الحمد لله رب العالمين، والصلاة والسلام على رسوله الكريم

وبعد

Kuyamikidwa konse ndi kwa Mbuye wa zolengedwa zonse, yomwe anatipanga ife kukhala Asilamu nachipanga Chisilamu kukhala Chipembedzo chokhacho chomwe chidzalandiridwe pamaso pake.  Akunena mu Surah Aali Imraan aayah 85

وَمَنْ يَبْتَغِ غَيْرَ الْإِسْلَامِ دِينًا فَلَنْ يُقْبَلَ مِنْهُ وَهُوَ فِي الْآخِرَةِ مِنَ الْخَاسِرِينَ

Ndipo amene angatsate Chipembedzo chosakhala Chisilamu, sichidzalandiridwa kwa iye. Ndipo iye tsiku Lomaliza adzakhala mmodzi mwa (anthu) otaika.

Choncho anachipanga Chisilamu kukhala Chipembedzo chokwana poikamo malamulo ake omwe ndi nsichi zisanu za Chipembedzo. Ndipo munsichi zimenezi tikudziwa kuti yomaliza ndi kupita ku Makkah,  ku nyumba ya Allah kukapanga mapemphero a Hajj kwa amene angakwanitse kutero kamodzi kokha mu umoyo wake.

Mtendere ndi madalitso zipite kwa Mthenga wake olemekezeka Muhammad salla Allah alaih wasallam, yomwe anatizidwa kuti adzakhale nyali yowunikira ku Chiwongoko cha Chisilamu. Mtumiki wake ndi uyo amene anatiphunzitsa ndikutilongosolera malamulo onse a Chisilamu.

Abale olemekezeka, mu nsanamira ya Chisilamu ya chisanu, tinalamulidwa kupereka nsembe pozinga chinyama cha myendo inayi Monga mbuzi,  ng’ombe, nkhosa, ngamira ndi zina zotero, potsatira sunnah ya Nambo wathu mchipembedzo, Ibrahim alaih salaam. Ibrahim alaih salaam anayesedwa mayeso aakulu mu umoyo wake, pamene analamulidwa kuti azinge mwana wake yemwe anampeza atakalamba pambuyo pokhala zaka zambirimbiri opanda mwana.

Ndipo Allah Ta’la anamupatsa mayesowa ndipo ataona kuti wakhonza,  anamusinthira chozinga China kikhala kankhosa komwe anakatsitsa kuchokera, ku mwamba. Nchifukwa chaketu inu ndi one tinalamulidwa kuzinga nkhosa kapena nyama ilitonse yofanana ndi nkhosa.

Zina mwa nkhani zikuluzikulu zomwe Qur’an yolemekezeka inakamba potilimbikitsa ife pa ibaada, ndi nkhani ya chiyambi cha lamulo, la kupereka nsembe ya chinyama pa 10 mwezi wa Dhul Hijjah. Ndipotu nkhani imeneyi ndi yomwe inachitika pakati pa Ibrahim ndi mwana wake Ismail alaihima Salaam.

Timakhala tikumva ma report osiyanasiyana pa nkhani imeneyi, komatu zimapweteketsa mutu tikamamva kuchokera mmabuku a anzathu a zipembedzo zina, ngakhalenso anzathu ena a Chisilamu amene amatengera kuchokera mmareport osatsimikizika. Alhamdulillah Chisilamu chinafotokoza nkhani yonse momveka mu, Qur’an ndi Sunnah. Ndipo yomwe angakhale ndi chikaiko pa zinthu ziwiri zimenezi ndiye kuti adakali mumdima,  Allah amuwongole.

Choncho tatiyeni timvere limodzi kuchokera mu Qur’an buku lopanda chikaiko mkati mwake.

Allah Ta’la akulongosola nkhani ya kuzingidwa kwa Ismail mu Surat Al Saaffaat,  aayah 101-113 motere:

فَبَشَّرْنَاهُ بِغُلَامٍ حَلِيمٍ * فَلَمَّا بَلَغَ مَعَهُ السَّعْيَ قَالَ يَا بُنَيَّ إِنِّي أَرَى فِي الْمَنَامِ أَنِّي أَذْبَحُكَ فَانْظُرْ مَاذَا تَرَى قَالَ يَا أَبَتِ افْعَلْ مَا تُؤْمَرُ سَتَجِدُنِي إِنْ شَاءَ اللَّهُ مِنَ الصَّابِرِينَ * فَلَمَّا أَسْلَمَا وَتَلَّهُ لِلْجَبِينِ * وَنَادَيْنَاهُ أَنْ يَا إِبْرَاهِيمُ * قَدْ صَدَّقْتَ الرُّؤْيَا إِنَّا كَذَلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ * إِنَّ هَذَا لَهُوَ الْبَلَاءُ الْمُبِينُ * وَفَدَيْنَاهُ بِذِبْحٍ عَظِيمٍ * وَتَرَكْنَا عَلَيْهِ فِي الْآخِرِينَ * سَلَامٌ عَلَى إِبْرَاهِيمَ * كَذَلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ * إِنَّهُ مِنْ عِبَادِنَا الْمُؤْمِنِينَ * وَبَشَّرْنَاهُ بِإِسْحَاقَ نَبِيًّا مِنَ

الصَّالِحِينَ * وَبَارَكْنَا عَلَيْهِ وَعَلَى إِسْحَاقَ وَمِنْ ذُرِّيَّتِهِمَا مُحْسِنٌ وَظَالِمٌ لِنَفْسِهِ مُبِينٌ

Ndipo tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wofatsa, (mwanayo ndi Ismail). Ndipo (adabadwa ndi kuyamba kukula.) Pamene adakwana msinkhu woyenda pamodzi ndi tate wake pochitachita za m’dziko (Ibrahim adayesedwa mayeso kupyolera m’maloto omwe adalota). Adati: “E, mwana wanga! Ine kutulo ndikuona maloto (oona ochokera kwa Mulungu omwe akundilamula) kuti ndikuzinge (monga nsembe yopereka kwa Mulungu). Nanga ukuti bwanji?” (Mwana wabwino) adanena: “Bambo wanga! Kwaniritsani chimene mukulamulidwa. Ngati Mulungu afuna, mundipeza ndili mmodzi mwa opirira.” Pamene adagonjera onse awiri (chofuna cha Mulungu), ndipo (Ibrahim) adam’goneka chakumphumi (ndipo adatsimikiza kumupha). Ndipo tidamuitana: “E, iwe Ibrahim. Ndithu, wavomereza maloto! (choncho usamuphe mwana wakoyo).” Umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino. Ndithu, amenewa ndimayeso oonekera, ndipo tidampulumutsa pompatsa nyama yayikulu (yoti apereke nsembe.) Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake). Mtendere ukhale pa Ibrahim! M’menemo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino. Ndithu, iye adali mmodzi mwa akapolo athu okhulupirira. Ndiponso tidamuuza nkhani yabwino (yoti akhala ndi mwana wotchedwa) Is’haq; mneneri; wam’gulu la olungama. Ndipo tidamdalitsa iye ndi (mwana wake) Is’haq; ndipo m’mbumba ya awiriwa mudapezeka abwino ndi odzichitira zoipa owonekera.

Tisanalongosole nkhaniyi mwatsatanetsatane, tikuyenera kuwadziwa kaye anthu amene tikuwatchulawa kuti ndi ndani.

Ibrahim ndi bambo wa Atumiki, chifukwa choti sanatumizidwe Mtumiki winanso posakhala ochokera mwa ana ake. Poyambilira penioeni, anali ndi ana awiri omwe Allah Ta’la anawasankha kukhala Atumiki, Ana amenewatu ndi Isma’il yemwe ndi gogo wa ma Arabs (Aluya), ndipo kuchokera mwa ana ake, anabadwa Mtumiki wathu Muhammad salla Allah alaih wasallam. Ndipo mwana wina wa Ibrahim ndi Is’haaq,  yemwe Allah Ta’la anamdalitsa ndi mwana yemwe analinso Mtumiki, Ya’qub alaih Salaam. Ndipotu Ya’qub ankatchedwanso dzina loti Israil. Kuchokera mwa ana a Ya’qub kapena kuti ana a Israil, ndi amene munabadwa Atumiki onse amene a Bani Israil.

Zonena kuti Ibrahim ndi bambo kapena gogo, wa Atumiki onse, zikuchokera mmawu a Allah Ta’la ochokera pa Surah Al An’aam aayah 84-86 pamene Allah Ta’la watchula ena mwa maina a gulu la Azitumiki omwe akuchokera pa Ibrahim alaih Salaam:

ووهبنا له إسحاق ويعقوب كلاً هدينا ونوحاً هدينا من قبل ومن ذريته داود وسليمان وأيوب ويوسف وموسى وهارون وكذلك نجزي المحسنين، وزكريا ويحيى وعيسى وإلياس كل من الصالحين وإسماعيل واليسع ويونس ولوطاً وكلاً فضلنا على العالمين

Ndipo tidampatsa (Ibrahim mwana wotchedwa) Is’haqa ndi (mdzukulu wotchedwa) Ya’qub. Onse tidawaongola. Nayenso Nuh tidamuongola kale (asadadze Mneneri Ibrahim). Ndipo kuchokera m’mbumba yake (Nuh, tidamuongola) Daud, Sulaiman, Ayubu, Yusufu, Musa, ndi Haarun. Ndipo umo ndi momwe timawalipilira ochita zabwino.

Tatiyeni tibwelere ku nkhani yathu ya kuzinga, mma aayah oyambilira aja: Allah Ta’la akutifotokozera mma aayah amenewa nkhani ya Ibrahim alaih salaam, pambuyo pomupulumutsa ku anthu ake. Chipulumutsochitu chinamfika Ibrahim pamene anthu sanakhulupilire da’wah yake yowaletsa kupembedza mafano, ndipo anaganiza zomuponya pamoto kuti apse, koma Allah anamupulumutsa modabwitsa. Allah Ta’la anaulamula moto kuti:

 يا نار كُونِي بَرْدًا وَسَلَامًا على إبراهيم

“E, iwe Moto! Khala kuzizira ndiponso mtendere kwa Ibrahim”. Surah Al An’biyaa Aayah 69

Komatu akanapanda kunena kuti:

وَسَلَامًا

(ndiponso mtendere), 

kukanatha kumupatsanso mavuto  kuzizira kwakeko, koma anati:

 بَرْدًا وَسَلَامًا

(kuzizira ndiponso mtendere). 

Anthu omwe anamuponya Ibrahim pamoto aja, anaona chodabwitsa chimenechi koma sizinawakhunze, ndipo sanakhulupilire, komanso sanavomereze. Choncho Ibrahim alaih ssalaam anaganiza zowachokera anthu aja pambuyo potaya mtima zoti angawongoke. Ibrahim anali atakhala ndi anthuwa nthawi yaitali kwambiri akuwaitanira ku Tawheed, komatu analibe mwana wina aliyense, ndipo anapempha kwa Allah kuti ampatse mwana:

رب هَبْ لِي مِنَ الصَّالِحِينَ

(O, Mbuye wanga! Ndipatseni mwana yemwe adzakhale (mmodzi) mwa olungama!”) Surah Al Saffaat aayah 100

Apatu Ibrahim anali kupempha mwana wabwino, choncho Allah Ta’la anamuyankha dua yake pomupatsa nkhani yosangalatsa yoti akhala ndi mwana wofatsa. Chomwe akutanthauza akamati mwana ofatsa, ndi kuti akadzakula adzakhale ofatsa, chifukwa mwana wamng’ono kwambiri kufatsa kwake sikumaonekera pamene ali msinkhu woyamwa…choncho mau oti Haleem akutanthauza kuti akadzakula adzakhala wofatsa. Pamenepanso pali chizindikiro komanso lonjezo la Allah Ta’la lonena kuti mwanayu adzakhala ndimoyo mpaka adzakula, sadzamwalira ali wakhanda….izi zikutsimikizika pa mau a Allah Ta’la onena kuti:

 فَبَشَّرْنَاهُ بِغُلَامٍ حَلِيمٍ

(Ndipo tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wofatsa, (Mwanayo ndi Ismail). Surah Al Saffaat aayah 101.

فَلَمَّا بَلَغَ مَعَهُ السَّعْيَ قَالَ يَا بُنَيَّ إِنِّي أَرَى فِي الْمَنَامِ أَنِّي أَذْبَحُكَ

Ndipo (adabadwa ndi kuyamba kukula.) Pamene adakwana msinkhu woyenda pamodzi ndi tate wake pochitachita za m’dziko (Ibrahim adayesedwa mayeso kupyolera m’maloto omwe adalota). Adati: “E, mwana wanga! Ine kutulo ndikuona maloto (oona ochokera kwa Mulungu omwe akundilamula) kuti ndikuzinge (monga nsembe yopereka kwa Mulungu).

Allah akulongosola kuti tinampatsa mwana ameneyo, ndipo atafika msinkhu woyenda naye ndikumudalira nkumagwira ntchito ndi bambo ake, anali akukhala pafupi ndi bambo ake nthawi zonse, anali kuyenda naye kulikonse, poti anasanduka kukhala chonyaditsa cha bambo ake. Msinkhu umene anafika mwanayutu unali msinkhu woti kuvutika konse komwe bambo ake anamuvutikira pomulera kwatha, tsopano ndi nthawi yoti apindule naye monga mwana wa mwamuna.

Ibn Kathir Rahimahullah anati: “Ibrahim alaih salaam anali kupitapita kukamuona mwana ndi mkazi wake. Anali kuchokera ku Shami kupita ku Makkah kumene kunali Hajra (mai wa Ismail) pamodzi ndi mwana wakeyo”. Ndipo anati anati “anali kukwera Burac pokafika kumeneko…” Pomaliza anati Allah ndamene adziwa zonse pa nkhani imeneyi, ndipo ikufunika umboni woona. Izi akulongosola pa Tafseer yake vol.5/35

Kuchokera kwa Ibn Abbas radhia Allah anhuma, Mujaahid, ‘Akramah, Sa’eed bun Jubair, ‘Ataa Al Kharsaani, Zayd bun Aslam ndi ena otero, anati: “mau oti

فَلَمَّا بَلَغَ مَعَهُ السَّعْيَ

akutanthauza kuti pamene anakula nkukhala mnyamata ndikuyamba kuyendayenda komanso kukwanitsa ntchito zomwe bambo ake anali kugwira…” Awatu ndi ena mwa maumboni ambiri omwe analongosoledwa pochita tafsir mau amenewa.

Tikupitiriza nkhani yath, ndipo kuchokera pamenepo Allah akunena kuti:

قال يا بني إِنِّي أَرَى فِي الْمَنَامِ أَنِّي أَذْبَحُكَ فَانْظُرْ مَاذَا تَرَى

(Adati: “E, mwana wanga! Ine kutulo ndikuona maloto (oona ochokera kwa Mulungu omwe akundilamula) kuti ndikuzinge (monga nsembe yopereka kwa Mulungu). Nanga ukuti bwanji?”)

Ibn Abbas radhiallah anhu anati: “Maloto a Atumiki anali wahy (chibvumbulutso chochokera kwa Allah)” Izi zikupezeka mu Al Mustadrak p3613 ndipo ndi hadith ya Hassan.

Al Tabari anatulutsanso report la hassan kuchokera kwa Qataadah potanthauzira aayah imeneyi

قال يا بني إِنِّي أَرَى فِي الْمَنَامِ أَنِّي أَذْبَحُكَ فَانْظُرْ مَاذَا تَرَى

anati: Maloto a Atumiki ndi owona, ndipo amati akalota amachita zomwe alotazo. Izi zikupezeka mu Jaami’ul Bayaan p22608.

Al Qurtubi ananena mu Tafsir yake vol.15 pg101 kuti: “Ibrahim alaih Salaam analota kokwana katatu, akuuzidwa kuti azinge mwana wake”.

Komanso kuchokera pa page yomweyo, Muhammad ibn Ka’b anati: “Chibvumbulutso chinali kuwafikira Atumiki kuchokera kwa Allah Ta’la ali mmaso ngakhale atagona (kutulo)…Ndithu Atumiki mitima yawo sigona”.

Kuchokera mu nkhani ya marfoo’ yomwe yafotokozedwa mu Al Twabaqaatil Kubra ya Ibn Sa’d, vol.1/171 ndipo anatsimikiza za kuona kwa nkhaniyi Sheikhul Albaani mu Assilsilatu Swaheehah p1705, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Ndithu Atumikife maso athu amagona pomwe mitima yathu sigona”.

Zonsezitu zikutsimikiza kuti Mtumiki akagona ndikulota, loto lakelo limakhala loona chifukwa mitima ya Atumiki sigona, imakhala yamoyo pamene thupi liugona. Choncho apa mpamene pakubweranso chitsimikizo choti Allah Ta’la anamulamula Ibrahim kuti azinge mwana wake Ismail kokwanira kangapo ndithu, koma kutulo. Choncho lamulo la Allah limayenera kukwaniritsidwa. Ndipotu Ibrahim alaih Salaam anamuuza izi mwana wake yemwe analamulidwa kuti amuzingeyo! ponena kuti:

يَا بُنَيَّ إِنِّي أَرَى فِي الْمَنَامِ أَنِّي أَذْبَحُكَ

(E, mwana wanga! Ine kutulo ndikuona maloto (oona ochokera kwa Mulungu omwe akundilamula) kuti ndikuzinge (monga nsembe yopereka kwa Mulungu). Nanga ukuti bwanji?). 

Anamuuza ndikumufunsa choncho, sanafune kuchita momupatsa judgment kapena kumulamula kuti alole poti iye ndi Mtumiki ndipo kuti maloto ake ndi oona…koma anampatsa mwayi wopereka maganizo pa nkhaniyo poti uwo ndi moyo wake komanso imfa yake. Komansotu anafuna kuyesa kupilira kwa mwana wakeyo pa kugonjera kwake kwa Allah Ta’la kapena bambo ake, malinga ndi mmene msinkhu wake unaliri panthawiyo. Pamenepatu tikutha kuona ubwino wa kulera ana mwa ubwino komanso moopa Allah Ta’la. Ndipotu umboni wake ndi umene tikuwupeza mu yankho la Ismail pamene ankawayankha bambo ake posaopa, komanso mosaipidwa, poti anali munjira ya utumiki, ngati mmene mwana wa sheikh akuyenera kukhalira. Ismail anayankha kuti

يَا أَبَتِ افْعَلْ مَا تُؤْمَرُ

(Bambo wanga! Kwaniritsani chimene Mukulamulidwa). 

Bambo, chitani mchilamulo cha Allah; chitani momwe Allah wakulamulirani. Sananenetu kuti: “ndilibe choletsa kuti mutero” koma anati: “chitani zomwe mwalamulidwa”, amatanthauza kuti limenelo ndi lamulo lochokera kwa Allah, ndipo inu bambo mwalamulidwa…chitani zomwe mwalamulidwa. Izitu zikutsimikizira inu ndi ine kuti mwanayu anali akukhulupilira chibvumbulutso chimenechi, anali kukhulupilira lamulo limeneli, ndipo chomwe chinatsala apa ndi kwa bambo ake kukwaniritsa lamulo ndipo iye anayenera kuwalimbikitsa, ponena kuti:

افْعَلْ مَا تُؤْمَرُ

(kwaniritsani chimene mukulamulidwa). 

 

Mayankhidwe amenewatu anapangitsa bambo ake kuti asabwelere mbuyo pokwaniritsa lamuloli. Akanayankha mayankhidwe ena ake, akanatha kuwapangitsa kumva chisoni kwambiri pa mwana wake. Koma anali osangalala podziwa kuti mwana wake wakhulupilira chibvumbulutso cha Allah Ta’la. Allah Ta’la anamulamula Ibrahim kuzinga mwana wake panthawi imene anafika msinkhu wakuzindikira zinthu, ndipo panthawi imene anali asanakule moti nkukhala ndi ana, chifukwa zikanapereka maganizo kuti asiya ana. Awatu anali mayesero aakulu ochokera kwa Allah Ta’al monga mmene akunenera pa aayah 106 mu Surah Al Swaaffaat:

إِنَّ هَذَا لَهُوَ الْبَلَاءُ الْمُبِينُ

(Ndithu, amenewa ndimayeso oonekera). 

Mayeso aakulu kwambir, kuzinga mwana wako. Osatitu kuombera ndi mfuti, ayi. Koma kutenga mpeni, ndikumugoneka mwana pansi, kumugwira pakhosi nkumuzinga mmene timachitira mbuzi muja. Ndi mayesero aakulu mopanda kukaika.

Anthu ena amatha kumanena kuti: Nchifukwa chani Allah anamuika pamwamba kwambiri Ibrahim, komanso anampanga kukhala wabwino kwa Aneneri onse komanso anali mmodzi mwa Atumiki eni mphamvu ndi kulimba pa chipembedzo, komanso anamsankha kukhala bwenzi?

Tinena kuti zonsezo nchifukwa choti mayesero onse omwe anali kuperekedwa kwa munthu wamkulu ameneyu, sanali ophweka; anapilira ku mavuto a bambo ake (aja anali kugwadira komanso kugulitsa mafano), anth ake anali kutsutsana naye mu zambiri, ndipo anali kuwapilira komanso ankalimbana nawo nthawi zonse pa nkhani ya Umodzi wa Allah Ta’la ndikupanga nawo mitsutso. Anamuponyera pamoto kuti angothana naye chifukwa cha kuwaswera mafano awo, koma anapilira ndikuyezamira mwa Allah. Kenako anawasamukira kuchoka kwawo ku Iraq, kupita ku Shami, kumene Allah Ta’la anamuyesa ndi mau ndipo anakwaniritsa. Analandira chisangalatso cha mwana patadutsa zaka zambirimbiri osakhala ndi mwana, ndipo atalamulidwa kuti azinge mwanayo, anapilira ndikukwaniritsa lamulo. Kuchoka pamenepo anamanga nyumba ya Ka’bah ndipo anawalera ana ake mu environment ya kugonjera Allah. Panthawi imeneyitu Msilamu analipo iye ndi Mkazi wake basi. Ndiye tangoganizani, munthu yekhayekha kumapempbedza Allah yekhayekha munyengonso ya mavuto ndi yachilendo pakati pa anthu. Kodi munthu otereyu pamaso pa Allah angakhale otani? Kuonjezera pamenepo, mwana wake nkudzatengera kugonjera kwa bambo ake, nthawi yomwe kunalibe ena omwe angatenger chikhalidwe koma bambo ake okha. Ana ambiritu amatengera chikhalidwe kuchokera kwa aphunzitsi ku sukulu, kapena anzawo malo osiyanasiyana, ndipo zikhalidwe zija zimasakanikirana ndi zomwe akutengera kwa makolo ake, mapeto ake amakula ndi chikhalidwe chachilendo chotiu si cha makolo ake, mchifukwa chake timapeza kuti mwana wa sheikh akukula mosemphana ndi zochita za bambo ake. Komatu ana a Ibrahim anali kukula ndi makolo awo ndipo sanachokere mchikhalidwe. Tangoonani pamene Ismail anauzidwa ndi bambo ake za kuzingidwa, ukutu kutanthauza kuphedwa, koma anayankha monga talongosolera kale muja, ndipo anapitiriza kunena kuti:

 سَتَجِدُنِي إِنْ شَاءَ اللَّهُ مِنَ الصَّابِرِينَ  (سَتَجِدُنِي إِنْ شَاءَ اللَّهُ مِنَ الصَّابِرِين

(Ngati Mulungu Afuna, mundipeza ndili mmodzi wwa opirira).

Tikapita ku chilankhulo cha Arabic, tipeza kuti anayamba ndikunena kuti

ستجدني

(mundipeza), 

apatu ambiri tikudziwa kuti zimathanthauza “nthawi ya mtsogolo”. Koma apa amatanthauza kutsimikiza za kuyandikira kwa kuchitika kwa ntchitoyo. Komansotu ananena kuti

إن شاء الله

Chifukwa choti ilo linali lamulo lakutsogolo ndipo munthu sangakwanitse kutsimikiza zamtsogolo, nchifukwa chaketu Ismail anatsimikiza ponena kuti In sha Allah ndidzakala opilira. Ndidzapilira ndipo ndiyezambira mwa Allah Ta’la. Pli phunzirotu lalikulu apa loti ngati tikuyermbekezera kupanga chitnhu munthawi yamtsogolo, tidzilumikiza ndi mau oti in sha Allah (Ngati Allah angafune) chifukwa palibe chomwe chingachitike popanda chifuniro cha Allah Ta’la. Komanso ngati tingapangapande kunena mau amenewa in sha Allah, kutheka chinthu chija osatheka malinga ndi kusatsimikiza kwathu podzipereka za mawa mmanja mwa Allah. Tamvatu zitsanzo zambiri za amene ntchito zawo komanso zofuna zawo sizinakwaniritsidwe chifukwa chosadzipereka mchifuniro cha Allah. Chitsanzo choyamba ndi Mtumiki Mfumu Sulaiman alaih salaam amene ananena kuti:

لأطوفن الليلة على مائة امرأة كل امرأة تلد فارس يقاتل في سبيل الله، قال له صاحبه: قل: إن شاء الله

(ndizungulira mwa akazi 100, mkazi aliyense adzabereka msilikali yemwe adzamenye nkhondo munjira yaAllah. Mzake anamuuza kuti: Nena kuti In sha Allah) ndipo anaiwala kunena

  فجاءت واحدة من النساء بشق إنسان

(Choncho anangokwanitsa mmodzi wa azimai 100 aja ndipo anabereka theka la munthu…) nkhaniyi ikupezeka mu Sahih Al Bukhari 2819.

Anabereka half ya munthu ndithu, ndipo azikazi onse 99 aja palibe amene anapeza mimba. Koma akananena kuti in sha Allah, at least zikanayenda, poti zonsezo zimatheka mchifuniro cha Allah, koma iye anangoyankhula ngati kuti zitheka mchifuniro chake basi. Pamene Ismil ananena kuti in sha Allah, chinachitika nchani? Allah anamulimbitsa ndikupilira pa chikhonzero chake.

  سَتَجِدُنِي إِنْ شَاءَ اللَّهُ مِنَ الصَّابِرِينَ

(Ngati Mulungu afuna, mundipeza ndili mmodzi mwa opirira) 

chifukwa nkhani imeneyo inafunika kupilira kwambiri komanso kukhulupirika pa lonjezo. Apantu nchifukwa chake Allah Ta’la akumuchemelera Ismail ponena kuti:

وَاذْكُرْ فِي الْكِتَابِ إِسْمَاعِيلَ إِنَّهُ كَانَ صَادِقَ الْوَعْدِ وَكَانَ رَسُولًا نَبِيًّا * وَكَانَ يَأْمُرُ أَهْلَهُ بِالصَّلَاةِ وَالزَّكَاةِ وَكَانَ عِنْدَ رَبِّهِ مَرْضِيًّا

(Mtchulenso M’buku (ili) Ismaila; ndithu, iye adali woona palonjezo, ndipo adali Mtumiki Mneneri. Adali kulamula anthu ake swala ndi zakat, ndipo kwa mbuye wake adali woyanjidwa.) Surah Mariam 54:55

Taonani bwinobwino pamenepa apa; Ibrahim alaih salaam anali atakula, atakalamba pamene ankamukhanzika Ismail ndi mai ake ku dziko lopanda anthu, ku dambo lopanda zomera, malo opanda madzi komanso komanso kwa dzuwa. Ibrahim anagonjera lamulo la Allah ndipo anawasiya kumeneko pomukhulupilira iye subhaanahu wa ta’la.

Pamapeto pake Allah anawapanga mavuto onse aja kukhala chisangalalo komanso madalitso ndipo anawatsegulira njira za rizq zambirimbiri kuchokera komwe sanadziwe. Pachiyambi Ibrahim anali akufunisitsa mwana makamaka pamene anakalamba, atakhala naye, anamusiya yekha ndi mai ake, kenako anabwera kudzamutenga kuti akamuzinge…pamenepotu mai ake atsala okha opanda mwana yemwe amvutikira kwa zaka zambiri. Mavutonsotu awa owonjezera. Moyo wonse kumangokhala mmavuto okhaokha, mayesero a Allah Ta’la kwa bwenzi lake.

Komatu monsemo Ibrahim anali kupilira komanso Islami anali kudzipereka mchifuniro cha Mbuye wake, Mbuye wa bambo ake.

Tatiyeni tipitirize nkhani yathu kuchokera mma aayah aja, Allah Ta’la akupitiriza kulongosola kuchokera pamene Ismail anadzipereka kuti ee bambo, kwaniritsani lamulo la Alla mundipeza ndili opilira, ndipo akunena kuti:

فَلَمَّا أَسْلَمَا وَتَلَّهُ لِلْجَبِينِ

(Pamene adagonjera onse awiri (chofuna cha Mulungu), ndipo (Ibrahim) adam’goneka chakumphumi (ndipo adatsimikiza kumupha). 

Pamene adangonjera onse awiri, apa akutanthauza kuti Ibrahim anatchula dzina Allah pozinga, poti kuzingako kunali mudzina la Allah yemwe analamula. Ndipo Ismail anapanga shahaada poti munthu amayenera kunena kalimah akamamwalira. Komanso kuyankhula kwina amanena kuti “pamene anagonjera”, kutanthauza kuti anachilandira chilamulo cha Allah ndipo anachita mchifuniro chake subhaanah wa ta’la, pamene analamulidwa kupha mwana wake yekha, ndipo sananene kuti nditumiza mngelo kuti adzazinge mwana wakoyo, kapena kuti ndidzangomupatsa imfa ya dzidzidzi. Koma anamulamula kuti atenge mpeni nkuzinga yekha ndi manja ake.

وَتَلَّهُ لِلْجَبِينِ

Ibrahim anamtembenuza Ismail chambali nkumugoneka kuti amuzinge nkhope yake ataiyang’anitsa pansi ncholinga choti asamuyang’ane, chifukwa akamuyang’ana amva chisoni ndikudandaula, zomwe zingamuchititse kusintha maganizo ndikuphwanya lamulo la Allah Ta’la.

Kuchokera mu report lina lomwe Allah ndi amene akudziwa, zikunenedwa kuti mwana wa Ibrahim, Ismail anayankhula kuwauza bamboo ake kuti: “ee inu bamboo, ndimangeni zolimba kuti ndisaphuphe kwambiri, komanso mumange mkanjo wanu kuti magazi asagwerepo kotero kuti mai akakaona magaziwo adzikandidandaula ine. Mudusitsenso mpeni pakhosi pangapa mofulumira kuti imfa yanga ikhale yofewa ndipo mundiyang’anitse pansi kuti musandione nkhope mkhundichitira chisoni, komanso kuti ndisaone mpeniwo. Mukabwelera kwa mai, mukandipelekere salaam”. Report ili likuchokera mu Al Jaami’u Li Ahkaamil Qur’an, vol.15/104/ Allah ndamene akudziwa.

Pamene Ibrahim anafuna kuyendetsa mpeni pakhosi la Ismail, Allah anatchinga mpeni uja kotero suna kwanitse kudula khosi la Ismail. Allah analepheretsa mpewni kugwira ntchito yake monganso mmene analepheretsera moto kuwotcha thupi la Ibrahim. Moto ntchito yake ndi kuotcha, komanso mpeni ntchito yake ndi kudula. Anthu omuotcha Ibrahim anasonkha moto wootcha kwambiri koti ufikire kumuwotcha kamodzi ndi kamodzi, chimodzimodzinzso Ibrahim anasankha mpeni wakuthwa kotheratu woti ufikire kudula khosi la Islamil kamodzi ndi kamodzi, koma zonsezo zisinatheke chifukwa Allah anafuna kupulumutsa Ibrahim komanso Ismail alaihima Salaam.

Pamenepo Ibrahim nadabwa kwambiri, ndipo mwachidziwikire munthu ukadabwa panthawi ngati imeneyi, sumalephera kuweramuka nkuyang’ana kumanja, kumanzere, kumwamba. Choncho Ibrahim atatembenuka, anaona khosa ili poteropo.

وَنَادَيْنَاهُ أَنْ يَا إِبْرَاهِيمُ * قَدْ صَدَّقْتَ الرُّؤْيَا

Ndipo tidamuitana: “E, iwe Ibrahim, ndithu wavomereza maloto! (choncho usamuphe mwana wakoyo

Pamenpo Ibrahim atatembenuka anaona nkhosa yaimuna yoyera, komanso yokongola ya maso akuluakulu. Allah anamuuza Ibrahim kuti ndithu wakwaniritsa maloto ako aja, pomugoneka mwana wako pansi ndikutenga mpeni wakuthwa kuti umuzinge, ndithu iwe unatsimikiza za kuzinga mwana wako monga mmene tinakulamulira kutulo, choncho usazinge mwana wako, koma zinga nkhosayo mmalo mwake.

Ndipo mayeso anathera pomwepo.

إِنَّا كَذَلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ

Umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino. Ndimmene timawalipilira amene atitsatira malamulo athu, timawachotsera zovuta zawo ndikuwasonjeza njira yotulukira mmavuto. Allah akunena mu Surah Al Talaaq aayah 2-3 kuti:

وَمَنْ يَتَّقِ اللَّهَ يَجْعَلْ لَهُ مَخْرَجًا * وَيَرْزُقْهُ مِنْ حَيْثُ لَا يَحْتَسِبُ وَمَنْ يَتَوَكَّلْ عَلَى اللَّهِ فَهُوَ حَسْبُهُ إِنَّ اللَّهَ بَالِغُ أَمْرِهِ قَدْ جَعَلَ اللَّهُ لِكُلِّ شَيْءٍ قدرا

Ndipo amene akumuopa Mulungu (potsatira malamulo Ake), Amkonzera njira yotulukira (m’mavuto). Ndipo ampatsa riziki kuchokera momwe samayembekezeramo. Ndipo amene akutsamira kwa Mulungu (pa zinthu zake zonse), ndiye kuti Mulungu ali wokwana kwa iye (kumkonzera chilichonse), ndithu, Mulungu ngokwaniritsa cholinga chake ndi chofuna chake. Ndithu, chinthu chilichonse Mulungu wachipatsa mlingo wake woyenera (ndipo sichingaupyole).

Mmenemo ndi momwe Allah anamulipilira malipiro a ochita zabwino, chifukwa anagwira ntchito yabwino pa ibaada ya Allah yekha, komanso anakwaniritsa lamulo lake.

إِنَّ هَذَا لَهُوَ الْبَلَاءُ الْمُبِينُ

Ndithu,amenewa Ndimayeso oonekera

Kuzinga mwana kuja anali mayesero basi, koma Allah sanaike zoti Ibrahim azinge mwana wake, anafuna kumuyesa, ndipo mu aayah iyi akutsimikiza kuti ndithu amenewa ndi mayesero oonekera. Malinga ndi kudzipereka komanso kugonjera kwa IUbrahim alaih Salaam, Allah Ta’la akumusimba Ibrahim mu Surah Al Naj aayah 37 kuchokjera mu aayah ya 36 kuti:

وَإِبْرَاهِيمَ الَّذِي وَفَّى

Kapena sadauzidwe zomwe zidali M’mabuku a Musa, ndi Ibrahim amene adakwaniritsa (lonjezo la Mulungu)?

وَفَدَيْنَاهُ بِذِبْحٍ

Ndipo tidampulumutsa pompatsa nyama yayikulu (yoti apereke nsembe.)

Allah Ta’la mmalo mwake adampatsa nyama yoti azinge, imeneyitu inali nkhosa yomwe Allah anaipanga kukhala cholowa mmalo mwa mwana wake. Choncho lamulo lozinga mwana linasintha ndipo linabwera lozinga nkhosa.

Ibrahim alaih salaam anakwaniritsa lamulo la Allah Ta’la. Ngati ife sitimapilira mwana wathu yekhayo akamadwala, kodi ndi ndani amene angapilire ndi kuvomereza lamulo la Allah kuti amuzinge mwana wabwinobwino komanso yekhayo yemwe tamuvutikira komanso akuoneka kuti adzakhala olungama? Nchifukwa chaketu Ibrahim alaih salaam analandira ulemelero komanso nyota zikuluzikulu kuchokera kwa Allah Ta’la, pambuyo pa kugonjera ndi kupilira ku mayesero ake. Choncho chifukwa cha mayesero amenewa, Allah Ta’la anamuonjezenjera Ibrahim alipiro komanso malo a ku Jannah. Ndipo chifukwa cha Chisomo chake Allah Ta’la, anafuna kuti bambo wathu Ibrahim asatimane ulemelero umenewu, choncho anatilamula nafe kuti tidzipereka nsembe monga mmene anachitira bamboo wathu Ibrahim. Akanathga kutilamula kuti tidzizinga mwana watrhu woyamba, koma izi zikanakhala zowawa kwambiri kwa ife poti ndife ofooka. Akanathanso kutilamula kuti tidzizinga nkhosa yaimuna yokongola, monga momwe anazingira Ibrahim, koma akanatero zikanakhala zovuta pakati pathu. Choncho mmalo mwake anatifewetsera nkutilamula kuti tidzizinga chinyama chirichonse cha myendo inayi chomwe chiribe chilema, komanso chathanzi ndithu.

Nzachisoni kwambiri Ummah uno waitenga nsembe imeneyi kukhala yopanda nrchito. Izitu nchifuklwa cha kusazindikira kufunikira kwa nsembe imeneyo komanso kufunikira kwa lamulo la Allah Ta’la pa nsembe imeneyo, komanso vuto lina ndi kusadziwa chiyambi cha nsembe imeneyi.

 وَتَرَكْنَا عَلَيْهِ فِي الْآخِرِينَ

Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake).

Nkhani iyi inali yabwino pakati pa anthu, ndfipo inali chitsanzoi chabwino kwa ogonjera alamulo a Allah. Choncho inali ikukambidwa pakati pa anthu kwa nthawi yaitali mpaka nkhani inayendelera mmibadwo yonse kufikira lero lino. Nchifukwa chaketu mibadwo yonse imamukonda Ibrahim alaih salaam! Ayuda amamukonda, Akristu amamukonda, Asilamu amamukonda; onse ndithu amamukonda Ibrahim alaih salaam chifukwa cha kugonjera kwake kwatunthu. Ndiye muona aliyense amatchula dzina la Ibrahim nkumati “Ibrahim ali mwa ife”…Ayuda amati Ibrahim anali Myuda, Akristu amati Ibrahim anali Mkristu. Ife Asilamu timati Ibrahim anali ndani??? Alhjamdulillah ife sitimangonena za mmitu mwathu zongokokera mbali yahtu. Koma timatenga zomwe ananena Allah Ta’la mwini wake, mu Qur’an SuraH Aali Imran aayah 67:

  مَا كَانَ إِبْرَاهِيمُ يَهُودِيًّا وَلَا نَصْرَانِيًّا وَلَكِنْ كَانَ حَنِيفًا مُسْلِمًا

Ibrahim sadali Myuda ndipo sadali Mkhrisitu, koma adali wolungama, wodzipereka; ndipo sadali mwa ophatikiza (Mulungu ndi zinthu zina).

 سَلَامٌ عَلَى إِبْرَاهِيمَ

Mtendere ukhale pa Ibrahim! Salaam yochokera kwa Allah Ta’la

 كَذَلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ

M’menemo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino.

Tsopano chifukwa cha kupilira kwake pa mayesero onse omwe anampatsa kuyambira ku umwana wake, iyi inali nthawi yoti Ibrahim alandire zabwinozabwino zochokera kwa Allah padziko pano, choncho anampatsanso mwana wina, p0osatengera kuti ndiwokalamba. Izi Ibrahim sanali kuyembekezera kuti angadzakhalenso ndi mwana wina, nchifukwa chake kuzinga mwna yekhayo amene anali woyamba komanso womaliza mmaganizo mwake kunali kowawa kwambiri. Allah akunena kuti:

وَبَشَّرْنَاهُ بِإِسْحَاقَ نَبِيًّا مِنَ الصَّالِحِينَ

Ndiponso tidamuuza nkhani yabwino (yoti akhala ndi mwana wotchedwa) Is’haq; mneneri; wam’gulu la olungama.

Adzakhala Mtumiki, sadzamwalira ali mwana, mpaka naye adzakhalanso ndi mwana wake (Ya’qub) monga mmene akunenera mu Surah Huda ayah 71:

 وَمِنْ وَرَاءِ إِسْحَاقَ يَعْقُوبَ

ndipo Pambuyo pa Is’haq, Yakubu

Anamuuzanso nkhani yosangalatsa kuti akhala ndi chizukulu chake (Ya’qub), nkhani zabwino zokhazokha kutsatizana pambuyo poti mayesero anatsatizana kwa nthawi yaitali. Anapilira nthawi yaitali ndipo anapeza zambwino zochuluka…utumiki, ana ake kukhala Atumiki, zizukulu zake kukhala Atumiki komanso ana a zizukulu kukhala Atumiki mpaka kufikira pa Muhammad salla Allah alaih wasallam.

وَبَارَكْنَا عَلَيْهِ وَعَلَى إِسْحَاقَ وَمِنْ ذُرِّيَّتِهِمَا مُحْسِنٌ وَظَالِمٌ لِنَفْسِهِ مُبِينٌ

Ndipo tidamdalitsa iye ndi (mwana wake) Is’haq; ndipo m’mbumba ya awiriwa mudapezeka abwino ndi odzichitira zoipa owonekera.

Allah Ta’la anaika mwa ana awo utumiki ndi mabuku. Apatu tikutha kuona kuti Atumiki onse a ku banja la Israel (Ya’qu) {zidzukulu za Is’haq}, anali ochokera ku banja la Is’haq mwana wa Ibrahim (mng’ono wake wa Ismail). Pomwe kubanja la Ia Ismail alaih Salaam kunabwera Mtumiki omaliza Muhammad salla Allah alaih wasallam. Sikunabwerenso Mtumiki waina kuchokera ku banja la Ismail kupatul Muhammad salla Allah alaih wasallam yekha. Koma kwa Is’haq kunadza Atumiki onse a Bani Israil. Onsewatu akukumana pa Ibrahim alaih salaam kukhala gogo wawo wamkulu.

Kuchokera mu zidzukulu zonsezi, munapezeka anthu otsatira malamulo a Allah, komanso ena oyipa pochita machismo osiyanasisyana. Apa tikuona Allah Ta’la akukamba mu Surah Al Baqarah aayah 124 kumuuza Ibrahim alaih ASlaam kuti:

إِنِّي جَاعِلُكَ لِلنَّاسِ إِمَامًا قَالَ وَمِنْ ذُرِّيَّتِي قَالَ لَا يَنَالُ عَهْدِي الظَّالِمِينَ

“Ndithudi, ine ndichita iwe kukhala mtsogoleri wa anthu.” (Ibrahim adayankha kuti): “Kodi ndi ana anga omwe?” Adati: “(inde; koma) lonjezo langa silingawafike ochita zoipa”

Yankho la Allah Ta’la likupereka umboni wolosera kuti mwa ana ako iwe Ibrahim mudzapezeka ochita zoipa.

Kodi Malo Omwe Allah Analamul Ibrahim Kuzinga Mwana Wake Akupezeka Kuti?

Ena anati ku Makkah, pa Maqaam (pamene Ibrahim anali kuimilira).

Ndipo ena anati pa Minhar, koma Allah ndamene akudziwa malo ake enieni.

Mu Taarikh Al Tabari vol.1/194, Ibn Abbas radhia Allah anhu anati: Nsdikulumbira Mulungu yemwe mzimu wanga uli mmanja mwake, kunali kumayambiliro kwa Chisilamu ndipo mutu wa nkhosa imeneyo unapachikidwa ndi nyanga zake kudenga la Ka’ba ndipo mutuwo unauma.

Apa akutanthauza kuti anthu omwe anali nkudza pambuyo pa Ismail alaih salaam anali kusungira nyanga za nkhosa imeneyi mu Ka’bah mpaka pamene inapsera limodzi ndi Ka’bah.

Yemwe Ankafuna Kuzingidwa Anali Ismail Osati Is’haq Monga Mmene Amakhulupilira Ayuda

Ayuda anayesetsa ndithu kusokoneza mbiri ya nkhaniyi kuti yemwe amayenera kuzingidwa akhale Is’haq ncholinga choti ubwino wa nsembe imeneyi ubwelere kwa iwo. Ndipo kamba ka jelasi yawo posafuna kuti ubwino wa nsembe imeneyi ukhale kuti unachitika kwa kholo la ma Arabs, Ismail alaih salaam. Iwo anati: “Ndithu mwana yemwe anali kuzingidwayu anali Is’haq. Nkhaniyi inakambidwa ndi ozindikira mwa iwo, koma zoona zenizeni ndi zoti ozingidwayu anali Ismail. Abu Huraira, Abu Al Tufail, Ibn Umar komanso Ibn Abbas anatsimikiza kutero.

Ibn Abbas anati: “Operekedwa nsembe anali Ismail, koma Ayuda ananama kuti anali Is’haq.” Izi zili mu Taarekh Al Tabari vo.1/188.

Komanso pomwepo kuchokera kwa Al Hassan Al Basri, anati palibe kukaikiranso zoti amene analamulidwa kuti azingidwe anali Ismail alaih salaam.

Apa malinga ndi mmene nkhani inayendera komanso malinga ndi mabadwidwe a ana awiri amenewa (Ismail ndi Is’haq), tili ndi chitsimikizo choti ozingidwayu anali Ismail osati Is’haq. Allah anam’beretsera Ibrahim nkhani yosangalatsa yoti akhala ndi mwana wina dzina lake Is’haq, ndipo kuchokera kwa Is’haq abwera Ya’qub. Ndiye funso nkumati, ngati anali Is’haq ozingidwa, nchifukwa chani analandiranso chisangalatso choti Is’haqayo adzakhala ndi mwana? Akanakhala bwanji ndi mwana munthu ozingidw? Apatu Allah anafuna kutipangira clear kuti tisakhale opombonezeka kuti ozingidwqa anali ndati.  akanakhala kuti ozingidwa uja anali Is’haq, ndiye kuti pakanapezeka ma contradiction pa nkhani ya cidzukulu cha Ibrahim chodzabadwa mwa Is’haq.

Komanso tikaonesetsa, tipeza kuti masimbidwe omwe Allah anawasimba ana awiri amenewa ndi osiyana; Anamusimba Ismail kuti ofasa, pomwe Is’haq anamusimba kuti odziwa. Kodi pakati pa kudziwa ndi kufasa, ndi mbiri iti yomwe ingapezenge mwa munthu yemwe akufunika kuzingidwa? Nzachidziwikire kuti kufasa kumafunika … ichitu nchizindikiro china choti ozingidwa anali Ismail.

Umboni winanso ndi pamene Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena kuti: أنا ابن الذبيحين (ine ndi mwana wa ozingidwa awiri) kuchokera mu Assiratul Halabiyya vol.6 pg81 (koma hadithiyi ndi ya dhaeef malinga ndi Sheikhul Albaani mu Assilsilati Ddhaeefa pg331).

Komabe, tikudziwa kuti Abdullah bambo ake a Mtumiki salla Allah alaih wasallam analinso mu chiyembekezo chozingidwa ndi bambo ake Abdul Muttalib. Choncho ngati ozingidwa analipo awiri, winayo sangakhalenso Is’haq chifukwa sanali mbali ya makolo a Mtumiki salla Allah alaih wasallam, koma Ismail alaih salaam.

Palinso Hadith yomwe ikukamba zoti ozingidwa anali Is’haq, imeneyo ndi ya dhaeef, yofooka. Chifukwa tikupeza maumboni okwanira mu Qur’an surah Al Anbiyaa aayah 85, pomwe Allah Ta’la wamusimba Ismail ndi kupilira:

 وَإِسْمَاعِيلَ وَإِدْرِيسَ وَذَا الْكِفْلِ كُلٌّ مِنَ الصَّابِرِينَ

Ndipo (mutchule) Ismail ndi Idrisa ndi Dhul Kifli, onsewa adali mwa opirira

Komanso tikaonesetsa, tipeza kuti nkhaniyi inachitikira ku Makkah, nyanga za nkhosa zinapachikidwa ku Ka’bah ku Makkah, Ismila ankakhala ku Makkah, pomwe Is’haq ankakhala ku Shami.

Ibn Al Qayyim rahimahullah anati: “Ismail ndi yemwe ankafuna kuzingidwa, malinga ndi zoyankhula za ma ulamaa, ma Swahaba komanso ma Taabieen ndi onse omwe anadza pambuyo pawo. Pomwe mau onena kuti anali Is’haq, amenewo ndi onama kuchokera mma report oposa twenty. Ndinamumva Sheikhul Islam Ibn Taimiya akunena kuti: “mau oti anali Is’ha ndi ochokera kwa Ahlul Kitaab (Ayuda) komanso ndi abodza, chifukwa mabuku awowo amakamba zoti Allah analamula kuti mwana oyamba komanso yemwe anali yekha, azingidwe, tsopano mwana oyamba wa Ibrahim anali Ismail osati Is’haq. Ndipo Asilamu ndi Akristu onse amadziwa zoti mwana oyambilira wa Ibrahim anali Ismail.” Apa zikutanthauza kuti mmabuku mwawomo (Akristu ndi Ayuda) muli zonena kuti Allah analamula Ibrahim kuti azingwe mwana oyambilira kubadwa, ndiye nzodziwika kuti Islami anali mwana wake oyambilira kubadwa asanabadwe Is’haq. Akanalamulidwa kuti azinge Is’haq, ndiye kuti sakanalamula kuti azinge mwana woyamba komanso mmodzi yekha, chifukwa Is’haq anabadwa pambuyo pa Ismail ndipo mmene amabadwa Ismail anali alipo kale. Komatu zomwe zinawasokoneza anthu amenewa ndi mau omwe analembedwa mu Taurat  onena kuti “zinga mwana wako Is’haq”…mau awa ndi owonjezera pamene anasintha Taurat yawo, chifukwatu pamenepa pali kupanga contradict ndi mau oti: “zinga first born wako yekhayo yemwe uli naye”. Koma Ayuda anachita jelasi kuwachitira ana a Ismail pa ulemelero umenewu ndipo anafunisitsa kuti ukhale pa iwo. Koma Allah amakana kupititsa ulemelero kosakhala kwa oyenera.

Ibn KJathir ananena mu Tafsir yake kuti: “pamene Ka’b Al Ahbaar analowa Chisilamu munthawi ya Umar radhia Allah anhu, anali kumfotokozera Umar zomwe mabuku achiyuda analemba zokhunza nsembe ya Is’haq, ndipo anthu omwe amavetsera kulongosolaku anadzitenga nkhani zija nkumadzifalitsa. Choncho report loti yemwe ankafuna kuzingidwa anali Is’haq, Mchisilamumu linachokera mkamwa mwa Ka’bul Ahbaar pamene ankalongosola zakale, koma sikuti ndi mmene zinakhalira.” Tafsit bun Kathir vol.4 p42.

نسأل الله عز وجل أن يرفع درجة إبراهيم عليه السلام، وأن يجعلنا من المنتفعين بسيرته وسيرة نبينا صلى الله عليه وسلم والله تعالى أعلم. وصلى الله على نبينا محمد

Timpemphe Allah Ta’la amuike Ibrahim alaih salaam pamwamba, komanso atipange ife kukhala omwe tikutsatira Sunnah zake komanso Sunnah za Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam.

Translated from: Sheikh Saalih Al Munajjid’s Khutbah for Eidil Adh’ha