Funso Loyamba:
Assalaam Alaykum Shekhy! Kodi ndi zizindikiro zanji zomwe amaonetsa mwana wamng’ono pomwe walozedwa ndiye wawelengeredwa ma Aayat a Ruqya; tingadziwe bwanji kuti ufitiwo watha?
Funso Lachiwiri:
Kodi mwana wamng’ono oti sayankhula ndiye walozedwa, tikamuwelengera ma Aayat a Ruqya chiwanda chakecho chimayankhulanso?
Yankho Loyamba
Walaikum Salaam
Mwana ali ndi zizindikiro zambiri zosonyeza kuti ali ndi chi/ziwanda:
  1. Mwana akakhala kuti sanayambe kuyankhula koma jinn lamulowa,  amangoyamba kulira kosalekeza komanso mau achilendo omveka ngati likhweru aja (kukuwa kwambiri) … Mukayesa kumutonthoza mpamene kulira kumaonjezereka … Ndipo izi zimatenga masiku ndithu.
  2. Amakhala obanika popanda chifukwa choonekera
  3. Khungu lake limasintha mtundu
  4. Khungu lake limaoneka tima spot takuda

Zoyenera kuchita mukaona zizindikiro zimenezi:

Choyamba, dziwani kuti zizindikiro zomwe ndatchulazi zimatha kupezeka pa matenda ena achilengedwe … choncho musangofikira kugamula kuti alI ndi ufiti …  thamangirani kaye kuchipatala ndipo akamuyeze, akakapanda kupeza vuto loti akhonza kumpatsa mankhwala nkuchira, bwelerani mupange izi:
Muwelengereni Ruqya: Surat Al Fatiha ndi Aayatul Kursiyy, Surat Al Ikhlaas, Surat Al Falaq ndi Surat Al Naas.
Mumtetezenso ndi chitetezo cha Mtumiki salla Allah alaih wasallam pomuwelengera izi:
1. Audhu Bikalimaatillaah ttaammaat min kulli shaytwaanin wa haammah,  wa min kulli ‘ainin laammah
2. Bismillah urqeek min shay’in yu’dheek,  wa min sharri kulli nafsin awu ‘ainin haasidin Allahu yashfeek (x3)
3. As’alu Allaha Al’adhweema Rabbal Arshil Adhweem an yashfeek (x7)
 أعوذك بكلمات الله التامة من كل شيطان وهامة ومن كل عين لامة.
بسم الله أرقيك من شيء يؤذيك ومن شر كل نفس أو عين حاسد الله يشفيك
أسأل الله العظيم رب العرش العظيم أن يشفيك.
Mukamawerenga dua iliyonse mudziwuzira mpweya pa mutu ndi pa chidali komanso pamimba ndi kumsana kwa mwanayo.
Komanso mukuyenera kuwapangira mai a mwanayo Ruqya chifukwa nthawi zambiri mavuto omwe amampeza mwana amakhala ochokera kwa mai.
Muyezamire mwa Allah ndikumabwerezabwerezaa ruqya imeneyo, in sha Allah mwana adzakhala bwino
KOMA MUSASIYE KUMAMUWELENGERA pogona paliponse.  Chifukwa mfiti ikaona kuti wachira imatumizanso ndi ufiti wina. Choncho ngati mudzimuteteza mwanayo ndiye kuti sudzaliwanso mwa iye.
Mungadziwe bwanji kuti Ufiti Watha?
Zizindikiro zija zikasiya kuoneka ndiye kuti ufiti watha.
Langizo:
Tisamadikire kuti tione zizindikiro za ziwanda mwa mwana wathu. Koma tidzikhala omuteteza mwana wathu tsiku lirilonse usiku pogona, komanso kumamuwelengera Qur’an kawirikawiri.
Yankho Lachiwiri:
Sindikudziwa kuchokera mmabuku, mwina ndikadzakumana nazo in sha Allah. Koma pakalipano ndikuuzani kuchokera mmaganizo anga poyerekeza ndi zomwe ndakhala ndikuwerenga:
Chiwanda sikuti chimayankhula muthupi la aliyense. Kutheka osayankhula mwa munthu oti amayamkhula, mpaka kukwanitsa kuchitulutsa.
Kuyankhulana kuja kumangokhala njira ina yomwe Allah wamufewetsera munthu ochita Ruqya.
Tili ndi anthu osayankhula, ana oti ngati atulutsa mau ndiye kuti kulira…koma panopa zomwe ndikudziwa nzoti chiwanda chimayankhula mthupi la amene amayankhula. Ngati Allah sanampatse munthuyo kuyankhula, shaytwaan sangampangitse kutero. Iye shaytwaanin amakanika kuyankhula mwayekha koma amadalira kuyankhula komwe munthuyo ali nayo kale. Choncho ngati munthuyo ali osayankhula ndiye kuti shytwaan naye sayankhula, koma zingobwera zizindikiro zina zokutheketsani inu kuthana naye losakhala kuyankhulako in sha Allah
—————————
Tiyeni Tiwateteze Ana Athu ku Ziwanda
Ana ena amapezeka kuti angoyamba kulira komanso kugwidwa nantha makamaka nthawi ya usiku pamene akugona. Bambo kapena mai akayesa kumutonthoza, mpamene kulira ndi mantha zimalimbikira ndipo zimamtengera masiku ndithu. nthawi zina makolo amakhala akumva kuti mwana akuyankhula ndi munthu oti sakuoneka, kapena kungogundika kulira ndikumawauza makolo ake kuti mchipinda muli munthu amene akufuna kummenya.
Zonsezitu nchifukwa choti nyumba za Asilamu ambiri masiku ano samalowamo Angelo. Manyumba ambiri masiku ano simumawerengedwamo Qur’an, ngakhale swalat simapempheredwamo, ngakhale ma dua, ma adhkaar samawerengedwamo. Choncho mnyumba zoterezi zimakhala mabwalo oseweleramo ziwanda chifukwa cha kuchuluka zoipa monga nyimbo, zithunzi zopachikapachika mmakoma, zidole zosemasema, ndi zina zotero.
Ana amasiyidwa kumasewera nthawi zonse popanda chitetezo chirichonse, ndipo makolo amakhulupilira kuti mwana ali pa chitetezo ngati palibe amene angamube, amaiwala kapena samadziwa kumene kuti kulinso okuba ena osaoneka ndi maso, amene ali oopsa kuposa owoneka ndi maso. ma jinn. Ana akuyenera kutetezedwa powelengeredwa ma dua a kummawa ndi kumadzulo. Adzituluka mnyumba imene ikuwerengedwa Qur’an. Ibn Abbas radhia Allah anhuma anati, Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali kuwateteza ana (Hassan ndi Hussein) ndipo ankayankhula kuti: “ndithu agogo anu (Ibrahim) anali kuwateteza ana awo (Ismail ndi Is’haaq), ndikukutetezani ndi Mau a Allah Okwanira kuchokera ku shaytwaan, ku mavuto komanso diso lirilonse loipa”.
Kuchokera mu Sahih Al Bukhari, Ibn Abbas radhia Allah anhuma anati: Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati kuwateteza Hassan ndi Hussain: “ndikukutetezani ndi mau a Allah okwanira ku shaytwaan ndi mavuto komanso ku disol lirilonse loipa” ndipo amati:  “ndithu agogo anu (Ibrahim) anali kuwateteza ana awo (Ismail ndi Is’haaq)”
Ana anu muwaphunzitse ma adhkaar, muwaphunzitse kuwerenga Laa ilaaha illa Allah, muwaphunzitse kuwerenga ma surah atat akumapeto (Al Ikhlaas, Al Falaq, Al Naas). Muwaphunzitse dua ya pogonera. Osamangowasiya adzigona ngati zinyama.
Mzifukwa zina zimene zimapangitsa ana kupeza mavuto kuchokera ku ziwanda, ndi kuwasiya ana kuti adzisewera panja nthawi ya kumadzulo pamene dzuwa likulowa mpaka usiku. Eni ake amati kuwasangalatsa ana, sadziwa kuti amakhala akuwapereka ku ziwanda. Nthawi imeneyi ndi yomwe ziwanda zimayamba kutuluka. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:
إذا كان جنح الليل ، فكفوا صبيانكم ، فإن الشياطين تنتشر حينئذ
“Ukabwera mdima aletseni ana anu (kusewera panja), chifukwa ziwanda zimafalikira nthawi imeneyo”
Komanso pali ma report ambiri pa hadith imeneyi. Choncho tikuyenera kuwaletsa ana athu kusewera panja dzuwa likangolowa. Imeneyo ndi nthawi yoti ana apezeke kumzikiti aswali maghrib, ndipo apezeke munthu owaphunzitsa Qur’an, monga Aayatul Kursiyy ndiu ma dua komanso ma adhkaar, mmalo moti adzisewera mpira padothi asakuzindikira zomwe zikuchitika mwa iwo
Zimenezo ndiye zina mwa njira zotetezera mwana. Koma ngati zavuta ndipo wakhunzidwa ndi ziwana komanso mukutha kuona zizindikiro zodabwitsa mwa iye, muwelengereni ruqya. Mwachundo cha Allah achira. Komanso muonesetse kuti mukutalikirana ndi zomwe zingapangitse ziwanda kuyandikira pahkhomo panu, monga mmene ndalongosolera muja.
Allah ndiye Mwini Kudziwa Konse