Kukhala pa Mpando Poswali
(Munthu yemwe akuloledwa kuswaali atakhala pampando akhale otani)
1. Akhale kuti akulephera kuimilira pa Swalaat
Kuphatikiza kulephera kupanga rukuu’ ndi sajda molongosoka. Choncho aswali chokhala. Monga mmene Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananenera: “pempherani choima, ngati simukwanitsa, pempherani chokhala”.
Hadith Sahih Al Bukhari, ndipo pa ruk’u ndi sujud apanga moyerekeza chokhala, koma sujud ikhasla yotsikirapo kwambiri kuposa ruku’u. Hadith yake inachokera kwa Jabir radhia Allah anhu (Al Baihaqi)
2. Akhale oti akukwanitsa kuima pang’ono
Ndipo sakukwanitsa kuima mokwanira chifukwa cha kumva kuwawa kapena kuopa kuonjezera matenda. Choncho ameneyu aswali choima mmene angathere, koma ngati zingamvute kutero, akhale. Allah Ta’la wanena mu Surah Al Taghaabun 16
فَاتَّقُوا اللَّهَ مَا اسْتَطَعْتُمْ
choncho muopeni Allah mmene mungathere.
Al Sa’diy ananena kuti: Aayah imeneyi ikupereka umboni woti waajib iliyonse yomwe munthu yamukanika, imachotsedwa mwa iye, ndipo amatha kuchita mbali yomwe angakwanitseyo, ndipo mbali inayo imakhululukidwa. Monganso mmene Mtumiki salla Allah alaih wasallam akunenera kuti:
“Ndikakulamulani chinthu, chipangeni mmene mungathere”
Al Bukhari & Muslim (Tafsir Al Sa’di p1031).
Kenako apange ruku’u choima, komanso apangire sujud pansi mmene angathere.
3. Ngati akulephera kuima kwatunthu
Chifukwa cha kumva ululu kapena kuopa kuonjezera matenda. Pamenepo aswali chokhala. Ibn Uthaymeen anati: “pena mupeza kuti munthu waima koma sali okhanzikika malinga ndi vuto lomwe ali nalo mthupi, ndipo akulakalaka ataimilira mpaka kumapeto kwa surat Al Fatiha kuti apange ruku’u; ameneyo akuyenera kungoswali chokhala chifukwa sakwanitsa kuimilira bwinobwino”  – Assharh Al Mumti’ vol.4/461.
Koma apange takbiratul Ihraam ali chimire kenako akhale, chifukwa akapanga atakhala, swalat yake sinalongosoke.”
Imam Al Nawawi anati: “Takbiratul Ihraam ikuyenera kubwera yonse pamene ali chimire, koma ngati angaibweretse chokhala, kapena zilembo zina za takbira wadzibweretsa atakhala, swalat yake sinalongosoke” Al Majmu’ 3/296.
Kenako apange ruku’u choima mmene angatyhere, chimodzimodzinso sujud apangire pansi mmene angathere.
4. Akhale oti sakwanitsa kupanga ruku’ mmene imakhalira koma akhonza kuimilira.
Pamenepo sakuloledwa kukhala, ndipo kuima komanso kuima pochokera ku ruku’u sikuchotsedwa kwa iye. apange ruku’u moyerekeza ali chimire.
Ibn Qudaamah rahimahullah anati: “yemwe angakwanitse kuima koma akulephera kuwerama (ruku’u) ndi sujud, kuima sikuchotsedwa kwa iye. Choncho aswali choima ndikuyerekeza ruku’u ndi sujud” –  Al Mughni vol.2/107
5. Akhale kuti akulephera kupanga sujud mmene imakhalira, koma akukwanitsa kuima.
Pmenepa sakuloledwa kuswali chokhala, komanso kuima sikuchotsedwa kwa iye ngakhale kuima kochokera pa ruku’u … choncho apange sujud moyerekeza ali chikhalire (akafika nthawi yokhala kuti apite pa sujud).
Ibn Qudaamah anati: “yemwe wakwanitsa kuima ndikulephera kupanga ruku’u ndi suju, kuima sikuchotsedwa kwa iye, kenako akhale ndikupanga sujud moyerekeza.” – Al Mughni 2/107.
Kenako apange ruku’u choima mmene imakhalira, ndipo ngati angakwanite kuika manja ake pansi pamene akupanga sujud, atero, koma ngati angalephere, aike pa maondo ake.
Ibn Baaz rahimahullah anati: “koma pa sujud, ndi waajib kuika manja ake pansi ngati angakwanitse, koma ngati sangakwanitse,aike pa maondo ake…izitu ndi malinga ndi Hadith ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam: “ndalamulidwa kupanga sujud ndi mafupa (ziwalo) 7; pa chipumi – kenako analozera pamphuno, manja awiri, maondo awiri, nzonga za mapazi awiri”
Al Bukhari & Muslim – Majmu’ Fatawa ibn Baaz 12/245-46.
Choncho mpando nawo uli ndi malamulo ake pofuna kugwiritsa ntchito munzikiti kwa anthu amene tawalongosola aja.
Amene samatsatira ma condition omwe talongosolawa ndi omwe amachititsa kuti anthu adziona ngati kuswalira pampando ndi tchimo, chifukwa choti iwowo amangosankha kuti akhale pampando, popanda vuto lirilonse. Ambiri amapanga zimenezo chifukwa chosasangalatsidwa ndi kukhala pansi – amenewo swala yawo silongosoka chifukwa KUKHALA PAMPANDO KUMACHITIKA CHIFUKWA CHA MAVUTO A MTHUPI.