Mtsikana wa Chisilamu akatha msinkhu ndiokakamizidwa kuvala Hijaab ngakhale niqaab monga mmene ali okakamizidwira kugwira ntchito zina zonse cha Chisilamu monga swalaat swiyaam ndi zina zotero. Tikamati Hijaab, sitikutanthauza kampango kamene mumavala kumutuko ayi, imeneyo si hijaab ya Chisilamu koma mpango chabe. Zimapezeka kuti mzimai kaya mtsikana wavala zodula manja, kapena dress lothing lalitali bwino, ndikuvala mpango kumutu nkumati wavala hijab ya Chisilamu, ayi ndithu palibe chomwe mwachita pamenepo. Hijab ndi chovala chomwe chimabisa thupi lonse, sichimaonetsa momwe mwadutsa ziwalo monga kuthina, sichimaonekera mkati, komanso sichimalembelera maonekedwe a thupi monga mmene zimakhalira akavala chitenje … mzimai asavale chitenje mchiuno poyenda munsewu, chifukwa chimasemphana ndi lamulo la hijab, chimalekanitsa chiuno ndi thupi nkunyamula mbuyo.

Hijaab ndi chimodzi mwa malamulo a Chisilamu ndipo mkazi yemwe watha msinkhu ndiolamulidwa kuvala. Yemwe akuvala amalandira palipiro ndipo yemwe sakuvala amapeza nsambi zomwe zikamuotche tsiku la Qiyaamah

Sindilowa kwambiri mu zina ndi zina, koma ndikufuna kukamba za chovala ichi chotchedwa Niqaab. Kodi pali kusiyana kwanji pakati pa Niqaab ndi Hijab? Niqaab ndihijaab (chophimba), imaphimba thupi lonse pomwe. Ndipo Hijab ndi chophimba mbali ina ya thupi. Zonsenzi ndi Hijaab.

Ambiri tikudziwa za hijaab ndipo palibe chomwe chmakambidwa chachilendo pankhaniyi, koma kuti anthufe timangonyozera tokha, kukhonzekera kukailowa ng’anjo yamoto. Pali kusiyana kwa ma Ulamaa akuluakulu pa mamvedwe a lamulo la Niqaab.

GULU LOYAMBA:

Anati ikumveka zoti ndi WAAJIB (chikakamizo), malinga ndi mmene Qur’an yanenera. Izi anatero poti ma Aayah onse a mu Qur’an okamba za kudziphimba mkazi sanapatule kuti manja kapena nkhope zikhonza kuoneka. Ndipo pa Surat Al Ahzaab Aayah 59:

يَا أَيُّهَا النَّبِيُّ قُل لِّأَزْوَاجِكَ وَبَنَاتِكَ وَنِسَاء الْمُؤْمِنِينَ يُدْنِينَ عَلَيْهِنَّ مِن جَلَابِيبِهِنَّ ذَلِكَ أَدْنَى أَن يُعْرَفْنَ فَلَا يُؤْذَيْنَ وَكَانَ اللَّهُ غَفُوراً رحيما} الأحزاب 59

“E, iwe Mneneri! Uza AKAZI AKO, ndi ANA AKO AAKAZI, ndi AKAZI A ASILAMU, kuti ADZIPHIMBE ndi nsalu zawo (akamatuluka m’nyumba), kutero kuchititsa KUTI ADZIWIKE, asazunzidwe (ndi anthu achipongwe). Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni”. Allah akulamula anthu awa kuti adziphimbe:

Pamenepo tikamvesetsa bwinobwino, tikumva kuti lamulo la kudziphimbaku likupita kwa Akazi a Mtumiki, Ana a Mtumiki ndi Akazi a Asilamu onse.

Komanso Surat AlNour Aayah 31:

وليضربن بخمرهن على جيوبهن

“… Ndipo afubde kumutu mipango yawo mpaka m’zifuwa zawo…”

Koma ngakhale ena amanena kuti niqaab ndi chovala cha akazi ndi ana a Mtumiki okha, ayi sichoncho ndithu, ndipo alibe umboni wa zimenezo.

GULU LACHIWIRI:

Ma ulamaa ambiri anagwira zoti niqaab ndi kusankha kwa munthu wamkazi malinga ndi environment yomwe ali. Komanso amayenera kugwira zinthu  pogula kapena kugulitsa, kulima kumene… Chachikulu ngati angasankhe kuti asavale niqaab aonesetse kuti wavala hijab yodzilemekeza komanso yosabweretsa matenda (fitna) mmitima mwa amuna.

Izi zili choncho chifukwa Allah samalimbitsa kwa munthu zinthu zoti sangakwanitse, choncho ngati mzimai ali mu environment yoti sangathe kuvala niqaab, akuyenera kutenga njira ya hijab ya shari’ah. Komanso choncho zili kwa iye kusankha hijab ya niqaab kapena yoonetsa manja ndi nkhope, hijab.

KODI MKAZI AYAMBE KUVALA NIQAAB NTHAWI YANJI?

Anthu ena omwe mmitima mwawo muli matenda a kusazindikira malamulo a Chisilamu omwe anakhanzikitsidwa zaka zopasa 1,400 zapitazo, komanso anayamwitsidwa ndi zikhalidwe za chikunja zomwe zikusokoneza dziko lino kuzera mma media osiyanasiyana, omwe akumayankhuila zogwetsa pansi malamulo a Chislamu, mu anthu oterowo muli opunzira za Deen omwe amati akayankhula anthu nkuvomereza, ngakhale zitakhala zonama zosemphana ndi Qur’an ndi Sunnah. Anthu amenewa akumanena kuti mtsikana asamva le niqaab chifukwa choti saaanakwatiwe. Akumanena kuti mkazi osakwatiwa adziyenda uku akuwonetsa thupi lake kuti amuna amuidziwe namufunsira.

Amenewot ndi maganizo omwe dziko lino likuyendera, maganizo omwe Allah subhaanah wa Ta’la anawatsutsa kumapeto kwa aaya ya hijaab ija, ponena kuti:

ذَلِكَ أَدْنَى أَن يُعْرَفْنَ فَلَا يُؤْذَيْنَ

Kutero kuchititsa kuti adziwike, asazunzidwe ndi anthu achipongwe. Kutanthauza kuti Allah akuwateteza kwa anthu achipongwe omwe cholinga chawo akufuna kungo muyalutsa mkazi. Pomwe dziko likuti avule ndipo adziwike kwa anthu, achitidwe chipongwe.

Banja ndi rizq lochokera kwa Allah Ta’ala, silimapezeka chifukwa choti munthu alkuonetysa thupi lake, komanso mkazi sikuti angasowe banja chifukwa cha kudziphimba kwa thupi lake lonse. Banja ndi rizq la Allah lomwe silichedwa komanso silifulumira, koma limadza munthawi yake yoyenera. Allah Ta’la amagawa rizq lake paskati pa akapolo ake mwaluntha lakuya poti iye Ngodziwa, ndipo palibe chomwe chingaletse zomwe wapereka komanso palibe c\yemwe angapereke chomwe waletsa.

لا مانع لمل أعطى ولا معطى لما منع  لا رادَّ لِمَا قَضَى سبحانه وتعالى والخيرُ كل الخير في الرضا بقضائه وقدَرِه

Iye Allah Ta’la akunena kuti :

وَعَسَى أَنْ تُحِبُّوا شَيْئًا وَهُوَ شَرٌّ لَكُمْ وَاللَّهُ يَعْلَمُ وَأَنْتُمْ لَا تَعْلَمُونَ 

Akunenanso kuti

،فَعَسَى أَنْ تَكْرَهُوا شَيْئًا وَيَجْعَلَ اللَّهُ فِيهِ خَيْرًا كَثِيرًا

mwina mungade chinthu chomwe Allah waika zabwino zambiri mkati mwake.

Choncho awa ndi malamulo a Allah ndipo palibe kusintha kuliknse pa malamulo ake.

Apa ndinenetse poyera kuti kuyankhula kapena kuganiza koti mtsikana ovala niqaab sangapeze banja choncho atsikana sakuyenera kusankha kuvala niqaab, mayankhulidwe kapena maganizidwe oterewo ndi olakwika kwambiri Mchisilamu. Kuvala niqaab sikungaletse munthu kukwatiwa, koma kuti munthuyo ndamene amakhala ndi maganizo osavuna kupeza banja, choncho niqaab imangonamiziridwa basi. Banja ndi lamulo lokhanzikika mu zokhonza za Allah zomwe anamukhonzera aliyensze padziko pano.

Amuna okhulupilira ndi kuopa Allah komanso odzitsata za deen bwinobwino ndamene amakhala akusakasaka akazi odziphimba, kuti iwo akhale oyambilira kuwaona komanso adziwaona okha. Koma onse omwe amalimbikitsa kuvala hijab ndi niqaab, zifukwa zake ziumakhala zofuna kukwaniritsa zofuna zawo ndi za dziko.

Kodi ngati niqaab imaletsa kukwatiwa, nfi akazi angati angati omwe amayenda miyendo pamtunda koma sakupeza mabanja? ndi akazi angati angati omwe amavala tima hijaab tothina koma samapeza banja? tisaipachike niqaab kukhala chifukwa cha kusakwatiwa kwa mkazi.

Tidziwe kuti Allah sanalamule kapena kuletsa zinthu ncholinga chotipondereza. Allah sapondereza munthu koma munthu ndamene amadzipondereza yekha pakupinda malamulo a Allah.

Anas bin Malik radhia Allah anhu anati Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: Ndithu Allah sapondereza  munthu okhulupilira pa zabwino; amampatsa zabwino za padziko lapansi ndikumudzamulipira tsiku lomaliza. Pomwe okanira amampatsa zabwino zomwe wachita mwa Allah padziko lapansi, koma tsiku lomaliza sakapeza kalikonse chifukwa cha kukanira kwake.

Choncho Asilamu ambiri lero lino tikutengeka ndi zoti zitithandize padziko pano koma tsiku lomaliza tikalangidwa.

Atsikana a Chisilamu omwe mukufuna kumavala niqaab, gwiritsani sunnah imeneyo ndipo mulipidwa nayo pano pa dziko ndi ku Aakhira. Koma musatengere zilakolako za anthu zomwe zikukongoletsedwa ndi shaytwaan yemwe cholinga chake ndikuitanira gulu lake kumoto. Limbikirani ibaada ya usana ndi usiku, kudzichepetsa komanso kuchita ma adhkaar.

Mukakumana ndi anthu okubwezeretsani mbuyo pa knhani ya kudziphimba, awuzeni kuti mukuchita izo potsatira malamulo a Chisilamu osati malamulo a azyngu. Awuzeni tanthauzo la Chisilamu, komwe ndikudzipereka kwatunthu kwa Allah Ta’ala, ndipo kutsatira malamulo a Allah ndi Mtumiki wake ndiyo njira ya Chisilamu. Hijab si chisankho cha munthu, it is not a choice but a command. Allah ndamene anakusankhirani ndipo inu munakakamizidwa kutsatira chisankho cha Allah, choncho onse omwe amanena kuti Hijaab is my choce, amalakwitsa.

Ngati mtsikana wasankha kuti adzivala niqaab kuyambira ali teenager, asaletsedwe chifukwa imeneyo ndiyo nthawi yoyambira mavalidwe oterowo, ndipo ndizoona kuti sadzampeza mwamuna omukwatira akamavala niqaab nthawi zinse, inde mwamuna wake yemwe ali osaidziwa deen ndikuigwiritsa ntchito. Koma mwamuna yemwe ali ozindikirak omanso amatsatira malamulo a Deen sadzasowa kumpeza mkazi oteroyo kuti amukwatire. Banja lomwe liri lolemekezeka pamaso pa Alla ndilomwe limayamba ndi kumuopa Iye Allah, komanso mwamuna ndi mkazi amakhala opilira mu zochitika za dziko lapansi ndi zilakolako zake.

Timpemphe Allah atifewetsere azimai anthu, azichemwali athu konso ana athu achikazi, ndikuti adziwadalitsa poakutsatira malamulo ake,