Olemba: Sheikh Qullab T Jim

Mneneri Nuhu (Nowa) ndi Mneneri wachiwiri kutumizidwa padziko lapansi pambuyo pa Mneneri Adam mwa Aneneri onse omwe Allah anawatumiza kwa anthu ndi cholinga chowawongelera ku njira yowongoka powayitanira iwo ku umodzi wa Mulungu (Tauhid), kukhulupilira mwa Aneneri  komanso za umoyo umene uli mkudza.   Padadutsa zaka mazanamazana pambuyo pa Mneneri Adam Mulungu asangalare naye, dziko lapansi linali litadzadza ndi ana a Adam. Chifukwa cha kutalika kwa nthawi, Ana a Adam anamuyiwala Mulungu ndipo anayamba kugwadira ndi kupembedza mafano owumbidwa komanso kusemedwa kuchokera ku mitengo ndi miyala. Iwo anadzadzidwa ndi makhalidwe oipa monga kugwadira mafano, kunama, kuba, umbombo ndi zina zambiri.

Pachifukwachi Allah wachifundo komanso wachisoni chosatha anamutumiza Mneneri Nowa (Nuhu) Mulungu asangalare naye kwa anthu amenewa ndicholinga chofuna kuwabwezera ku njira yowongoka. Nuhu anawayitana anthu kuti abwelere ku umodzi wa Umulungu (Tauhid). Anawaletsa kugwadira mafano ndi zina zambiri zomphatiza Mulungu ndi zinthu zina zomwe aamazikonza kha ndi manja awo. Ndipo anawachenjeza iwo za kuwopsa kwa ng’anjo ya moto.

Nuhu anayesetsa kuwayitanira anthu pogwiritsa nthito njira ina iliyonse yomwe ingathandize kuti anthu abwelere ku umodzi wa Allah ndi kusiya zoipa mobisa, mowonekera komanso molimbikira, koma iwo anali agonthi ndipo kuitanira kwake sikunathandize chilichonse kupatula kuwonjezera pa kudzitukumula ndi kupitiliza kuchita kwawo zoipa. Iwo anali kumuseka, kumunyogodola, kumchitira zipongwe zosiyanasiyana ndipo anamuyitana iye ndi mayina osiyanasiyana achipongwe monga wabodza, openga, komanso wamisala. Allah akuchitira umboni pankhani imeneyi m’bukhu lake lolemekezeka motere: “Anthu a Nuhu adatsutsa Atumiki. Pamene adawawuza Nuhu m’bale wawo kuti: “Kodi simufuna kuwopa (Mulungu ngakhale nditakuwuzani zowopsa zimene zikukudikirani)?Ndithu ine kwa inu ndi Mtumiki okhulupirika. Choncho muwopeni Mulungu ndipo ndimvereni. Ndipo sindikukupemphani malipiro pa zimenezi, malipiro anga ali kwa (Mulungu) Mbuye wa zolengedwa zonse. Choncho muwopeni Mulungu ndipo ndimvereni.  (26:105:117)

Uku kunali kuitanira kwa Nuhu powayitana anthu ake kuti abwelere kwa Allah koma iwo anamuyankha iye modzitukumula motere: “Ndithu ife tikukuwona iwe kuti uli mkusokera kowonekera (Potiletsa izi zomwe tidawapeza nazo makolo athu)”. (7:60).

Nuhu anakhala kwa nthawi yokwana chikwi chimodzi kupatula mazana makumi asanu (950) koma ngakhale kuti anakhala zaka zochuluka chotere, anthu ochepa okha ndi omwe anamukhulupilira ndi kuvomera kuyitanira kwake ngakhale mkazi wake komanso ena mwa ana ake sanamukhulupilire Iye. Allah akulankhula motere: “Ndipo ndithu tidamtuma Nuhu kwa anthu ake ndipo adakhala nawo zaka chikwi chimodzi kupatulapo zaka makumi asanu (koma mnthawi yonseyi sadatsatire ulaliki wake). (29:14)

Nuhu adatopa komanso kudabwa ndi kulimba ngati miyala kwa mitima ya anthu ake. Iye anali odabwa kwambiri ndi kukanira kwa anthu ake pa chowonadi ndi kukamira kwawo pakugwadira mafano komanso pa kukakamira kwawo pa zinthu zomwe sizingawathandize iwo china chilichonse kapena kuwapezetsa mavuto. Ndipo iye atatsimikiza mumtima mwake za kukanira kwa anthu ake, anawapemphera iwo chiwonongeko. Iye anapempha motere: “Ndipo adanena Nuhu (atataya mtima za anthu ake): Ambuye musasiye aliyense mwa osakhulupilira kukhala padziko. Ndithu Inu ngati muwasiye (popanda kuwawononga ndikuwathetsa)  asokeretsa akapolo anu (kunjira yolungama) ndipo sangabeleke (ana abwino) Koma oipa, osakhulupilira (okhala kutali ndi chowonadi komanso onyoza Inu). Komanso iye anapempha momulilira Mbuye wake motere: “Nuhu anayitana Mbuye wake nati: “Ine ndagonjetsedwa ndi anthu anga choncho ndipulumutseni”. (54:10). Komanso iye anamupempha Allah kuti ampulutse iye pamodzi ndi omutsatira ake omwe anakhulupilira motere: “Nuhu adati (kwa Mulungu): “Mbuye wanga ndithu anthu anga anditsutsa. Choncho weruzani pakati panga ndi pakati pawo (chiweruzo chabwino) Ndipo ndipulumutseni pamodzi ndi amene alinane mwa okhulupilira.”. (26:118).

Allah anavomera mapempho a Nuhu ndipo anamulamura Iye kuti akhome chombo. Apa Nuhu anayamba kukhoma chombo monga momwe Allah anamulamulira. Iyi siyinali ntchito yaying’ono. Koma Mneneri Nuhu  anakwanitsa kutero ngati m’mene Allah akulankhulira m’bukhu lake lolemekezeka motere: “ Ndipo khoma chombo moyang’aniridwa ndi Ife. Ndi ulangizi wathu (satha kukuchitira choipa) Ndipo usandilankhulitse za iwo amene achita zoipa (kuti ndiwakhululukire). Ndithudi iwo amizidwa.” (11:37).

Pomwe anthu anamuwona Nuhu akukhoma chombo anamuseka mwachipongwe ndipo anaganiza kuti Nuhu wachita misala. Iwo sanawone chifukwa chokhomera chombo kumachita kuti dera lawo linali lotalikirana kwambiri ndi Nyanja pachifukwachi iwo anali kunchitira iye zitonzo komanso zipongwe zosiyanasiyana. Allah akulankhula motere: “Ndipo (Nuhu) adayamba kukhoma chombo. Nthawi iliyonse akamdutsa akuluakulu a mwa anthu ake, adali kumchitira chipongwe. Naye ankanena kuti: “Ngati Inu mukutichitira chipongwe, nafenso tidzakuchitirani chipongwe momwe mukutichitira chipongwe”. (11:38).

Iwo anali kufunsana wina ndi nzake kuti kodi cholinga chokhomera chombo chinali chiyani mdera lopanda mitsinje komanso lotalikirana ndi nyanja? Mosakhalitsa anazindikira kuti zonsezi ndi chifukwa cha chikonzero cha Allah chofuna kuwawononga anthu onse osakhulupilira kupatula okhawo mwe anakhulupilira ndi kumuthandiza Nuhu.

Nuhu anawawuza anthu omwe amkamuchitira iye chipongwe kuti kudzabwera chigumula cha madzi chomwe chidzawapsipsitize onse osakhulupilira ndipo sadzapeza malo othawira. Izi zidangowonjezera phwete lawo pa iye. Koma chikonzero cha Allah chinawonekera ndi kutsimikizika  ndipo osakhulupilira anadziwonera okha ndi maso awo.

Patadutsa masiku ambiri a ntchito yadzawoneni, Nuhu anamaliza kukhoma chombo mumphamvu ya Allah. Kenako Allah anamulamula Nuhu kuti akweze m’menemo mtundu uliwonse wa nyama ziwiziwiri (yaikazi ndi yaimuna). Kenako iye ndi omutsatira ake anakwera mchombo muja. Musayembekezera, mitambo ya mvula inasonkhana komanso ziphariwari zinang’anima ndi kugunda mochititsa manda komanso kunagwa mvula yosalekeza.  Mvula inagwa mosalekeza ndipo nthaka yonse inasefukira ndi madzi. Madzi anali ponseponse. Chamoyo china chilichonse chinamira kupatula zomwe zinali mchombo cha Nuhu chomwe chinali kuyenda pamwamba pa mafunde akuluakulu ngati mapiri. Qur’an yolemekezeka ikuchitira umboni za nkhaniyi motere: “Ndipo Nuhu adati: “Kwerani m’menemo mwadzina la Mulungu mkuyenda kwake ndi mkuyima kwake. Ndithu Mbuye wanga mngokhululuka kwambiri mngwachisoni. Ndipo chombocho chinali chikuyenda nawo m’mafunde onga mapiri. (11:40-41) . Komanso Allah akulankhula mundime ina motere: “Tidatsekula kumwamba ndi madzi otsika mopitiliza, mwamphamvu. Ndipo tidaying’amba nthaka kukhala ndi akasupe ofwamphuka ndi madzi mwamphamvu. Choncho adakumana madzi (akumwamba ndi amnthaka  kuti awawononge)  pamuyeso opimidwa ndi kulamuridwa ndi (Mulungu). Ndipo Tidamunyamula Nuhu pa chombo chokhomedwa ndi matabwa okhomedwa ndi misomali (yamitengo) Chinkayandama pamadzi ndi kuyang’aniridwa ndi Ife. Iyi ndi mphoto ya Nuhu yemwe anakanidwa ndi anthu ake. Ndipo ndithu tidachisiya (chigumula) kukhala phunziro (pakuonongeka kwa osakhulupilira ndi kupulumuka kwa okhulupilira). Kodi alipo olikumbukira ndi kupeza nalo malango abwino? Kodi chidali bwanji chilango change ndi machenjezo anga (kwa onyoza?).

Chigumula cha madzi osefukira chinapitilira kwa miyezi isanu (5) ndipo chinawawononga onse osakhulupilira kuphatikizapo mwana wake odzibelekera yekha yemwe anali osakhulupilira. Huhu anapepmha chilorezo kwa Allah kuti amukweze mwana wake mchombo koma Allah anakana. Anamuwuza iye kuti mwana  osakhulupilirayo sanali m’modzi mwa am’banja lake. Nuhu anapepesa kwa Allah pomupempherra chipulumutso mwana osakhulupilira ndipo Allah anamukhululukira. Ndipo Nuhu ndi onse omwe anamutsatira anali otetezedwa mchombo. Allah Akuyankhula motere:  “Ndipo Nuhu adafuulira Mbuye wake Nati: “E Mbuye wanga! Ndithu mwana wanga ali mgulu la anthu akubanja langa (akuwonongedwa). Ndipo ndithu lonjezo lanu ndi lowona, Ndipo Inu ndi oweruza mwachowonadi kuposa aweruzi onse”. (Mulungu) Adati: E Iwe Nuhu!  Ndithu Iyeyo simwana wa m’banja lako. Iye zochita zake sizili zabwino. Choncho usandipemphe zomwe siukuzidziwa Ine ndikukulangiza kuti usakhale mgulu la anthu osazindikira (mbuli). (Nuhu) Adati: “E Mbuye wanga! Ndikudziteteza mwa inu kuti ndisakupempheninso zomwe sindikuzidziwa. Ngati simundikhululukira ndi kundichitira chifundo, ndikhala mwa anthu otaika”. Kudanenedwa; E Iwe Nuhu! Tsika (panthaka yowuma) mwamtendere ochokera kwa Ife .”. (11:45-47).

Pamapeto pake, mitambo inayamba kuyera ndipo chombo cha Nuhu chidayima paphiri lotchedwa Jud (ku turkey). Kenako Nuhu ndi anthu ake anatsika mchombo ndipo Iwo anapululumuka pomwe osakhulupilira anawonongedwa ndi chilango cha madzi. Qur’an yolemekezeka ikutsindika za nkhaniyi motere: “Ndipo pambuyo powonongeka onse ndi zonse zomwe Mulungu adafuna kuti ziwonongeke; Kudanenedwa: E! Iwe nthaka! Meza madzi ako ndipo Iwe thambo amange madzi ako amvula. Choncho madzi adaphwa ndipo lamulo lidakwaniritsidwa (lowononga anthu oipa). Ndipo chombo chidaima (paphiri lotchedwa) Jud. Ndipo kudanenedwa: Awonongeke onse ochita zoipa”. (11:44). Komanso pokhudzana ndi m’mene Allah anamupulumutsira Nuhu ndi anthu  ake kuchigumula cha madzi, mundime ine Allah akulankhula motere: “Tidampulumutsa Iye ndi anthu ake mchombo; ndipo Tidachita izi kuti likhale phunziro kwa zolengedwa. (29: 15). Umu ndi m’mene Allah anampulumutsira a Nuhu ndi anthu ake.

Kenaka Allah anapeleka madalitso komanso chifundo chake pa ana a Nuhu kotero kuti anabelekana ndi kuchulukana padziko lapansi. Nkhani imeneyi ikutiphunzitsa ife kuti zotsatira za kusakhulupilira ndi kulandira chilango chowopsa kuchokera kwa Allah Mbuye wa zolengedwa zonse. Allah akulankhula mu Qur’an yolemekezeka motere: “Ndipo tidawamiza aja otsutsa aya zathu. Ndithudi iwo adali akhungu. (7:64).

Nkhaniyi ikutiphunzitsa kuti anthu akale adakana komanso kutsutsa Aneneri a Mulungu monga momwe ma Quraish adamkanira Mtumiki wathu Muhammad madalitso ndi mtendere zikhale pa iye, koma Mulungu adawawononga ndi kuphwasula midzi yawo powapatsa iwo zilango zosiyanasiyana monga Ngati momwe anthu a Nuhu adamkanira Mneneri  wawo ndi zotsatira za chilango chomwe Iwo adalandira chifukwa cha kusakhulupilira kwawo.

Komanso nkhaniyi ikutiphunzitsa kuti Allah anali kumubvumbulutsira Mtumiki wathu Muhammad madalitso ndi mtendere zikhale pa Iye nkhani  za mibado ya anthu akale ndi Aneneri  awo ndicholinga chofuna kumulimbikitsa iye kuti ayenera kupitiliza kufalitsa uthenga wa Mbuye wake ngakhale atakanidwa ndi anthu ake chifukwa choti Iye si Mneneri oyamba  kukanidwa ndi anthu ake.  Komanso kufuna kumutsimikizira Iye kuti sizingamulake Mulungu kuwapatsa osakhulupilira chilango ngati m’mene Iye adawalangira anthu a Nuhu komanso onse omwe adakana  ndi kutsutsa Aneneri awo koma kuti wawasungira chilango chowopsa.

Komanso ikutiphunzitsa kuti tiyenera kutengerapo phunziro ngati m’mene Allah akulankhulira m’bukhu lake lolemekezea motere: “Ndithudi mnkhani zawo izi mulu phunziro kwa eni nzeru” (12:111).

Komanso mundime ine Allah akuyankhula motere: “Ndipo ndikusimbira zonse mwa nkhani za Aneneri zomwe tikukulimbikitsa nazo. Ndipo mzimenezi chowonadi chakufika ndi ulaliki komanso chikumbutso kwa okhulupilira”. (11:120-121).

Ndikumpempha Allah kuti  atipange ife kukhala ogwiritsa pa chowonadi komanso atitalikitse ndi zonse zomwe zingapangitse kuti tikhale otalikirana ndi mtendere komanso chifundo chake!! Ameen!!!

Allah ndi Amene ali odziwa zonse