Mitala mu Chisilamu si LAMULO LOKAKAMIZIDWA, koma ndi chilolezo kwa yemwe wafuna.
Allah Ta’la analoleza mitala mu Surat Al Nisaai Aayah #3.

Nkhani ya mitala imavuta mbali zonse; kwa mwamuna ndi kwa mkazi komwe, chifukwa cha kusatsatira ndondomeko komanso malamulo omwe mitala inalolezedwera. Mapeto ake mitala imaoneka ngati ndi yachabe. Koma Allah sangaloleze zinthu zachabe zopereka mavuto.

Amuna ambiri ikawakwanira nthawi yofuna mkazi wina, amagwiritsa ntchito mau oti “mkazi alibe ufulu womuletsa kapena kumuloleza mwamuna kutenga mkazi wina…” koma samadziunikira kuti kodi n’chifukwa chani mkazi alibe ufulu umenewo. Iyi imakhalanso njira ina yom’ponderezera mkazi pogwiritsa mfundo zoona koma mosayenera.

Pali vuto limodzi lomwe limapezeka mwa mkazi nthawi zonse, makamaka pamene mwamuna akuganiza zotenga mkazi wina, ndipo vutoli likhonza kupezekabe ngakhale mkazi atagwirizana nazo mosangalala:

NSANJE

Nsanje palibe amene angaligonjetse. Ngakhaletu azimai omwe amakhala mmabanja amitalawa sikuti amakhala alibe nsanje. Koma chifukwa cha chilungamo komanso chikondi cha mwamunayo chomwe akukwanitsa kuwachitira onse mofanana, nsanje lija limangogwera mkati osatulukira kunja.

Zifukwa zokwatilira mitala zizikhala zoti mkazi akhonza kugwirizana nazo. Sindikutanthauza kuti zikhale zoti amuloleze, koma agwirizane nazo (zikhale zomveka zoti sizingabweretse mavuto kwa mwamunayo kapena mkazi).
Komanso zizikhala zoti ngakhale mkaziyo akhonza kukhala Woyambilira kumupempha mwamuna kuti “bwanji mupeze mkazi mzanga?”

Zifukwa zokwatilira mitala ndizifotokoza mmagawo awiri:
Gawo loyamba:
Zifukwa za General (zomwe sizikuchokera mwa anthu awiriwo okha)

1. Kuthetsa vuto la kuchepa kwa amuna ndi kuchuluka kwa azimai komanso kuwateteza azimai ku umbeta chifukwa cha kuchuluka kwawo.
Chifukwa chimenechi ngakhale mkazi akhonza kuthandizapo mkazi mzake.
Tichotse nsanje. Chifukwa tikamaikapo nsanje lija mbali ina, tipeza kuti zifukwa zonse zokwatilira mitalazi ziribe ntchito kwa mkazi.

2. Kuchulukitsa mtundu, kuti gulu la Mtumiki Muhammad lichulukenso kotero kuti opembedza Mulungu mmodzi yekha achuluke, ndipo zimenezo zimapangitsa kuti Asilamu akhale amphamvu.
Ena ndiye amakwatira mkazi wachiwiri kaafir nkumusiya akhale kaafir choncho. Kuononga kumeneko.

Gawo Lachiwiri:
Zifukwa za Special (zimene zimapezeka kuchokera mwa mkazi ndi mwamuna omwe akwatirana awiri)

1. Kuchuluka kwa mphamvu za mwamuna kotero kuti mkazi mmodzi samawam’kwanira.
Izi zikhonza kuchitika chifukwa cha kukula kwa mkazi pomwe mwamuna adakali wachinyamata ndi mphamvu, ndipo mkazi sakonda kuchipinda mwakawirikawiri.
Kapenanso kutheka onsewo ali bwinobwino koma mkazi amakhala nthawi yaitali mu nyengo yake yopuma, choncho mwamuna amasowa mtendere zikavuta. Ndipo ngati sangakwanitse kupilira, ali ndi ufulu kutenga wachiwiri.

2. Kusabereka kwa mkazi, kapena matenda omwe angampangitse kupewa kukumana ndi mwamuna wake, kapena chikhalidwe chake choipa. Pamenepa ndikutanthauza kuti mkazi amatha kukhala osabereka, koma mwamuna akufuna kukhala ndi mwana. Mkazi amatha kukhala ndi matenda oti sangathe kukwaniritsa chilakolako cha mwamuna wake, kapena kukhala ndi chikhalidwe choipa chomwe chingapangitse mwamuna wake kukanika kugona naye mmene akufunira.

3. Kuipidwa kwa mwamuna pa mkazi wake, pa chifukwa cha kusemphana pakati pawo, kapena pakati pa iye ndi abale a mkazi (kusemphana kwake koti sikungakhale chifukwa chothetsera banja), koma pamatha kudutsa nthawi osakhala ndi chilakolako chokumana ndi mkaziyo (chilakolako nkumakhala nacho ndithu koma osafuna kuthetsera mwa mkazi wakeyo chifukwa cha zomwe asemphanazo), ndiye popewa kuti akhonza kukathetsera mwa akazi ena omwe sanakhale nawo pa banja, Mulungu analoleza kuti mwamuna akwatire akazi angapo cholinga choti nthawi ngati zimenezi adzipeza pothawira pa halaal komanso apewe kupanga chiwerewere.
Ndipo izi zikhonza kukhala solution ya kusemphana komwe kulipoko, chifukwa cha kansanje kamene kadzimpeza mkazi oyambayo akamaona kuti palinso mkazi yemwe akutha kusamalira mwamuna wake yemwe iye wamukwiyitsa.

4. Mwamuna akaona mkazi wina oti mwamuna wake anamwalira ndiye akusowa omusamalira, akhonza kukambirana ndi mkazi wake zomutenga ngati mkazi wachiwiri. Koma kukambiranako sicholinga choti alole kapena akane.

5. Mkazi akakhala kuti saabereka, kapena ali ndi matenda omuletsa kukhala ndi ana, koma mwamuna akufunisitsa atakhala ndi ana, amuuze mkazi woyambayo ndipo asam’bisire. Pamenepa mpamene pamayambira CHILUNGAMO, chifukwa popanda chilungamo mitala imakhala haram kwa iye.

6. Pamene mkazi ali mu haidh (period) kapena nifaas (wangobereka kumene); nthawi zimenezi nzoletsedwa kwa iyeyo kugona ndi mkazi wake. Popewa kupanga za haraam, ndi bwino kukwatira wachiwiri ngati akuona kuti sangamapilire nthawi zonse.
Zimenezo ndiye zifukwa zina mu zifukwa zomwe mwamuna akulolezedwa kukwatira mitala mopanda kupondereza wina wake.
Tsopano tione topic ina imene sichoka mkamwa pankhani ya mitala…

Ndizoona kuti mwamuna sali wokakamizidwa kupempha chilolezo kapena maganizo kuchokera kwa mkazi wake woyamba pamene akufuna kukwatira mkazi wachiwiri.
Koma masiku ano ambiri mmene amapangira mitala yawo, zimapangitsa kuti akuyenera kutenga chilolezo kapena kukambirana kaye ndi mkazi woyamba, ndipo akapanda kutero mitalayo imasanduka chipsinjo kwa mkazi ngakhale ana omwe alipo kale.

Chilungamo chake ndichoti banja lomwe likuyenda moopa Allah komanso kulemekeza malamulo a Chisilamu, mkazi sangafunikire kupereka maganizo pakusankha kuti mwamuna atenge mkazi wina kapena ayi. Ndi zachidziwikire kuti ambiri sangasangalatsidwe nazo ngakhale atakhala otsatira malamulo chifukwa nsanje siona malamulo.

Choncho mitala simalabada za nsanje. Koma akuyenera kungodziwitsidwa, adziwitsidwe zifukwa zimene akutengera mitalazo, ndipo mwamuna awonesetse kuti ndizovomerezeka mu shari’ah osati kungotengera kuti poti mkazi alibe ufulu woletsa ndiye kungopanga zifukwa zakezake.

Awonesetse kuti akupereka chisamaliro chokwanira kwa mkazi yemwe alipoyo, komanso akhonza kupanga chilungamo pakati pa akazi angapo.

Ndi zabwino kwambiri kumudziwitsa kuti azidziwa alipo awiri atatu kapena anayi. Osati kupanganso mozemba.
Palibe kuponderezedwa kulikonse pa mitala ngati tingatsatire ndondomeko ya shari’ah. Ndipo mkazi asadane ndi mitala koma adane ndi nsanje lakelo ndikuligonjetsa, kupatula ngati waona kuti mwamunayo alibe zomuyenereza kutenga mkazi wachiwiri ndipo zikhala kuti akulakwira malamulo posachita chilungamo.

Koma chisakhale chifukwa cha nsanje.
Surat Al-Nisaai 3:
“kwatirani omwe ali abwino kwa inu mwa akazi; awiri, atatu kapena anayi…”

Timamva akazi ambiri akunena kuti mitala imabweretsa matenda. Zimenezo ndi zabodza. Media ndiyomwe imafalitsa bodza limenelo. Makwatiridwe a mitala ndi chimodzimodzi mmene munthu amakwatilira mkazi woyamba. Nayenso amatha kukhala oti sanakwatiwepo, ndipo amayenera kupanga dongosolo lonse loyenera kutsimikiza kuti ali safe, monga kukayezetsa. Koma mfundo za kuletsa mitala zinadza ndi azungu pofuna kukwaniritsa campaign yawo yochepetsa chiwelengero cha anthu padziko, ndiye mmenemo anaikamo mfundo zambiri monga za kufalikira kwa matendendazo.

Allaha kuchita zinthu zomwe zingaononge miyoyo yathu. Kodi matendawo apezeka chifukwa choti akukwatiwa ngati mkazi wachiwiri?

Ena amanena kuti “tikumaopa chifukwa zimalowa ufiti”
Kulozanako kumachitika chifukwa cha kusatsatira njira yoyenera ya mitala. Komanso Msilamu wokhulupilira samaopa kulozedwa. Zodzitchinjirizira ku ufiti ziripo zambirimbiri monga Msilamu. Ngati tingapange moyenera komanso kutsatira njira ya shari’ah moopa Allah, mfiti ilibe mpata kwa ife. Koma tikaopa kulozedwa, ndiye kuti tikuopa shaytwaan.