Ma ulamaa akuluakulu amakhulupilira kuti Shuaib alaih salaam anali munthu wachikulire yemwe anateteza Musa alaih salaam. Mneneri Musa alaih salaam anakwatira mwana wa Mneneri Shuaib alaih salaam asanapite ku Egypt. Koma palibe maumboni ovomereza kapena kutsutsa zimenezi. Komabe Qur’an ikutiuza kuti Mneneriyu anali ochokera ku Madian ndipo mmenemo ndi momwe Mneneri Musa alaih salaam anapeza chitetezo.

Anthu a ku Madian anali aluya omwe anali kukhala dziko la Maan, mbali ya dera lomwe likudziwika pakalipano kuti Syria. Anali anthu okanira Allah subhaanah wa Ta’la ndipo moyo wawo unali woipa. Ambiri mwaiwo anali akuba komanso achifwamba; anali kuchita chinyengo pakati pawo. Anali kulanda katundu wa anthu odutsa.

Anthu a ku Madian ambiri anali a malonda, anali kuchita chinyengo poyeza katundu wawo ndipo anali kuwabera ogula kudzera poyeza mulingo wabodza. Mmalo mopembedza Allah Mmodzi yekha, anali kupembedza mitengo. Ndipamene Allah subhaanah wa Ta’la anatumiza Mneneri wake kuti adzawaitanire anthu kupembedza Allah mmodzi yekha. Shuaib alaih salaam anawalalikira powakumbutsa maubwino a Allah ndikuwachenjeza kuopsa kwa zomwe anali kuchita. Koma anthu anamunyoza pomuuza kuti: “ukufuna ife tipembedze Mulungu yemwe ukupembedza? Ukufuna tisiye chipembedzo cha makolo athu? Ukufuna kuti tidzichita chilungamo pamalonda athu? Ukufuna tivutike chifukwa cha chilungamo?”

Pamene Mneneri anati: “inde”, anati: “Osatheka! Sitingakumvere iweyo. Tikanakugenda chipanda kjti ndiwe wamkulu komanso uli ndi ana” Anamuchenjeza chotero.

Koma Mneneri sanalabadire za chenjezo lija ndipo anapitiriza kuwalalikira anthu. Anawauza kuti asadane ndi chilungamo ndikukana kuitana kwa Allah. Anawakumbutsa za chilango chomwe Allah anatumiza kwa anthu a Lut alaih salaam.

Anthu a ku Madian ndi oyambilira kutenga misonkho ndi malipiro kuchokera kwa omwe anali kudutsa mdziko lawo.

Mneneri anayesetsa kuwalalikira kuti adzikhala ndi moyo wokhulupirika, koma anakakamira kuti adzikhala moyo wachinyengo ndikubera anthu. Mneneri sanataye mtima ndipo anawalalikira usana ndi usiku. Anawakumbutsa kuti iye anali kuchita zowapindulira iwo osati zompindulira iye. Anthu osakhulupilira aja anakwiya naye koopsa. Analanda katundu wa Mneneri ndi omutsatira ake ndipo anawathamangitsa mumzinda ndikuwauza kuti awalanga.

Tsopano Mneneri anataya chiyembekezo mwa anthu aja ndipo anabwelera kwa Mbuye wake kuti amuthandize. Pempho lake linayankhidwa mosakhalaitsa ndipo tsiku la chilango lidafika. Allah analipanga dzuwa kukhala lotentha kwambiri kwa anthu a ku Madian kwa masiku 7. Anthu anayesetsa kuziziziritsa ndi madzi koma sizinathandize ngakhale pang’ono ndipo anavutika kwa masiku 7. Zitsime zinauma ndipo mimera inafa. Kenako Allah anatumiza thambo lalikulu lakuda.

“Onani, mvula ikubwera!” anthu anatero ataona mitambo. Anaganiza kuti mitamboyo ibweretsa mvula ndikuchotsa kutentha kuja. Choncho anatuluka uku akusangalala poganiza kuti mitamboyo ndi ya mvula.

Sanadziwe kuti chimenecho nchinali chilango cha Allah kwa iwo. Anthu osakhulupilira onse anasonkhana, ndipo mosakhalitsa kunabwera phenzi zamoto kuchokera mmitambo muja. Zomwe zinapangitsa kuti nthaka igwedezeke kotero kuti anthu aja mmodzimmodzi anafa. Moto uja unawotcha anthu onse.

Pamene Mneneri anabwelera kumzinda kuja tsiku lotsatira, anapeza kuti panalibe yemwe anali wamoyo. Monga mmene analiri anthu a Thamud, onse anapezeka akufa, chimodzimodzi awa osakhulupilira onse anaonongedwa. Chuma chawo sichinawateteze ku chilango cha Allah.

Poona chinonongeko chija, Shuaib alaih salaam anati sanamve chisoni poti anali kulimbana ndi Allah ndipo anayesetsa kuwachenjeza  nthawi zambiri.

Mneneri Shuaib alaih salaam anakhala Mmadian kwazaka zambiri. Ameneyu ndi yemwe anapereka malo okhala kwa Mneneri Musa alaih salaam pamene anathawa kuchokera ku Egypt

Musa alaih salaam anathawa kuchokera ku Egypt. Anayenda masiku ambiri mu chigwa mpaka anakafika ku Madian. Mneneriyu anali ndi ludzu kotero anapita pa chitsime kuti akamwe madzi. Koma atafika pa chitsimepo, anapeza anthu ambiri akumwetsa ziweto zawo. Anaona atsikana awiri ataima pambali kudikira kuti atunge madzi.

“nchifukwa chani mwangoima pamenepa?” anawafunsa

“Sitingakwanitse kutunga madzi mpaka abusa atamaliza kumwetsa ziweto zawo.” Mmodzi wa iwo anatero. “Bambo athu ndi achikulire ndipo akutidikira kuti tiwatengere madzi” wina anatero.

Atamva izi, Mneneri anapita pachitsime ndikutenga chidebe cha m’busa. Aliyense anapereka mpata kwa Mneneri mpaka anatunga madzi ndikuwapatsa atsikana aja. Kenako Mneneri anapita kukakhala pansi pa mtengo.

Sipanadutse nthawi nkumatulukira mmodzi wa atsikana aja atapita kwawo nkubwelera, ndipo ananena kwa Mneneri uja: “Bambo anga akukuitana kuti akakulipire ntchito yomwe watigwilira” anamuuza. Anavomera ndikupita naye.

Mneneri Musa alaih salaam anakumana ndi Mneneri Shuaib alaih salaam ndikumuuza nkhani yake.

“Wapulumuka kuchokera kwa anthu oipa” Mneneri Shuaib anatero.

Pamenepo mmodzi wa ana ake akazi aja ananena kuti amulembe ntchito chifukwa anali wamphamvu ndi okhulupirika.

“Mwaona mphamvu zake pa chitsime” Mneneri anatero. “koma tsopano kukhulupirika kwake mukukudziwa bwanji?” anafunsa. Mwana uja anayankha: “Mmene timabwera kuno anatiuza kuti tidziyenda pambuyo pake, ndipo anati akuchokera komwe amuna samayang’ana akazi”

Mneneri Shuaib alaih salaam anali osangalala naye. Ndipo anamuuza kuti: “ndikufuna utakwatira mmodzi mwa ana angawa molingana ndi kundiyang’anira ziweto zanga kwa zaka 8”.

Mneneri Musa alaih salaam analola kukwatira Safoora , ndipo anayang’anira ziweto zija zaka 8 monga mwa pangano.