Imeneyi ndi swalaat yomwe imapempheredwa dera lina lotalikira komwe swalat janaza yachitikira. Maswalidwe a swalaatul ghaaib ndichimodzimodzi swalaatul janaaza, koma swalat imeneyi (swalaatul ghaaib) ili ndi lamulo lina losiyana ndi swalaatul janaza makamaka pa munthu yemwe akuyenera kupempheredwa.

Zimenezi zikuchokera mmabuku awiri awa:

أحكام الجنائز للشيخ سعيد بن علي بن وهف القهطاني ص244

komanso

تلخيص أحكام الجنائز وبدعها للشيخ محمد ناصر الدين الألباني ص47

Sheikh Muhammad Naasir Al Albaani akulongosola popitiriza kulongosola pamutu wa swalaatul janaaza, ndipo pamfundo ya no. 7 akunena kuti:

Yemwe wafera kudera lomwe kulibeko oti angamuswalire swalaatul haadhwir (swalaatul janaza – mwachitsanzo kulibeko Asilamu, kapena aliko koma sadziwa za swalaatul janaza), gulu la Asilamu omwe ali kudera lina aswali (yomwe ndi swalaatul ghaaib). Zimenezitu zikuchokera poti Mtumiki salla Allah alaih wasallam anamuswalira Al-Najaashiy (mfumu yaku Habasha nthawi imeneyo).

Komanso Imaam Al-Qahtaaniy rahimahu-Allah, akulongosola pa nkhani yomweyi mubuku lawo, ndipo pa mfundo yawo ya no. 8 akuti:

Oswali swalaat ya yemwe palibe (yemwe swalat janaza yake ili kutali), akhale ndi niyyah, kenako alunjike ku qibla ndikumuswalira, ngati zili zoti sanaswaliridwe, kapena waswaliridwa koma anali ndi kufunikira kwakukulu Mchisilamu.

Zimenezitu zikuchokera mu Hadith yomwe inachokera kwa Jaabir radhia Allah anhu, yemwe anati Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaswalira Al-Najaashi (Mfumu yaku Habash), ndipo ine ndinali pamzere wachiwiri kapena wachitatu. Mukuyankhula kwina anati: Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “ndithu wamwalira lero lino munthu wabwino ku Habash, tiyeni muswalireni”, ndipo (Jaabir) anati kenako tinandandana mizere ndipo Mtumiki anatiswalitsa. Mmayankhulidwe ena anati: Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaswalira As’hamata Al-Najashiy ndipo anapanga ma takbeera anayi. Mukuyankhula kwina, Mtumiki anati: “imilirani mumswalire m’bale wanu As’hamah” Sahih AlBukhari.

Hadith inachokera kwa Abi Hurairah radhia Allah anhu, Mtumiki salla Allah alaih wasallam analengeza za imfa ya Al-Najashi patsiku lomwe anamwalira ndipo anatuluka kupita kumalo oswalira ndikuwayala (anthu) mizere, ndipo anapanga ma takbeera anayi. Mayankhulidwe ena, anati: “mpemphereni chikhululuko mzanu”.

Maswahaba anafunsa: E Mtumiki, mukuswalira kapolo wachi Habashi? Kenako Allah anavumbulutsa aayah poyankha funso lija:

وَإِنَّ مِنْ أَهْلِ الْكِتَابِ لَمَنْ يُؤْمِنُ بِاللَّهِ

“Ndithudi mwa amene adapatsidwa Buku, alipo amene akukhulupirira Allah”

Ibn Al-Qayyim rahimahu Allah mu Zaadul Ma’d vol.1/205-206 anati: sizili muchiphunzitso cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam, komanso mu chizolowezi chake (sunnah) kuswaliraaliyense yemwe wamwalira kutali (swalaatul ghaaib); Asilamu ambiri anamwalira munthawi yake koma sanaswalire swalaatul ghaaib, koma zoona ndizoti anamuswalira Al-Najaashiy swalaatul ghaaib.

Tsopano zomwe zikulimbikitsa kusapezeka kwa swalaat ya aliyense yemwe ali kutali ndizoti ma Khulafaa Raashidoon komanso ma Swahaba ambiri anali kumwalira koma palibe yemwe anawaswalira swalaatul ghaaib, ndipo zikanakhala kuti zinkachitika, ndiye kuti zikanapitilira kukhala zodziwika mpaka lero lino. Zimenezo ndi kumbali ya munthu wina aliyense yemwe wamwalira.

Potengera mmene Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaswalira Al-Najaashiy, mfumu yaku Habasha yomwe inateteza Asilamu oyambilira kusamukira mdzikomo kuchokera ku Makkah, Asilamu lero lino ngati akufuna kuswalira munthu swalaatul ghaaib, akuyenera kutengera mmene anachitira Mtumiki salla Allah alaih wasallam powunikira mfundo izi:

  1. Munthuyo akhale kuti wamwalira kudziko kapena dera loti kulibe yemwe angamuswalire.
  2. Ngati anali wothandiza kwambiri mu community ya Chisilamu; monga kukhala kuti anali ‘Aalim wamkulu yemwe kudzera mmaphunziro ake apindula anthu ambiri, kapena kuti anali Imaam wamkulu yemwe anapindulitsa dziko lake pokhanzikitsa chiulungamo pakati pa anthu komanso analimbikitsa shariah, koamnso zina ndi zina zomwe zili zothandiza Asilamu. Zonsezi chitsanzo chake ndi monga mmene tadziwira Al-Najaashiy anapanga chani mumbiri ya Chisilamu kuti mpaka Mtumiki amuswalire iye ali ku kwina.

Kuchoka pamenepo, ma ulamaa ena anati choncho sakuyeneranso kwaswaliridwa wina wake swalaatul ghaaib pambuyo pa Al-Najaashiy. Pomwe ena anati ayi koma aswaliridwe opkhawo omwe ali ndi mbiri mChisilamu monga mmene talongosolera muja, potengera mmene anachitira Mtumiki pakumwalira kwa Al-Najaashiy; ndipo mfundo imeneyi ndiyomwe inatengedwa ndi maulamaa ambiri mpaka lero lino.

(Taqreer Ibn Baaz ‘alaa Muntaqal Akhbaar Hadith #1821-1825, Majmoo’ Fataawa ibn Baaz 13/158-160)

Tsopano pa zanyengo yomwe swalaatul Ghaaib ikuloledwa kuchitika, Imaam ibn Qudaama rahimahu Allah anati: Swalaatul Ghaaib ikuyenera kuimitsidwa pakadutsa mwezi, monga mmene kuswalira jeneza pamanda kukuyenera kuimitsidwa (pakutha pa mwezi). AlMughni vol.3/447

Allah ndiye Mwini kuweruza komanso Ndiye Mboni pa zomwe zili zoona.