Kuchokera mu buku:
“Ighaathatu Llahafaan min Maswaaid Shaytan”
Lolembedwa ndi Ibn AlQayyim AlJawziy

Nkhani ya nyimbo inali yomveka kalekale pamene kunalibe zomwe zikuchitika masiku ano. Ngakhale zili zomveka kuti nyimbo zogwiritsa ntchito zida ndi haraam, mpovuta kuti pakali pano munthu amvesetse chifukwa choti ana akubadwa nkuwapeza anthu akumvera, kuimba ndi kuvina nyimbozo mu zochitika za Chisilamu. Ndipo  nyimbozo nzimene zimakometsa miyoyo ya anthu masiku ano. Oimba adzisandutsa kukhala njira yolalikira za Deen, kuti zikhale ngati halal.
Koma izi si zachilendo, chifukwa ndi zochokera kwa shaytan kuyambira pamene ananena kwa Allah pambuyo pa kumulola kuti adzakhala pa dziko la pansi mpaka tsiku la Qiyaamah:
قَالَ رَبِّ بِمَا أَغْوَيْتَنِي لأُزَيِّنَنَّ لَهُمْ فِي الأَرْضِ وَلأُغْوِيَنَّهُمْ أَجْمَعِينَ
“(Satana) adati: “Mbuye wanga! Pakuti mwanena kuti ndine wosokera, choncho ndikawakometsera za m’dziko (kufikira kuti akakulakwireni) ndithu, ndikawasokeretsa onse,” Surah Al Hijr 39.
Kodi mumaganiza kuti mmene Shytwaan amapempha kuti adzakhale mpaka Tsiku la Qiyaamah, ntchito yake pa dziko pano ndi yotani? Phindu lake kwa iyeyo ndi lotani?
Cholinga chake amafuna adzagwire ntchito yosocheretsa akapolo a Allah mmoyo wake onse. Ndiye ndi ntchito yomwe akugwira panopa.
Nyimbo zogwiritsa ntchito ma instruments:
Ndikamba mwachidule kwambiri poti nkhaniyi inatambasulidwa momveka kale koma anthufe kukometseredwa ndi shaytan nkumene kumapangitsa kuti tidzikokerakokera za haraam kuti mpaka  zikhale halaal chifukwa choti tikudzikonda. Dziwani kuti kukonda chinthu cha haraam sikumapangitsa kuti chikhale halaal – mtima umakonda zirizonse. Koma zokhazo zomwe zinalolezedwa ndi zomwe zinaletsedwa ndi zomwe ife tikuyenera kudzitengera mmene ziliri.
ZOFUNIKA KWAMBIRI: Zomwe ndikulembazi mulibemo maganizo anga. Ndangotanthauzira kuchokera mu chi Arab kuchokera mu buku la “Ighaathatu Llahafaan min Maswaaid Shaytan” lolembedwa ndi Ibn AlQayyim alJawziy, lafotokoza za kuletsedwa kwa nyimbo momveka.
Kuimba pogwiritsa ntchito musical instruments kapena kumvera nyimbozo ndi HARAAM. Palibenso debate pankhaniyi. Mu Qur’an Surah Luqman Aayah 6-7 malinga ndi tafseer za ma Sahaba akuluakulu opanda chikaikitso monga Ibn Mas’ud, Ibn Abbas ndi Ibn Umar anati aayah imeneyi ikukamba za nyimbo chifukwa mau oti “Lahwul hadith” akutanthauza sound kapena mau a masewera.
وَمِنَ النَّاسِ مَن يَشْتَرِي لَهْوَ الْحَدِيثِ لِيُضِلَّ عَن سَبِيلِ اللَّهِ بِغَيْرِ عِلْمٍ وَيَتَّخِذَهَا هُزُواً أُولَئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ مُّهِينٌ{6} وَإِذَا تُتْلَى عَلَيْهِ آيَاتُنَا وَلَّى مُسْتَكْبِراً كَأَن لَّمْ يَسْمَعْهَا كَأَنَّ فِي أُذُنَيْهِ وَقْراً فَبَشِّرْهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٍ
“Koma alipo ena mwa anthu amene akusankha nkhani ya bodza (ndi kumaifotokoza kwa anthu) ndi cholinga choti awasokeretse ku njira ya Mulungu. Popanda kuzindikira. Ndipo akuichitira zachipongwe (njira ya Mulunguyi), iwo adzapeza chilango chowasambula.” 
Mu Qur’an Surah Al Israai Aayah 63-64, mau onena kuti
 …وَاسْتَفْزِزْ مَنِ اسْتَطَعْتَ مِنْهُمْ بِصَوْتِكَ
“Ndipo apusitse (iwe shaytan Iblees) amene ungawathe mwa iwo ndi MAWU AKO…”
Potambasula tanthauzo la Aayahyi, Mujaahid rahimahu-Allah anati: “mau a shaytan ndi musical instruments: ndipo Murrah anati: “mau a shaytan ndi monga kulira kwa flute, reedpipe, ndi zina zotero (musical instruments)”
Ibn Abbas radhia Allah anhu anati “mawu a shaytan ndi zomveka zomwe zimalondolera ku machimo” ndipo no doubt kuti musical instruments zimalondoloera ku machimo mwa pang’ono pang’ono.
Mu Hadith yochokera kwa Abi Umamah radhia Allah anhu, polongosola za kugula za masewera monga mmene Aayah yoyamba ija yakambira, Mtumiki salla Allah alaih wasallam analetsa kupanga hire akazi oimba, anati:
“Musagulitse kapena kugula mkazi oimba (songstress) ndipo musaphunzitse atsikana kuimba, chifukwa mu business imeneyi mulibe zabwino…” chimodzimodzi zida zoimbira.
Palibenso kunena kuti poti ine ndimatsatira madh’hab akuti akuti ndiye ndidzimvera nyimbo, chifukwa pa Hadith imeneyi, madh’hab onse anayi ananeza zoletsa nyimbo:
IMAM MAALIKI (Maalikiy) rahimahu-Allah analetsa kumvera nyimbo ponena kuti: “amati munthu akagula mzakazi nkumupeza kuti ndi oimba, anali kum’bweza chifukwa cha vuto la kuimbako”. Ndipo atafunsidwa Imam Maliki pa zomwe zimalolezedwa kwa anthu a ku Madina pa nyimbo, anati: “Ndithu kuimbako kumachitidwa ndi anthu otuluka mmalamulo a Mulungu”
IMAM ABU HANIFA (Hanafiy) rahimahu-Allah ananena kuti ndi tchimo kuimba, ndipo analesa kumvera nyimbo zonse even za duf kapena zoyerekeza ndi pakamwa zija, chifukwa kugwiritsa ntchito pakamwa posakhala kutulutsa mau omveka, kumatanthauza kuti akupanga imitate chida china chake.
IMAM SHAFI’ (Shaafi’y) rahimahu-Allah ananena mu buku lake “Adabu alQadhaai” kuti: “ndithu nyimbo ndi masewera omwe ali makrooh ndipo yemwe amamvera kapena kuimba, sitikuyenera kulandira umboni wake pa chinthu chifukwa ndi safiih” Kusonyeza kuti Msilamu sakuyenera kumaimba kapena kumvera zoimbidwa ndi zida. Makrooh ndi zosafunikira/zonyansa mu Chipembedzo.
IMAM AHMAD (Hanbaliy) rahimahu-Allah anati: Abdullah anafunsa bambo ake za nyimbo ndipo anati: “Nyimbo zimayambitsa nifaaq (hypocrisy) mumtima ndipo sizimandisangalatsa” kenako ananena mau omwe ananena Imam Maliki: “Ndithu kuimbako kumachitidwa ndi anthu otuluka mmalamulo a Mulungu”
Mu Hadith yochokera kwa Abi alAsh’ariy radhia Allah anhu, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “idzafika nthawi mu Ummah wanga anthu adzapanga zovala za silk, mowa, ndi ma MUSICAL INSTRUMENTS KUKHALA HALAL….” Sahih AlBukhari 5590.
Hadith imeneyi ndi umboni wokwanira kuti MTUMIKI salla Allah alaih wasallam ANALETSA MA MUSICAL INSTRUMENTS chifukwa anawatchula direct, polongosolapo pali indication yoti ma instrument (nthawi ya Mtumiki) anali HARAAM ndipo anawauza anthu kuti zimenezi ndi haraam koma idzafika nthawi mu ummah womwewu ena adzazipanga kukhala halal. Ndiye ndi zomwe tikudzionazitu. Ma sheikh akutulutsa ma fatwa opindika kufuna kusangalatsa zofuna zawo.
Mu Hadith yochokera kwa alBazzar, Anas (ra) anati Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “mau (ma sound) awiri omwe ali otembeleredwa pa dziko lapansi komanso ku aakhirah:
(1) Musical instruments panthawi ya mtendere (yosangalala).
(2) Zolira pa nthawi ya mavuto.”
Komanso anati: “Ine sindinaletse kulira, koma ndaletsa mawu (ma sound) awiri oipa: sound yomwe imatuluka panthawi ya mtendere, posewera komanso pazisangalalo, imeneyo ndi sound ya shaytan (musical instruments), mawu omwe amatuluka pa nthawi ya mavuto (maliro) pamene anthu amadzimenya kunkhope…”
Mu Hadith ina yomwe ikupezeka mmabuku a Imam Ahmad, alTirmidhi, alBaihaqi, ibn Habbaan ndi Tabari ndipo inachokera kwa ibn Abbas, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Ndithu Allah anandiletsa ine mowa, juga, ng’oma ndi zolezeretsa zonse”. Ng’oma ndi chimodzi mwa ma musical instruments ndipo ndi yoletsedwa.
Ma musical instruments onse ndi ma sound a shaytan, ndipo ma shaytan akamva kulira kwa zimenezi, amasonkhana nkumavina. Allah akanakhala kuti amamuonetsa munthu mmene asatana amapangira pamene musical instruments zikulira, akanakomoka chifukwa cha mantha.
Koma chifukwa choti sitimaona ndi maso athu, zimangotifika mma feelings nkumamva kusangalatsa koma zinthu zopanda pake zosamveka matanthauzo. Kusangalatsa kumeneku, zinthu zoti nzopanda uthenga uliwonse, zopanda mawu ngakhlae tanthauzo, kumabwera chifukwa cha kuchuluka kwa ma shaytan omwe amasonkhana pa malopo.
Mnyumba kapena malo omwe nyimbo zoterezi zikulira, Angelo obweretsa madalitso amachokapo ndipo amabwera ma shaytan.
Inu simukuona kuti satanic yafalikira mu anthu oimba nyimbo? Komanso munthu ngati ukufuna kuti mnyumba mwako musalowe shaytwaan udziwerengamo Surat Al Baqara malinga ndi hadith:
إن الشيطان تنفر من البيت الذي تقرأ فيه سورة البقرة
*Ndithu shaytwaan amathawa mnyumba momwe Suratul Baqarah ikuwerengedwa”
Sananene kuti mudziimbamo nyimbo. Chifukwa nyimbozo zimaitanitsa shaytwaan osati kuthamangitsa
Ananenanso, mu hadith yochokera kwa Sahl bun Sa’d radhia Allah anhu:
إن لكل شيء سناما، وإن سنام القرآن سورة البقرة، ومن قرأها في بيته ليلا لم يدخل الشيطان بيته ثلاث ليال، ومن قرأها نهارا لم يدخل الشيطان بيته ثلاثة أيام.
Ndithu chirichonse chiri ndi msana (peak), ndipo msana wa Qur’an ndi Surah Al Baqarah. Yemwe angawerenge Surah Al Baqarah mnyumba mwake usiku, ma shaytwaan sangalowe mnyumbamo mausiku atatu, ndipo yemwe angawerenge masana, ma shaytwaan sangalowe mnyumbamo masiku atatu…
Kodi pamenepo Msilamu ofuna madalitso komanso kutcinjirizidwa kwa shaytwaan nkumapezekanso nthawi ina yoika nyimbo mnyumba?