Qur’an Yolemekezeka yatchula munthu mmodzimmodzi momveka bwino, omwe omwe sali oyenera kumanga nawo banja.

Anthu amenewa ndi awa:
حُرِّمَتْ عَلَيْكُمْ أُمَّهَاتُكُمْ وَبَنَاتُكُمْ وَأَخَوَاتُكُمْ وَعَمَّاتُكُمْ وَخَالاَتُكُمْ وَبَنَاتُ الأَخِ وَبَنَاتُ الأُخْتِ وَأُمَّهَاتُكُمُ اللاَّتِي أَرْضَعْنَكُمْ وَأَخَوَاتُكُم مِّنَ الرَّضَاعَةِ وَأُمَّهَاتُ نِسَآئِكُمْ وَرَبَائِبُكُمُ اللاَّتِي فِي حُجُورِكُم مِّن نِّسَآئِكُمُ اللاَّتِي دَخَلْتُم بِهِنَّ فَإِن لَّمْ تَكُونُواْ دَخَلْتُم بِهِنَّ فَلاَ جُنَاحَ عَلَيْكُمْ وَحَلاَئِلُ أَبْنَائِكُمُ الَّذِينَ مِنْ أَصْلاَبِكُمْ وَأَن تَجْمَعُواْ بَيْنَ الأُخْتَيْنِ إَلاَّ مَا قَدْ سَلَفَ إِنَّ اللّهَ كَانَ غَفُوراً رَّحِيما

Kwaletsedwa kwainu kukwatira:
 • Amayi anu,
 • ana anu,
 • alongo anu,
 • azakhali anu,
 • amayi anu aang’ono kapena aakulu,
 • ana achikazi a m’bale wanu,
 • ana achikazi a mlongo wanu,
 • amayi anu amene adakuyamwitsani,
 • alongo anu oberekedwa ndi amene adakuyamwitsanipo.
 • mayi a akazi anu, 
 • ana achikazi owapeza amene mukuwasunga woberekedwa ndi akazi anu omwe mwalowana nawo. Koma ngati simudalowane nawo, nkosaletsedwa kwa inu kukwatira amayi awowo;
 • akazi a ana amuna omwe ngochokera kumisana yanu,
 • ndiponso nkoletsedwa kwa inu kukwatira mophatikiza mkazi ndi mchemwali wake obadwa naye, kupatula zomwe zidapita.
Ndithudi Allah ngokhululuka kwambiri ngwachisoni zedi. (Surat Al Nisaai, Aayah 23)

Allah Ta’la waletsanso Msilamu wa mwamuna kukwatira mkazi wosakhulupilira (mushrik), kapena kholo la Chisilamu kukwatitsa mwana wamkazi kwa munthu osakhulupilira

Sikololedwa Msilamu okhulupilira wamwamuna kapena wamkazi kupanga ubale wa banja ndi munthu osakhulupilira. Izi ndizoletsedwa mu chiphunzitso cha chi Islam monga momwe Allah akunenera kuti:
وَلاَ تَنكِحُواْ الْمُشْرِكَاتِ حَتَّى يُؤْمِنَّ وَلأَمَةٌ مُّؤْمِنَةٌ خَيْرٌ مِّن مُّشْرِكَةٍ وَلَوْ أَعْجَبَتْكُمْ وَلاَ تُنكِحُواْ الْمُشِرِكِينَ حَتَّى يُؤْمِنُواْ وَلَعَبْدٌ مُّؤْمِنٌ خَيْرٌ مِّن مُّشْرِكٍ وَلَوْ أَعْجَبَكُمْ أُوْلَـئِكَ يَدْعُونَ إِلَى النَّارِ وَاللّهُ يَدْعُوَ إِلَى الْجَنَّةِ وَالْمَغْفِرَةِ …

“Ndipo musakwatire akazi opembedza Mafano (mushrikah) Mpaka atakhulupirira. Ndithudi, mdzakazi Wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa Mfulu yachikazi yosakhulupirira, Ngakhale itakukondweretsani. (Ndipo ana anu aakazi a Chisilamu) Musawakwatitse kwa amuna Osakhulupirira, opembedza ma fano (ma mushrik), mpaka  akhulupirire. Ndipo kapolo wokhulupirira (Allah) Ngwabwino kuposa mfulu yosakhulupirira, Ngakhale ikukukondweretsani. Iwowo akuitanira kumoto. Koma Allah akuitanira kumunda Wamtendere…”

Surat Al Baqarah, Aayah 221

Mushrik ndi munthu yemwe amapembedza mafano, monga myala, zosema komanso zina zirizonse zomwe siziri Allah. Ndipo ngati Msilamu akwatira mushrik, ndiye kuti adzachulukitsa shirk pa dziko la pansi. Komanso ngati Msilamu wamkazi akwatitsidwa ndi mushrik, adzachulukitsa shirk pa dziko lapansi. Izi nchifukwa chake ziri zoletsedwa kutero.