Dowload PDF (direct link)

Listen/Download MP3

Munthu ofuna kupanga hajj ayenera kutsimikiza imodzi mwa mitundu ya Hajj iri m’munsiyi asanalowe mu Ihram pofuna kupanga Hajj. Mitundu yake ndi iyi:

 1. Ifrad (Yapayokha) yomwe imatanthauza kupanga Hajj yokha.
 2. Qiran (Kuphatikiza) Yomwe imatanthauza kupanga Hajj mophatikiza ndi Umrah. Ndipo munthu openga mtundu wa Hajj umenewu amatchedwa kuti Qarin (ophatikiza).
 3. Tamattu-u (Chisangalalo), yomwe imatanthauza kupanga kaye Umrah poyamba. Kenako munthuyo akhoza kusiya Ihram yake ndi kulowa mu umoyo wake wa nthawi zonse kufikira tsiku la chisanu ndi chitatu (8) la mwezi wa dhul Hijjah lomwe adzapitilize kupanga malamulo a Hajj . Ndipo munthu opanga mtundu wa Hajj umenewu amatchedwa kuti Mutta (Osangalala).

Imeneyi ndi mitundu ya Hajj malingana ndi Hadith’ yomwe inalandiridwa ndi Mayi Aishah radhia Allah anha yomwe iye akufotokoza motere:

“Tinapangira limodzi ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam Hajj yake ya malawirano. Ena mwa ife tinatsimikiza za kupanga Ihram pofuna kupanga Umrah poyamba, ndipo ena anaphatikiza Hajj ndi Umrah, ndipo ena anatsimikiza za Ihram pofuna kupanga Hajj yokha”.

Malo Osonkhanirana

Malo omwe anthu omwe amakapanga Hajj amasonkhana asanavale zovala zawo za Ihram pofuna kupanga Hajj kapena Umrah, ndi malo osiyanasiyana omwe ali kunja kwa mzinda wa Makka omwe anasankhidwa malingana ndi malamulo a chipembedzo cha chisilamu ndi cholinga chimenechi. Ngati anthu afika malo amenewo, iwo amakonzeka muthupi ndi uzimu pofuna kupanga ntchito yotamandika komanso yopatulika ya Hajj. Mtumiki salla Allah alaih wasallam anakhazikitsa malo amenewo kum’mwela, kum’mawa komanso kumpoto kwa mzinda wa Makkah. Tatiyeni tiwone tsatanetsatane wa malo amenewa motere:

 1. Dhul-Hulaifah: amanewa ndi malo omwe anakhazikitsidwa cha kumpoto kwa mzinda wa Makka pamtunda wa Makilomita 450. Amenewa ndi malo omwe anakhazikitsidwa kwa anthu omwe ndi mzika za mumzinda wa Madina ndi onse omwe ali cha kumpoto kwa mzindawu.
 2. Rabigh: amenewa ndi malo omwe anakhazikitsidwa kwa anthu ochokera cha kumpoto kwa dziko la Syria, Lebanon, Turkey, ndi madera ena. Komanso onse ochokera kumpoto chakumadzulo monga anthu ochokera ku mayiko a ku Africa kapena omwe amadutsa ku Africa ngati akuchokera cha kumpoto cha kumadzulo.
 3. Yalamlam: Limeneli ndi phiri lomwe liri cha kum’mwera kwa mzinda wa Makka lomwe Mtumiki salla Allah alaih wasallam anakhazikitsa ngati malo ofikirapo anthu a ku Yemen ndi onse ochokera kumayiko ali cha kum’mwera.
 4. Qarnul-Manazil: Limeneli ndi phiri lomwe liri cha kum’mawa kwa mzinda wa Makka ndipo ndi malo omwe anakhazikitsidwa kwa anthu a mtundu wa Najd ndi onse ochokera kum’mawa.

Anthu omwe amachokera m’madera osiyanasiyana omwe ali pakati pa malo amanewa ndi mzinda wa Makkah ayenera kupangiratu Ihram yawo kumalo komwe iwo akonzekera ulendo wawo okachita Hajj.

Kwa anthu omwe ndi mzika za mzinda wa makka, ayenera kupangira Ihram yawo mnyumba zawo. Koma ngati iwo apanga Ihram ya Umrah, iwo ayenera kupita kumalo oyera ndikupanga Ihram yawo kumeneko kenako ayenera kupitiliza kupanga miyambo yonse ya Umrah.

Wina aliyense yemwe wafika pamalo ake omwe anayikidwa ngati malo ake ofikira malingana ndi dera lomwe akuchokera ayenera kukonzekera Ihram yake pamalo amenewo.

Koma chifukwa choti anthu okapanga Hajj omwe amayenda chowuluka pa ndege, sangapange Ihram yawo mundege ngati akuwadutsa madera amenewo, m’malo mwake ayenera kupanga Ihram yawo pamalo okwelera ngati akupita ku Makkah.

 

Kukonzekera

Ngati munthu akufuna kupanga hajj ayenera kupanga zinthu zingapo asanayambe ulendo wake. Ndipo zinthu zimenezi ziri motere:

 1. Ayenera kupempha chikhululuko kwa Allah pamachimo ake onse omwe anatsogoza ndi zoipa zonse zomwe iye anatsogoza m’mbuyo. Komanso ayenera kulonjeza kuti sadzabwereza kuchita machimo amenewo mtsogolo.
 2. Kuyanjana komanso kulazanitsa mitima ndi anthu onse omwe iwe unawalakwira kapena kuwapondereza munjira ina iliyonse ndi kuwapempha anthu amenewa kuti akhale okhululuka.
 3. Kubweza ngongole zonse zomwe unali nazo.
 4. Kulisiyira banja lako ndi onse omwe umawayang’anira ndalama kapena chithandizo chilichonse chokwana zowathandiza iwo panthawi ya kusapezeka kwako mpakana utabwelera ku ulendo wako.
 5. Kudziyeretsa wekha ku makhalidwe onse oyipa ndikudziyeretsa pochita makhalidwe onse otamandika komanso abwino.
 6. Uyenera kuwonetsetsa kuti wabayitsa katemera wa chikuku, kolera, ndi matenda ena komanso kulandira chitupa cha zaumoyo ku unduna wa za umoyo chosonyeza kuti thupi lako ndilangwiro komanso lathanzi.

Ihram

Usanakonzekere zonse zokhudzana ndi Ihram, lamulo la chisilamu likukupempha kuti uyenera kutsata zinthu izi:

 1. Kumeta tsitsi lonse loyenera kumetedwa komanso kuwenga zikhadabo.
 2. Uyenera kusamba ngati kuli kotheka komanso uyenera kudziyeretsa popanga Udhu.
 3. Amuna popanga Ihram yawo ayenera kuchotsa zovala zawo zonse ndi kuvala chovala cha Ihram, chovala choyera chosasokedwa chomwe chimavalidwa mopingitsidwa pathupi posiya nkono komanso phewa lakumanja pamtunda. Chovala cha Ihram chimakhala ndi nsalu ziwiri zosasokedwa komanso zosakongoletsedwa ndi mitundu ya mtundu wina uliwonse. Ina imamangidwa mchiwuno ndipo ina imavalidwa modutsitsa pakhosi ndi mapewa posiya phewa komanso nkono wakumanzere pamtunda. Nsalu zimenezi zili ndi mayina. Ina imatchedwa Rida ndipo ina imatchedwa Izar. Kumutu sikumavalidwa chilichonse angakhale kuti okalamba amaloredwa kumanga china chake m’mutu koma ayenera kupeleka chopeleka chomwe chimapelekedwa kwa osauka. Mapazi ayenera kukhala pantunda mpakana m’misomali, pachifukwachi nkhwayila ndi zomwe zimavalidwa m’malo mwa nsapato. Nsapato zikhoza kuvalidwa ngati sizikubisa misomali.
 4. Ndipo akazi amavala chovala chovala chachitali chomwe chimayambira kumutu mpakana ku miyendo kupatula kubisa nkhope ndi zikhatho. Ndipo ndizofunikira kwambiri kwa iwo kuvala nkhwayila zomwe zimakonzedwa mwapadera kwa anthu opanga Hajj.
 5. Tiyenera kuti, ngati tayenda pandege, tipange Ihram yathu tisananyamuke pamalo onyamukira.
 6. Anthu onse ayenera kupemphera Maraka’at awiri ndi chitsimikizo chofuna kupanga Ihram.

Iwo akamalowa mu mwambo wa Ihram, amachita chitsimikizo chawo pantchito yodalitsikayi ponena mokweza mawu awa:

“Labbaiykallahumma Labbayka. Labbayka La Sharika laka Labbayka, Innal-hamda wanni’mata laka wal mulk la sharika laka.  Omwe amatanthauza kuti:

“Ndavomera Mbuye wanga ndavomera! Ndavomera Mbuye wanga ndavomera! Mulibe opaphatikizana nanu. Ndavomera! Kutamandika ndi mtendere zonse ndi za Inu. Muli ndi ufumu onse. Mulibe ophatikizana nanu”

Tiyenera kudziwa kuti munthu amene akupanga Hajj, ngati ali mu mwambo wake wa Ihram, sayenera kukhalira limodzi ndi mkazi, kumeta tsitsi, kuwenga zikhadabo kapena kuvala chovala kumutu. Ndipo akazi adzabisa thupi lawo lonse kupatula nkhope ndi zikhatho.

Chovala china chilichonse sichimaloledwa kupatula chovala cha Ihram. Mkanjo, Amama , chisoti, china chilichonse chosokedwa komanso china chilichonse chokongoletsedwa ndi mitundu yosiyanasiyana sichololedwa. Ngakhale kuti akazi amaloledwa kuvala zovala za kufuna kwawo, samaloledwa kuvala zophimba zikhatho, Chophimba kumaso, komanso sayenera kugwiritsa ntchito mafuta onunkhiritsa (Perfume). Komanso sayenera kuvala zovala zowonekera mkati komanso zokongoletsa ndi mitundu yosiyanasiyana.

Choncho tawona kuti chinthu choyambilira mu zichitochito za Hajj kapena Umrah ndi kulowa m’mwambo wa Ihram womwe umasonyeza kuti munthu watsimikiza kupanga miyambo yonse ya Hajj kapena Umrah. Ndipo Gawo lina ndi Tawaf.

Tawaf (Kuzungulira Ka’bah)