Malamulo a Chiyuda okhunzana ndi mkazi yemwe akusamba, ndi ovuta kwambiri kuwamvetsa. Chipangano Chakale chimaona kuti mkazi yemwe akusamba ndi wodetsedwa, komanso kudetsedwa kwake “kumapangitsa ena kuti akhale odetsedwa (opanda twahara)”. Aliyense kapena chirichonse chimene angachikhudze chimakhala chodetsedwa kwa tsiku lonse:

“Ngati mkazi akukha ndipo zimene akukhazo ndi magazi, azikhala masiku 7 ali wodetsedwa chifukwa cha kusamba kwakeko, ndipo aliyense womukhudza azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Chilichonse chimene angagonepo pamene ali wodetsedwa chifukwa cha kusamba kwake chizikhala chodetsedwa, ndiponso chilichonse chimene wakhalapo chizikhala chodetsedwa. Aliyense wokhudza bedi lake azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Aliyense wokhudza chilichonse chimene mkaziyo anakhalapo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo ngati mkaziyo anakhala pabedi kapena pachinthu china, wokhudza chinthu chimenecho azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. (Levitiko 15:19-23).

Chifukwa cha chilengedwe chake “chosokonekerachi”, mkazi yemwe akusamba anali “kuthamangitsidwa” pa gulu la anthu pofuna kupeŵa kuthekera kwina kulikonse kokhunzana ndi ena kapena zinthu. Anali kutumizidwa ku nyumba yapadera “ya odetsedwa” mpaka nthawi yonse ya kudetsedwa kwake ithe. 9

Talmud imawona kuti mkazi yemwe ali kumwezi ndi “wakupha” ngakhale osayanjana naye:

“A Rabbi (atsogoleri Achiyuda) athu anatiphunzitsa: … Ngati mkazi yemwe ali kumayambiliro kwa kumwezi wadutsa pakati pa amuna awiri, (adzakhala ngati) wapha mmodzi wa iwo, ndipo ngati ali kumapeto kwake nkudutsa pakati pa amuna awiri, achititsa mikangano pakati pawo” (bPes. 111a).

Komanso mwamuna wa mkazi wakumwezi ankaletsedwa kulowa m’sunagoge ngati anaadetsedwa ndi mkazi wake ngakhale ndi pfumbi lakunsi kwa mapazi ake chabe. Wansembe yemwe mkazi wake kapena mwana wake wamkazi kapena mayi ake ayamba kusamba, samaloledwa kulalikira kapena kugwira ntchito ya usembe wake m’sunagoge. 10 Sizachilendo kuti akazi ambiri a Chiyuda amatengedwa kuti ndi “temberero”. 11

Chisilamu sichimampanga mkazi yemwe akusamba kukhala ndi “mtundu uliwonse wa kudetsedwa” monga mmene enawa achitira. Mkazi oteroyo siwoletsedwa kumugunda komanso alibe tembelero lirilonse. Amagwiritsa ntchito zonse zoyenera mmoyo wake kupatula zochepa kwambiri: Okwatira saloledwa kugonana pa nthawi ya kusamba, koma kukhunzana kulikonse pakati pawo nkololedwa. Mkazi yemwe akusamba saloledwa kupanga ena mwa mapemphero monga salaat ndi kusala.

Kuikira Umboni kwa Mkazi