Mzimayi ndi okakamizidwa (Faradh) kubisa thupi lonse kupatula nkhope yake ndi manja ake. Ili ndi lamulo la Chisilamu lomwe mzimai wa Chisilamu akuyenera kutsatira ndipo palibe kupatula. Ena amanena kuti hijab ndi choice (kuisanklha kwawo)..ayi ndithu, kuteroko ndikulakwitsa, koma adziti Hijaab ndi kusankha komwe anawasankhira Allah ndipo iwo alibe kusankha kulikonse pa lamulo la Allah.
Lamuloli likhale chomwecho popanda kuonjezera kapena kupungula potengera mmene dziko likuyendera. Tikatsatira bwinobwino lamuloli momuopa yemwe analamula komanso amalamula dziko lapansi ndi kumwamba, tipeza kuti mu Chisilamu mulibe modern hijab (yomwe imasemphana ndi hijab ya mu Qur’an ndi Hadith). Koma tikatsatira lamulo ndi zofuna za shaytan ndi azibale ake, omwe amasoka zovala za azimai mokomera zofuna za shaytan, tivomereza ndikutsimikiza kuti hijab ndi imeneyo komanso tikhonza kuisintha mmene shaytan akufunira.
MPANGO/DUKU+T-SHIRT  —  MKANJO WAUTALI WOTHINA
Pakali pano bodza loti HIJAB ndiye mpango wa mmutu linakhanzikika ndipo linasanduka choonadi. Bodza la kuvala t-shirt kapena trousers lirilonse nkumayenda panja linakhanzikika ndipo anasanduka kukhala mavalidwe a Chisilamu.
Mzithunzi zomwe akumagawa azichemwali athu mma social networkmu akumati hijab atavala mpango kumutu, malaya odula mikono komanso osalabada kumusiku .. pamenepo ndiye kuti ali mu jeans, T-shirt kapena dress lalitali lothina lowonetsa mmene ziwalo zake zadutsa. Nkumati hijab fashion.
MPANGO SI HIJAB,  koma ndi gawo chabe la hijab. Ngati mzimayi angavale mpango okha kumutu ndikuvala zovala zodula manja kapena miniskirt (zovala zazifupi), kapena trouser, kapena mkanjo wothinitsa nkumawonetsa mmene thupi lake ladutsa, ameneyo adziwe kuti ali maliseche ndipo sakuyenera kuchoka pakhomo pake atavala motero. Ngati atero ndiye kuti amakhala haram kumuyang’ana mpakana atavula zovalazi mkuvala zozilemekeza. Ndipo pachifukwa chimenechi amapeza NSAMBI nthawi yonse imene zovala zimenezi zili pathupi pake nkumaonedwa ndi amuna achilendo kwa iye.
Tikamakamba zokhunza Hijab, ma sisters ambiri amayankha kuti “nchifukwa chiyani mumalimbana ndi ife ngati kuti inu mumavala molongosoka?” Astaghfirullah! Mau awa amasonyeza kuti zomwe zikuyankhulidwazo zikupita kwa yemwe sakuzindikira kuti kodi lamuloli lachokera kwa ndani. Ngati tingamayankhe choncho tidziwe kuti sitikuyankha munthu yemwe akuyankhulayo, koma tikutsutsa molimbana ndi Allah Yemwe walamula zimenezo. Choncho sister ngati tikukaikira pa nkhani yomwe tikulangidzidwa ndibwino kupempha nzeru pa nkhaniyo kuti tidzipanga mozindikira chabwino ndi choipa ena ake asanatizuzule.
Za chisoni kwambiri lamulo limeneli lasanduka ngati khala lamoto moti yemwe angavale mmene Chisilamu chikunenera, amaoneka kwa anzake ngati otsalira wa chimidzi.
Sisters, mukutsatira malamulo ati? inu timakulemekezani ngati azimayi athu, zisungileni ulemu wanu, tsatirani malamulo a kavalidwe kachisilamu. Akazi a Mtumiki salla Allah alaih wasallam anali ma Ummahaatul Mu’mineen ‘azimai a okhulupilira’ choncho inu ngati muli Asilamu, pangani zomwe azimai amenewa ankapanga, monga mmene mukumatengera maina awo. Tisanyozetse mbiri ya Akazi a Mtumiki…tisanyozetse Chisilamu.
Mzimayi akavala modzilemekeza ngakhale amuna amakhala ndi mantha, koma akavala zominula zothina zopanga attract amuna, ngakhale wamisala amamuimika nkumufunsila chifukwa cha mavalidwe ake osadzilemekeza…owoneka bwino mmaso a wamisala…iye nkumadzidandaulira amvekere: “anthuwa bwanji kodi?  Kundiona kutchipa eti?” pomwe wayamba wadzitchipitsa yekha.
Azimayi a maSheikh, ana a maSheikh, atsikana athu a school tiyeni tisatayilire, tikhale oyambilira kukhala chitsanzo powalimbikitsa ena. Ndizinthu zomvetsa chisoni kuona mkazi wa Sheikh akuvala ngati…., akuti bola avala mpango kumutu kwao. Ayi sichoncho. HIJAB SIMPANGO. HIJAB SI MPANGO! Onani mmene azimai a Sheikh wamkulu Salla Allah alaih wasallam ankavalira (ofcourse simingawaone koma kungofufuza mbiri zawo).
Nanunso Ma Sheikh agulireni akazi anu zovala zoyenera monga Msilamu wa chizimayi. Inutu mwakhalira mpando wa Mtumiki….choncho azikazi anuwonso akhalira mipando ya akazi a Mtumiki….udindo womwe mukafunsidwe.
Si a sheikh okhatu nkhaniyi..komanso Msilamu aliyense.
Ndithu Allah tsiku lomaliza adzafunsa bambo aliyense za udindo wake umene anali nao pa mkazi wake ndi ana ake komanso pa azibale ake. Ngati tingalephere kukwaniritsa ma udindo athuwo Allah akatilanga.
MTUMIKI salla Allah alaih wasallam ananena kuti ndithudi Mulungu ndi okongola ndipo amakonda zinthu zokongola.
Ndiyeno kwabwera system yomavala hijab munsewu masana wokha. Akuti kuimvesetsa aayah yoti waja’alna llayla libaasa (ndipo takuikirani usiku kukhala chofunda) kkkk. Pamenepo akuti poti usiku ndi chofunda basi palibenso chovalira hijab! Sisteri wa Chisilamu ameneyo, subhaanallah.
Tikamakamba za hijab, Alhamdulillah ena amavala, koma vuto ndi loti amavala pochita manyazi ndi anthu, nchifukwa chake dzuwa likangolowa amavula nkumakayendayenda mma lodge. Ena amakalowa malo amenewa ndi ma hijab..zomvetsa chisoni akuti poti azibale awo sakuwaona. Kodi hijab analamula ndi m’bale wako? Upange zoti umusangalatse Allah yemwe anakulenga nkukusankhira Deen nkukupatsa malamulo oti udzitsatira ukalowe ku jannah.