Ndimafunsidwa kawirikawiri: “…ndinu wa Sunni … Qadriyya … Shia … Ashaaira … kapena Muutazila??
Koma ine mainawa ndimangomva sindikudziwa kuti ndichani. Ndiye ndimafuna ntadziwa kuti zikutanthauza chani, komanso ndikufunikira kwanji koti munthu akhale mu chimodzi mwa izo.
~~~~~~~~~~~
Ndingofotokoza matanthauzo ake, poti nkhani zimenezi zili pa list kale tikulowera komweko in sha Allah.
1. Sunni:
Ndiyambe kaye ndi Ahlu Sunnah wal Jamaah. Awa ndi anthu omwe amatsatira Sunna za Mtumiki salla Alaih wasallam ndi ma Sahaba ake, ndipo sanagawanike timagulu. Zikhulupiliro zawo zimachokera mu Qur’an ndi Sunnah, zomwe zinalongosoledwa ndi Mtumiki komanso ma Sahaba komanso omwe anadza mibadwo iwiri pambuyo pawo. Ahlu Sunna wal Jamaah amadana ndi zinthu za bid’ah.
Aliyense wotsatira chiphunzitso chimenechi amatchedwa Ahlu Sunnah wal Jamaah. Ndipo chifukwa choti zonse zomwe amatsatirazo zimachokera kwa Mtumiki ndi ma sahaba komanso ma imaam olungama oyambilira omwe amatchedwa kuti ma Salaf Swalih (anthu olungama omwe anapita), otsatira amatchedwa kuti ma “Otsatira Manhaj ya ma Salafi, kapena kuti ma Salafiy mwachidule”.
Ili ndi gulu lolungama lomwe silinagawanike timagulu, koma onse anagwirizana kutsatira sunnah .. ndipo Mtumiki analitchula mu Hadith pambuyo pofotokoza kuti Ummah wake udzawanika magulu ndipo onsewo akalowa kumoto kupatula limodzi, limodzi lake la Iye Mtumiki ndi ma Sahaba ake.
Koma pali timagulu ta bid’ah tambirimbiri tomwe timadzitcha kuti ndi ma Sunni osati Ahlu Sunnah wal Jamaah.
2. Shia:
Ndi gulu loipisitsa mu chikhulupiliro lomwe linatuluka mu gulu la Ahlu Sunnah wal Jamaah, ndipo chiyambi chakupezeka kwa ma Shia kunali pa chikhulupiliro choti Ali radhia Allah anhu amayenera kutsogolera pambuyo pa Mtumiki, osati Abubakar. Ndiye amawatembelera achina Abubakar, Umar, Uthman ndi Mkazi wa Mtumiki, Aaisha, amanena kuti onsewa ali kumoto … pali ndithu zikhulupiliro zambiri zosemphana ndi Ahlu Sunna, zomwenso zimawatulutsa mu Aqeeda yolondola, ndipo amakanira Sunnah, zambiri mwa izo ndi za shirk, za haram komanso za bid’ah. Timagulu tina ta Sunni timatenganso zikhulupiliro zina ku mashia….
3. Qaadiria:
Ndi limodzi mwa timagulu tochokera mu gulu la Sufi. Sufi ndi gulunso lomwe linatuluka mu Aqeeda yolondola ya Mtumiki ndi ma Sahaba ake, ndipo timagulu ta Sufi timeneti timatchedwa ndi maina a ma imaam omwe anayambitsawo, amayamba ndi Twariqatu … (monga twariqatu Qadiriya, twariqatu Ahamdiya, twariqatu Qadiyaniya, Shadhiliya, Rifa’iya ndi ena ambiri).  Tsopano Twariqatu Qadiriya amene anayambitsa ndi Sheikh Abdul Qaadir Jilani, nchifukwa chake inatchedwa Qaadiriya. Mirza Ghulam Ahmad anayambitsa Ahmadiya, etc.
Timagulu tonseto (tima twariq) tadzadza ndi shirk, bid’an ndi haram, monga kupempha kwa anthu akufa ndi zina zotero. Zonsezi chifukwa chiyambi chawo kunali kutuluka mu Sunnah. Ndipo zochitika zawo zambiri sizimasiyana ndi za ma Shia. Koma ngakhale amadzitcha kuti ndi ma Sunni, u Sunni wawo si wotsatira sunna za Mtumiki ndi ma Sahaba… Otsatira za Mtumiki ndi ma Sahaba popanda kugawanika komanso kubweretsa malamulo awo amatchedwa Ahlu Sunnah wal Jamaah (Jamaah – kutanthauza kuti anagwirizana pa kutsatira sunnah ndipo sanagawanike timagulu)….
4. Mu’tazila:
Ndi otsatila a Waaswil bun ‘Atwaa, yemwe anali student wa Imaam Al Hasan Al Basri. Chomwe chinachitika nchoti Al Hasan Al Basri atafunsidwa kuti kodi judgment ya munthu yemwe wachita tchimo lalikulu ndi yotani,,,ndi kaafir, kapena mu’min? Al Hasan anayankha kuti: ameneyo ndi kaafir koma ukafir wake wakupunguka imaan osati wa kafir weniweni.
Pamenepo  Waaswil bun ‘Atwaa anatsutsa kuti: “koma ine sindikugwirizana nazo, ine ndikuti: ameneyo sangakhale mu’min komanso sangakhalee kaafir, koma ali pakatikati.
Kuchokera pamenepo panayambika madh’hab onena kuti munthu akhonza kukhala pakatikati pa kafir ndi mu’min. Koma mfundo imeneyo ndiyosalondola chifukwa munthu amayenera kukhala mbali imodzi (Mu’min kapena kaafir), Msilamu amatha kukhala ndi imaan yopunguka kapena yokwanira.
Ndiye pokakamira mfundo yakeyi, anangotuluka mu kalasi ya Al Hasan Al Basri ija (yemwe anali kuphunzitsa za Ahul Sunnah wal Jmaah), ndipo anayambitsa kagulu nkutsatidwa ndi anthu ena…kanakula kagulu kameneko ndi mfundo zolakwika ngati zimenezi, mpaka panopa.
Tsopano dzina loti Mu’tazila linachokera pa word yoti _i’tazala = wapanga withdraw_, chifukwa choti anapanga withdraw kalasi ya Ahlu Sunnah wal Jamaah, basi anthu omutsatira onse amatchedwa ma Mu’tazila (anthu opanga withdraw kalasi ya Ahlu Sunnah wal Jamaah).
5. Al Ashaa’ira:
Ndi gulu lomwe anayambitsa Abu Al Hasan Al Ash’ariy amene anatuluka kuchokera mu gulu la Mu’tazila. Abu Al Hasan anali mu Mu’tazila ndiye anatulukamo nkutsatidwa ndi anthu ena ndikuchitika kagulu mudzina lake (Al Ash’ariy = Al Ashaaira). Anthu amenewa maumboni awo pa deen yawo ya Chisilamu amagwiritsa ntchito mau ndi maganizo awo (philosophy). Amakanira mbiri za Mulungu zambiri ndipo amakhulupilira 7 zokha….
Tikaonesetsa tipeza kuti anthu amene amatsatira magulu 2,3,4,5 aja, ndiye kuti amatsatira asakudziwa mbiri zake, komanso zoona zake. Chifukwa magulu onsewa nthawi ya Mtumiki kunalibe. Ndiye munthu pakalipano akumasankha kuti mtsogoleri wake mu deen akhale munthu yamwe anayambitsa kagulu,,,kusiya utsogoleri wa Mtumiki ndi ma swahaba ake.
­­Zimenezo ndiye matanthauzo ake a zomwe munafunsazo, koma zambiri ndidzatambasula polongosola gulu limodzilimodzi palokha in sha Allah
Khalani “Ahlu Sunnah wal Jamaah” kutanthauza kuti  Msilamu yemwe amatsatira Qur’an ndi Sunnah za Mtumiki ndi ma Sahaba ake”. Ndipo mupewe kujoina timagulu tiyambitsidwa ndi anthu.
Mupeza kuti munthu kungomuyankha kuti Nadine Msilamu basi ndilibe gulu mmagulu omwe mwatchulawo, amakunena zachipongwe, akufuna kuti uwauze kuti ndiwe wa magulu  awowo, omwe ngakhale iwo sakudziwa kuti zimatanthauza chani.
Allah atiwongolere ku njira yowongoka.