aaisha radhia Allah anha pa maliro a Sa’d bun Abi Waqqaas. Sahih Muslim 3/63, Al Bayhaqiyy 4/51

Ngakhale zili choncho, koma zomwe zili zabwino kwambiri ndi kuswalira pamalo otseguka, panja pa mzikiti, pamene pakhonzedwa kuti swalaat ya Janaza idzichitikira. Zimenezo ndi mmene zinaliri nthawi ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam komanso ndi zodziwika kwambiri mchiphunzitso chake. Izi zikupezeka mma Hadith angapo, monga yochokera kwa Ibn Umar radhia Allah anhu ndipo ikupezeka mu Sahih Al Bukhari 3/155

Malo oyenera kuima Imam: Imaam aime pafupi ndi mutu wa omwalirayo akakhala wamwamuna, ndipo akakhala wamkazi, aime pakati pake. Zili choncho malinga ndi ma Hadith awiri, imodzi yochokera kwa Abi Ghaalib Al Khayyaat, yomwe anailandira Abu Dawud 2/66-67, Al Tirmidhi 2/147, Ibn Maajah ndi ena otero … Hadith ina ndiyochokera kwa Sumrah bun Jundub, imene ikupezeka mu Sahih Al Bukhari 3/156-157, Muslim 3/60, Abu Dawud, Al Nasaai, Al Turmidhi ndi ena otero. (Page 140 – أحكام الجنائز وبدعها)

Chiwelengero cha Jamaah

Chiwelengero choyambira pa jamaah ya swalaatul Janaaza ndi anthu atatu malinga ndi hadith ya Abdullah bun Abi Talha, pamene anaswalira jeneza ya ‘Umayr bun Abi Talha motsogozedwa ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam, ndipo pambuyo pa Talha panali Ummu Sulaym. Hadithiyi ikupezeka ndi Al Haakim 1/365, Sunan Al Bayhaqi 4/30, 31.

Koma ngati jamaah ingakhale yochuluka mpaka anthu 100, ndi zothandiza kwambiri chifukwa ndiye kuti amachuluka omupemphera zabwino munthu omwalirayo, malinga ndi kulankhula kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam mu Hadith ya Sahih Muslim 3/35, Sunan Al Nassai 1/281, 282, Sunan Al Tirmidhi 2/143, 144 ndi ena ambiri.

Komanso ndizotheka kupemphera Asilamu ochepa omwe ali ndi Aqeeda yabwino yosasakanikirana ndi dontho lirilonse la shirk, malinganso ndi kulankhula kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam koti “palibe Msilamu yemwe angamwalire ndikupempheleredwa ndi anthu 40 omwe sapanga shirk iriyonse kwa Allah, popanda kulandiridwa mapemphero awo”. Hadithiyi ikupezeka mu Sahih Muslim, Sunan Abi Dawud 2/46, Sunan Ibn Maajah, Suna Al Bayhaqi ndi Musnad Imaam Ahmad 2509, ndipo inachokera kwa Ibn Abbaas radhia Allah anhu.

Ndizabwino komanso zokondedwa (Mustahabb) kuti miswaff kapena kuti mizere ya swalaatul Janaaza iyambire itatu pambuyo pa imam, nkumakwera 4, 5… Izi ndimonga mmene Mtumiki salla Allah alaih anali kuchitira, malinga ndi hadith ya Al Tabaraani mu (AlKabeer 7785), Al Haythamiyyu (AlMujma’u 3/432); akunena kuti “Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaswalira Jeneza pamodzi ndi anthu 7, ndipo anakhonza mizere itatu powaika atatu munzere woyamba, awiri munzere wachiwiri ndipo awiri munzere wachitatu”. Ma Hadith alipo ambiri pamutu uliwonse womwe ndizilongosola, koma malinga ndi kuchulukako, ndizingotchula imodzimodzi ndipo ofuna kudziwa ma Hadith enawo akhonza kupita mu chitabu ichi cha أحكام الجنائز وبدعها. Pano tikuyendera page 128…

Ndipo ngati alipo munthu mmodzi yekha pambuyo pa imam, ndiye kuti maimidwe ake asaime mogundana phazi ndi imam monga mmene timaimira pa swalaat zina zonse tikamaswalitsana anthu awiri; koma mmalo mwake, aime kumbuyo kwa imam pa mzere woyamba. Izitu ndi malinga ndi mmene anaimira mu Hadith ija ya Abu Talha: “Mtumiki salla Allah alaih wasallam anatsogola, ndipo Abu Talha adadza pambuyo pake, Ummu Sulaym pambuyo pa Abu Talha ndipo panalibenso wina.”

Mapangidwe a pemphero la Jeneza (Swalaatul Janaaza)

Tidziwe kuti swalaat Janaaiz ndi swalaat yokhayo yomwe ilibe rakaah, ilibe kuwerama, kupanga sajda, kupanga tahiyyaat ngati mmene tichitira swalaat zina zonse. Inde, swalaat Janaaza ndi swalaat ya faradh koma ilibe nthawi monga mmene ziliri swalaat zina, chifukwa imachitika pakagwa maliro, ndipo siili mu gulu la swalaat zisanu za patsiku zija. Komabe, pali nthawi zingapo zomwe ndi zoletsedwa kuswalira maliro, mpaka zidutse kaye nthawizo.

Chiwerengero cha ma Takbeera

Tikapita pa page 141, akutifotokozera chiwerengero cha ma takbeera a pa swalaatul Janaaza.

Ndiye monga mmene Mtumiki wathu swalla Allah alaih wasallam ndi ma Swahaba ake anafotokozera, swalaatul Janaza imakhala ndi ma takbeera anayi. Mmenemo ndi momwe anali kuchitira Mtumiki salla Allah alaih wasallam,

Mu Hadith ya Abi Hurayrah, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaswalira swalaat ya maliro a Najaashiy ndipo anapanga ma takbeera anayi.. Ikupezeka mu Sahih AlBukhariy 3/90, 145, 155, 157 – Sahih Muslim 3/54 ndi ena ambiri. Komanso Hadith ya Abdullah bun Abi Aufa anati: Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kupanga ma takbeerah anayi… Al Bayhaqiy 4/35 (Sahih). Imeneyo ndi nkhani ya ma Takbeera.

Tiyeni pa page 147 ya chitabuchi, ndipo akunena kuti:

Ndipo ndizolamulidwa kunyamula mikono popanga takbeera ndikuika mkono wamanja pa mkono wamanzere. Ibn Hazm 5/128

Zoyenera kuwerenga pambuyo pa ma Takbeerah

Takbeera yoyamba: Werengani Surat Al Fatihah. Al Bukhaari 3/158, ndi sura iriyonse yaifupi kapena ma aayah ochepa, mositsa mawu. Izi ndi malinga ndi hadith ya Abi Umamah bun Sahl yemwe anati: Ndi Sunnah pa swalaat ya Jeneza kuwerenga Ummul Qur’an (Al Fatiha) pa takbeera yoyamba, kenako apange matakbeera atatu ndikupanga salaam mu takbeera yomalizayo. Sunan Al Nasaai.

Takbeera yachiwiri: Mpemphereni madalitso ndi mtendere Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam. Izitu zili choncho mu Hadith ya Abi Umamah yomwe ikupezeka ndi Imaam Al Shafi’i mu chitabu chake chotchedwa Al Umm vol.1/239-240 ndi ena otero. Ndipo mau ake ndi monga mmene mumachitira kumapeto kwa swalaat: (Allahumma swalli ala Muhammad wa ‘alaa aali Muhammad kamaa swallayta ‘alaa Ibrahima wa ‘alaa Aali Ibrahim innaka Hameedun Majeed. Allahumma baarik ‘alaa Muhammad wa ‘alaa Aali Muhammad kamaa baarakta ‘alaa Ibrahima wa ‘alaa Aali Ibrahima innaka Hameedun Majeed). Koma monga mmene tikudziwira, mau amenewa ali ndi mayankhulidwe osiyanasiyana, choncho palibe umboni wonena kuti mapangidwe ake ndi awa, kupatula mapangidwe omwe tikuwadziwa kuchokera ka Mtumiki salla Allah alaih wasallam.

Takbeera yachitatu: Achitireni duaa omwalirawo (duaau ‘alal mayyit), monga mmene ziliri mu Hadith yomwe ija ya Abi Umaamah: Mukamaswalira maliro, khulupirikani pomuchitira dua.

Tsopano ma dua omwe mungawerenge panthawi imeneyi, alipo angapo ndithu koma mukhonza kuwerenga iriyonse mwa iwo:  (Allahumma ighfir lihayyinaa wa mayyitnaa wa shaahidnaa wa ghaaibinaa wa swagheerinaa wa kabeerinaa wa dhakarinaa wa unthaanaa. Allahumma man ahyaytahu minnaa fa ahyihi ‘alal Islaami, waman tawaffaytahu minnaa fatawaffih ‘alal imaan). Kapena

(Allahumma ighfir lahu warhamhu, wa’aafihi wa’f ‘anhu, wa akrim nuzulahu, wawassi’ madkhalahu, waghsilhu bilmaai wa tthalji wal bardi, wa naqqihi minal khatwaayaa kamaa yunaqqa tthawbul abyadh mina ddanas. Wa abdilhu daaran khayran min daarih wa ahlan khyran min ahlih. Wa zawjan khayran min zawjihi, wa adkhilhul jannata wa a’idh’hu min ‘adhaabil qabri wa min ‘adhaabi nnaari, wafsah lahu fi qabrihi a nawwir lahu feeh). Kapena

(Allahumma laa tahrimnaa ajrahu, walaa tadhwillunaa ba’dah). Kapena

(Allahumma in kaana muhsinan fazed fi ihsaanih, wa in kaana musee’an fatajaawaz ‘an sayyiaatih. Allahumma ighfir lahu wathabbit’hu bilqawli tthaabit).

Kapena

(Allahumma inna fulaana ibn fulaan fi dhimmatika wahabli jiwaarika, faqih fitnatal qabri wa’adhaaba nnaar, wa anta ahlul wafaai wal haqq, fa’ghfir lahu warhamhu, innaka antal Ghafooru Rraheem).

Takbeera yachinayi: Khalani chete pang’ono pambuyo popanga takbeera yomalizayi, kenako mupereke salaam imodzi ndikutembenukira kumanja ponena kuti (Assalaam ‘alaykum warahmatullah). Koma ngati mungapange ma salaam awiri, palibe vuto malinga ndi hadith yochokera kwa Ibn Mas’ud radhia Allah anhu, anati: “zinthu zitatu zomwe anali kudzichita Mtumiki salla Allah alaih wasallam, zomwe anthu azisiya: kupanga salaam pa jeneza monga mmene amachitira pa swalat.” Al Bayhaqiyy 4/43, Imaam Nawawi 5/239. Ndipo kupanga salaam imodzi ndikomwe kuli kokhanzikika malinganso ndi ma hadith ambiri.

Zimenezo ndiye zoyenera pa swalaatul Janaaza