Gawo Loyamba:

Banja ndi chinthu chofunika kuchikhonzekera pambuyo pa imfa pamoyo wadziko lapansi, chifukwa banja:

1. Limakulowetsa mu chikhalidwe chatsopano chomwe umalidzire nacho moyo wapadziko.

2. Komanso banja ndi chinthu chomwe chimamukwaniritsira munthu half ina ya deen.

Choncho munthu yemwe akufuna kupeza zinthu ziwirizi, asanakwatire akuyenera kukhonzekera motere:

  • Kupewa kukhala pa relationship yamtundu uliwonse ndi mkazi kapena mwamuna.
  • Ngati wamukonda mkazi wina wake, asamufunsire iyeyo; koma atsate njira ya Chisilamu yomwe ndiyokhayo Allah amalowelerapo, ndipo amamuthandiza munthu kupeza mkazi woyenera, poti iye ndamene amadziwa bwino zamunthu kuposa mmene munthuyo amazidziwira yekha.
  • Ayezamire mwa Allah nthawi zonse polingalira za mkazi yemwe akumuganzira kuti angakhale naye pa banja; achulukitse kumupempha Allah kuzera mu Istikhaara komanso Istishaarah.

Istikhaara ndi Istishaarah ndi zinthu ziwiri zofunikira kwambiri kwa yemwe akufuna kukwatira kuti adzasangalale ndi banja lake moyo wonse. Zachisoni Asilamu lero tikuyenda ndi dziko lomwe likupangidwa control ndi shytwaan ndiye tikumatenga njira zake pofuna kukwatira/kukwatiwa. Timaganiza kuti popanda kupanga dating ndiye kuti banja silingalongosoke.

  • Apewe kuchita chirichonse cha haraam monga zibwenzi; ngati angamakhale ndi chilakolako koma mkazi omukwatira sakupezeka, azikakamize kugwira ntchito zomwe zingamuiwalitse zilakolako za mkazi, monga:

– Kusala – Kuswali ma nawaafil – Kuwerenga Qur’an ndi mabuku ena a deen – Kukhala ndikucheza ndi anthu olungama pa deen. Kuzikakamiza pakulimbana ndi zoipa zomwe mtima ukufuna ndi mtundu woyamba wa Jihaad.

عن عبد الله بن مسعودقال : قال لنا رسول الله صلى الله عليه وسلم يا معشر الشباب ، من استطاع منكم الباءة فليتزوج فإنه أغض للبصر ، وأحصن للفرج ، ومن لم يستطع فعليه بالصوم فإنه له وجاء

Hadith inachokera kwa Ibn Mas’ud radhia Allah anhu, anati: Mrumiki wa Alah salla Allah alaih wasallam anatiuza kuti”E inu achinyamata, yemwe angakwanitse kukhala ndi mkazi akwatire, chifukwa kutero ndikuzolika maso kwabwino komanso kusunga maliseche. Koma akapanda kukwanitsa, adzisala, chifukwa kutero ndi chitchingo (ku machimo) kwa iye

Dziwani kuti Allah amapereka mkazi wabwino kwa mwamuna wabwino ndipo amapereka mkazi oipa kwa mwamuna oipa. Iye sapondereza popereka zabwino kwa oipa kapena zoipa kwa wabwino. Izi akunena Mwiniwake kuti

الْخَبِيثَاتُ لِلْخَبِيثِينَ وَالْخَبِيثُونَ لِلْخَبِيثَاتِ ۖ وَالطَّيِّبَاتُ لِلطَّيِّبِينَ وَالطَّيِّبُونَ لِلطَّيِّبَاتِ ۚ أُولَئِكَ مُبَرَّءُونَ مِمَّا يَقُولُونَ ۖ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَرِزْقٌ كَرِيمٌ

“Akazi oipa ndi a amuna oipa, nawonso amuna oipa ndi a akazi oipa; ndipo akazi abwino ndi a amuna abwino, nawonso amuna abwino ndi a akazi abwino…”

Choncho ngati tikufuna kupeza zabwino zomwe Allah waakhonzera akapolo ake, tidzikhala ndi moyo wa ndondomeko yomwe imamusangalatsa Allah. Ngati munapanga tawbah ndikuyambiranso tchimo lomwe munapangira tawbah, ndiye kuti tawbah yanu sinali yolongosoka. Chifukwa popanga tawbah munthu umalumbira kuti sudzabwerezanso. Kulumbirako osangolimbira nkudzisiya mmanja mwa Allah, koma umayenera kukhala pa chintchito cholimbana ndi machimo aja komanso mayesero aliwonse omwe angakuyandikitseni ku tchimolo. Imeneyo ndi jihaad. Allah akunena kuti

وَلاَ تَقْرَبُواْ الزِّنَى

“Ndipo musachiwandikire chiwerewere” Kuyankhulitsana popanda chifukwa chovomerezeka ndi mkazi otheka kukwatirana naye ndiko kuchiwandikira chiwerewere… Tsopano ngati analetsa kuchiwandikira chabe, nanga kuchichita kuli ndi machimo ochuluka bwanji? Pangani tawbah yamphamvu komanso mokhulupirika ndipo mugwiritse ntchito njira zoyenera zopezera banja. Osachedwetsa nkupereka mpata kwa shaytwaan.

Werengani gawo lachiwiri >>