Mkazi ndiwololedwa kugwira ntchito. Koma pali zingapo zofunika kutsatira komanso zina zofunika kupewa.
Pachiyambi penipeni, tiona shari’ah, ndipo tisiye zomwe society imafuna.

Mkazi ndimunthu amene amayenera kukhala panyumba, kusamalira m’nyumba, ana komanso chuma chamwamuna wake.
Mkazi ndi administrator wa panyumba, msunginyumba. N’chifukwa chake amatchedwa kuti

ربة البيت
Msunginyumba.

Umboni wa izi Allah akunena mu Surah Al Ahzab kuti:

وقرن في بيوتكن
Ndipo khalani mnyumba zanu

Apa sizikutanthauza kuti basi adzikhala mnyumba ngati kapolo, malinga ndi mmene anthu ena amapotozera tanthauzo. Koma akhonza kutuluka panja mmene angatulukire ndi mwamuna wake kapena abale ena. Ndipo ngati alibe kuchitira mwina koma kudzithandiza pogwira ntchito, akuyenera kutsatira malamulo:

Asadzikongoletse kapena kuonetsa zomwe zingabweretse fitna pakati pa anthu ngakhale iye mwini.

Allah Ta’la akunena popitiriza aayaha ya mu Surah Al Ahzab ija:

ولا تبرجن تبرج الجاهلية الأولى

ndipo musadzionetsere kwa amuna uku mutadzikongoletsa ngati mmene ankaonetsera zokongoletsa zawo (akazi) a munthawi ya umbuli. [Kale azimai ankayenda myendo ili pamtunda, makosi akuonekera osadziphimba, komanso zodzikongoletsera zina monga ma necklace, zibangiri, ndolo, zinkaonekera panja. Zonsezi nzaletsedwa].)

Koma tikaonesetsa lero lino, zimene zinaletsedwa ndi zimene zikuchitika pakati pa ma sisters athu. Allah akhululuke.

Ntchito isakhale yosakanikirana ndi amuna;
Allah Ta’la akunena mu Surah Al Qasas:

قال ما خطبكما قالتا لا نسقي حتى يصدر الرعاء وأبونا شيخ كبير

(Musa) adati (powafunsa atsikana awiri): kodi mwatani? (Bwanji simukudzimwetsa ziweto zanu?) Iwo adati: sitingamwetse (ziweto zathu) mpaka abusa atachotsa (ziweto zawo, chifukwa sitingsthe kulimbana nawo). Ndipo bambo athu ndi nkhalamba yaikulu kwabasi.

Izi zinachitika pamene Musa alaih ssalaam anadutsa pachitsime chomwetsera ziweto nkupeza atsikana awiri akuyesetsa kudzipatula pakati pa amuna kuti asasakanikirane. Ndipo anapeza kuti atsikanawo sanangobwera pachitsimepo mwachisawawa, koma chifukwa choti bambo awo anali okalamba; sanakwanitse kupita okha kukagwira ntchitoyo. Nchifukwa chake anamuuza Musa kumapetoko kuti: “ndipo bambo athu ndi okalamba” kuti asadabwe chifukwa chani atsikana akupezeka pamalo pomwe pali amuna.

Allah anapereka kwa mwamuna udindo wogwira ntchito pabanja chifukwa iye ndi muyang’aniri wa banja lonse.

Allah akunena mu Surah Al Nisaai aayah 34:

الرِّجَالُ قَوَّامُونَ عَلَى النِّسَاءِ بِمَا فَضَّلَ اللَّهُ بَعْضَهُمْ عَلَى بَعْضٍ وَبِمَا أَنفَقُوا مِنْ أَمْوَالِهِمْ ۚ فَالصَّالِحَاتُ قَانِتَاتٌ حَافِظَاتٌ لِّلْغَيْبِ بِمَا حَفِظَ اللَّهُ ۚ

Amuna ndi ayang’aniri pa akazi chifukwa choti Mulungu watukula ena paulemelero pamwamba pa ena chifukwa cha chuma chawo chimene apereka. Choncho akazi abwino ndi omwe ali omvera, odzisunga ngakhale amuna awo palibe, pakuti Mulungu walamula kudzisunga…

Ndipo Mtumiki salla Allah alaih wasallam analongosola za maudindo a pabanja motere:


وَالرَّجُلُ رَاعٍ فِي أَهْلِهِ وَهُوَ مَسْؤولٌ عَنْ رَعِيَّتِهِ، وَالْمَرْأَةُ رَاعِيَةٌ فِي بَيْتِ زَوْجِهَا وَمَسْؤولَةٌ عَنْ رَعِيَّتِهَا

ndipo bambo ali ndi udindo woyang’anira pa banja lake ndipo adzafunsidwa za udindo wake; mkazi ali ndi udindo woyang’anira nyumba yake ndi mwamuna wake, ndipo adzafunsidwa za udindo wake…

Apatu deen ndiye mopanda chibwibwi ikunenetsa poyera maudindo a mnyumbamo. Ndipo mkazi akamafika pogwira ntchito kunja pa company ina yake, ndiye kuti mwamuna zamvuta zenizeni.

Zikukhalatu choncho chifukwa chofuna kupewa fitna komanso mavuto amene amayambika mkazi akamayenda wakuntchito komanso akamagwira ntchitozo.

Komanso mavuto ambiri amapezeka m’banja lomwe Allah wadalitsa ndi ana, mai amasowa nthawi yolelera ana, mapeto ake ana amakula ndi watchito, mai samawazolowera. Mai samakhala ndi nthawi ya ana ake. Tidziwe kuti mai ndi mphunzitsi oyamba wa ana.

Komanso chisamaliro kwa mwamuna wake chimachepa.

Amuna ambiri amasowa ntchito chifukwa choti ntchito zawo zonse akwaniramo azimai okhaokha, choncho zimapezeka kuti amuna akukhala pakhomo, akazi kuntchito. Kusiya udindo umene Allah Ta’la anatipatsa, kusemphanitsa ubwino umene shariah inatipangira mogwirizana ndi chilengedwe chathu.

Komanso mtsikana (yemwe sanakwatiwe) akakhala kuti akugwira ntchito bambo ake akungokhala, ambiri samasangalatsidwa kumupereka mwanayo kubanja munthawi yake, poganiza kuti basi adzasiya kuwathandiza kuchokera ku ntchito yomwe akugwirayo.
Izi zimachitika mmabanja ena, koma sizikuletsa kugwira ntchito.

Ena mwa malamulo oyenera kutsatira mkazi yemwe akufuna kugwira ntchito:

Choyambilira chenicheni akhale ‘taqiyyah’, oopa Mulungu, kotero kuti apewa ndikutseka njira zonse zomwe zingamchititse kufalitsa kapena kutenga fitna.

Komanso aonesetse kuti akangotuluka kupita ku ntchito, asamayankhule-yankhule ndi amuna chisawawa, kupatula pazomwe ziri zofunikira kwambiri.
Komatu mtundu wa akazi oterewu nkovuta nthawi zino kuti upezeke; chifukwa choti ma society anazolowera zolakwika.
Mkazi amene amasakanikirana ndi amuna pa zochitika, noor ya Allah mwa iye imachoka, mapeto ake amakhala opanda manyazi, nthawi zonse amakweza mau pakati pa amuna, mpaka zimafika poti ngati iyeyo palibe, amuna ntchito imaima.
Kukhala mu umoyo woyendera adab ya Chisilamu amaona ngati ali mu umoyo wovuta. Zonsezitu nchifukwa cha kugonjera ulamuliro wa shaytwaan.

Lamulo lina ndi loti aonesetse kuti ntchito yomwe akukagwirayo ikhale ya munthu wamkazi osati ya amuna. Isakhale ntchito yomwe ingamusokoneze ntchito yomwe anamulengera Allah; isakhale yomusokoneza udindo wake wa panyumba.

Zina mwa ntchito zoyenera kwa mkazi ndi monga kuphunzitsa azimai komanso ana, kuyang’anira odwala (nursing) mmagawo za azimai (female ward) kapena ana, komanso ntchito zina zoyenera munthu wamkazi.

Aonesetse kuti wavala motsatira mavalidwe a Chisilamu.
Akuyenera kumatsanzika kwa amene akumusunga, komanso waliyyu wake adziwe zoti akugwira ntchito.

Choncho gwirani ntchito ngati amuna anu akulolezani kutero, komanso ntchitoyo ikhale yopanda za haram zobweretsa fitna komanso kusokoneza udindo wanu wapakhomo.
Ngati amuna anu akuuzani kuti musagwire ntchito, musakakamire, ndiye kuti akwanitsa udindo wa kusamalira inu. Komanso ngati ali operewedwa akhonza kukulolani kugwira ntchito kuti mudzithandizana mbali ya chuma, poti moyo wamasiku ano waima pa ndalama.