Mtumiki salla Allah alaih wasallam analangidza Asilamu kuti likafika tsiku la Chisanu adzidzikongoletsa posamba,  kuwenga zikhadabo,  kusamalira tsitsi,  Kuala zovala zokongola, kudzola zonunkhiritsa ndi zina zotero.
Swalat ya Jum’ah ndi fardh kwa Msilamu wamwamuna yemwe ali pakhomo komanso alibe vuto. Pomwe mzimai akuyenera kuswali Al Dhuhr kunyumba ndipo sizokakamizidwa kwa it’s kupita kumzikiti. koma ngati angafune kupita ncholinga choti akamvere khutbah, akhonza kutero potsatira malamulo amene anaikidwa pa mkazi yemwe akutuluka panja pa nyimba yake.

Sunnah zomwe Mtumiki salsa Allah Alain wasallam ananena kuti tidzichita lachisanu zina,  zikugwera kwa aliyense ngakhale mkazi. Koma kupatula kugwirotsa ntchito zonunkhiritsa potuluka mnyumba;  zimenezo ndi kwamwamuna yekha.

Ndi haraam kwa mzimai kudzola zonunkhiritsa ndikutuluka kukayenda. 
Choncho nkhani yathu tikukamba za kuletsedwa kwa kugwirotsa ntchito perfume , kwa mkazi, kudzera mmahadith ovomerezeka.

Mkazi asazole perfume potuluka mnyumba. Ngati akufuna kufafaniza fungi la thukuta,  ndibwino asinthe chovala kapena kusamba ndi sopo, ndipo ngati ali ndi fungo losatha pathupi pake,  ndibwino agwiritse ntchito  mafuta ochotsa fungolo, koma asaonjezere kununkhiritsa.

Masiku ano malinga ndi kuchuluka kwa zozolazola zonunkhiritsa, ma perfume a chizimai, munthu akakamba za kuletsedwa kogwiritsa ntchito zinthuzi pokayenda,  zimakhala ngati kuwabwezeretsa mbuyo mu umoyo wawo…kenako timafunso timachuluka ncholinga chofuna kupeza njira yoti zipezeke kuti ndi za halal pomwe zili za haram.

Funso:
Ndinamva kuti munthu wamkazi akadzithira perfume ndikuchoka pakhomo, amakhala ngati wachita chigololo. Pamenepo kutanthauzatu kuti akazi ambiri masiku ano akupeza nsambi za zinaa (chigololo) ndipo akapsya tsiku la qiyaamah akapanda kupanga tawba nkusiya? chifukwa ma sisters mu perfume ndiye akusambamotu. Kapena pali kupatula?

Yankho:
Dziwani kuti mkazi aliyense sali ololedwa kutuluka mnyumba atadzifaira perfume ngakhale atamapita kumzikiti.
Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:

أَيُّمَا امْرَأَةٍ أَصَابَتْ بَخُورًا فلا تَشْهَدْ مَعَنَا الْعِشَاءَ الْآخِرَةَ
Mzimai yemwe wakhunzidwa ndi zonunkhiritsa asakhale nafe pamapemphero a Isha…

Komanso anati:

إذا شَهِدَتْ إِحْدَاكُنَّ الْعِشَاءَ فلا تَطَيَّبْ تِلْكَ اللَّيْلَةَ
Yemwe (akufuna) kupezeka pa Isha mwa inu (azimai), asadzinunkhiritse mu usiku umenewo.

Mu kuyankhula kwinanso anati:

إذا شَهِدَتْ إِحْدَاكُنَّ الْمَسْجِدَ فلا تَمَسَّ طِيبًا
Pamene mmodzi wa inu (azimai) akupita kumzikiti, asagwire zonunkhiritsa.

Komanso ananena kuti:

أيما امرأة استعطرت فمرت على قوم ليجدوا ريحها فهي زانية… 
mzimai aliyense amene angadzinunkhiritse nkudutsana ndi anthu, (anthuwo) ndikuwapeza fungolo, mzimai ameneyo wapanga zina (chigololo)…

Kuti tiwamvetse ma hadithiwo, ma ulamaa akutinji?
Mu “Faidhul Qadeer,  buku la Al Min’yaawi, akulongosola kuti:

Mzimai akazola zonunkhiritsa ndikudutsa pamene pali anthu, anthu aja akamva fungolo mmitima enawo mumabwera zachilendo, kachilakolako kenakale kamabwera ndithu,  ndipo makhalidwe awo komanso zoyankhula zawo panthawiyo zimakhala zasintha chifukwa cha kudutsa kwa mzimai ameneyo, ndipo amakhala akumuyang’ana mpaka atabisika. Choncho aliyense amene akumuyang’ana nthawi imeneyo amakhala kuti wapanga naye zinaa kudzera mu diso. Mu hadith yomaliza ija kumapetoko kuli mau awa:

وكل عين زانية 
…ndipo diso lirilone (lomwe lingamuyang’anelo) limapanga zinaa.

Choncho Nayenso amakhala kuti wapanga zinaa.  Choncho pamenepa tchimo la zinaa lagwira kwa mzimai yekhayo chifukwa ndi amene wachititsa komanso walowetsa matenda mmitima ya anthu nkuwasokoneza zochita zawo.

China chofunika kumvesetsa mma hadithiwo ndi choti sikuti akamati wapanga zinaa ndiye kuti agendedwe kapena kukwapulidwa (kwa amene amayendera Shari’ah), komanso zisapangitse kuti amuna amutchule mzimai ameneyo kuti ndi wa chigololo, hule kapena maina ena onyoza. Chifukwa Mtumiki samatanthauza kuti mzimaiyo ndi wa chiwerewere, koma kuti zomwe wachitazo, zichititsa kuti anyamule nsambi za anthu ena amene akhale ndi chilakolako cha zinaa kuchokera kwa iye, maganizo opanga naye zinaa amene angawafikire anthu panthawi imene wadutsana nawo, akubwera chifukwa cha iyeyo.

Choncho mwamuna yemwe angamutchule,  kapena kumulengedza mzimai ameneyu kuti ndi hule chifukwa cha perfume, apeza nsambi zomuponya mkazi mudzjenje laa chiwerewere, ndipo ali otembeleredwa padziko pano mpaka ku aakhira,  komanso akalowa kumoto…. monga mmene akunenera pa Qur’an surah Al Noor 23. Zimenezo nchifukwa choti sanabweretse mboni zinai zoikira umboni kuti mkaziyo amupezadi akupanga zinaa.
Imaam Ibn Khuzaimah anati:
Mzimai yemwe wazola zonunkhiritsa ndikutuluka mpaka anthu kumva fungolo, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anamutchula kuti ndi wachiwerewere. Komano zimenezo sizikubweretsa lamulo lomukwapula kapena kumugenda.

Zinaa yapa perfumeyi ikanakhala kuti ikubwera ndi malamulo onse oyenera pa zinaa ya maliseche, ndiye kutinso bwenzi Mtumiki atanena mmahadithimo kuti agendedwe kapena akwapulidwe. Koma siIingatero chifukwa lamulo la kugendedwa kapena kukwapulidwa linaperekedwa kwa yemwe wapanga zinaa ya maliseche.
Hadith:
…Zinaa ya lirime ndi kuyankhula, zinaa ya diso ndi kuyang’ana. Mtima ukalakalaka ndi kukhumba ndipo maliseche amavomereza kapena kukanira zomwe mtima wafunazo…

Ndipo Imaam Ahmad anati:
Zinaa ya mmanja ndi kusisita, zinaa ya myendo ndi kuyenda, zinaa ya kamwa ndi kuphyophyona (kiss)

Choncho tikamvesetsa bwinobwino tikumva kuti Shari’ah inadzitchula zinthu zimenezo kuti ndi zinaa…chifukwa choti ndi zomwe zimachititsa kuti zinaa yeniyeni ya maliseche ichitike mwamphamvu komanso mopanda manyazi. Koma sizikutanthauza kuti zinaa ya pakamwa, ya myendo, ya manja, ya perfume etc ndi chimodzimodzi zinaa ya maliseche mmagamulidwe ake.

Apa tiphunzireponso kuti mmene Shariah ikutiuza kuti mkazi yemwe watuluka ndi perfume ndiye kuti wapanga zinaa, zikuchokeranso mmau ena a Mtumiki onena kuti:
“Yemwe wabweretsa Sunnah (njira yoti ena atsatire) yoipa Mchisilamu, anyamula machimo a onse omwe angamutsatire (kapena kukhunzidwa ndi zoipa zomwe wayambitsazo) mpaka Tsiku la Qiyaamah.”

Komanso ananena kuti:

“من دعا إلى هدى كان له من الأجر مثل أجور من تبعه، لا ينقص ذلك من أجورهم شيئاً، ومن دعا إلى ضلالة، كان عليه من الإثم مثل آثام من تبعه، لا ينقص ذلك من آثامهم شيئاً”.
“Yemwe angaitanire ku chiwongoko,  adzapeza malipiro  ofanana ndi malipiro a yemwe watsatirayo, popanda kupungula  kulikonse. Ndipo yemwe waitanira ku chionongeko, apeza machimo ofanana ndi machimo a yemwe watsatirayo popanda kupungula kwina kulikonse”

Sister, ndi amuna angati omwe mwawapezetsa nsambi ya zinaa chifukwa cha perfume wanuyo? Dziwani kuti pa mwamuna mmodzi aliyense yemwe mwamunkhiritsa munsewu iye nkudziwa kuti padutsidwapo apa, chilakolako chilichonse chomwe chingampezecho, inuyo mutsenza machimo ake. Chifukwatu pamenepo ndiye kuti mwamulowetsa ka virus kumene kamuyambitsire chilakolako choti mpaka agwere mmachimo.

Sister, mukakhala kunyumba kwanu, zolani zonunkhiritsazo, komanso mukhonza kusambira mmabotolomo momwe mungathere, kuti zimusangalatse mwamuna wanu komanso asakutalikireni.
Azimai ena amachita opposite; akakhala pakhomo amakhala ndi uve, osadzisamalira,  osadziphoda, komanso osadzithira zonunkhiritsa. Koma akamachoka pakhomopo, amachita kukhala 1 hour kudzikongoletsa,  kukhonzekera kutuluka ncholinga akamunone anthu kunja, kumusiya mwamuna akumva kununkhira mnyumba koma mwini wa fungolo wachoka…Izi zimachititsa kuti mwamuna achoke akaone zina kunsewu, akapeze kafungo kamene wasiyiridwa kunyumba kaja …

Ndikhulupilira tadziwa pang’ono chifukwa chimene Mtumiki salla Allah alaih wasallam analetsera mkazi kudzola zonunkhira akamatuluka pakhomo.

Chenjezo:
Tisaganize molakwika kuti Chisilamu chikuletsa mkazi kudzisamalira…
  إِنَّ فِي ذَلِكَ لَذِكْرَى لِمَنْ كَانَ لَهُ قَلْبٌ أَوْ أَلْقَى السَّمْعَ وَهُوَ شَهِيدٌ
Ndithu mzimenezi muli chikumbutso kwa yemwe ali ndi mtima ndi yemwe akutchelera khutu (uku) iye ali pompo (ndi maganizo ake) surah Qaaf 37

 1. Kodi nanga mzimai apange bwanji kuti athane ndi fungo lomwe ali nalo, poti anazolowera kuti zikatero angodzifaira perfume?
  2. Kodi ndi zoona kuti mzimai yemwe wazola zonunkhiritsayo kudziyeretsa kwake akuyenera kusamba monga mmene amasambira munthu wa janaabah chifukwa akuti nchoti wakhala ngati wachita zinaa?
 2. Ngati ali ndi fungo la thukuta (mwachitsanzo), akuyenera kusamba,  ndikusintha zovala. Basi pamenepo sizoyeneranso kwa iye kudzithira zonunkhiritsa
  Koma ngati ali ndi fungo losatha ngakhale atasamba, akuyenera kugwiritsa ntchito mafuta amene akhonza kufafaniza fungolo … asakhale obweretsa fungo Lima lomafalikira ma meters mpaka ena kulimva.
  2. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
  إِذَا خَرَجَت الْمَرْأَةُ إِلَى الْمَسْجِدِ فَلْتَغْتَسِلْ مِن الطِّيبِ كَمَا تَغْتَسِلُ مِن الْجَنَابَةِ.
  Mkazi akamafuna kutuluka kupita ku mzikiti,  akuyenera kusamba kuti achotse zonunkhira (zomwe anazola pakhomo), kusamba kwake ngati kwa munthu oti anali ndi janaabah.

  Kusamba kumeneko sikuti ndi kwa Farah monga mmene ziliri kwa wa janaaba. Koma malinga ndi mmene akulongosolera Al Min’yaawi mu Faidhul Qadeer,  kusamba kumeneko ndi kwa Sunnah komanso Oofuna kuonetsetsa kuti achotse fungolo. Ndondomeko ya masambidwe a janaaba ndi ndondomeko yomwe ili yamasambidwe abwino kwambiri,  Choncho munthu ngakhale alibe janaabah akhonza kusamba ngati wa janaabah pongofuna kuonetsetsa kuti wasamba, kusamba kotheratu.

  Choncho mzimai yemwe ali ndi perfume thupi lonse nkudzasamba masambidwe oterewa, amakhala kuti paliponse wadusitsapo madzi ndi sopo kutero kuti palibe fungo lomwe lingatsalire.
  Nchifukwa chake amati mzimai wa perfume asambe ngati wa janaabah

  Tsopano akakhala kuti perfumeyo anazola malo ena ake osati thupi lonse,  akuyenera kungotsuka malo amenewo basi osati kusamba. Ndipo ngati anapaka mu zovala ndipo sanakhunze thupi lake, akuyenera kungosintha zovala zokhazo basi.
  Izi achite panthawi imene akufuna kutuluka kupita koyenda.
  Nkhani yaikulu apa  ndiyoti ma sisters ndi azimai athu apewe kudzola zonunkhiritsa potuluka mnyumba kukayenda.

  إِنْ أُرِيدُ إِلَّا الْإِصْلَاحَ مَا اسْتَطَعْتُ ۚ وَمَا تَوْفِيقِي إِلَّا بِاللَّهِ ۚ عَلَيْهِ تَوَكَّلْتُ وَإِلَيْهِ أُنِيبُ
  …sindifuna china koma kukonza mmene ndingathere; ndipo kupambana kwanga (pazimenezi) kuli kwa Allah,  kwa Iye ndatsamira,  ndipo kwa Iye ndikutembenukira. 11:88

  Allah ndi amene ali odziwa zonse…