Pali ma hadith omwe anapekedwa nalembedwa mu buku kuti tidziwerenga poikira umboni kuti kuwerenga Qur’an ku Manda ndi Sunnah. Ma hadith amenewa ndi osafunika kuti tidziwagwiritsa ntchito tikawaona. Chifukwa ndi ma hadith oipa omwe amanamizira Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Mtumiki analetsa kumunamizira ndipo kuopsa kwakutero ndi moto.
Mu book la Alfawaaidul Majmoo’ah,  analongosola za kuipa kwa ma Hadith awa: “yemwe angayendere manda a makolo ake awiri Tsiku la Chisanu amakhululukidwa”.
Ndipo mu chain cha opeka omwewo, ena ananena kuti Mtumiki anati: “yemwe angayendere manda a makolo ake, malume ake, azakhali ake, kapena m’bale wake, amalembedwa ngati wapanga hajj”
Ndiye kuti ngakhale osapita ku hajj, kungokayendera manda a achibale basi? Ena amati mwezi wa Dhul Hijja ukafika amachulukitsa kuyendera manda nkumakawerenga Qur’an, potsatira ma hadith amenewa,  Komanso ena ndi nthawi imene amachulutsa sadaqa,  kulima ku manda etc,  koma zonsezi sizovomerezeka.  Ku manda osaika nthawi kuti ya hajj yokha. Ukhondo ndi nthawi iliyonse.
Komanso hadith ina akuti “yemwe angayendere manda a makolo ake kapena amodzi mwa iwo Tsiku la chisanu, adzakhululukidwa”. Koma anthu saapha nazo makolo awo kuti adzawayendere kumanada kuti adzakhululukidwe machimo onse?
Yemwe anatulutsa hadith imeneyi anakambidwapo ndi Imam Ahmad rahimahu-Allah kuti ankapeka ma hadith,  choncho hadith imeneyi komanso ma hadith ena ofanana nayo ndi opeka chifukwa choti samapezeka ndi chain chovomerezeka kukafika kwa Mtumiki.
Hadith imeneyi anaipeka anthu opeka pambuyo pokhala ndi chizolowezi choyendera ku manda tsiku la Jum’ah, ndipo anaona kuti ntchito yabwino yomwe angamakagwire kumandako ndi kuwerenga Qur’an, choncho anaganiza zolimbikitsa chikhalidwechi ndi hadith.  Koma poti hadithiyo panalibe,  n’chifukwa chake anangopeka. Kumunamizira Mtumiki.
Kodi nanga mwini chitabu chimene mukupezeka ma hadith amenewa ndi ndani? Nanga chitabu chake ndi chiti?
Sheikh Ahmad bun Ibrahim alHashimi           Yemwe anabadwira ku Egypt ndipo anakhala mzaka za pakati 1878 – 1943. Ndipo ndi mmodzi wa ma sheikh a nthawi imeneyo, analemba mabuku ake angapo,  limodzi mwa iwo ndi momwe mukupezeka ma hadith opeka ambiri lotchedwa Mukhtaarul Ahaadith Al Nabawiyyah wal Hikamul Muhammadiyyah.
Ma hadith omwe ndawatchula mu nkhaniyi akupezeka mchitabu chimenecho.