GAWO LACHIWIRI
 
Imodzi mwa nkhani zovuta kudzimvesetsa chifukwa cha kuchepekedwa kwa maphunziroku ndi yomwe ndikufuna kulongosola lero…ndipo pankhaniyi ndakhala ndikuona ma sheikh omwe akhala akuyesetsa kuwalongosolera anthu, akunyozedwa poyankhuliridwa mau osiyanasiyana, monga kunena kuti: “inutu mukubweretsa zachilendo mu deenimu. Ma sheikh omwe analemba zitabu zomwe tinaphunzira ifewo ngati zimenezi sanalembe ndiye kuti sanaphunzire koma inu? Nthawi yonseyi inu musanabadwe makolo athu anali kuphunzira zimenezi munalibe zomwe mukukamba inuzi, mwabwera inu mwati mwaphunzira zitabu zolembedwa ndi ma shia mwati musocheretse nazo anthu.
Nkhani yaketu ndi NDIZOLOLEDWA KUSWALI NDI NSAPATO KUPHAZI
Nkhani ya kuswali utavala nsapato ndi imodzi mwa nkhani zomwe ambiri samayankhula, amati ndi controversial issue (nkhani yobweretsa kusempahan pakati pa anthu, nkhani yomwe ma ulamaa anasemphanapo). Koma zimenezo nzabodza. Anthu amatero chifukwa mmene ndanenera muja kuti anangozolowera kuvula nsapato nkumaona kuti ngati kuvala nsapato swalat singalandiridwe. Contoversial issue imakhala yodziwika, yomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam sanayankhulepo kanthu, sanachiter komanso ma swahaba sanachite. Imeneyo imakhala mmanja mwa ma Ulamaa mpamene amasiyana maganizo nkusanduka kukhala controversial. Koma nkhani ikakhala kuti Mtumiki anayankhulapo straight forward, ife tisayiope powauza anthu, tiwauza zomwe Mtumiki anayankhula zomwe ziri zoona sizompekera, chifukwa imeneyo ndiye deeniyo.
 
Nkhani ya kuswali ndi nsapato kuphanzi, inasonkhanitsidwa mu buku lotchedwa
 السنن والمبتدعات المتعلقة بالأذكار والصلوات زمعه رسالة في الأمر بالمعروف والنهي عن المنكر 
Lolembedwa ndi
 محمد بن أحمد بن محمد عبد السلام خِضر الشقيري الحوامدي, 
yemwe amangotchulidwa kuti
الشقيري.
Ameneyu ndi founder wa
جمعية السلفية بالجوامدية.
Ndipo anaikira ndemanga pa bukuli
الشيخ محمد بن حامد الفقي
komanso anawunika ma hadith ndi nkhani zonse mu bukuli
الشيخ محمد ناصر الدين الألباني.
Ndipo mubukuli mukupezeka ma fatwa ofunikira kwambiri pa nkhani za Sunnah ndi ma Bid’ah, ma Fatwa ochokera kwa
الشيخ محمد بن صالح العثيمين رحمهم الله تعالى.
 
Pamene anthu anaona chithunzi cha asilikali a Chisilamu a dziko lina lake akuswali mu nkhalango atavala nsapato, anali odabwa kwambiri ndipo kachithunzi kameneko kanazungulira ndithu mma social media; kuchokera ku facebook, ku whatsapp, mma group, mma inbox … nkhani yake nkumati zimenezitu nzachilendo izi, mpaka kuswali ndi nsapato zoona?
Choncho izi zinabweretsa mpungwepungwe ndithu mma social media kotero kuti ena anatulutsidwa Chisilamu, ena anatchedwa ma Shia, ena anatchedwa a bid’ah, ena anatchedwa ambuli, ena anatchedwa ma Wahabi ndi zina zotero. Allah atipatse kuzindikira mu deen.
Zonsezitu sikuti anthu amasutsana kuchokera mu Qur’an kapena Sunnah, koma kuchokera ku zomwe anazolowera kuti kutero ndi haram. Akanakhala kuti anakhala chete nkufufuza mu Sunnah, ndithu akanapeza hidaaya yochokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam ili straight forward.
Choncho lero lino ndikubweretserani sunnah ya kuswali ndi nsapato kuphazi, yomwe ife timasemphana nayo poganiza kuti ndi uve. Tikangomvatu nkhani imeneyi, timaganizira zinthu zitatu izi:
 1. Tikamafuna kuswali timayenera kuonesetsa kuti zovala zathu zili ndi twahara, thuhpi lathu liri ndi twahara, komanso malo omwe tikuswalira ali ndi twahara. Kodi tikavala nsapato, sindiye kuti tikulowetsa nyansi paswalat?
Funso ili Mtumiki anayankha, tingomvetsera kutsogoloku in sha Allah
 1. Akristu amapemphera ndi nsapato, kodi ife tikamavala sitimafanana nawo? Nanga poti Mtumiki anati “Yemwe adzifanizire ndi gulu lina ndiye kuti ali mu gululo” sitikhala ngati akhristu?
Funso ilinso anayankha Mtumiki salla Allah alaih wasallam timva kutsogoloku
 1. Mu Qur’an timawerenga kuti Allah Ta’la anamuuza Musa alaih Salaam kuti avule nsapato poti ali pa chigwa choyera cha Tuwa…kuchokera pamenepo timatengera kuti tikakhala malo olemekezeka monga pa swalaat tidzivula nsapato. Kodi pamenepa sitikusemphana ndi sunnah ya Mtumiki Musa alaih Salaam? Ngati zimenezi zili zolondola kuti tidzivala nsapato, umboni wake uli kuti?
Mafunso onsewa, mayankho ake ndi omwe ndabweretsa mu ulaliki umenewu, ndipo ndikupempha kuti timvetsere modekha.
Kuswali ndi nsapato kuphanzi ndi mustahab, ndi zololedwa ndithu, ndipo izi maumboni ake ndi ma hadith opanda zigamba, omwe akupezeka mu mabuku kapena kuti mzitabu zonse 6 za Hadith.
 
 1. Akulongosola pa page 55 mu chitabu ichi cha
  السنن والمبتدعات,
  kuchokera mu hadith yomwe ikupezeka mu Sahih Al Bukhari ndi Muslim, komanso mu Sunan Al Tirmidhi, yochokera kwa Abi Muslimah Saeed bun Yazeed, yemwe anati: “Ndinanena kwa Anas bin Maliki kuti: Kodi Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kuswali ndi nsapato? Anati: inde.
Hadithiyi ikupezeka mu Sahih Al Bukhari #279 ndi #5512, komanso mu Sahih Muslim #555
 1. Abu Daud kuchokeran mu Sunan yake (mu chitabu chake cha Sunnah), hadith yomwe inachokera kwa Saeed Al Maqbari, kuchokera kwa bambo ake omwe anamva kuchokera kwa Abi Huraira, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “ngati mmodzi wa inu waponda zoipa ndi nsapato zake, ndithu dothi ndi twahara yake (ya zoipazo).
Hadithiyi ikupezeka mu Suna Abi Daud #385, komanso mu Al Mustadrak ya Al Haakim vol.1/271, ndipo ndi ya sahih (yabwinobwino)
 
 1. Kuchokera mu Sunan Al Nasaai, Hadith yochokera kwa Ummil Mu’mineen ‘Aaisha radia Allah anha anati: Ndinaona Mtumiki salla Allah alaih wasallamakumwa chiimire komanso chikhalire, ndipo akuswali asanavale nsapato komanso atavala nsapato, komanso akutembenukira kumanja ndi kumanzere kwake.
Hadithiyi ikupezeka mu Sunan Al Nasaai #1361 ndipo isnaad yake, kapena kuti chain chake ndi chabwinobwino
 
 1. Kuchokera mu Sunan bun Maajahnso chimodzimodzi, ndipo muli hamdith yoti: Agogo anga Ausi nthawi zina amati akamaswali, anali kundilozera ine ali pa swalat, pamenepo ndimawapatsa nsapato zawo ndipo amanena kuti: “Ndinamuona Mtumiki salla Allah alaih wasallam akuswali ndi nsapato” Komanso mu buku la
  الجامع الصغير,
  Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Mudziswali munsapato zanu, ndipo musafanane ndi Ayuda.”
Hadithiyi ikupezeka mu
الجامع الكبير
ya Al Tabaraani vol.7/290 ndipo ndi hadith ya sahih yopanda mphenya.
 1. Komanso kuchokera mu buku lomweli la Al Tabaraani, hadith yochokera kwa Shaddaad bun Aus, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Musiyane ndi Ayuda, chifukwa iwo samapemphera atavala nsapato, ngakhale Khuff
Hadithiyi ikuchokera mu Sunan Abi Daud #652, komanso Al Baihaqi, ndipo ndi ya sahih, yabwinobwino
 
Zimenezitu ndiye ndi zitabu zonse za Hadith, zokwana 6 zomwe tikuzidziwa zija, ndipo ma Hadith onse okamba za kuswali ndi nsapato kuphazi ndamenewo owona ohkaokha, palibe ya dhaeef kapena kuti yofooka. Tikupeza kuti mma hadith ena, Mtumiki salla Allah alaih wasallam waloleza molamula kumene kuti valani nsapato poswali. 
Zikafika pamenepo pamakhala palibenso kusemphana kwa ma Ulamaa pa zokamba zawo, ngati Mtumiki wayankhula directly. Ma Imaam onse anayi aja omwe ndi madh’haba Abi Hanifa, Maliki, Shaf’i, Hanbali, onsewo palibe amene anasemphanapo kuchokera mu zomwe anakamba Mtumiki salla Alaih wasallam mwachindunji, moonekera mosakaikira. Kodi lero lino inu ndi ine ndichani chomwe chingatiletse kulongosola mmene Mtumiki analongosolera? Kuopa kuti tisokoneza anthu pa zomwe anazolowera? Tiwasiya anthu adzichita zinthu mwaumbuli momwemo asakudziwa haqq yeniyeni, tisabise haqq…kubisa ‘ilm ndi chilango kwa Allah Ta’la. Palibenso controversy apa ma Sheikh, tiwauze anthu momveka zinthuzi.
 
Tatiyeni tsopano tione zomwe ma Imaam athu anayi aja anayankhula pa nkhani imeneyi … pambuyo pa zonse, ma Sheikh mokuprmphani, musakhalenso ndi zokamba zanuzanu pankhaniyi kuposera zomwe ma Ulamaa anakamba zochokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.
Palibe kusiyana kwa madh’hab pankhaniyi, mwina ena nkumati “Ife timatsatira madh’hab akutiakuti, zimenezo sitipanga…” Dziwani kuti madh’hab onse anayi omwe ndi a Sunnah, amayendera zomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kuchita, ndipo ngati madh’hab anu omwe mukuti mumayenderawo akusemphana ndi Sunnah, dziwani kuti simuli mmadh’hab a Sunnah za Mtumiki koma a bid’ah kapena a ajawa omwe amadana ndi ma Imaam onse anayi a Ahlu Sunnah…sindiwatchula…
 
Madh’hab a Abi Hanifah (A Hanafiyyah) akutinji pa nkhani yoswali ndi nsapato kuphazi:
Sheikh Abdul Majid Salim, Mufti wakale wadziko la Egypt, anapereka Fatwa yomwe inatsindikizidwa mu newspaper mchaka cha 1928, pambuyo pa kulongosola ma hadith a Sahih, ndipo analongosola motere:
Kuchokera mu
شرح منية المصلي
buku la Ibrahim Al Halabi, mmau omwe anachokera mu
فتاوى الحجة
oti: “Swalat ya munsapato ili bwino kuposa swalat yopanda nsapato, chifukwa pali kusiyana ndi Ayuda…”
Ndipo anati: kuchokera pamenepa, zikudziwika kuti swalat ya munsapato za twahara zopanda nyansi, ndiyololedwa, ndipo ma ulamaa ambiri ananena kuti ndi zokondedwa – mustahabba…
 
Madh’hab a Malik (Al Maalikiyyah) akutinji pa nkhani yoswali ndi nsapato kuphazi:
Al Hafidh Abu Bakr Muhammad bun Abdillah, yemwe amadziwika ndi dzina loti Ibnul ‘Arabi Al Maalikiy rahimaullah ananena mu
شرح على سنن الإمام الترمذي
mmawu omwe akupezeka pa khomo lokamba za kuswali mu nsapato: Zinatsimikizika kuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam  kuti anaswali ali munsapato, monganso mmene zinatsimikizidwa kuti anali kupanga wudhu ali munsapato.
 
Madh’hab a Shafi’i (Al Shafi’iyyah) akutinji pa nkhani yoswali ndi nsapato kuphazi:
Ngakhalenso Imam Al Ghazaaliy, ananena mu buku lake la
الإحياء
kuti: Swalat ya munsapato ndiyololedwa ngakhale kuvula nsapatozo kuitakhala kosavuta, ndipo sikuti zikulolezedwa kuswalira mma khuff  chifukwa cha kuvuta kwake povula, koma kuti najs yake yamunsapatoyo imakhala yokhulukidwa – akutanthauza zomwe zapondedwa ndi nsapatozo…
Mtumiki salla Allah alaih wasallam anaswali ndi nsapato zake, kenako anadzavula, ndipo anthu anavula zawo chimodzimodzi. Mtumiki anati: “nchifukwa chani mwachotsa nsapato zanu?” anati: takuonani inu Mtumiki mutavula, choncho nafe tavula pokutengerani zomwe mwachita. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “ndithu Jibril alaih salaam anandifikira nkundiuza kuti nsapato zanga zili ndi zoipa, choncho mmodzi wa inu ngati wafuna kulowa munzikiti, adzitembenu7za nsapato zake ndikudziyang’ana, ngati ziri ndi zoipa adzichotse ndi dothi (adzipukutitse pansi) ndipo aswali nazo”. Apatu ena anayankhula moonjezera kuti: kuswali munsapato ndikwabwino chifukwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam ataona kuti anthu avula nsapato zawo, anafunsa kuti: “nchifukwa chani mwavula nsapato zanu?”. Kumeneku nkuonjezera, koma Mmtumiki salla Allah alaih wasallam mmene amawafunsa anthu aja cholinga chake kunali kufuna kudziwa chifukwa chomwe chawapangitsa kuti avule, ndipo anadziwa kuti anavula pomutsatira iye salla Allah alaih wasallam.
 
Al Zubaidiy Shaarih wa buku limeneli la anati: Ma Ulamaa anagwirizana muzokamba zawo, sanasiyane kuti kuswali munsapato komanso zina zomwe zimavalidwa kuphazi ndi kololedwa  pa swalaat za faradh ngakhale za nafl, komanso pa swalatil Janaazah, swalaat ya wa paulendo ngakhale ngakhale wokhanzikika. Ndipo anati chimodzimodzi ngakhale munthu atakhala kuti akumayenda nazo nsapatozo munsewu kapena ayi, chifukwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndi ma Sahaba ake anali kuyenda munjira za Mmadina ndikumaswali atavala, komanso anali kulowa nazo muthengo…
 
Madh’hab a Ahmad bun Hanbal (Al Hanbaliyyah) akutinji pa nkhani yoswali ndi nsapato kuphazi:
Imaam Ibn Al Qayyim ananena mu buku lake la
إغاثة اللهفان 
kuti: ndipo muzinthu zomwe sizimakhalira bwino mmitima ya anthu omwe amasokonezedwa ndi manong’onezi oipa, ndi nkhani ya kuswali ndi nsapato kuphazi, yomwe ndi sunnah ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndi ma Sahaba ake, analamula komanso anachita. Anas bun Maalik radhia Allah anhu anati: ndithu Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kuswali ndi nsapato” Hadith ya Sahih Al Bukhari ndi Muslim monga mmene tanenera kale mbuyomu. Ndipo anapitiriza ndi hadith ija ya Shaddaad bun Aus ponena kuti: ndipo Imaam Ahmad anafunsidwa kuti: Kodi munthu angaswali ndi nsapato kuphazi? Anayankha kuti: Ndipotu Wallah, anthu omwe amasokonezedwa ndi manong’onezi (omwe amaganiza kuti sizololedwa), thawi ya swalatil Janaaza, amaima pansapato zawo ndi zitendene, kukhala ngati aima pa khala lamoto, ncholinga choti asaswali atavala nsapato
 
Umotu ndi mmene ziphunzitso za ma imaam onse anayi omwe tikuwadziwa komanso timawatsatira ziphunzitso zawo, akunenera.. Koyamba kaja tamba mau ochokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndi ma Shaba ake, kuti ndithu, kuvala nsapato pa swalaat ndi kololezedwa komanso kulolezedwa kwake kosakaikidra, kochita kulamula kuti swalini munsapato. Nawo ma imaam athu awa palibe chomwe anganene chosemphana ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam ndi ma sahaba ake. Anadutsanso momwemo ndithu. Ndiye lero inu ndi ine nkumati ayi tisawauze anthu kuti adziswali ndi nsapato chifukwa tiwasokoneza…kuwasokoneza nkumene tikuchitako powabisira mmene Mtumiki ankaswalira, yet timawalalikira anthu hadith yoti
صلوا كما رأيتموني أصلي
uku nkumabisa mmene anali kuswalira. Allah atikhululukire.
 
Enatu amanena kuti aaah zimenezo panthawi inoyo zilibe ntchito chifukwa mmizikiti yathu masiku ano timayalamo, ndiye kuti aliyense adzilowamo ndi nsapato sitiipitsamo ndi dothi? timayalamo ma carpet odula sitingamawadetse ndi nsapato, pomwe nthawi ya Mtumiki munzikiti sankayala zokongola ngati zathuzi. Ena amati oo inu ngati mumavula nspato zanu polowa mnyumba mwanu, pogona mumavula nsapato…mnyumba mwanu ndi mnyumba ya Mulungu momwe muli molemekezeka ndi muti? 
Ehe, apa tikuyendera maganizo athu tsopano. Zofunika ngati tamva kuti nkhaniyi ananena ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam, tisachuluke nzeru zosemphana ndi hadith, komanso tisapange react pomuyankha yemwe akuyankhula. Koma tifatse nkuchetelera mau a Mtumiki kuti amatanthauza chani. Ineyo mukhonza kundiyankha mmene mungathere, koma palibe chomwe ndikulakwitsa poti ndikungokupatsani zomwe Mphunzitsi wamkulu anatiuza. Choncho mtsutso uliwonse ndiye kuti mukuchita ndi ma Hadith, osati ine.
Dziwani kuti mizikiti yathuyi ngakhale tingaimange motani, ngakhale titaikongoletsa chotani, kaya tiyala pansipa carpet ya golide, koma zonsezo sizingakhale zokongola kapena kulemekezeka kuposa mzikiti wa Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Palibe mzikiti umene ungamangidwe padziko lapansi lero ngakhale kutsogoloku nkukhala wolemekezeka kuposa Makka ndi Madina. Ndipotu kuti tionesetse mmalamulo, tipeza kuti kukongoletsa mizikiti komwe anthu akumachita mmizikiti masiku anoku ndikoletsedwa mu Chisilamu. ukhondo umafunikira, koma tikupyola nazo muyeso mpaka kugwera mu zolakwika nkumadana ndi zovomerezeka komanso zomwe zili sunnah.
 
Ndiye apa tiuzane chilungamo. Nzololedwa munthu kuswali ndi nsapato, komanso kuvula nsapato. Zonsezo nzololedwa ndithu. Ngakhale nthawi ya Mtumiki munzikiti ankayalamo, sikuti amaswali padothi malinga ndi mmene ena amaganizira. Komanso kukongoletsa mmizikitiko kumapangidwa design chifukwa choti timapanga zoti anthu samadzalowamo ndi nsapato. Koma sizinachokere kwa Mtumiki kuti tidzitero.
Choncho nkhani ndi imeneyo, zili kwa ife kudzitenga kapena ayi. 
zili kwa ife kutsatira sunnah kapena ayi. Tikakhala ife ndiye talamulidwa kufalitsa zoona ndipo taletsedwa kubisa zoona za mu deen chifukwa cha kuopa munthu. 
 
Zimenezo ndi zomwe ndinakutengerani kuchokera mu
السنن والمبتدعات
page 55 mpaka 57 ndipo muzomwe ndalongosolazi mulibemo maganizo anga, koma zonse zikuchokera mma Hadith, komanso mma aqwaalul Ulamaai.
 
Nkhani imeneyi ikupezeka mu zitabu zambiri makamaka zolongosola nkhani ya swalaat, ndipo ma hadith ake ndi omwe mwawamva pakalipanowo…tayangananinso mu chitabu ichi cha
 الشيخ محمد ناصر الدين الألباني 
chotchedwa
أصل صفة صلاة النبي صلى الله عليه وسلم  من التكبير إلى التسليم كأنك تراه, 
chija chomwe chikufotokoza momveka bwino mapempheredwe enieni a Mtumiki salla Allah alaih wasallam, ndipo nkhani imeneyi muipeza pa page 108 pa mutu woti:
باب الصلاة في النعال والأمر بها 
(Khomo la kuswali mu nsapato komanso kulamulidwa kwake).
 
Pomaliza ndikupempha Allah Ta’la kuti awupange uthengawu kukhala imodzi mwa njira zowongolera ummah ku chiwongoko komanso kuwonjezera ‘ilm. Komanso isakhale njira yopititsira Ummah ku chisocheretso, ndipempha Allah Ta’la abise mau onse omwe ndakamba oti akhonza kusocheretsa ummah, ndipo awaonetsere poyera mau omwe ali othandiza kulondolera Ummah ku Chiwongoko chake Allah Ta’la.
Ndikupempha nonse kuti mu zomwe mwawerengazi mutenge zomwe zikuchokera kwa Mtumiki salla Allah alaih wasallam, zomwe zikuchokera kwa ma Imaam athu a Olemekezeka, zomwe zikuchokera kwa ma Ulamaa, muzomwe zatuluka mkamwa mwangamu, ndipo musiye zomwe ndayankhula moonjezera zolakwika, malinga ndi kuthamanga kwa lirime lodya za mchere. 
Ntchito iriyonse ya munthu silepherea zolakwika, kupatula ya Mulungu Allah Ta’ala. Choncho tiyeni tikhale mu anthu aja omwe Allah Ta’la anawachemelera kuti ndi akapolo ake abwino omwe akumvetsera mawu ndikutsatira amene ali abwino kwambiri  ndi owongolera ku choona, iwo ndi amene Allah awawongola ndipo iwowo ndi eni nzeru. Surah Al Zumar 17-18
 
Wassalam Alaikum warahmatullah wabarakaatuh