Funso:

Kodi ndichifukwa chani akazi wa Chisilamu tikamawafunsira amanyada kwambiri ndipo akakulola amapanga zamwano zoyelekedwa, ndye tikamakwatira achikunja ndikulakwa ??

Yankho: Allah Ta’la akunena mu Qur’an kuti:

وَمَا كَانَ لِمُؤْمِنٍ وَلَا مُؤْمِنَةٍ إِذَا قَضَى اللَّهُ وَرَسُولُهُ أَمْراً أَن يَكُونَ لَهُمُ الْخِيَرَةُ مِنْ أَمْرِهِمْ وَمَن يَعْصِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ فَقَدْ ضَلَّ ضَلَالاً مُّبِيناً

“Ndipo sikoyenera kwa wokhulupirira wachimuna ndi wokhulupirira wachikazi, Allah ndi Mtumiki wake akalamula chinthu, iwo kukhala ndi chifuniro pazinthu zawo. Ndipo amene akunyoza Allah ndi Mtumiki wake, ndithu, wasokera; kusokera koonekera.”  33:36

Allah ndiyemwe analetsa kukwatira osakhulupilira:

وَلاَ تَنكِحُواْ الْمُشْرِكَاتِ حَتَّى يُؤْمِنَّ وَلأَمَةٌ مُّؤْمِنَةٌ خَيْرٌ مِّن مُّشْرِكَةٍ وَلَوْ أَعْجَبَتْكُمْ

“Ndipo musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndithudi, mdzakazi wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu yachikazi yosakhulupilira, ngakhale itakukondweretsani. 2:221

Choncho ngati Iye amaletsa, ife tisakhale ndi kusankha kwina, chifukwa Iye ndiyemwe akutidziwa ife kuposa momwe tikuzidziwira tokha.

Pafunso lanu loti: “ndiye tikamakwatira achikunja ndikulakwa?” Inde mukulakwa kwambiri. Ngati mukukumana ndi mavuto oterowo, bwelerani kwa Allah yemwe anakulamulani kuti muwakwatire iwowo (omwe akukuvutaniwo) ndipo mupeza yankho la mavutowo. Allah sangaike chithandizo munyansi.

يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُواْ إِنَّمَا الْمُشْرِكُونَ نَجَسٌ

“E inu amene mwakhulupilira! Ndithu, opembedza mafano ndi nyansi… 4:28

Funanifunani akazi oyenera inu kuchokera mu akazi abwino:

فانكِحُواْ مَا طَابَ لَكُم مِّنَ النِّسَاء مَثْنَى وَثُلاَثَ وَرُبَاعَ فَإِنْ خِفْتُمْ أَلاَّ تَعْدِلُواْ فَوَاحِدَةً

“Choncho kwatirani amene mukuwafuna mwa akazi; awiri, kapena atatu, kapena anayi (basi). Koma ngati mukuopa kuti simungathe kuchita chilungamo, (kwatirani) mmodzi basi. 4:3

Zomwe mukudandaula inuzo zimachitika kuchokera mu imodzi mwa zinthu ziwiri izi:

1. Kutheka inuyo khalidwe lanu silomusangalatsa Allah, makamaka kumbali ya ubale wapakati panu ndi azimai. Zikakhala choncho, Allah samachita chinyengo, chifukwa

الجزاء من جنس العما

“Malipiro amachokera pamtundu wantchito yako”

Ndipo Allah ndi Wachilungamo, sachita chinyengo pogawa akazi kwa amuna komanso pogawa amuna kwa akazi:

الْخَبِيثَاتُ لِلْخَبِيثِينَ وَالْخَبِيثُونَ لِلْخَبِيثَاتِ وَالطَّيِّبَاتُ لِلطَّيِّبِينَ وَالطَّيِّبُونَ لِلطَّيِّبَاتِ أُوْلَئِكَ مُبَرَّؤُونَ مِمَّا يَقُولُونَ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَرِزْقٌ كَرِيمٌ

“Akazi oipa ndi aamuna oipa, naonso amuna oipa ndi aakazi oipa; ndipo akazi abwino ndi aamuna abwino, naonso amuna abwino ngaakazi abwino.” 24:26

Koma ifeyo anthu ndamene timadzipondereza tokha pogwira ntychito yomwe ikusemphana ndi zabwino zomwe tikudzifuna:

إِنَّ اللّهَ لاَ يَظْلِمُ النَّاسَ شَيْئاً وَلَـكِنَّ النَّاسَ أَنفُسَهُمْ يَظْلِمُونَ

“Ndithu Allah sapondereza anthu kalikonse, koma anthu amadzipondereza okha” 10:44

Choncho mudzikhonze kaye nokha ndipo simudzavutika pofunafuna mkazi wabwino wa Chisilamu.

2. Koma ngati inuyo muli wabwinobwino, mavuto ngati amenewo amatha kuchokera mmayeso a Allah amene amawapatsa amuna okhulupirika omwe akufuna kukhanzikika pa imaan yawo potenga mkazi wa Chisilamu komanso wokhanzikika pa imaan yake. Allah sangangotayira imaan ya munthu pa munthu wina (pomukwatitsa ndi osayenera).

Dziwani kuti Allah amakhala kuti waika kupambana kwanu mwa mkazi amene akukuvutaniyo, ngati mutayenda mundondomeko yoikidwa ndi shariah pa ukwati wanu.

Kukwatira wachikunja ndi tchimo. Ndipo chomwe mwaletsedwa ndi Allah inu nkuchichita, mukuyenera kuchisiya ndikupanga tawbah chifukwa mwachita ntchimo; mukapanda kulapa mukazingidwa ndimoto.  Ngati mwakonda mkazi wachikunjayo, musamukwatire pokhapokha mutamusandutsa kukhala okhulupilira, ndipo mumukwatire ali okhulupilira ngati mmene munakapezera wa Chisilamu koyambilira, ndipo asalowere Chisilamu kuti ingokhala bridge yowolokera ku banja.

Kuvuta kwa atsikana a Chisilamu mukamawafunsira kusakhale chifukwa chotengera mushrik. Mukatero mukuyesera kumenya nkhondo ndi Allah, nkhondo yoluzaluza kale.

Ndipo mafunso monga “kumwa mowa nkulakwa? … kukwatira osakhulupilira nkulakwa? Kumwa mowa nkulakwa…etc) ndimafunso olimbamba ndi Allah, kupatula yemwe sakudziwa kuti Allah anati chani pa zinthu zoterozo.

Kwa munthu yemwe akudziwa, ndibwino kufunsa kuti “kodi ndipange bwanji kuti ndipeze mkazi wokhulupilirayo poti akumavuta ukamufunsira?” Kapena ngati mwapeza mkazi wachikunja, funsani njira yovomerezeka Mchisilamu kuti mpaka mutengane naye popanda kuchimwa. Koma osayankhula zoipa monga kunena kuti “akazi a Chisilamu amanyada, amachita mwano … mbiri zimenezo ziri mwa mkazi aliyense popanda kuyang’ana Chipembedzo koma chikhalidwe. Ndipo kunyada kapena mwano umatha kuoneka malinga ndi njira yomwe inu mukugwiritsa ntchito mofunsira.

Pewani kufunsa option ya haramma chifukwa nthawi zambiri zimatanthauza kuti nzimene mukulakalaka zitakhala halaa kuti mudzichite – kumeneko kumakahala kulimbana ndi lamulo la Allah lomwe liri lofewa kwambiri kuposa chitsankho chomwe mukufunacho. Dziwani kuti Allah samamukakamiza munthu chinthu chomwe sangakwanitse. Allah amafuna zofewa pa munthu.

Choncho lamulo lirilonse komwe limaoneka kuti ndilovuta analiikira njira yofewa … fatsani musafikire kuganiza zosemphana ndi malamulo a Allah. Kumeneko ndi kudzitulutsa mu Chisomo chake.

أَحَسِبَ النَّاسُ أَن يُتْرَكُوا أَن يَقُولُوا آمَنَّا وَهُمْ لَا يُفْتَنُونَ

“Kodi anthu akuganiza kuti azasiyidwa popanda kuyesedwa ndi masautso pakungonena kuti: “Takhulupilira?” (Iyayi, ayenera kuyesedwa ndithu, ndi masautso osiyanasiyana pamatupi pawo ndi pachuma chawo kuti adziwike woona ndi wachiphamaso). 29:2

Kukhala ndi imaan sichinthu chophweka. Imaan timagula ndi mayesero.

Mwalamulidwa kukwatira okhulupilira chifukwa choti ndinu okhulupilira, ndipo mwapatsidwa mayeso kuti akuoneni ngati kukhulupilira kwanu kuli kwamphamvu. Dziwaninso kuti Allah akamukonda munthu kuti apeze zabwino, amamuyesa kaye. Choncho mukafooka nkutenga yemwe sali okhulupilira pamene muli mkati mwa mayeso a Allah. Ndiye kuti mwalephera ndipomupezeka kuti simuli oyamika Chisomo chomwe Allah anakupatsati pamene ananena kuti:

وَأَتْمَمْتُ عَلَيْكُمْ نِعْمَتِي وَرَضِيتُ لَكُمُ الإِسْلاَمَ دِيناً

“…ndipo ndakukwaniritsirani Chisomo changa komanso ndasangalatsidwa nanu pokupatsani Chisilam kukhala deen yanu”. 5:3

Choncho inu ngati muli Msilamu okhulupilira, pilirani mutengenso mzanu okhulupilira kotero kuti mukwaniritse deen, ndipo mudzidikira Tsiku lomaliza limene mudzakhale naye ku Jannah. Mukatenga wosakhulupilira mudzapanga bwanji balance Chisilamu chanu, poti mmenemo mukulamulidawa kuwaongolera akazi anu ku jannah?

Pezani Msilamu mzanu, kapena wachikunjayo mulowetseni Chisilamu musanamkwatire, kuti ndondomeko ya nikaah yanu idzakhale 100% ya Chisilamu komanso moyo wanu udzayende Wachisilamu pamodzi ndi ana anu mpaka kumwalira kwanu.

Omwe ali Ololedwa Kuwakwatira mwa Athu oti si Asilamu