Musa alaih salaam anakulira m’banja la Chifumu. Mafumu omwe anali kutsogolera dziko la Egypt anali kuchitira nkhanza ana a Ya’qoub alaih salaam, omwe amadziwikanso ndi dzina loti ana a Israel. Iwo anali kugwiritsidwa ntchito nthawi yaitali ndi malipiro ochepa komnanso nthawi zina popanda malipiro. Farawo sanalole kuti ma Israel adzimvera wina kupatula iye komanso kuti azipembedza milungu yake, chimodzimodzi mafumu ena onse omwe anali kudza anali kudzitcha kuti ndi milungu.

Patadutsa nthawi kunadza Farawo wina yemwe anali wankhanza kwambiri komanso anali kuwada ma Israel. Sanali kusangalatsidwa kuona iwo akuchulukana.

Usiku wina pamene Farawo anali kugona, analota moto wochokera kumwamba utatentha nyumba zonse za ma Egyptian ndikusiya za ma Israel. Atadzuka anali ndi mantha poti sanali kudziwa tanthauzo la malotowo. Kutacha anaitanitsa mlosi wake kuti amulongosolere tanthauzo la maloto aja; iye anamuwululira kuti mwana wamwamuna abadwa posachedwa ndipo ma Egyptian adzaonongekera mmanja mwake. Farawo anakwiya ndipo analamula kuti mwana wamwamuna aliyense yemwe wabadwira m’banaja lachi Israel aphedwe.

Imeneyo ndi nthawi yomwe Mneneri Musa alaih Salaam anabadwira m’banja la chi Israel losawuka, ndipo anali ndi mchimwene wake Harun alaih salaam, komanso mlongo wake.

Allah anawauza mai a Musa kuti amuike mwana m’basketi ndipo amuponye munsinje wa Nile. Iwo anachita zomwe anauzidwa koma ngakhale kuti anadandaula kwambiri, anadziwa kuti palibe choipa chomwe chimufikire.

Anamuuza mwana wamkazi kuti aitsatire basket ija komwe ikulowera, ncholinga choti awonesetse kuti choipa chisampeze. Allah anaiteteza basket ija ndipo patadutsa kanthawi inalunjika ku kamtsinje kakang’ono komwe mkazi wa Farawo anali kusamba. Pamene anaona basket ija anawauza antchito ake kuti ayipititse kumtunda. Kenako anaona kuti munali mwana, ndipo atamutenga anamukonda kwambiri.

Mkazi wa Farawo anali osiyana kwambiri ndi Farawo; anali okhulupilira komanso wachikondi ndi chisoni. Ankafuna mwana kwanthawi yaitali, ndipo atamuona Musa anamunyamula ndikumupsopsona. Farawo anali odwabwa kumuona mkazi wake akulira chifukwa cha chisangalalo pa mwana uja. Iye anamupempha kuti amulole amulere mwana uja kuti akhale mwana wawo, ndipo Farawo analola.

Patadutsa nthawi mwana anamva njala ndikuyamba kulira . Mkazi wa mfumu uja anampatsa bere lake koma sanalole. Asilikali a Farawo anamubweretsa mlongo wake wa mwana uja ndikuwauza kuti anamuona akuitsatira basket kumtsinje kuja. Atamufunsa anayankha kuti anali kutsatira basket ija kamba ka kudabwa.

Atawona kuti mlongo wake akulira, anadandaula ndipo ananena kuti akumudziwa mzimai yemwe angakwanaitse kumuyamwitsa. Mai uja analamula asilikali kuti amubweretse, ndipo atabwera nkuyamba kumuyamwitsa, mwana analola bere lake ndipo anasiya kulira. Farawo ataona izi anali odabwa kwambiri ndipo anafuna kudziw kuti mzimai uja ndi ndani poti mwana anakana kulandira bere la mai aliyense kupatula la iye. Mai uja sanawulule kuti anali mai wa mwanayo, chifukwa akanatero ndiye kuti akanawaupha. Iye anamuyankha kuti palibe mwana yemwe amakana bere lake chifukwa ndi la fungo labwino komanso mkaka wake ndiwokoma. Yankho ili linamukwanira Farawo ndipo anamutenga uja kukhala olera mwana, osadziwa kuti anali mwana wake.

Musa alaih salaam anakulira mnyumba yachifumu mwamphamvu, ndipo Allah anampatsa thanzi ndi nzeru. Anali ndi mtima wabwino kotero kuti anthu ofowoka ndi oponderezedwa anali kulunjika kwa iye kufuna chithandizo.

Tsiku lina akuyenda anapeza msilikali wa chi Egytian akupanda munthu wa chi Israel. Pamene mu Israel anaona Musa alaih salaam, anamupempha kuti amupulumutse, ndipo Musa atamupempha msilikali uja kuti asiye kumenya mu Israel, anamufunsa kuti iye ndi ndani..  anayankhula zina zomupsetsa mtima Musa koma anayesetsa kukambirana naye mwamtendere ndipo sanamvere. Pamene anaona kuti sakumumvera, Musa anamumenya ndipo anagwa ndikufera pompo. Ataona izi, Musa anatsimidwa mumtima ndikunena kuti imeneyi ndithu ndi ntchito yoipa ya shaytwaan yemwe anamusokoneza mmaganizo. Iye anali kudziwa kuti kupha aliyense ndi tchimo ndipo ndi mlandu waukulu. Pamenepo anagwada pansi ndikupempha kwa Allah kuti amukhululukire pa tchimo lomwe anachita.

Tsiku lotsatira anamupeza munthu yemwe anamupulumutsa dzulo uja akumenyananso ndi munthu wina. Iye anamugwira wina uja ndikumudzudzula m’bale wake uja chifukwa cha kupezeka akumenyana tsiku lirilonse.  Koma tsopano munthuyo anaopa ndikupempha kuti asamuphe ngati mmene anachitira dzulo ndi mu Egytian uja. mEgyptian uja atamva zoti Musa anapha munthu dzulo, anakanena kwa atsogoleri.

Tsiku lotsatira pamene Musa anali kuyenda, munthu wina anadza mothamanga ndikumuchenjeza kuti asilikali akumufunafuna kuti amumange, ndipo anamuchenjeza kuti athawe asanamupeze. Musa anadziwa kuti chilango cha kupha ndi kuphedwanso, choncho anatuluka mu Egypt mosakhonzekera moti sanapeze nthawi yosintha zovala kapena kutenga chinyama chokwera.

Zinamuchitikira zotani pa ulendo wake?