Timamva kuti shaytwaan amamangidwa mwezi wa Ramadhan, kodi ruqya yochotsa ziwanda ndiyololedwa kupanga mwezi wa Ramadhan? Ngati zili zololedwa, ziwanda zingapezeke bwanji?
Ruqya ndiyololedwa kupanga nthawi iriyonse, tsiku lirilonse komanso mwezi uliwonse. Palibe kugwirizana kwa Ruqya ndi mwezi wa Ramadhan monga mmene ena amaganizira, amati poti shaytwaan wamangidwa ndiye kuti ruqya sitingamachite chifukwa Allah watitchinjiriza kale potimangira shaytwaan yemwe amabweretsa mavuto amenewa. Kumeneku ndi kuganiza kolakwika. Kumangidwa kwa shytwaan sikutanthauza kuti basi ma shaytwaan kulibiretu kotero kuti tikhonza kusiya zichitochito zomwe timayenera kuchita podzitchiriza ku shaytwaan. Komanso tidziwe kuti akamati Ruqya simokhamo mmene anthu ambiri amaganizira kuti Sheikh abwere kunyumba kwa yemwe akugwa majinn kapena yemwe ali ndi majinn kapena kuli ufiti, ndiye awerenge Qur’an ma aayah aja omwe ambiri tikuwadziwa aja. Ruqya si zokhazo ayi. Komanso munthu aliyense akuyenera kumadzichitira ruqya mamawa uliwonse, pogona paliponse chimodzimodzi nthawi zonse pamene ali bwino kapena wadwala nthenda iliyonse, osati ya ziwanda yokha. Tikhonza kubwelera ku thanthauzo la Ruqya mu audio #16 ya program yathu ya “Mgwirizano wa pakati pa munthu ndi ziwanda”, itanitsani audio pa Whatsapp 
Malinga ndi kuyankhula kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, jinn wachi shaytwaan amamangidwa mwezi wa Ramadhan; iyi ndi imodzi mwa ma Hadith ofunika kuwamvesetsa kwambiri pankhani ya shaytwaan, osati pamwambamwamba. Si ma shaytwaan onse omwe amamangidwa, ena amangochepetsedwa mphamvu ndipo samatha kukwaniritsa ntchito zawo monga mmene amakwaniritsira nthawi zina zonse. Mwachidule, sikuti ma shaytwaan amatheratu padziko, umboni wa izi timaona anthu ena akuchitabe machimo pomwe ali mu Ramadhan.
Ndiye ndizofunika kupitiriza kudzitchinjiriza ku shytwaan mwamphamvu mmwezi umenewu, komanso kudzichitira ndikuwachitira ana athu Ruqya, poti ndi pamene imakhala yopambana kwambiri kuposa myezi ina. Chifukwa chomwe chimapangitsa kufowoka kwa ma shytwaan, chimapangitsanso kuti Ruqya ikhale ndi mphamvu monga mmenenso ma ibaada ena amakhalira amphamvu. 
Ngati tingamadzichitire Ruqya nthawi iriyonse ndiye kuti pomatuluka mu Ramadhan ma shaytwaan tidzakhala tawagonjetseratu. Ngati amalephera kulowa kudikira kuti tidzamasule, adzapeza matupi athu atakutidwa ndi chitetezo cha Allah Ta’ala ndipo adzasowa polowera. Kupatula okhawo omwe amapanga zabwino mwezi wa Ramadhan wokha komanso samadziteteza potengera kuti basi shytwaan wamangidwa, sipadzakhala kusiyana kulikonse … poti adzakhala kuti abweleranso mwakale muja … kusala kwawo sikunapindule kwa iwo mbali imeneyi.
Odwala (nthenda iriyonse) mmwezi wa Ramadhan amakhala ndi mwayi waukulu pa kuchira (akawugwiritsa ntchito mwayiwo), chifukwa amenewa ndi masiku olemekezeka kwa Allah Ta’ala; masiku omwe Barakah imakhala pafupi, masiku oyankhidwa ma Dua mosavuta usana ndi usiku … Umenewu ndi mwezi umene kuopa, imaan komanso kukhanzikika kwa mtima kumakhala kwamphamvu kuposa masiku ena onse. Munthu amakhala akugwiritsa ntchito ma means onse a Dhikr yomwe Allah watsimikiza kuti imakhanzikitsa mtima, ponena kuti
ألا بذكر الله تطمئن القلوب.
Kuwerenga Qur’an ndi Dhikr yaikulu. Swalat ndi dhikr yaikulu … onsewa ndi ma ibaada opambana mwezi wa Ramadhan.
Mwezi uwu afiti (anthu omwe amagwiritsa ntchito shaytwaan) ndi ena onse omwe amagwira ntchito mu field imeneyi, ntchito zawo zimakhala zofowoka kwambiri poti ma shaytwaan awo akuluakulu omwe amawatumikirawo amakhala kuti mphamvu alibe pamunthu yemwe akudzitchinjiriza – choncho Qur’an, ma Adhkaar ndi ma Dua zimakhala kuti zikulowa mwamphamvu, zonyansa zonse zimaonongeka munthu akagwiritsa ntchito mwayi umenewu. Tsopano anthu awo omwe amapezeka kuti akupitirizabe za ushaytwaan mmwezi wa Ramadhan, akugonana ndi zibwenzi usiku poganiza kuti kutero sikuononga swawm, asatipatse maganizo komanso mafunso oti pamenepa zimakhala bwanji poti iyi ndi ntchito ya u shaytwaan ,,, asatibweretse chikaiko mmitima mwathu chifukwa amenewo ndi omwe amamukonda shytwaan nthawi zonse ngakhale kunja kwa swawm…amenewo ndi aja omwe shytwaan akuwadikira, iwonso akumudikira kuti mwezi ukatha apitirie kupanga naye cooperatee ponyoza malamulo a Allah Subhaanah wa Ta’ala. 
Ndiye ndikumamva ena akumayankha mafunso nkumawauza anthu motsimikiza kuti “kugonana usiku wa Ramadhan ndi mkazi oti sunapange naye nikaah palibe vuto lina lirilonse .. koma wapeza machimo a double sikuti waononga swawm yako” Allah atimvere chisoni ndithu. Kodi swawm yakeyop ngati siikumuletsa machimo; akumasala masana koma akamasula iftaar yake ikumakhala zinaa, pamenepo tiwapange encourage kuti adzipanga palibe vuto? Werengani zambiri pa nkhaniyi kapenso mutha kuitanitsa audio pa Whatsapp
Choncho ndibwino kwambiri kupitiriza kupanga ruqya, kudzitchinjiriza kwa shytwaan, kuwerenga Qur’an tsiku lironse ndikuchulukitsa ma twaa’aat mmwezi umenewu; zimenezo ndizomwe zingatithandize kupewa shytwaan, osati kungokhala kuti basi shytwaan ali mundede. Tipange zotheka kuti potuluka mwezi umenewu tikhale ngati tabadwa mwatsopano; ndipo ntchito zabwino zomwe tikuchitazi tisadzasiye chifukwa chakutha kwa mwezi wa Ramadhan. Ngati swawm yathu ikulongosoka, ngati swalaat ndi ntchito zonse zabwino zikuyenda ndi niyyah yabwino ,,, ngati kuwerenga Qur’an, kupanga ma adhkaar, kutalikirana ndi anthu omwe amatha kutikhotetsera nthawi zina kuzachabe kudzapitilira pambuyo pa mwezi wa Ramadhan; ma shaytwaan kudzakhala kovuta kuti atiseweretsenso.
Allah atiteteze ku mayesero a shytwaan ndi anthu.