Bodza loyamba: 
“Akazi pa mitala amakhala m’nyumba imodzi”
Anthu ena amaganiza kuti mitala ikutanthawuza kuti mwamuna atenge akazi awiri ndikumakhala nawo m’nyumba imodzi, komanso kuti mikangano imene ingakhalepo pakati pa akaziwa itha kumusokoneza mwamunayu, ndipo ana ndi anthu ena okhala m’nyumbamo azisautsidwa; iwo amati izi ndi zina mwa zoipa za mitala ndipo iyenera kupewedwa mu njira ina iliyonse.
Tidziwe kuti, mikangano m’banja imakhalapo ngakhale mwamuna atakwatira mkazi m’modzi. Ndipo mikangano yochuluka lero lino ikukhalapo makamaka mu maanja amene sali a mitala. Amuna ochuluka amene lero lino akumwa mowa, kugonana ndi akazi ena mu njira ya haraam, kuchita nkhanza kwa akazi awo powamenya ndi zina zambiri, zikumachulukira ndi mu maanja amene sali a mitala.
Choncho, mitala siikukakamiza kuti mwamuna awaike akazi onse m’nyumba imodzi ngati akaziwo sakufuna.
Adayankhula Ibn Qudaamah mu Al-Mughniy, (vol. 10, tsamba 234) kuti:
‌وَلَيْسَ ‌لِلرَّجُلِ ‌أَنْ ‌يَجْمَعَ ‌بَيْن ‌امْرَأَتَيْهِ فِي مَسْكَنٍ وَاحِدٍ بِغَيْرِ رِضَاهُمَا، صَغِيرًا كَانَ أَوْ كَبِيرًا؛ لِأَنَّ عَلَيْهِمَا ضَرَرًا؛ لِمَا بَيْنَهُمَا مِنْ الْعَدَاوَةِ وَالْغَيْرَةِ، وَاجْتِمَاعُهُمَا يُثِيرُ الْمُخَاصَمَةَ وَالْمُقَاتَلَةَ، وَتَسْمَعُ كُلُّ وَاحِدَةٍ مِنْهُمَا حِسَّهُ إذَا أَتَى إلَى الْأُخْرَى، أَوْ تَرَى ذَلِكَ؛ فَإِنْ رَضِيَتَا بِذَلِكَ؛ جَازَ؛ لِأَنَّ الْحَقَّ لَهُمَا، فَلَهُمَا الْمُسَامَحَةُ بِتَرْكِهِ.
Mwamuna alibe ufulu (ulamuliro) wopanga akazi awiri kukhala limodzi m’nyumba imodzi popanda chilolezo chawo, kaya akawizo ndi aakulu kapena aang’ono (mu zaka); chifukwa zimenezi zitha kuwabweretsera vuto malinga ndi udani ndi nsanje (zomwe zilipo pakati pawo). Choncho, kuwapanga awiriwa kukhala limodzi kumabweretsa mikangano ndi ndewu, ndipo aliyense mwa iwowa atha kumamva mawu pamene mwamunayu akukhala malo amodzi ndi mkazi winayo, kapenanso atha kumaona kumene. Koma ngati akaziwa avomereza (kukhala m’nyumba imodzi), basi pamenepo zili zololedwa, chifukwa onse awiriwa ali ndi ufulu umenewu (wokhala paokha paokha), komanso ndi zotheka ufuluwu kuwusiya (pokhala mnyumba imodzi).
Tikaonanso mu kufotokoza kwake Al-Kaasaaniy mu Badaai’ As-Swanaai’, (vol. 4, tsamba 23), iye akuti:
‌وَلَوْ ‌أَرَادَ ‌الزَّوْجُ ‌أَنْ ‌يُسْكِنَهَا ‌مع ‌ضَرَّتِهَا ‌أو ‌مع ‌أَحْمَائِهَا ‌كَأُمِّ ‌الزَّوْجِ ‌وَأُخْتِهِ ‌وَبِنْتِهِ ‌من ‌غَيْرِهَا وَأَقَارِبِهِ فَأَبَتْ ذلك، عليه أَنْ يُسْكِنَهَا في مَنْزِلٍ مُفْرَدٍ، لِأَنَّهُنَّ رُبَّمَا يُؤْذِينَهَا ويضررن بها في الْمُسَاكَنَةِ وَإِبَاؤُهَا دَلِيلُ الْأَذَى وَالضَّرَرِ ولأنه يحتاج إلى أن يجامعها ويعاشرها في أي وقت يتفق ولا يمكنه ذلك إذا كان معهما ثالث.
Ngati mwamuna akufuna kuti iye (mkazi wake) akhale ndi mkazi wina, kapena abale ake a mwamunayo, monga mayi ake, mlongo wake kapena mwana wake wa mkazi (wa mwamunayu) kuchokera mwa mkazi wina, kapena ena mwa abale ake, ndipo mkaziyu wakana; mwamunayu akuyenera kumupatsa mkaziyu malo akeake, chifukwa anthuwa atha osamusangalatsa mu zochitika zawo kapena kumubweretsera vuto ngati angakhale nawo. Mkaziyu kukana izi ndi chisonyezo choti sakufuna kusokonezedwa kapena kubweretseredwa vuto. Komanso iyeyu (mwamunayu) akuyenera kumagonana ndi mkaziyu ngakhalenso kumaseweretsana mu nthawi ina iliyonse yomwe iye wafuna, ndipo izi sizingatheke ngati pali munthu wina wachitatu.
Tikuzindikira kuchokera mu mawu amenewa kuti sizoona zoti mkazi amene akufuna kukwatiwa ndi mwamuna woti ali ndi mkazi wina kale azikakhala m’nyumba imodzi ndi mkazi winayo. Izi sizingatheke ngati mkazi woyambayu sakufuna kuti azikhala ndi mkazi wachiwiriyu. Ndipo akaziwa ali ndi ufulu wokhala m’nyumba zosiyana.