بسم الله الرحمن الرحيم
الحمد لله رب العالمين والصلاة والسلام على رسوله الكريم وعلى آله وأصحابه ومن تبعهم إلى يوم الدين أما بعد
Pali mitu yomwe imakambidwa ndi ma Sheikh, yomwe ndiyofunikira kwambiriimene munthu amati akangoyankhula, anthu omwe sazindikira – Allah atipatse kuzindikira – amafulumira kumunena munthuyo kuti ndi mShia, chifukwa choti nkhani yomwe akulongosolayo ndi ya chilendo kwambiri kwa iwo. Indetu, chifukwa choti sanayambe amvapo kuchokera kwa Sheikh wina aliyense akuyankhula. Chifukwa choti zikusemphana ndi zomwe anazolowera kuchokera ku umwana wawo. Chifukwa choti ndi zomwe anaphunzira ku madrasa ali mwana ndipo atasiyira panjira, anaganiza kuti basi zimenezo ndiye zomwe ziri zoona palibenso zina zomwe zatsala chemwalimu sanatiphunzitse.
 
Choyamba, ndichenjeze kwa Asilamu anzathu kuti Chisilamu chimafunika kuchiphunzira mopitiriza osati kusiyira panjira. Osati kungomaliza Tarteebu Sswalat kapena Mabaadiul Fiqhiyaa basi pamenepo Chisilamu taphunzira. Dziwani kuti zomwe timaphunzitsidwa ku madrasa tili achichepere zija zimakhala kalambula bwalo wa maphunziro enieni. Zimakhala zongofuna kutisuntha standard 1 kupita 2, kenako 3 mpaka 4, poti timakhala ana achichepere, ndiye ma Sheikh amafuna kuti tidziphunzira pang’onopang’ono za size yathu, kenako tipite kutsogolo, kutsogolokonso tipite kutsogolo kwake kuti tikakumaneno ndi zotambasulidwa zenizeni zolingana ndi nzeru zathu zomwe zakhwima kuchokera mu akalambula bwalo aja. Choncho mistake yaikulu imene ambiri tinachita komanso timachita mpaka pano ndiyoti sitimapitiriza pamene tinasiya tili ana, ambiri madrasa timaphunzira ku Primary, ndipo chongolowa Secondary basi madrasa timasiya kuphunzira, akuti kuopa kusokoneza mutu. Tikangomaliza secondary ija basi timafuna kukhala ma Sheikh pogwiritsa ntchito Tarteeb Swaalat kapena Mabaadiul Fiqhiya zija ngati ma source athu akuluakulu ku Fiqh. Ndiyetu basi timakhala natilimbana ndi ma Sheikh omwe aivutikira ‘ilm kukafika nayo patali akuzungulirazungulira mwa ma Sheikh akuluakulu mMalawi muno ngakhale kunja, kutolera zambiri. Tikakuma ndi ma Sheikh amenewa mma platform monga facebook kaya whatsapp, akamalongosola zinthu zikuluzikulu, chifukwa choti sizikupezeka mu tizitabu ta kalambula bwalo tija, timayamba kutsutsa kuti ayi zimenezo nzabodza mu Chislamu mulibe. Ndiye timawapatsa reference ija kuti akawerenge mu Tarteeb Salaat, mukawerenge Fiqh 2…yaa salaam! Osadziwa kuti ifeyo pamenepo ndamene tili mbuyo kwambiri. 
Ndikufuna tidziwitsane lero kuti zitabu zomwe timaphunzira ku primary zija ndi dontho chabe la maphunziro, mmene ndanenera muja kuti okhonza mabuku amenewo anakhonza malingha ndi ma level athu. Choncho munthu ukamapitabe kutsogolo, umakhumana ndi mabuku oti mutu uliwonse wa mu buku la ku primary lija awulongosola motambasula.Tipeza kuti ku primary timaphunzira kuti poswali tikuyenera kupanga niyyah, ndipo pofuna kuti tidzikumbukira kufunika kwa niyya poyamba ibaada iriyonse, amatiphunzitsa kuti tidzinena kuti “nawaytu uswali swalaatal fajr rakatain lillahi ta’la maamuman…Allah Akbar” tikamafuna kusala, usiku timayenera kupanga niyya p[onena kuti “nawaytu swauman ghadi, ‘an adaail faradhwa Ramadhan lillah ta’ala…” choncho ndi ibaada ina yonse.. Komatu izi zimapezeka ku primary kwa ana ang’onoang’ono malinga ndi kuzindikira kwawo, komano akamakula napita patsogolo ndi maphunzirowo, amayamba kukumana nszo tsopano zochokera muFiqh yomwe ija, zikuwauza kuti “Niyyah sitimayankhula ndi lirime, koma timangotsimikiza mumtima”. Ndiye zimapezeka kuti munthungati maphunziro amenewa anwajowa nkuthamangira usheikh, akakuma ndi anzake omwe anaphunzira mopitilira, amayamba kusutsa kuti ayi zimenezo ife tinapohunzira kuti niyyah timayankhula zakutizakuti.
Vuto lachokera pati? Kuphunzira mwachidule za deen…kuphunzira pofananitsa ndi za secular. Za secularso chabwino ngati mwapeza MSCE, za deen pitirizani mupeze ‘ilm osati MSCE. 
Pali nkhani zambiri zomwe ma sheikh akamalongosola ndi maumboni ochokera mu Quran ndi Sunnah, anthu omwe sadziwa amakanira kuti izo ndi zachilendo ndipo nza ma Shia.
Nkhani zina ndi monga 
a. Kunyamula manja pa dua
b. Kupanga dua ya pagulu pambuyo pa swalaat
c. Kupukuta knkhope pambuyo pa dua
d. Mkazi kuzinga nkhuku
e. Mkazi kusambitsa maliro ali ku mwezi kapena mwamuna ali ndi janaba ndi zina zambiri, zomwe anthu tinangozolwera poti tinawapeza azigogo athu omwe anamenyera ufuludeeniyi kuti tiyipeze, akuchita. Ndiye timangoti deen ndi choncho.
Tiwapemphere ma dua komanso chikhululuko makolo athu omwe anamenyera ufulu wa Chipembedzi chathu mdziko kuti mpaka tichiopeze, Allah awaie malo a Mtendere. Komanso awakhululukire zolakwika zomwe anali kuchita pa ibaada, poti nthawiyo kunalibe njira zokwanira zopezera maphunziro a deen, kwa iwo anangokwanitsa kusamala ufulu wa deen. Chonchoi ife tiphunzire mwakathithi kuti tiyendetse deen mmene Qur’an ndi Sunnah ikufunira, osati kulimbana ndi za makolo, deen ndi ndi ya Allah ndi Mtumiki wake. Tiyeni maso pa lemba osati pa makolo athu. 
Analikotu kale anthu omwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam anawapeza, ngati mmene amatipezera ife ma shemikh nthawi zino; anthuwa amati akawalalikira za kulakwika kwa zomwe anali kuchita, ankayankhanso chimodzimodzi mmene tikumawayanhkuira lero ma sheikh, ponena kuti “tinawapeza azigogo athu akupanfga zimenezi”. Izi zatsimikizika mu Qur’an pamnene Allah TYa’la akunena kuti:
 
{وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ تَعَالَوْاْ إِلَى مَا أَنزَلَ اللّهُ وَإِلَى الرَّسُولِ قَالُواْ حَسْبُنَا مَا وَجَدْنَا عَلَيْهِ آبَاءنَا أَوَلَوْ كَانَ آبَاؤُهُمْ لاَ يَعْلَمُونَ شَيْئاً وَلاَ يَهْتَدُونَ }
Ndipo akauzidwa: “Tadzani kuchilamulo cha zomwe Allah wavumbulutsa ndi (zomwe akunena) Mtumiki,” Akunena: “Tikukwaniritsidwa ndi zomwe tidawapeza nazo makolo athu,” Kodi chinkana kuti makolo awowo sadali kudziwa chinthu chilichonse ndipo sadali oongoka, (awatsatirabe)?
Allah Ta’ala akamafunsa funso mu Qur’an sikuti kumakhala kusadziwa, Iye ndi Odziwa chirichonse; koma kumakhala kuipidwa komanso kuonetsa kuipa kwa chikhalidwe chimene akukuletsanicho.
Choncho ndi zinthu zoipa kwambiri komanso nzonyansa kwambir mu Chisilamu, kuti munthu adzinena kuti “ife ndiye ndambuli palibe chomwe tidziwa” nkungokhala osaphunzira. Mmene ndanenera kale muja kuti oteroyo ndiye kuti akuchita zolakeika kumachita akudfziwa kuti nzolakwika, ngati akudziwa kuti sakudziwa. Tiyeni tiphunzire deen mopanda malire, osadzikweza, osachita manyanzi. Anthu awiri awa sangaphunzir: odzikweza (poganiza kuti maphunziro ndi a ana ndipo iye wakula sangaphunzire ndi ana kapena kuphunzitsidwa ndi mwana). Wamanyazi (pochita manyazi kufunza za deen zomwe ndi zoti akachita mwaumbuli zimuponyera ku tchimo)
 
Chisilamu sichimafuna mbuli. Umbuli wochita kudzimva kuti ndine mbuli nkumangokhala nawo kuti poti ndine mbuli, ndiwoletsedwa. Chifukwa pamenepo ngati mwazidziwa kuti ndinu mbuli koma mukungokhala osaphunzira, kalikonse kamene mungachite mwaumbuli nkulakwitsa, mumalembedwa machimo chifukwa choti mwachita mwaumbuli pomwe mukudziwa kuti ndinu mbuli koma simukufuna kuphunzira. Choncho Msilamu asadziyanike padwale nkumanena kuti ndine mbuli ndidzingopanga choncho basi Allah adzandikhululukira. ayi. 
Ena  ndinamva akuyankhula kuti “Ma sheikh inu mukungosutsana zinthu tsopano ambulife ndiye tidziti chani? aa basi ine nditsala ndi umbuli wangawu bola ndidzipanga zomwe ndinazolowerazo, bola ndidzipanga zomwe ndinawapeza azigogo akupangazo, ngakhale mudziti ndi bid’a koma ine basi ndidzipanga.” kuyankhula uku ndi kwa umbuli poti yemwe akuyankhulayonso ndi mbulidi. Allah atipatse kuzindikira.
 
Chomwe chimafunikira ndi choti Msilamu adzikhala ofunafuna  maphunzioro. Dziwani kuti maphunziro a Chisilamu sali ngati a za dziko (secular) komwe mumaphunzira kuti mupeze certificate mukhale ndi ulemelero pa dziko. Maphunziro oterowo amakhala a kanthawi, ndipo amayendera msinkhu wa munthu, chifukwa ndi zinthu zoti zikuthandize pa dziko pano. Pomwe maphunziro a deen ndi okuthandiza padziko pano, mu deen komanso ku aakhira … ndiyetu 3 vs 1. Choncho pachifukwachi, maphunziro a deen alibe malire. Alibe kuti basi pelepa njekulwipe nginalijiganya atamose syome chiingamuchisye china ya? iyayi, maphunziro a deen si choncho.
 
Ndiye chifukwa cha kudzipatsa malire a kuphunzira deen, zimapezeka kuti tikukanira zomwe anzathu akuphunzira nkumatilongosolera. Mapeto ake timawaona ngati kuti akuphunzira za ma Shia, ndipo timawapanga kuti ndi ma Shia poti akubweretsa zomwe sitikuzidziwa. Dziwani kuti maphunziro a deen ali ngati nyanja, sitingawamalize. Choncho chomwe tingamachite nchoti ngati tamva zachilendo, tidzifufuze kaye tisanamuponye munthuyo mu bid’ah, kufr kapena shirk. 
Apa pali mavuto awiri ofunika kukhonzedwa ku Malawi: 1. Kuwadziwa ma Shia. Mashia sikuti tingawadziwe powaona kuti akupanga zomwe ife sitikuzidziwa. Mashia samaswali ndi nsapato kuphazi, koma Sheikh wina akangoti nzololedwa kuswali ndi nsapato, timampanga kuti ndi mShia.
2. Kuphunzira deen molongosoka, kupitiriza pamene tinasiyira paja. Masiku ano alhmadulillah maphunziro a deen ali ponseponse. Tili ndi ma bureau mmene mukupezeka zitabu ndi mabuku a ma level osiyanasiyana, komanso mmenemo muli ma Sheikh amene amalongosola ndikuyankha mafunso kwa omwe adza kudzaphunzira. Tili ndi ma social media mmene tikumangoseweramu, tikakumana ndi Sheikh mmalo mopezera mwai woonjezera maphunziro, tikumayamba kulimbana naye kumuwukira. Kufuna kutsalira ndithu.
Allah atipatse kuzindikira.