KUCHOTSA KUSAMVETSETSA PA MA HADITH OMWE ABWERA KUTI “MLIRI SUDZALOWA MU MZINDA WA MADINAH”

(Abu Shareef C Idris)

Download PDF>>

الحمد لله، القائل ﴿ أَحَسِبَ النَّاسُ أَنْ يُتْرَكُوا أَنْ يَقُولُوا آمَنَّا وَهُمْ لَا يُفْتَنُونَ ﴾ وقال ﴿ وَلَنَبْلُوَنَّكُمْ بِشَيْءٍ مِنَ الْخَوْفِ وَالْجُوعِ وَنَقْصٍ مِنَ الْأَمْوَالِ وَالْأَنْفُسِ وَالثَّمَرَاتِ وَبَشِّرِ الصَّابِرِينَ﴾ والصلاة والسلام على رسول الله،  الذي قال “عجبا لأمر المؤمن إن أمره كله خير وليس ذاك لاحد إلا للمؤمن وإن أصابته سراء شكر فكان خيرا له، وإن أصابته ضراء صبر فكان خيرا له” وعلى آله وصحبه ومن والاه أما بعد

Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Yemwe akunena kuti: Kodi anthu akuganiza kuti adzasiyidwa popanda kuyesedwa ndi masautso pakungonena kuti: “Takhulupilira?” (Iyayi, ayenera kuyesedwa ndithu, ndi masautso osiyanasiyana pamatupi pawo ndi pachuma chawo kuti adziwike woona ndi wachiphamaso)” Sûrat Al Ankabût 2

Akunenanso kuti:

“Ndipo tikuyesani ndi chinthu choopsa (monga nkhondo), njala, kuchepa kwa chuma, kutaika kwa miyoyo ndi kuonongeka kwa mbeu. Tero auze nkhani yabwino opirira” Sûrat Al Baqarah 155

Tikumpemphera zabwino Mtumiki wa Allah, yemwe ananena kuti: “Nzodabwitsa kwa wokhulupilira, ndithu zochitika zake zonse ndizabwino, komatu zimenezo sizili choncho kwa wina aliyense kupatula kwa okhulupilira; zikampeza zosangalatsa, amayamika ndipo zimakhala zabwino kwa iye. Komanso akamgwera masautso, amapilira ndipo zimakhala zabwino kwa iye” Sahih Muslim 2999, komanso tikuwapemphera zabwino akubanja lake, ma Swahaba ake ndi onse omwe akumutsatira.

Ndikupempha Allah adalitse ntchitoyi ndi kuti andipatse kuthekera kwa kulongosola mfundo zomwe ndaona kuti zithandiza kuchotsa kusamvetsetsa pa ma Hadith omwe abwera kuti “mliri sudzalowa mu Mzinda wa Madinah”. Ndipo ndikupempha Allah kuti akhululuke pa kulakwitsa kulikonse komwe kungapezeke, ndipo asakuchite kukhala njira yosochelera Ummah.

Panthawi ino dziko lonse lapansi liri kalikiliki kufunafuna mankhwala ochizira matenda omwe avuta dziko lonse. Matendawa akutchedwa Covid-19 omwe ayambika ndi kachirombo (virus) kotchedwa Corona, ndipo akhudza mbali zonse ngakhale ku Chipembedzo. Izi zachititsa kuti anthu omwe sachifunira Chisilamu zabwino komanso ena omwe samvetsa za Chisilamu m’mamvedwe olondola, ayambe kunena nkhani zabodza ndikuchipanga Chisilamu kukhala ngati chipembedzo chabodza.

Chifukwa cha kusamvetsa komanso udani wawo ndi Chisilamu, afika ponena kuti Abu Hurayrah ndiwabodza, komanso ma Hadith ena omwe ali oona ndiabodza. Ena mpaka apyola malire kufika ponena kuti Mtumiki Muhammad صلى الله عليه وسلم ndiwabodza.

لا يجوز تأخير البيان عن وقت الحاجة 

Sikololedwa kuchedwetsa kufotokoza tsatanetsatane munthawi yofunikira.

Potengera mawu amenewa, kufotokoza kwake kuli chonchi;

Funso lomwe lazunguza anthu ndilakuti:

“Kodi Covid-19 ndi mliri (twāûn/الطاعون)? Ngati uli mliri zitheka bwanji kulowa mu Madinah kumachita kuti Mtumiki صلى الله عليه وسلم adati mliri (twāûn) sudzalowa mu Madinah?”

Poyankha funso limenelo,

Choyamba tione kaye ma Hadith omwe alipo onena za twāûn ku Madinah.

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال :قال رسول الله صلى الله عليه وسلم “على أنقاب المدينة ملائكة لا يدخلها الطاعون ولا الدجال

Hadith inachokera kwa Abi Hurayrah رضي الله عنه anati; adayankhula Mtumiki wa Allah صلى الله عليه وسلم;

Muzipata zolowera mu mzinda wa Madinah muli Angelo (olondera), simungalowe mliri (twāûn) ngakhale Dajjāl”Hadith, muttafaqun ‘alayh (Sahih Al-Bukhari 1880, Sahih Muslim 1379)

Hadith yachiwiri:

عن أنس بن مالك رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم “المدينة يأتيها الدجال، فيجد الملائكة يحرسونها فلا يقربها الدجال”، قال: “ولا الطاعون إن شاء الله”

Hadith inachokera kwa Anasi bin Mālik رضي الله عنه Mtumiki صلى الله عليه وسلم adati; “Adzafika Dajjāl kuti alowe M’madinah koma adzapeza Angelo akulondera, ndipo sadzayandikira”, ndipo adati “ngakhaleso mliri (sudzalowa) in shaa Allah.” Sahih Al-Bukhari 7473

Kuchoka m’ma Hadith awiri a Sahih amenewa, pali umboni wokwanira woti Dajjāl sadzalowa mu Madinah komanso mliri sudzalowa.

Nanga Covid-19 walowa bwanji? Si mliri (twāûn)?

Pali kusiyana pakati pa twā’ûn (الطاعون) ndi wabaa’a (الوباء)

فكل طاعون وباء وليس كل وباء طاعونا

Potsata mfundo yakuti;

Mliri wina ulionse ndi matenda ndipo simatenda aliwonse kuti ndi mliri, dziwani kuti matenda (wabaa’a) akhonza kulowa mu Madinah koma mliri (twā’ûn) sungalowe.

Motero zimatheka matenda kutchulidwa kuti mliri mongofanizira kaonongedwe kake kapena kufulumira kwa kafalikiridwe kake, komanso kutenga miyoyo ya anthu ambiri mukanthawi kochepa.

Kuitchula nthenda (wabaa’a) kuti ndi mliri (twā’ûn)

قال ابن حجر؛ “وأن غير ذلك من الأمراض العامة الناشئة عن فساد الهواء يسمى طاعونا بطريق المجاز لِاشتراكهما في عموم المرض به أو كثرة الموت”

Ibn Hajar رحمه الله anati: Ndipo ena mwa matenda wamba omwe amafalikira kudzera mu mpweya, amatchedwa mliri (twā’ûn) munjira yongofanizira chabe pakuti onse ndi matenda kapena kuchuluka kwa okufa nawo (matendawo).”

Kuchokera pa zimenezo ndiye kuti matenda akhonza kulowa mu Madinah koma mliri sungalowemo. Choncho mu Hadith muja akunena za mliri kuti sungalowe koma matenda wamba achangu pofalikira ndi kufa nawo anthu, akhonza kulowa.

Tisanabweretse kusiyana kwina kwa wabaa’a ndi twā’ûn (mliri) pofuna kutsimikizira kuti Covid-19 ndi matenda chabe osati mliri nchifukwa chake walowa mu Madinah, tiyeni tione maumboni a kupezeka kwa wabaa’a.

Maumboni akupezeka kwa wabaa’a

Pamene Mtumiki صلى الله عليه وسلم anasamuka ndi ma Swahaba ake, ena mwaiwo anafikira kudwala, monga Abu Bakr ndi Bilaal رضي الله عنهما, ndipo Aaisha رضي الله عنها pakupita kwa nthawi adati:

قدمنا المدينة وهي أوباء أرض الله

“Tinafika mu Madinah uli mzinda umene Allah adaupatsa matenda” Sahih Al-Bukhari 1889

Kusonyeza kuti mu Madinah akhonza kulowamo matenda. Ndipo liwu lomwe adagwiritsa ntchito Aaisha رضي الله عنها ndi la awbaau kuchokera ku wabaa’a; zomwe zikupereka chitsimikizo chakuti matenda analiko ku Madinah.

Umboni wina ndikuyankhula kwa Bilaal رضي الله عنه mwini wake:

 أخرجونا إلى أرض الوباء”

“Atitulutsa ku Makkah kupita ku dera lomwe kuli nthenda

Umboni wina ndi kuyankhula kwa Abi As’wad:

“قدمت المدينة في خلافة عمر وهم يموتون موتا ذريعا”

“Ndinafika ku Madinah munthawi ya ulamuliro wa Umar رضي الله عنه anthu ambiri ali kufa mowirikiza (ndi matenda, wabaa’a)”

Umboni womaliza ndi Hadith imene yafotokozedwa kumayambiliro kuja, yomwe Mtumiki صلى الله عليه وسلم ananena momveka bwino kuti:

لا يدخلها الطاعون ولا الدجال

“Simudzalowa mliri (mu Madinah) ngakhale Dajjāl”.

Mtumiki صلى الله عليه وسلم sanatchule wabaa’a. Zomwe zikusonyeza kuti Covid-19 ndi wabaa’a ndipo akhonza kulowa mu Madinah, komanso izi sizikusemphana ndi mawu a Mtumiki صلى الله عليه وسلم chifukwa iye mu Hadith ija amanena mliri osati matenda wamba.

Kusiyana kwa wabaa’a ndi twā’ûn kuli m’magawo angapo:

Gawo loyamba: Wabaa’a الوباء ndimatenda wamba omwe amadza kawirikawiri chifukwa cha kuonongeka kwa mpweya (amafala kudzera mu mpweya), ndipo twā’ûn ndimatenda omwe amapatsiridwa ndi ma jinn/ziwanda.

Kuchokera mu Hadith ya Abu Musa:

فناء أمتي بالطعن والطاعون” قالوا يا رسولَ اللهِ هذا الطعنُ قد عرفناه فما الطاعونُ؟ قال “وخزُ إخوانِكم من الجنِّ وفي كلٍّ شهادة”

“Ummah wanga ambiri adzafa ndi twa’an {kuphedwa} komanso twā’ûn. Adafunsa: E inu Mtumiki wa Allah twa’an taidziwa, nanga twā’ûn ndi chani?  Adati; “ndimatenda opatsiridwa kuchokera kwa abale anu ma jinn, ndipo omwalira nawo (matenda amenewa) ndi shahid adaitulutsa Ahmad ndi Ibn Khuzaymah. Musnad Twayaalisi 536, komanso Ahmad 19528

Gawo lachiwiri: Twā’ûn ili ndi kadwalidwe kake, kapena malo okhanzikika ngati kunkhwapa, mphechepeche mwa miyendo, kuseli kwa khutu ndi malo ena monga tsonga mwa ziwalo zina.  Chitsanzo nkhate.

Potsindikizira kuti twā’ûn amakhala mu ziwalo komanso malo oikika pa thupi lamunthu, Imaam Al Nawawi رحمه الله رحمة واسعة adati;

الطاعون قروح تخرج في الجسد فتكون في الآباط أو المرافق أو الأيدي أو الأصابع وسائر البدن، ويكون معه ورم وألم شديد… ألخ

“Mliri (twā’ûn) ndi zilonda zomwe zimatuluka mthupi mwamunthu ndipo zimakonda kupezeka kunkhwapa, muzigongono, mmanja, kapena muzala ndi thupi lonse, ndipo amakhala ndi zotupa ndi ululu waukulu…” Shareh Muslim Al-Nawawi

Imaam Ibn Al Qayyim yemwe anali m’modzi mwa ma imaam odziwa za chipatala, atafotokoza kusiyana kwa wabaa’a ndi twā’ûn komanso kutchula m’malo omwe mliri umakonda pa thupi lamunthu, anadzasindika motere;

هذه القروح والأورام والجراحات، هي آثار الطاعون

“Matuza ndi zotupatupa komanso mabala ndizizindikiro (zotsatira) za mliri”. Zaadul Ma’adi

Ndipo mawu amenewa agwirizana ndi mmene Qaadhwi ‘Iyaadh ananenera:

أصل الطاعون القروح الخارجة في الجسد والوباء عموم الأمراض فسميت طاعونا لشبهها بها في الهلاك وإلا فكل طاعون وباء وليس كل وباء طاعونا

“Phata (zoona zake) za mliri ndi zilonda, matuza amakhala panja (pa thupi) pamene wabaa’a ndi matenda chabe ndipo amanenedwa kuti twā’ûn (mliri) chifukwa chofanana mu kaonongedwe ka miyoyo ya anthu, koma mliri wina ulionse ndi matenda pamene si matenda alionse omwe angakhale kuti ndi mliri”.

Kuchokera m’maumboni omwe atchulidwa m’mwambamu, ndim’menenso aliri matenda omwe azunguza lerolino. Amenewa ndi matenda chabe omwe akufanana ndi mliri pakuononga miyoyo ya anthu, koma si twā’ûn (mliri) ngati mmene ziliri ku ma Hadith aja. Nchifukwa chake alowa M’madinah ndipo ukanakhala mliri sukanalowamo.

ZOFUNIKA KUDZIWA PA CHIKHULUPILIRO CHA MAHADITH

Msilamu kukhulupilira zakuti ku Madinah sikungalowe mliri (twā’ûn) ndikokakamizidwa, ndipo amene angakanire, akukanira mawu a Mtumiki صلى الله عليه وسلم amene samayankhula zabodza, ndipo zomwe watiuza iye zimakhala zochokera kwa mwini Allah komanso zimakhala kuti zavumbulutsidwa kwa iye.

Ndipo mundime yotsimikizira izi, Allah wanena motere;

 (وَمَا يَنْطِقُ عَنِ الْهَوَى * إِنْ هُوَ إِلَّا وَحْيٌ يُوحَى)

“Ndipo sayankhula zofuna za mtima wake, kupatula zomwe zachita kuvumbulutsidwa kwa iye”. Sûrat Al Najm 3-4

Msilamu akuyenera kukhulupilira zimenezi, ndipo asakaikire zakuti mu mzinda wa Madinah simudzalowa twā’ûn ngakhale Dajjāl.

Chenjezo loyamba:

Ena chifukwa cha kusamvetsa ma Hadith awiri omwe tabweretsa kumayambiliro okamba zakuti mliri siungalowe ku Madinah, akusokonezeka ndikulowa kwa Covid-19 mpaka afika ponena kuti ma Hadithiwo ndiabodza, ena afika ponena kuti Abu Hurayrah ndiwabodza, makamaka omwe amadana naye Swahaba wolemekezekayu monga magulu a Shia.

Dziwani kuti ma Hadithiwo siabodza ndipo sali gulu la ma Hadith ofooka, koma ndi ma Hadith amene akupezeka m’mabuku odalirika a ma Hadith (Sahih Al-Bukhari ndi Sahih Muslim). Yemwe angatsutse, kapena kunena kuti Mtumiki صلى الله عليه وسلم ananena zabodza, ndiye kuti wamuchita Mtumikiyo kuti ndimunthu wabodza. Kumukanira Mtumiki ndichimodzimodzi kumunamizira. Choncho yemwe angaganize kuti ma Hadith amenewa ndiabodza, ameneyo wamunamizira Mtumiki صلى الله عليه وسلم kuti ananena zabodza ndipo malipiro a munthu otero ndimmene wanenera mwini wake:

من  كذب علي متعمدا فليتبوأ مقعده من النار

“Amene angandinamizire ine mwadala wadzikonzera yekha malo ake ku moto” Sahih Al-Bukhari 1229

Kumupekera Mtumiki صلى الله عليه وسلم bodza ndi tchimo m’machimo akuluakulu.

Chenjezo lachiwiri: 

Kukhala ndi maganizo olakwika mwa Allah kapena kuti kumuganizira Allah zosayenera, makamaka pa matenda amene avutawa, dziwani kuti ndi tchimo m’machimo akuluakulu. Komanso zikhoza kumuika munthu pachionongeko chifukwa ndizokhudza chikhulupiliro chake (aqeedah). Ngati aqeedah yamunthu ili yolongosoka, ntchito zimakhala zolongosokanso, ndipo chipembedzo chake chimalongosoka. Ena akhonza kumaganiza kuti nanga Allah waloleranji kuti matendawa afike potere? Ena malingana ndi nyengo yomwe ali akhonza kuganiza kuti Allah wawataya, maganizo onsewa ndikumuganizira Allah zolakwika.

Ndipo Al Allaamah Ibn Al Qayyim رحمه الله adati:

إن أعظم الذنوب عند الله إساءة الظن به

“Ndithu tchimo lalikulu pamaso pa Allah ndiko kukhala ndimaganizo olakwika pa iye.” Al-Daau wa Al-Ddawaau p.163, Amraadhul Quloobi (Ummu Tamima)

Allah wanenaso kuti amenewo ndianthu otayika, oluza.

(وَذَلِكُمْ ظَنُّكُمُ الَّذِي ظَنَنْتُمْ بِرَبِّكُمْ أَرْدَاكُمْ فَأَصْبَحْتُمْ مِنَ الْخَاسِرِينَ)

“Ndipo amenewo ndi maganizo anu omwe mudali kumuganizira, Mbuye wanu adakuonongani, ndithu muli m’gulu la otayika” Sûrat Fussilat 23

Pomaliza, nthawi ya matenda ngati amenewa Asilamu tiyenera kumupempha Allah chikhululuko ndi kulapa pa uchimo womwe takhala tikuchita, ndi kumupempha Allah machiritso munjira ya sharia, ndi kuti adalitse ife tonse ndi kutipanga kukhala otsata malamulo Ake.

Download PDF>>