Zaka zisanu zapitazo, ndinawerenga m’nyuzipepala ya Toronto Star ya pa July 3, 1990, nkhani yoti “Chisilamu sichili chokha mu ulamuliro wa amuna (patriarchal Doctrine)“, yolembedwa ndi Gwynne Dyer 1.

Mlembi anafotoko munkhaniyi za momwe anthu anayankhira mokupsa mitima pamsonkhano wa “Amayi ndi Mphamvu” womwe unachitikira ku Montreal, kuchokera pa zomwe anayankhula  mayi wina wotchuka wa ku Egypt, Dr. Nawal Saadawi.

Mau ake omwe anali “olakwika”, anati: “Mfundo zikuluzikulu zomwe zikuletsa mayi zina ndi zina, zikupezeka mu buku la Chiyuda la Chipangano Chakale, kenako buku la Chikhristu, kenako mu Qur’an. Zipembedzo zonsezo ndi zolamulidwa ndi amuna chifukwa zikuchokera pa phata limodzi.” Ndipo “kuziphimba kwa mayi sikuliMchipembedzo cha Chisilamu chokha, koma ndi chikhalidwenso chakale pakati pa zipembedzo zimenezi.”

Omvera sanathe kukhanzikika pamene zikhulupiliro zawo zinali kufananitsidwa ndi Chisilamu. Kotero, Dr. Saadawi adatsutsidwa kwambiri. “Mfundo za Dr. Saadawi sizovomerezedwa. Zikusonyeza kuti sakudziwa za zikhulupiliro za ena,” adatero Bernice Dubois wochokera ku bungwe la World Movement of Mothers.

Alice Shalvi, mmodzi wa alangizi a ­Israel Women Network, anati: “Ndikuyenera kutsutsa, mu Chiyuda mulibe lingaliro la chophimba chamayi (hijaab).”

Mlembi wankhaniyi analongosola kuti mfundo zomwe anthu okwiyawa amapereka poyankha, kunali kutHawaa chikhalidwe chomwe Chisilamu chiri nacho, chomwenso chikugwirizana ndi chikhalidwe cha Kumadzulo chakale. “Amayi a Chikhristu ndi a Chiyuda sakanalola kukhala nkumanenedwa kuti ndi ofanana ndi Asilamu oipawo,” analemba Gwynne Dyer.

Sindidadabwe kuti anthu omwe adasonkhana pamsonkhanowu adamva maganizo olakwika kuchokera kwa Asilamu, makamaka pamene nkhani za amayi zidayamba kukambidwa. Maiko a Kumadzulo, Chisilamu chimawonedwa kuti ndi chizindikiro chabwino cha kugonjera kwa amayi. Pofuna kumvetsetsa mmene chikhulupilirochi chiliri pa kulimba kwake, tiyeni tiwone zomwe zinachitika ku France; nduna ya za maphunziro kudera la Voltaire, posachedwa idalamula kuchotsedwa kwa atsikana a Chisilamu onse omwe amavala hijaab popita ku sukulu mdzikomo. Kumeneko mwana wamkazi amamanidwa maphunziro chifukwa cha kuvala mpango kumutu, pomwe mtsikana wa Chikatolika akavala mtanda wake kapena mnyamata wa Chiyuda akavala chisoti, samaletsedwa.

Sitingaiwale mchitidwe wa apolisi a ku France poletsa akazi a Chisilamu kuvala mipango akamalowa mmasukulu. Zina zochititsa manyazi kwambiri zidachitika ndi Bwanamkubwa (Governor) George Wallace wa dera la Alabama mu 1962, pamene anaimilira pa chipata cha sukulu ndikuletsa ana akuda kulowa pakhomo la sukulu ndicholinga chofuna kupewa chisokonezo mma sukulu a Alabama.

Kusiyana kwa zinthu ziwiri zimenezi, ndikoti anthu akuda anali ochitiridwa chifundo ndi anthu ambiri ku U.S. komanso padziko lonse lapansi. Pulezidenti Kennedy adatumiza achitetezo kuti akawalowetse ana akuda mu sukulumo. Koma atsikana a Chisilamu sanalandire thandizo lirilonse. Vuto lawo likuoneka kuti palibe yemwe angawachitire chifundo mdzikomo kapena kunja.

Zonsezi ndichifukwa cha kusamvetsetsana kwakukulu komanso kuwopa chilichonse cha Chisilamu padziko lapansi lero lino.

Chimene chinandichititsa chidwi kwambiri pa msonkhano waku Montreal chinali choti; kodi mawu omwe anayankhula Saadawi, kapena anthu otsutsa onse aja, ndi oona? Kapena kodi Chiyuda, Chikhristu, ndi Chisilamu zili ndi lingaliro limodzi pa amayi, kapena ndi osiyana? Kodi Chiyuda ndi Chikhristu zimasamalira bwino amayi kuposa momwe Chisilamu chimachitira? Pamenepo choona ndi chiti? Nchachidziwikire kuti yankho lake ndilovuta kulipeza. Kuvuta koyamba kuli pa kusowa chilungamo pakati pa anthu; munthu akuyenera kuyesetsa kukhala wachilungamo pazochita, monga momwe Chisilamu chimaphunzitsira. Qur’an imalimbikitsa Asilamu kunena zoona ngakhale iwo omwe ali pafupi nawo sakonda chilungamocho:

“ndipo pamene mukunena, (popereka umboni), nenani mwachilungamo ngakhale (umboniwo) uli wokhudza achibale.” (6:152)

“E inu amene mwakhulupirira! Khalani oimiritsa chilungamo, opereka umboni chifukwa cha Mulungu; ngakhale kuti ubwere ndi masautso kwa inu, kapena kwa makolo anu, kapena kwa abale anu, ngakhale ali olemera kapena osauka, (musayang’ane zimenezo).” (4:135).

Kuvuta kwina ndikoti nkhaniyi ndiyaikulu kwambiri; ndakhala ndikuwerenga Baibulo kwanthawi yaitali zaka ziwiri zapitazo, kuwonjezerapo Encyclopaedia ya zipembedzo ndi Encyclopaedia ya Chiyuda, pofufuza mayankho. Ndinawerenganso mabuku angapo omwe akukamba za udindo wa amayi muzipembedzo zosiyanasiyana; olembedwa ndi akatswiri, komanso kuchokera kwa olemba za Chipembedzo ndi otsutsa ena. Choncho, zomwe zafotokozedwa m’bukumu ndi zotsatira za kafukufuku ameneyu. Cholinga changa sikufuna kuzionetsera kudziwa kwambiri, koma ndagwira ntchitoyi molingana ndi kuthekera kwanga, pofuna kukwaniritsa mau a mu Qur’an onena kuti “tiziyankhula chilungamo”.

Ndikufuna kutsindika kumayambiliro kwa bukuli kuti cholinga changa polemba mutu umenewu sikuzembera Chiyuda kapena Chikhristu. Monga Asilamu, timakhulupilira kuti ziwirizi zinachokera kwa Mulungu pachiyambi, ndipo palibe amene angakhale Msilamu popanda kukhulupilira Mose ndi Yesu monga Aneneri akuluakulu a Mulungu. Ndikufuna kutsimikiza kuti Chisilamu ndi uthenga woona kuyambira kale mpaka lero lino, komanso ndi uthenga womaliza womwe watsala wochokera kwa Mulungu kupita kwa anthu. Choncho, ndaima kwambiri pakulongosola mmene zipembedzo zitatuzi (Chiyuda, Chikhristu ndi Chisilamu) zimawaonera akazi, osati momwe zimaonekera ndi myandamyanda yomwe ikutsata za dziko lapansi. Nchifukwa chake ndikugwiritsa ntchito maumboni ambiri kuchokera mu Qur’an, mawu a Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam, Baibulo, Talmud, ndi mawu a Atsogoleri azipembedzo amphamvu kwambiri, omwe maganizo awo athandizira kwambiri pakufotokoza Chikhristu.

Kukhala ndi chidwi pa kufufuza kuchokera mmaumboni oterewa kukuthandiza kudziwa kuti kuchimvetsetsa chipembedzo kuchokera mu zikhalidwe za ongotsatira chabe ndikosocheretsa. Anthu ambiri amasokoneza chikhalidwe ndi chipembedzo, ndipo ambiri sadziwa zomwe mabuku awo achipembedzo akunena, komanso ena ambiri salabada zimenezo.

Kulakwa kwa Hawa