Funso: 

Ma Sheikh ena akaitanidwa kuti athandize odwala amabwera awiri, ndipo mmodzi akamasomera odwalayo winayo amakhala pambalipa ndikumaonetsa ma action ena ake, monga kumangoyasamula, kumangoziongola basi manjawa kumapanga zinazake, mkumakhala ngati akumunong’oneza odwalayo zosamveka koma. Koma zonsezi amapanga atasidzina. Kodi zimenezi zilibe vuto?

Kutamandidwa konse nkwa Allah Mbuye wa zooengedwa zonse, Mtendere ndi madalitso zipite kwa Mtumiki wake. 

Zili ndi vuto lalikulu zimenezo. Mmachiritso a Shariah mulibe zichitochito zoterozo. Kuyankhula zosamveka popanga ruqya ndi zoletsedwa chifukwa zikhonza kukhala kuti akulumikizananso ndi ziwanda.
Ruqya amapanga munthu mmodzi osati awiri.Ngati angafunike wachiwiri akhale othandizira zina monga kumugwira odwalayo pamene akusunthasuntha mkati mwa ruqya, ndipo ngati ali wamkazi zingakhale bwino othandizirayo kukhala mkazi, m’bale wake, kapena mwamuna wake. Koma osati izo momwe mwakambiramo.

Opanga ruqya asakhale yekhayekha ndi odwala, koma akuyenera kupezekapo achibale a munthu odwalayo, monga mwamuna wake kapena abale ake ena. 

Funso: Ndiyeno pamenepopo ziwandazo sizimachoka?

Ngakhale zitamtheka kuchoka koma zichitochito zimenezo sizili mu Ruqya ya Sharia. Adzipanga ruqya kuchokera mu chiphunzitso cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam osaonjezera zosamveka matanthauzo
Ziwanda ngakhale kwa asing’anga zimatha kuchoka, ngakhale mmatalasimu zimatha kuchoka. Koma sizikutanthauza kuti njira zimenezo ndi zololedwa.

Allah ndiye Mwini kudziwa Konse