Ambiri masiku ano amasokonezeka nthawi ya swalat yomwe anaphunzitsa Mtumiki salla Alaih waallam, ndi  wotchi makamaka akapita dziko lina.
Ena anati “mzikiti womwe timaswali kuno ndi wa Mashia chifukwa akumachita adhaan ya Dhuhr past 1, pomwe ku Malawi timaswali 12:30”
Pamenepo pali mavuto awa:
1. Sakudziwa kuti Mashia ndi ndani nanga zochitika zawo ndi zotani, ndiye akaona kenakake kakusemphana ndi zomwe akudziwa, basi amenewo ndi Mashia. Si Choncho.
2. Sakudziwa kuti nthawi ya Swalat sinalongosoleredwe pa watch, koma timagwiritsa ntchito watch poti ndi chinthu chimene chimagwirizana ndi nyengo, timakhala nacho pafupi komanso pena dzuwa limatha kubitsika.
Pa Swalaat, nthawi ndi yofunikira kwambiri, Allah taala akunena kuti
إِنَّ الصَّلاة كَانَتْ عَلَى الْمُؤْمِنِينَ كِتَاباً مَوْقُوتاً
Ndithu swalat kwa okhulupilira zinalembedwa munthawi zake.
Choncho Swalat zisanu zinalamulidwa nthawi zisanu kapena zitatu.
Zitatu kwa amene ali ndi vuto lowaloleza kuphatikiza Dhuhr ndi Asr nthawi imodzi, komanso Maghrib ndi Isha nthawi imodzi. Ndipo amene alibe vuto lowalola kuphatikiza, ali ndi nthawi zisanu patsiku.
Mtumiki salla Allah alaih wasallam analongosola nthawi za swalat zonse mu hadith iyi:
وَقْتُ الظُّهْرِ
إِذَا زَالَتْ الشَّمْسُ وَكَانَ ظِلُّ الرَّجُلِ كَطُولِهِ مَا لَمْ يَحْضُرْ الْعَصْرُ
وَوَقْتُ الْعَصْرِ
مَا لَمْ تَصْفَرَّ الشَّمْسُ
وَوَقْتُ صَلَاةِ الْمَغْرِبِ
مَا لَمْ يَغِبْ الشَّفَقُ
وَوَقْتُ صَلَاةِ الْعِشَاءِ إِلَى نِصْفِ اللَّيْلِ الأَوْسَطِ
وَوَقْتُ صَلاةِ الصُّبْحِ
مِنْ طُلُوعِ الْفَجْرِ مَا لَمْ تَطْلُعْ الشَّمْسُ فَإِذَا طَلَعَتْ الشَّمْسُ فَأَمْسِكْ عَنْ الصَّلَاةِ فَإِنَّهَا تَطْلُعُ بَيْنَ قَرْنَيْ شَيْطَانٍ
Swalat Duhr ndi pamene dzuwa lapendeka (lachoka pakatikati) ndipo kutalika kwa chithunzi cha chinthu kuli chimodzimdzi ndi mwiniwake…
Swalat Al Asr ndi kuyambira pamene dzuwa lisanasanduke chikasu….
Swalat Al Maghrib ndi kuyambira kulowa kwa dzuwa mpaka pamene mitambo yofiira yachoka…
Swalat Al Isha kuyambira kulowa kwa mitambo yofira mpaka pakati pa usiku…
Swalat Al Fajr kuyambira pamene Fajr yatuluka (kuyera kwa kum’bandakucha) mpaka kutuluka kwa dzuwa…koma dzuwa likangotuluka kumene musaswali chifukwa limatulukira pakati pa nyanga za shaytwaan.
Choncho kuyendera nthawi ya watch kumasiyana malinga ndi mmene nyengo zimasiyanira maikomu.
Allah atipatse kuzindikira