“Ndi zoletsedwa mu Chisilamu mkazi kuvala buluku (thalauza) lothina ndikuonetsa mmene thupi lake liliri. Ndipo chilango chake ndi choopsa zedi chifukwa mchitidwe umenewu umafalitsa machimo pa dziko.” Darul Iftail Misriy
Allah anaika ndondomeko ya momwe mkazi wa chisilamu ayenera kuvalira. Ndipo pa mavalidwe amenewa, sipakupezeka kuvala chovala chonga ngati buluku, chomwe chiri chovala cha mwamuna. Kotero ndikoletsedwa mkazi kuvala za mwamuna ndinso mwamuna kuvala za mkazi.

Buluku likhonza kuvalidwa mu tnhawi izi:1. Pamene mukugona
2. Pamene muli mnyumba ndi amuna anu (ndipo muli ndi ufulu kuvala mmene mungathere)
3. Pamene mwavala mkanjo, mukhonza kuvala buluku kapena t-shirt mkati.
Hadith ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati:

لعن الله المتشبهين من الرجال بالنساء، والمتشبهات من النساء بالرجال
>”La’ana Nnabiyyu (s.a.w) al mutashabbiheena mina rijaal binnisaai wal mutashabbihaati mina nnisaai birrijaal” Bukhari
>”Anatembelera akazi odzifananitsa ndi amuna komanso amuna
odzifananitsa ndi akazi” Al Bukhari

JEANS – T-SHIRT Ndizoletsedwa Msilamu wa mkazi kuvala jeans ndi t-shirt pamwamba, ngakhale kuti zafalikira padziko pano. Ndipo zikusutsana ndi lamulo la hijab mu Qur’an 33
Choncho posayang’ana kuti dziko likuyenda bwanji, tikaona mmene Chisilamu chikutiphunzitsira, tipeza kuti nzofunika kulapa kwenikweni.
يُدْنِينَ عَلَيْهِنَّ مِن جَلَابِيبِهِنَّ”

…yudneena ‘alayihinna min jalaabieebihinna…” Qur’an 33:59
…adziphimbe ndi nsalu zawo (akamatuluka mnyumba)…

Mpango wakumutu si hijab