Funso:
“Mwamuna achoke muchipembedzo chake cha Chisilamu mkumtsatira muchipembedzo chake (ndikhulupilira mukutanthauza kumtsatira mkazi). Ndafunsa funsoli chifukwa ndakhala ndikuona ambiri kuno ku Joni akupanga zimenezo akuti chifukwa chofuna kukhala mwa mtendere”.
 
Yankho:
Hasbuna Allahu wa Ni’mal Wakeel.
Choyamba, inuyo musamatenge zomwe Asilamu akupanga, koma mudzitenga zomwe Chisilamu chikukamba. Chisilamu ndi Asilamu ndi zinthu ziwiri. Msilamu akuyenera kutsatira Chisilamu koma osati Chisilamu chimtsatire munthu. Yemwe wasiya Chisilamu sichidzamthandiza komanso Mwini Chisilamu (Allah) sadzamuthandiza ngakhale kumuyang’ana Tsiku Lomaliza.
Uthengawu upite kwa onse omwe abale awo anatuluka Chisilamu, mwina angawathandize kuwaonetsa njira ya Chiwongoko, komanso tidziwapemphera nthawi zonse kuti Allah awabwezeretse njira yomwe anabadwira nkuisiya.
Chisilamu ndiye Mtenderewo. Ndipo iwowo ngati akuona kuti sakukhala mumtendere, nchifukwa choti sakuchigwiritsa ntchito Chisilamu. Akufuna kukhala pamtendere wa padziko umene uli kanthawi kochepa, akufuna kuti adzipanga za haraam zomwe Chisilamu chinaaletsa, akufuna kuti adzikhala mwa democracy Mchidilamu.
Brother, anthu akhonza kuchita mmene akufunira…koma sizikutanthauza kuti ndi mmene Chisilamu chiliri. Inuyo mukaona oterowo dziwani kuti angovala Chisilamu ngati malaya koma mulibemo Chislamu. Choncho tengerani za Chisilamu ndipo musatenge za Asilamu.
Chisilamu cha Allah, munthu yemwe anali Msilamu okhulupilira mwa Mulungu mmodzi yekha ndi Mtumiki wake, ndiye wasiya zonse zija nkulowera kwina, Allah Ta’ala akunena ndi mau ake, akukuuzani kuti musaope kuwadzudzula pa mchitidwe umenewo, Iye akunena kuti:
يا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا مَنْ يَرْتَدَّ مِنْكُمْ عَنْ دِينِهِ فَسَوْفَ يَأْتِي اللَّهُ بِقَوْمٍ يُحِبُّهُمْ وَيُحِبُّونَهُ أَذِلَّةٍ عَلَى الْمُؤْمِنِينَ أَعِزَّةٍ عَلَى الْكَافِرِينَ يُجَاهِدُونَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَلَا يَخَافُونَ لَوْمَةَ لَائِمٍ ذَلِكَ فَضْلُ اللَّهِ يُؤْتِيهِ مَنْ يَشَاءُ وَاللَّهُ وَاسِعٌ عَلِيمٌ 
“E inu amene mwakhulupirira! Amene wa inu asiye chipembezo chake, ndiye kuti posachedwapa Mulungu adzabweretsa anthu omwe awakonda, nawonso amkonda; odzichepetsa kwa Asilamu anzawo; amphamvu kwa osakhulupirira; omenyera nkhondo chipembezo cha Mulungu, saopa kudzudzula kwa odzudzula. Umenewu ndi ubwino wa Mulungu; amaupereka kwa amene wamfuna. Ndipo Mulungu ndi Mataya; ngodziwa kwambiri. 5:54
Dziwani kuti kusiya Chisilamu ndi mistake yaikulu kuposa yemwe ali kaafir kuyambira kuumwana wake. Nchifukwa chake shari’ah inaika chilango choti oteroyo angopangidwa eliminate basi kwake kwatha padziko pano, ndipo ku aakhira ndi nkhuni yakumoto imeneyo osatuluka mpaka kale.
 Ndiye Allah Ta’ala akunenanso zotsatira za otuluka mChipembedzo motere:
وَمَنْ يَرْتَدِدْ مِنْكُمْ عَنْ دِينِهِ فَيَمُتْ وَهُوَ كَافِرٌ فَأُولَئِكَ حَبِطَتْ أَعْمَالُهُمْ فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ وَأُولَئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ
“Ndipo mwainu amene atuluke m’ chipembedzo chake, kenako namwalira uku ali osakhulipirira, iwo ndi omwe ntchito zawo zaonongeka padziko lapansi mpaka Tsiku Lomaliza. Ndipo iwo ndi anthu akumoto. M’menemo adzakhalamo mpaka muyaya.” 2:217
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا بَعْدَ إِيمَانِهِمْ ثُمَّ ازْدَادُوا كُفْرًا لَنْ تُقْبَلَ تَوْبَتُهُمْ وَأُولَئِكَ هُمُ الضَّالُّونَ
*”Ndithudi, anthu amene Atuluka M’chikhulupiriro pambuyo Pokhulupirira, kenako Naonjezera kusakhulupirira, Kulapa kwawo sikudzavomerezedwa konse. Ndipo iwo ndi osokera.” 3:90
إِنَّ الَّذِينَ ارْتَدُّوا عَلَى أَدْبَارِهِمْ مِنْ بَعْدِ مَا تَبَيَّنَ لَهُمُ الْهُدَى الشَّيْطَانُ سَوَّلَ لَهُمْ وَأَمْلَى لَهُمْ – ذَلِكَ بِأَنَّهُمْ قَالُوا لِلَّذِينَ كَرِهُوا مَا نَزَّلَ اللَّهُ سَنُطِيعُكُمْ فِي بَعْضِ الْأَمْرِ وَاللَّهُ يَعْلَمُ إِسْرَارَهُمْ – فَكَيْفَ إِذَا تَوَفَّتْهُمُ الْمَلَائِكَةُ يَضْرِبُونَ وُجُوهَهُمْ وَأَدْبَارَهُمْ
“Ndithu, amene akubweمera m’mbuyo (نusiya chipembedzo chawo nkubwerera ku zosakhulupilira Mulungu) chiongoko chitawaonekera poyera Satana ndiamene wawanyenga, ndipo Mulungu akuwapatsa nthawi. Zimenezo nkaamba kakuti iwo adanena kwa omwe amada zimene Mulungu wavumbulutsa (kuti): “Tidzakumverani m’zinthu zina (zimene mukutsutsana ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam” Ndipo Mulungu akudziwa zobisika zawo. Kodi adzakhala bwanji pamene Angelo azidzatenga mizimu yawo uku akumenya nkhope zawo ndi misana yawo?”  47:25-27
KODI M’BALE WATHU YEMWE WASIYA CHISILAMU TIDZIKHALA NAYE MOTANI?
Dziwani kuti otuluka Chisilamu amatchedwa Murtad (Yemwe wabwelera mu Kufr). Ndipo satchedwa Kaafir chifukwa iyeyo tsopano ndi oipisitsa kwambiri kumposa kaafiriyo. Murtad ndi dzina lonyansa kwambiri.
MURTAD: Ndi munthu yemwe watuluka Chisilamu nkubwelera ku kufr, potsimikiza ndi mau ake, ntchito zake, kapena kusiya kugwiritsa ntchito Chisilamu komanso kusiya Chikhulupiliro cha Chisilamu.
Koma dziwani kuti si onse omwe achita kufr amakhala murtad, chifukwa pali zifukwa zina zimene zimatha kumuletsa Msilamu kuti asakhale Kafir wotuluka Chisilamu pa zomwe wachita, monga umbuli, kumva molakwika, kukakamizidwa komanso kulakwitsa. Chimodzi mwa zinthu zimenezi chikapezeka mwamunthu yemwe wachita kufr yomtulutsa Chisilamu kuti ndi chomwe chamchititsa, samayenera kugamulidwa kuti ndi kafir.
Choncho langizo langa kwa abale anga Mchisilamu, ngati wina wake watiuza kuti watuluka Chisilamu, tidziyang’ana zinthu zimenezi tisanamutchotche, chifukwa akhonza kukhala kuti wachita mwaumbuli … makamaka kuchuluka kwa umbuli pa deen komwe kuli masiku athu ano. Kutuluka mChisilamu nchimodzimodzi maliro…mudzimulilira m’bale wanu monga mmene mumalilira akmwalira…chifukwa akangotuluka shariah ikuti ndi maliro amenewo basi.
Ndiye pali matulukidwe ena Chisilamu) omwe simapangitsa kuti asakhale kaafir, koma akangopezeka nazo mbiri zimenezo basi ameneyo palibe zokambirana, watuluka. Monga kutukwana Mulungu Allah, kutukwana Mmtumiki wake salla Allah alaih wasallam, kapenanso kulengeza poyera kusakhulupilira kwake (kukhala atheist – munthu osakhulupilira za Mulungu). Yemwe angachite chimodzi mwa zimenezo nkusabwelera kupanga tawba pambuyo pakuzindikira, ndithu ameneyo ndi murtad woonekera.
Tsopano kwa yemwe m’bale wake zatsimikizika kuti ndi murtad mopanda kukaikira, makhalidwe ake adzikhala naye chonchi:
  1. Mumulangize ndipo mulimbikire kumulangizako ndikumuitanira kwa Allah Ta’ala mpaka abwelere ndikupanga tawba.
  2. Muli ololedwa kumuyendera ndikumakambirana naye komanso kukhala naye ncholinga chomupanga da’wah komanso kulimbikira kumuwongola kuti Allah amuike mchiwongoko. Izitu koma kwa amene ali ndi ‘ilm komanso angakwanitse, chifukwa pali kumuyendera nkumakhala naye pansi mapeto ake nkupangidwa da’wah iwe nkupanganso riddah.
  3. Muli ololedwa kumamuonetsera chikhalidwe chabwino panthawi imene mukuyesetsa kumupanga da’wayi, pomupatsa tima gifts tosiyanasiya tomusintha mtima kuti aganize zopanga tawbah.  Tsopano akalephereka ndipo watsimikiza kuti sangabwelerenso,
  4. Mumusamukire, kapena kumutalikitsa ndi inu, ngati mukuona kuti kutero kuthandiza kumupewa poti anali okondedwa wanu tsopano wasanduka m’dani, ndiye mukuyenera kuchita zotheka kuti ena asapangidwe ta’atheer influence ndi u ridda wakewo…akhale yekha mmenemo.
  5. Mudzitsalikitse ndi momwe alirimo, monga kufr ndi riddah (musamuthandize kalikonse kamene kakupanga promote status yake ya ukafir komanso u murtad.
  6. Musamuthandize pa zochita zake, komanso kukhala naye pa ubwenzi uliwonse ngakhale kumukonda. Chifukwa mmene wangoteromo ndithu wadula link iriyonse pakati pa iye ndi Asilamu. Bolanso kaafir timalangizidwa kuti tidzikhala naye mwachikondi kuti mwina angalowe Chisilamu malinga ndi chikhalidwe chathu, koma uyuy ndiye maliro ndithu.
Zonsezitu mukuyenera kuchita podziwa kuti munthuyo zotsatira za kusiya Chisilamu ndi zoti tsopano ndi okwiyiridwa ndi Allah Ta’ala, kwiyo waukali kotheratu, ndipo shari’ah sikumulola kuti akuyenera kutsala mu condition ya riddah imeneyo. Komanso oteroyo mu Shari’ah sakuloledwa maufulu onse a Asilamu. Choncho simukufunika kungomusiya kuti poti wafuna kutuluka, koma muyesetse ndithu kutaya nthawi yanu pa iyeyo pomupanga da’wah yokwanira yomuonetsa chiwongoko, kudzeranso mu chikhalidwe chanu chabwino ndi mbiri zanu zokongola.
Ndiye mwachidule pa zonsezi, kukhala naye munthu otereyu kukuyenera kukhala munjira ziwiri izi:
  1. Kumuitanira ku deen kuti mumupulumutse ku kufr yakeyo
  2. Ngati walephereka kotemetsa nkhwangwa pamwala, kwiyani naye ndikumusamukira.
Chisilamu sichili ngati zipembedzo zinazi zopanda address kwa Allah, zoti anthu amangosintha ngati malaya popanda ma divine reaction based on the legislation.
Allah ndiye Mwini kudziwa Zonse