Allah Ta’la amayandikira (ndi ulemelero wake) usiku uliwonse pa thambo la dziko lapansi, ndipo amaitana: “kodi alipo yemwe akundipempha ndimuyankhe? nanga alipo yemwe akupempha chikhululuko ndimukhululukire? kodi alipo yemwe akufuna kulapa machimo ake ndimulandire kubwelera kwake?”. Amakhala akuitana choncho mpaka kutuluka kwa Al Fajr (mamawa).
Yemwe ali wofunisitsa chikhululuko, kuyankhidwa ma dua ake, ndamene amauchita usiku kukhala nthawi yake yolumikizana ndi Allah.
Pomwe wosayamika komanso wokonda kupanga complain zomwe akudzimana yekha, amakhala akuwanamiza anthu komanso kudzinamiza yekha kuti amamukonda Allah komanso amakhala ndi imaan pa iye … koma ukangolowa usiku amagona chitulo chofa nacho, kumugonera Mbuye wake yemwe akumuitana kuti ampatse zomwe akulakalaka mmoyo mwake! Kodi ngati umamukonda okondedwa wako ungamusiye pamene akuitana kuti akupatse zabwino iwe nkumangogona?
Allah Ta’la amakukonda kwambiri kuposa mmene iwe umadzikondera wekha … ndipo iye safuna kalikonse kuchokera kwa iwe koma iweyo ndamene umasaukira chilichonse kuchokera kwa Iye, nchifukwa chake samakuiwala; usiku uliwonse amakufikira chifupi pamene suli otangwanika ndi za dziko .. amakufikira kuti umutulire nkhawa zako zonse, akusinthire madandaulo kukhala chisangalalo. Komatu pamenepo iwe mpamene ukudzikutira bulangeti lako mpaka kumkhope! Kukacha nkumawadandaulira anthu za moyo wako, anthu omwe sangakuthandize kalikonse. 
Dzuka ndipo panga wudhu uswali at least ma rakaat awiri umupemphe akukhululukire, akupatse madalitso pa ntchito kapena business yako, akulandire ibaada yako ndikukufewetsera moyo wako!
Mwezi uno wa Ramadhan mwayi ndi waukulu usana ndi usiku 24/7 pamene kalikonse komwe ungachite kakukuyandikitsa kwa Allah. Koma iwe munthu mkusayamika kwako, ukulekelera mwayi ukudutse, kumachita kuona kuchedwa “Eid ibwere timasule tidye masana!” 
وَقَلِيلُ مِنْ عِبَادِيَ الشَّكُورُ
“Ndi ochepa mwa akapolo anga omwe ali oyamika”
Munthu akanadziwa maubwino amene akupezeka m’mwezi umenewu, akanalakalaka Ramadhan itakhala chaka chonse.
Palibe chomwe chingamuletse munthu kupemphera mkati mwausiku kuposa mtima wake womwe wakutidwa ndi machimo ake. Munthu wina anadandaula kwa Abdullah bun Mas’ud radhia Allah anhu kuti: “ife sitimakwanitsa kupemphera usiku” Iye anati: “ndithu akukhalirani machimo anu”. 
Wina anati: “Machimo anu akumangani kuti musapemphere.”
Al Fudhail anati: “Ngati sukukwanitsa kuimika mapemphero usiku ndi kusala masana, dziwa kuti machimo ako akumanga.” wadzadza ndi machimo ofunika uchitepo kanthu.
Tipemphe Allah atichitire Chisoni ndikutilimbitsa imaan yathu