Sulaiman analowa ufumu pambuyo pa imfa ya Dawud alaih salaam ndipo anapempha Allah kuti ampatse ufumu womwe sanayambe wapatsidwa wina aliyense mbuyomo. Allah anampatsa zofuna zake pamodzi ndi zina zambiri, monga kutha kuilamula mphepo, komanso anali kumva zilankhulo za mbalame ndi nyama.

Sulaiman analamulira mwanzeru ndipo anamanga nyumba zikuluzikulu zopempheleramo ndi zina zosiyanasiyana. Tsiku lina akuyenda ndi asilikali ake paulendo wa ku Askalon, akudutsa pa dambo lina nyerere inamva mapazi awo, ndipo inalengeza kwa anzake kuti athawire mnyumba zawo kuwopera kuti Sulaimana ndi asilikali ake angawaponde mosazindikira. Sulaiman anadabwa ataimva nyerere ija. Atazindikira zoti nyerere imadziwa kuti iye ndi Mneneri, anamuyamika Allah populumutsa miyoyo ya nyererezo.

Sulaiman alaih salaam anali ndi majinn ndi mbalame zomwe zimamugwilira ntchito. Iye anaziika mundondomeko yabwino ndipo zonse zimatsatira malamulo ake. Koma tsiku lina anazindikira kuti mbalame ina yotchedwa Hudhud sinapezeka pagulu lake. Posakhalitsa anawona ikubwera ndipo inamuuza kuti inatulukira malo omwe iyeyo sanali kuwadziwa, dera la Sabai lomwe linkalamulidwa ndi Mfumukazi dzina Bilquis. Bilquis ali ndi chirichonse komanso mpando wake unali wapamwamba zedi. Komatu ngakhale zinali choncho, iye ndi anthu ake ankapembedza dzuwa mmalo mwa Allah.

Pamenepo Sulaiman anafuna kuona ngati zomwe Hudhud amayankhula zinali zoona; iye anampatsa kalata kuti akapereke kwa Bilquis.

Hudhud anapititsa kalata ija ndipo anamuponyera Bilquis ndikubisala. Mfumukazi inatsegula kalata ndikuyamba kuwerenga. Mfumu Sulaimana anaiwuza mfumukazi kuti idzipereke kwa Allah Ta’la. Pamenepo Bilquis anasokonezeka mutu ndi uthenga uja ndipo anafunza nzeru kwa alangizi ake, omwe anayankha kuti iwo ntchito yawo ndiyoteteza mdzinda basi.

Kenako anaganiza zotumiza mphatso kwa Mfumu Sulaiman kuzera mwa atumiki a ku nyumba yachifumu. Anawalangiza kuti akafufuze bwinobwino mmene asilikali a Mfumu Sulaiman aliri.

Atumiki atafika kunyumba ya Mfumu Sulaiman, anapeza kuti Sabai sinali kanthu kuyerekeza ndi Mfumu Sulaiman. Anaona mikango, akambuku ndi mbalame zikuthandizira asilikali.

Atalowa mnyumba, anaona kuti simungafanane ndi nyumba ya Bilquis poti ngakhale pansi pake panali popangidwa ndi golide.

Sulaiman anazindikira kuti atumiki aja anabwera kudzatenga nkhani zokhunza ufumu wake. Koma atapereka mphatso yawo ija, asilikali anazizwa kuona mmene Sulaimana anachitira; iye anawauza kuti Allah anampatsa chuma chochuluka zedi pamwamba pa ufumu, komanso anampanga kukuhla Mneneri. Anawauza kuti asatsegule mpatso ija koma abwelere nayo kwa mfumukazi pamodzi ndi uthenga woti adzaononga dziko lake akapanda kulandira Chisilamu.

Atumiki aja atabwelera ndi mphatso ija, anaifotokozera mfumukazi za zodabwitsa zomwe anadziona kwa Sulaiman.

Mmalo modana nazo, anaganiza zomuyendera Mfumu Sulaiman. Iye anamuuza mmodzi wa atumiki ake kuti amudziwitse Sulaiman kuti akubwera kwawo.

Pamene Sulaiman anamva za kubwera kwa Mfumukazi, anaganiza zomuyesa; anawauza majinn omwe anali naye pafupi ngati mmodzi mwa iwo angabweretse mpando wachifumu wa Bilquis iye asanafike. Mmodzi mwa iwo anavomera ndipo anabweretsa mpandowo maso ake asanayang’ane pambuyo pa kuphethira. Sulaiman anaukhonza mpando uja motero kuti amuyese Bilquis ngati angavomwere kuti ndi mpando wakedi.

Atalowa mnyumba muja, analandiridwa mwansangala ndi chimwemwe, kenako Sulaiman anamufunsa ngati mpandowo unali wake. Iye anazizwa poona mpando wake uli kutsogolo kwake, anawuyang’ana kangapo kuti akhulupilire, ndipo anayankha kuti inde ukufanana ndi mpando wake, namuyamikira mmene anayankhira ndi nzeru.

Kenako anamutenga ku hall yaikulu yomwe pansi pake panayalidwa glass lolimba. Bilquis ataona anaganiza kuti ndi madzi, ndipo anayamba kukwezera dress lake kuwopera kuti lisagunde madzi, koma Sulaiman anamuuza kuti  asaope, limenelo ndi glass. Bilquis anadabwa kwambiri poti sanayambe waona zoterozo. Anadziwa kuti anali kunyumba ya munthu ozindikira kwambiri yemwe sanali mfumu wamba, koma analinso Mtumiki wa Allah.

Atabwelera ku Sabai, anazindikira kuti dzuwa lomwe wakhala akupembedza lija sikanthu koma cholengedwa cha Allah. Pamenepo analapa ndikusiya kupembedza dzuwa, komanso anawauza anthu ake kuti atero.

Sulaiman alaih salaam anakhala moyo wolemekezeka ndipo zolengedwa zonse zinali kumuvomera iye. Imfa yake inali yopatulika monga mmene unaliri moyo wake. Tsiku lina anakhala atagwirizira ndodo yake, uku akuyang’anira majinn akugwira ntchito. Iye anamwalira patadutsa nthawi yaitali ali chikhalire pampando, ndipo ma jinn anali kulimbikira kugwira ntchito poganiza kuti Mfumu Sulaiman anali kuwaonabe.

Tsiku lina chitswe chinayamba kudya ndodo ija mpaka inaduka ndikugwera pansi. Thupi la Sulaiman linali litayezamira kundodo ija kwanthawi yaitali ndipo pamene inagwa, naye anagwa pansi.