Swalaat Laylatul Qadr…??

Kuchokera mu Sahih Al Bukhari ndi Muslim, Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam anati:

“Yemwe waima kupemphera usiku wa Lailatul Qadr mwa chikhulupiliro (Imaan) komanso moyembekeza malipiro, amakhululukidwa machimo ake”

Kuima kupemphera usiku ndikofunika Mchisilamu ndinso kokondedwa, koma kuchitike potsatira njira yomwe anaika Mtumiki salla Allah alaih wasallam monga mmene ananenera mu Hadith yochokera kwa Ibn Umar radhai Allah anhu kuti: Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: 

“Swalaat ya usiku ndi (ma rakaat) awiriawiri, ndipo ngati mungaopere Subh, muswali rakah imodzi ngati witr ya zomwe mwaswali zija”

Amenewo ndiye mapempheredwe a usiku wa Lailatul Qadr, ndipo yemwe amakhulupilira kuti Lailatul Qadr ili ndi swalaat special, yomwe ndi Swalaat Lailatul Qadr, komanso ili ndi maswalidwe ake ake, ndithu ameneyo ali kutali ndi chiphunzitso cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndipo wagwera mu mchitidwe wa bid’ah.

Indetu, pali ma Shia komanso ma Sufi ena omwe amaphunzitsa kuti pali swalaat Lailatul Qadr! Kwa iwo imeneyo ndi swalat yomwe imayenera kuswalidwa mu usiku wa pa 27 Ramadhan mmaswalidwe osiyanasiyana, monga mmene akufotokozera  Imaam Abdul Hayy Allucknawi mu buku lake lotchedwa Al Aathaaril Marfoo’ah pge 115: akuti swalaat imeneyi ndi ya ma rakaat 12, mu rakaat iriyonse amawerenga Surah Al Faatihah kenako Surah Al Ikhlaas katatu, akamaliza kuwerenga amanena kuti Subhaana Allah wa Bihamdih Subhaana Allah Al Adhweem ka 100. Mu report lina, akuti amaswali ma rakaat 100 ndipo pa rakaat iriyonse amawerenga Surah Al Ikhlaas ka 5.

Kuchokera pa page 359 mpaka 360 mu buku lotchedwa الصلوات المبتدعة la Ahmad bun Abdul Aziz Al Jammaaz, momwe analongosola ma swalaat opeka okwana 150, ma swalaat omwe alibe chiyambi mu deen ya Allah subhaanah wa Ta’la ndipo Mtumiki wake salla Allah alaih wasallam sanaphunzitse. Komanso zikupezeka pa page 156 mu buku lotchedwa السنن والمبتدعات la Al Shuqairiyy.