Zofunika pa nthawi ya nikaah
Pangani Download PDF yake
  1. Okwatira

Pamene mwambo wa nikaah ukuchitikira malo aliwonse omwe anthu asankha (monga munsikiti, m’nyumba ngakhalenso mu office ya Sheikh), malo aliwonsewo omwe tikufuna kuchitiramo mwambo wa nikaah siziri zofunikira kuti mkazi yemwe akukwatiwa apezeke pa gulu koma mmalo mwake ayimilira waliyyu amr ولي أمر (muyang’aniri wa mkaziyo, yemwe akuyembekezera kumpereka kwa mwamuna).

2&3. Mboni ziwiri

Mboni ziwiri zikhale zochokera kuchimuna ndi kuchikazi, zomwe zingakhale zodalirika pokumbukira zonse zomwe zingachitike pa nikaah. Ngati mboni zakuchimuna ndi kuchikazi sizipezeka, ndi zovomerezeka kutenga mboni zirizonse kuchokera mwa anthu omwe ali odziwika kwa okwatiranawo, kuti achitire umboni wa ukwatiwo. Mbonizo zikhale zakutha kukumbukira bwinobwino zonse zomwe zichitike pa nikaapo.

  1. Omukwatitsa mkazi (waliyyu amr ولي أمر)

Awa ndi bambo, bamboo aang’ono, kapena mchimwene, kapena munthu yemwe ali ndi udindo wa uyang’aniri pa mkaziyo.

Amenewa ndi anthu anayi omwe amapangitsa kuti nikah ichitike.

Zoyenera Kuyankhulidwa ndi waliyyu amri kwa mkwatibwi

Omukwatitsa mkazi (waliyyu amr ولي أمر) ayenera kuyankhula kamodzi kokha basi kumuwuza mwamuna (mkwati) kuti “ndakukwatitsa mwana wanga” (kapena mchemwali wanga) potengera ubale wake ndi mkaziyo. Angathenso kugwiritsa ntchito mau aliwonse womwe angatanthauze kupereka mkaziyo kwa mwamuna kuti akhale mkazi wake.

Mwamuna (mkwati) ayankhulenso kamodzi kokha basi kuti: “ndavomera.”

Ndizabwino kuti poyambilira pakhale khutbah (khutbatul-haajah). Koma khutbah imeneyi siyokakamizidwa ndipo ingathe kuwerengedwa ndi wina aliyense. Atha kuwerenga yemwe akumuimira mkazi (waliyy), atha kuwerenga mkwati, kapena mmodzi mwa mboni ziwiri zija, ngakhalenso wina aliyense yemwe alipo panthawiyo. Nikaah ingatheke popanda kuwerenga khutbah.

  1. Chiwongo (mahri)

Nzothekanso osapereka mahri nthawi yomweyo mmalo mwake kuzapereka mtsogolo ngati ngongole. Ikakhala ngongole, palembedwe mgwirizano wa ngongoleyo potsatira malamulo olemberana ngongole, ndipo mboni ziwiri zija zichitire umboni pa nthawi yopereka ngongoleyo.

Amenewa ndiye ndi malamulo a nikaah yovomerezeka, ndipo ma Sheikh akupemphedwa kuphunzitsa anthu kutsatira ndondomekozi mofewa ndi mosakhwimitsa monga momwe Chisilamu chaphunzitsira.

Pangani Download PDF yake