بسم الله الرحمن الرحيم

ٱلْيَوْمَ أُحِلَّ لَكُمُ ٱلطَّيِّبَٰتُۖ وَطَعَامُ ٱلَّذِينَ أُوتُوا۟ ٱلْكِتَٰبَ حِلٌّ لَّكُمْ وَطَعَامُكُمْ حِلٌّ لَّهُمْۖ وَٱلْمُحْصَنَٰتُ مِنَ ٱلْمُؤْمِنَٰتِ وَٱلْمُحْصَنَٰتُ مِنَ ٱلَّذِينَ أُوتُوا۟ ٱلْكِتَٰبَ مِن قَبْلِكُمْ إِذَآ ءَاتَيْتُمُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ مُحْصِنِينَ غَيْرَ مُسَٰفِحِينَ وَلَا مُتَّخِذِىٓ أَخْدَانٍۗ وَمَن يَكْفُرْ بِٱلْإِيمَٰنِ فَقَدْ حَبِطَ عَمَلُهُۥ وَهُوَ فِى ٱلْءَاخِرَةِ مِنَ ٱلْخَٰسِرِينَ

“Lero mwalolezedwa zonse zabwino ndi chakudya cha omwe adapatsidwa buku nchololedwa kwa inu, ndiponso chakudya chanu nchololedwa kwa iwo ndipo (mukuloledwa kukwatira) akazi abwino a mwa  Asilamu ndi akazi abwino a mwa omwe adapatsidwa mabuku kale, ngati mwawapatsa chiwongo chawo mnjira yomanga nawo ukwati, osati mochita chiwerewere, osatinso mochita zibwenzi. Ndipo amene akane kukhulupilira ndiye kuti yaonongeka ntchito yake; ndipo iye tsiku lomaliza adzakhala mwa oluza” 5:5

Mu aayah iyi tikutolamo izi:

  1. Zonse zomwe zili zabwino nzololezedwa kwa ife, ndipo zoipa zones ndi zoletsedwa.
  2. Chakudya cha anthu omwe anapatsidwa buku nchololedwa, komanso chakudya chathu nchololedwa kwa iwo.
  3. Tikuloledwa kukwatira akazi abwino mwa Asilamu, komanso akazi abwino mwa amene adapatsidwa mabuku kale.
  4. Tikuletsedwanso kungotengana nkumati takwatira, kapena kumangochita nawo zibwenzi.

Tikapita mu ndemanga ya Qur’an yotanthauzidwa Mchichewa ndi Sheikh Khalid Ibrahim, nkololedwa kwa mwamuna wa Chisilamu kukwatira mkazi wa Chiyuda komanso mkazi wa Chikristu ngati makolo awo adali Ayuda kapena Akristu munthawi ya umbuli (Mtumiki salla Allah alaih wasallam asanalandire Utumiki). Koma awa a mission omwe alowa chikristu posachedwapa nkosaloledwa kuwakwatira pokhapokha atayamba alowa Chisilamu…

Ena amaganiza kuti surah Al Baqarah 221 ikutsutsana ndi Surah Al Maaida aayah 5, haasha Lillah! Qur’an simadzitsutsa yokha, koma ifeyo ndamene timafunika kumvesetsa.

Aaya yoletsa kukwatira mushrik ija ikunena awo amene amaphatikiza Allah ndi zinthu zina. Pomwe aayah yololeza Ayuda ndi Akristuyi ikunena za okhulupirila kuti (Allah ndi mmodzi)  odzisunga (posachita chiwerewere)  mwa anthu omwe anapatsidwa mabuku (Akristu ndi Ayuda), osati a shirk.

Tingobwelera mbuyo kaye, Ayuda ndi Akristu ndi amene anapatsidwa mabuku (Tauraat ndi Injeel) kuzera mwa Musa ndi Isa alaihima Salaam, ndipo anali okhulupilira ndithu osati ma mushrik.

Choncho akamati “mpaka atakhulupilira” tikudziwa kuti kukhulupilira kuti:

– Allah ndi mmodzi, Muhammad salla Allah alaih wasallam ndi Mthenga wake.

– Akhulupilirenso Atumiki onse komanso kuti Isa ndi Mtumiki osati mwana kapena mulungu,

– Akhulupilire mabuku onse amene anatumizidwa kwa Aneneri

– Akhulupilire Angelo

– Akhulupilire Tsiku lomaliza

– Akhulupilire kuti zabwino ndi zoipa zimachokera m’chikhonzero cha Allah.

Mwachidule, zimenezo ndi zimene aayah ija ikukamba pa chikhulupiliro. Komanso mabuku onse anayi ndi Atumiki onse omwe anatumizidwa kwa Ayuda ndi Akristu, anali kuitanira ku chikhulupiliro chimenecho, ndipo ankaletsa shirk.

Tsopano aayah yomwe akunena kuti: “zili halal kukwatira Ayuda ndi Akristu…” akutanthauza Ayuda ndi Akristu omwe akhulupilira zomwe ndalongosola zija monga mmene zinatumuziridwa kwa iwo mabuku mwawo. Komanso odzisunga…

Ndiye ngati tingampeze mkazi kapena mwamuna wachikunja yemwe ali ndi chikhulupiliro chimenecho,  timtenge ndithu.

Funso nkumati: Koma aliposo ayuda ndi akhristu okhulupilira kuti Yesu ndi Mtumiki wa Allah osati mwana wake kapena Mulungu amene? Komanso zoti Muhammad ndi Mtumiki wa Alla?

Palibe oterowo masiku ano, ndipo akangopezeka oteroyo ndiye kuti ndi Msilamu basi.

N’chifukwa chake timati munthu asatenge Mkristu nkumusiya osamulowetsa Chisilamu chifukwa cha aayah yololeza ahlul kitaab. Ahlul kitaab omwe aayayo ikukamba panopa sakupezeka.

Muonenso tafsir ya aayah 221 mu Al Baqarah, komanso aayah 5 Surah Al Maidah.

Kapena ndemanga za ma aayahwa mu Qur’an yotanthauzidwa  mChichewa.

Allah Ndi Mwini Akudziwa Konse