Mneneri Musa alaih salaam anayenda mchipululu usana ndi usiku kulunjika ku Madian, womwe ndi mzinda wapafupi ndi Syria komanso Egypt. Palibe yemwe anali naye paulendowu kupatula Allah Ta’la ndipo chakudya chake chinali mapemphero.

Ngakhale anali kumva kutentha mchipululu, anapitilira kuyenda powopa Asilikali omwe anali kumufunafuna. Anayenda masiku 8.

Musa alaih salaam anakwanitsa kuwoloka chipululu mpaka anatulukira mumzinda wa Madian.

Patadutsa nthawi, anafika pamtengo pamene anapumula, kenako anaona atsikana awiri ali chimire ndi nkhosa zawo, ndipo anadziwa kuti akufuna chithandizo. Iye anawapitira ndikuwafunsa vuto lawo. Mmodzi wa iwo analongosola kuti akudikira gulu la amuna omwe akumwetsa ziweto zawo kuti amalize, chifukwa bambo awo ndi munthu wachikulire ndipo sangapite pa chitsime kukamwetsa ziweto. Choncho monga mwa masiku onse, akamaliza kumwetsa amuna iwo amapita kukamwetsa ziweto zawo.

Musa alaih salaam anawatenga atsikana aja ndikupita nawo pa chitsime ndipo atawakankha anthu anapeza kuti anatseka pachitsimepo ndi chimwala cholemera. Iye anakankha yekha chimwalacho ndipo ziweto za atsikana zija zinamwa madzi. Anthu anali ozizwa poona kuti wakankha chimwala cholemera yekha.

Kenako anabwelera kukakhala pansi pa mtengo, koma anakumbukira kuti anaiwala kumwa madzi pamene anali pa chitsime, ndipo anapempha Allah kuti amudalitse ndi zabwino zake.

Pamene tsikana anabwelera kunyumba, bambo awo anadabwa poona kuti abwelera mofulumira, ndipo iwo analongosola nkhani yonse. Bambo anafuna kumuthokoza munthu wachilendo uja, choncho anatumiza mtsikana mmodzi kuti akamutenge. Musa alaih salaam analola ndipo anapita kunyumba kuja limodzi.

Atafika, Mneneri Musa analongosola zamoyo wake komanso mmene anathawira potuluka mu Egypt. Iwo anamulimbitsa mtima pomuuza kuti ali otetezeka.

Bambo aja pamodzi ndi ana ake anali osangalatsidwa ndi chikhalidwe cha Musa alaih salaam, choncho anamuuza kuti akhale naye kwa Masiku angapo. Iye anasangalala kwambiri pakulandiridwako.

Bambo atazindikira kuti Musa alaih salaam anali munthu okhulupirika, anamuitana ndikumuuza kuti akufuna kumukwatitsa mmodzi mwa ana ake, ndipo Musa anavomera. Koma bambo anapereka condition yoti amugwilire ntchito yoyang’anira ziweto zake kwa zaka 8. Koma chifukwa choti Musa anali mlendo, analibe kuchitira mwina ndipo condition imeneyo inamukwanira.

Musa anakwatira mwana wa bambo aja pambuyo pa kuweta ziweto kwa zaka 10.

Zaka zomwe anakhala kutali ndi abale akezi zinali zofunikira kwa Mneneri Musa alaih salaam; inali nthawi ya kukhonzekera kwakukulu.

Tsiku lina anayamba kuganizira kwambiri abale ake omwe anasiyana nawo kalekale ku Egypt. Iye anafunisitsa kubwelera ku Egypt ndipo mu usiku umenewo anamuuza mkazi wake kuti akuyenera kupita ku Egypt, ndipo anavomera.

Ananyamuka ndi banja lake kupita ku Egypt kuzera mu chipululu, ndipo anayenda masiku ochuluka kufikira pamene anatulukira pafupi ndi phiri la Sinai. Pamenepo anaganiza kuti wasochera  ndipo anakhala usiku umenewo osayenda.

Usiku anatuluka kukafunafuna nkhuni zoyatsira moto, mpaka anafika pa phiri la Tur pamene anaona moto pamwamba paphiliro. Analunjika komwe anaona motowo ndipo atawandikira anamva mawu “E iwe Musa, Ine ndine Allah Mbuye wa zolengedwa zonse”. Musa anadziwa kuti yemwe anali kumuyankhulayo anali Allah mopanda chikaiko. Iye anayenda kupita patsogolo, ndipo Allah anamulamula kuti achotse nsapato zake chifukwa anali malo oyera. Anamuuza kuti wamusankha iye kuti agwire ntchito yofunikira ndipo akuyenera kutsatira malamulo omwe angampatsewo.

Atamufunsa za dondo yomwe ananyamula kumanja kwake, Musa anayankha kuti ndi ndodo yomwe amayendera ndikukusira nkhosa zake. Pompo Allah anamuuza kuti ayiponye pansi, koma atangoiponya, nthawi yomweyo inasanduka chinjoka chachikulu!

Musa alaih salaam anadzadzidwa ndi mantha poona chinjoka chija ndipo anathawa. Koma mau ochokera kwa Allah anamuuza kuti asawope, abwelere ndipo aisandutsa kukhala ndodo mmene inaliri. Ngakhale anali ndi mantha ndi njoka, Musa alaih salaam anakhulupilira mau aja ndipo anabwelera ndikuigwira, pamene inabwelera kukhalanso ndodo.  Pamenepo mantha onse anachoka poti anakhulupilira kuti anali kuyankhula ndi Allah.

Kenako anamulamula kuti alowetse mkono wake mu mkanjo, atatulutsa anaona kuti ukuwala utasandula woyera. Ndipo Allah anamulamula Musa kuti apite ku Egypt akakumane ndi Farawo, chifukwa iye anali odzikweza ndikuvutitsa ma Israel. Koma Musa alaih salaam anaopa kuti akhonza kukagwidwa akabwelera ku Egypt; poti anapha mmodzi wa iwo. Allah Ta’ala anamulimbitsa mtima ndikumutsimikizira chitetezo chake pa iye pomuuza kuti apite akawauze uthengawo ndipo akawaonetse njira yoona. Anamuuzanso kuti amutenge m’bale wake Harun kuti akamuthandize ndipo sakamupatsa mavuto aliwonse. Musa alaih salaam anakhutira ndi lonjezo la Allah Ta’ala.