Allah Subhaanah wa Ta’la anatumiza Mneneri Nuh alaih salaam patadutsa zaka 100 pambuyo pa Mneneri Adam alaih salaam. Chiwelengero cha anthu padziko chinachuluka zedi.Panthawiyi, shaytwaan anawasokoneza anthu kotero anali kupembedza mafano, kotero Allah anatumiza Nuh alaih salaam, kuti awawongole anthu kubwelera ku Chikhulupiliro cha Allah. Koma inali ntchito yovuta  kwambiri.

Nuh alaih salaam anawalalikira anthu kuti amuope Allah ndipo adzichita zomwe walamula.Koma anthu sanafune kumvera; anakana ndikupitiriza kulambira mafano awo.Nuh anali odziwa kuyankhula ndipo opilira kwambiri.

“Kodi simudziwa kuti Allah ndi amene analenga dziko lonse?Allah ndiyemwe analenga dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zomwe mukudziona mmwambazi.Analenga mitsinje, mapiri, mitengo ndi zina zonse zomwe mukudzionazi.Anakuchitirani inuyo zonsezi, tsopano nchifukwa chani sikumuyamika?Nchifukwa chani mukulambira mafano?”Iye anali kukalipa motero.

Koma anthu sanalabadire ndipo anali kukana ulaliki pomuuza kuti sangawalangize poti iye ndi munthu monga iwo, komanso anali kumuganizira kuti amanama.

Komatu padziko panalinso Asilamu abwino. Ambiri mwa iwo anali ofooka komanso osauka. Amenewa ndi amene anamvera mau a Mneneri ndipo anazindikira kuti anali kuchimwa polambira mafano. Choncho padziko panali magulu a anthu awiri; omwe anali kupembedza Allah Subhaanah wa Ta’ala, ndi ena omwe anali kupitiriza kupembedza mafano.

Nuh alaih salaam anapitiriza kulalikira anthu kwa zaka zambiri. Pamene opembedza mafano anatopa ndi ulaliki waMneneri Nuh, anamuopseza kuti akapanda kusiya kulalikira amugenda.Koma Mneneri sanawalabadire ndipo anapitiriza kuwalalikira mwamphamvu usana ndi usiku. Nthawi zambiri anali kugendedwa ndi opembedza mafano pamene anali kulalikira ku makamu a anthu, komanso anali kukwapulidwa ndi ndodo. Anali kunenetsa kuti iye sanali osiyana ndi anthuwo, sanali mneneri ndipo sangamumvere.

Nuh alaih salaam anawatsimikizira kuti anali kuwauza zoona za tchimo la kupembedza mafano, koma sanamve ndipo anapitiriza kumumenya.Anawachenjeza za chilango cha Allah chomwe chidzawapeze tsiku lina.Komabe anthu analibe manyazi, ndipo anamunyoza kuti iye ndi opusa ndipo anawalangiza ena kuti azamumvere.

Mavuto onsewo sanamuletse Mneneri kulalikira anthu ake. Anapitiriza kulalikira kwa zaka 950! Koma osakhulupilira aja anapitiriza kumuvutitsa.

Nuh alaih salaam anali okhumudwa kwambiri, pamene chiwelengero cha osakhulupilira chinali kukulirabe.

Usiku wina pamene anali kupemphera, Allah anamuuzakuti asadandaule poti anakwaniritsa kufalitsa uthenga womwe anatumizidwira.Anamuuza kuti awalanga anthu onse chifukwa cha zochimwa zawo ndipo aliyense afa kupatula Asilamu ndi zinyama.

Anamuuza kuti adzale mitengo yambiri.Koma Nuh alaih salaam sanali kudziwa chifukwa chake; anangomvera lamulo la Allah ndikuwauza anthu omwe anali kumvera iye kuti achite chimodzimodzi. Anachita zimenezi kwa zaka zoposa 100.

Patatha zaka zambiri, Allah amulamula Mneneri kuti ayambe kumanga Chombo chachikulu chomwe chingatenge zinyama ziwiriziwiri pa dziko lonse.Mneneri anali ozunguzika poti sanali kudziwa kumanga chombo komanso palibe yemwe anamangapo.

Ngakhale zinali choncho, Mneneri anayamba kumanga mothandizidwa ndi Angelo.Choyamba anapanga plan koma palibe yemwe akudziwa kuti chinali chokula bwanji; ena amanena kuti chinali chotalika 600 feet pomwe ena amati 2400 feet. Komabe mulimonsemo, chombocho chinali chachikulu zedi.

Ana ake pamodzi ndi Asilamu onse anamuthandiza kumanga chombo.Iye anasankha kuti akamangire chombocho kumapiri otalikira kwambiri ndi anthu.Anatenga zida ndikuyamba kudula mitengo yomwe anadzala zaka 100 zapitazo.Ndipo anayamba kumanga chombo malinga ndi plan ija.Anthu anagwira ntchito molimbika usana ndi usiku.

Pamene anthu osakhulupilira anamuona Mneneri akumanga chombo pamwamba pa phiri, anali kumuseka kuti ndi opusa, chifukwa choti anali kumanga chombo chachikulu pomwe anali kutali ndi Nyanja.Anali kuganiza kuti sizidzatheka kuchipititsa kunyanja. Koma pazonsezi,  Mneneri anawayankha kuiti adziwa posachedwa. Anthu sanadziwe chimene Mneneri ankamangira chombo ndipo anaganiza kuti mutu wake sukugwira.

Mneneri ndi anthu ake anapitiriza kugwira ntchito molimbika, ndipo chombo chinatheka patadutsa myezi yambiri.Anamuyamika Allah powathandiza kumaliza kumanga chombo.

Nthawi ya chigumula inali kuwandikira pang’onopang’ono.Usiku wina Allah anamuuza Mneneri kuti tsiku lomwe adzaone madzi akutuluka mnyumba mwake pamalo ophikira, ndi tsiku lomwe chigumula chidzachitike.

Pamene tsiku la chigumula linkawandikira, nyama ndi mbalame zinayamba kufika ziwiriziwiri; chachimuna ndi chachikazi.Kunali njovu, mikango, makoswe, mbalame ndi zina zotero.Ndipo chombo chinadzadza ndi mitundu yonse ya nyama za padziko.

Tsiku lina, monga mmene Allah anamuuzira Mneneri, madzi anayamba kutulukira pamalo ophikira.Ichi chinali chizindikiro chomwe Nuh alaih salaam anali kuyembekezera ndipo anadziwa kuti nthawi ya chigumula yafika.Atatuluka panja anaona kuti kwayamba kugwa mvula.Mosataya nthawi anatuluka ndikuitana Asilamu onse omwe anamuthandiza kumanga chombo.Anawauza kuti akalowe mchombo mwachangu.Osakhulupilira aja sanamvesetse chomwe chinali kuchitika, ndipo anali kumuseka Mneneri, koma sanawalabadire. Aliyense anamumvera kupatula mmodzi wa akazi ake ndi mwana wake omwe sanali okhulupilira. Mwana wake anati adzipulumutsa yekha koma sizinathandize.

Madzi anakwera ndipo Mneneri anathamanga ndikulowa mchombo.Kenako chigumula choopsa chinachitika ndipo madzi anali kukwera mothamanga! Nthaka inanyowa ndipo madzi anasefukira.Mvula sinasiye kwa maola ambiri. Pamenepo tsopano anthu anazindikira kuti zomwe Mneneri anawauza zija zinali zoona.Anathawira kumapiri kuti akadzipulumutse.

Mneneri ataona mkazi ndi mwana wake atakwera pa phiri, anawaitana kuti adzakwere chombo kuti apulumuke, koma anakana. Funde lalikulu loposa phirilo linadza nkuwamiritsa ndikuwapha onse pamodzi ndi osakhulupilira ena onse.

Madzi anali kukwelerabe ndipo dziko lonse linamira.Pamene Nuh alaih salaam ananena kuti “Bismillah”, chombo chinayamba kuyenda.Tsopano mvula inasiya koma dziko lonse linadzadza ndi madzi, ndipo Mneneri anadziwa kuti akuyenera kupitiriza kuyenda kwanthawi yaitali.

Chombo chinatenga anthu 80, ndipo Mneneri analangizidwa kuti atenge chakudya chokwanira anthu ndi zinyama zonse. Allah anapanga kale plan; anachipanga chombo moyenera nkhosa yofatsa ndi mkango wolusa.Zinyama zolusa zonse anadzifowoketsa ndipo zinakhalira limodzi.Koma Mneneri anavutika ndi khoswe yemwe anali kuthamangathanga paliponse kupereka mavuto ndithu.Iye anapempha Allah ndipo analenga mphaka yemwe anagwira khoswe, kenako khoswe anadekha ndikukhala ndi khalidwe.

Kudzera njira imeneyi, Allah Ta’la anamufewetsera Mneneri mavuto omwe anali kukumana nawo paulendo.

Anayenda masiku okwana 150 tsopano koma sanathe kupeza nthaka. Mneneri ndi anthu ake anadikira kwa masiku ochuluka. Kenako anatumiza khwangwala kuti aone ngati angapeze nthaka, koma sanabwelerenso.Anatumizanso nkhunda yomwe inauluka ndikubwelera patatha masiku angapo, inabweretsa masamba a mtengo wa Zitona pakamwa pake. Mneneri ndi banja lake anali osangalala poti anadziwa kuti awandikira nthaka.

Chombo chinafika paphiri la Judi ndipo Mneneri anati  “Bismillah” pamene chombo chinaima. Pambuyo pa kuyenda masiku oposa 150, tsopano ulendo watha!

Mneneri anatulutsa zinyama ndi mbalame zonse ndipo zinadzadzanso padziko.Anthu onse anatuluka ndikutsika pansi, ndipo choyambilira chomwe anachita Nuh alaih salaam ndi kugwetsa mutu pansi kulambira Allah Ta’la.

Chimenecho chinali chiyambi chatsopano cha anthu.