Kusiyana kwa veil ndi wedding dress

Ma Sheikh odalirika pamaphunziro a Chisilamu akhala akuchilimika kuletsa chovala chija chotchedwa “veil” pa nikaah. Lero tikufuna tichitirepo chidwi ndi kufotokoza momveka bwino pa nkhani imeneyi kuti aliyense atenge choonadi cha chovala chimenechi.

Kodi veil ndo chovala cha Chikhrisitu? Kodi Asilamu ndiololedwa kuvala?

Liwu loti “Veil/ Veiling ndi liwu la English ndipo mu Chichewa likutanthawuza kuti “kuphimba/kuvinkira”. Mu Arabic kutanthawuza Tahajjub/Hijaab.

Wedding dress ndi Veil

Tikuyenera kusiyanitsa pakati pa wedding dress ndi veil; veil ndi chovala cha Msilamu aliyense wamwamuna ndi wamkazi pobisa maliseche ake (hijaab). Hijaab ndi chovala chovindikira maliseche a munthu wina aliyense, ndipo kuvala kobisa maliseche kuli kokakamizidwa mbali zonse za azibambo ndi azimayi omwe, komanso malamulo ndi ma conditions a chovala chobisa maliseche ndi ofanana kwa mkazi ndi mwamuna; kuti chikhale chokhuthala komanso chosathina. Kuvala zovala zothina komanso zopyapyala zoonekera mkati ndi koletsedwa kwa mwamuna ndi mkazi yemwe.

Kusiyana kwa mavalidwe a veil ndi oti mwamuna amavindikira mbali ya thupi lake lochepa pamene mkazi amavindikira thupi lonse kupatula nkhope ndi manja ake okha basi, kapena thupi lonse nkusiya maso okha (niqaab).

Wedding dress ndi chovala chomwe mkazi kapena mwamuna amakhonza kuti adzavale pa ukwati wake.

Kutanthauza kwa wedding dress ndiko kuti chovala cha tsiku la ukwati/Nikah pa walimah. Munthu aliyense wamkazi kapena wamwamuna amakonzekera chovala chake chomwe adzavale pa mwambo uliwonse womwe uli wa pamwamba, ndipo chovalacho chimakhala chovala cha mwambo umenewo. Ukakhala ukwati Nikah/walimah kapena wedding, chovalacho chidzatenga dzina la mwambo wa nikah/walimah kapena wedding malingana ndi chilankhulo chomwe anthu achikonda.

Tsopano malamulo a wedding dress akhala malamulo a kuvala kwa Chisilamu, kaya mwamuna kaya mkazi; atsatire malamulo akuvala kwa Chisilamu pa chovala chake chomwe akufuna kuvala malingana ndi pa gulu pomwe akapezekepo.

Tsopano nkhani ya malamulo a kuvala kwa mtsikana yemwe akukwatiwa, ndi yosasiyana ndi mnyamata yemwe akukwatiwa.

Tisaiwale, azimayi azikhala kwa azimayi okhaokha pa walimah ndipo ngati atakhala limodzi (azibambo ndi azimayi malo amodzi), onsewo ayenera kuvala motsatira malamulo a Chisilamu ndipo azimayi ayenera kukhala chete, asalongolole komanso asadzigwedezegwedeze. Ndipo adzakhala m’mbuyo mwa azibambo, sakuyenera kuimba chirichonse kapena kukweza mawu awo. Kwawo azimayi kudzakhala kumvera zolankhula za azibambo pa mwambo uli onse omwe azimayi ndi azibambo apezekera pamodzi.

Koma ngati azibambo ali kwawo azimayinso kwawo sakuonana, onse adzakhala otakasuka pakati pawo; azimayi pakati pa azimayi avale momasukirana, chimodzimodzinso azibambo.

Choncho sitikuona cholinga chilichonse chopelekera malamulo a wedding dress kwa azimayi, chifukwa Walimah yabwino ndi yomwe azimayi akhala kwawokha azibambonso kwawokha; kuti azimayi akhale omasuka kupanga zinthu zomwe sangapange pamaso pa azibambo.

Masheikh omwe amalimbikitsa mtsikana okwatiwa kuvala modziphimba tsiku la walimah amafuna kuti mtsikana okwatiwayo azikafika kugulu la azibambo, izi sizololedwa mu Chisilamu. Azimayi azikhala kwawo azibambonso kwawo kuti onse azitha kumasuka ndi kusangalala mokwanira, chifukwa tsiku la walimah ndi tsiku la chisangalalo, si tsiku lomangana.

Veil ndi liwu la “English” kutanthawuza kuti “Chodzivindikira nacho”. Veiling ndi kuvinikira.

Kuvala Chovala Choyera:

Chovala choyera ndi chokondedwa ndi Mtumiki ndipo kuvala chovala choyera ndi zabwino mu Chisilamu nthawi ina iliyonse, kuphatikizapo mma walimah. Choncho ngati timaona akhristu akuvala zoyera mmaukwatui awo, anatengera Asilamu, koma kuti iwowo amachikhonza mmakhonzedwe osemphana ndi Chisilamu. Choncho Msilamu sakuyenera kusiya kuvala zovala za white kamba koti akhristu amavala. Kukakhala kutengera, iwowo ndamene anatengera Asilamu ndipo kutengera koletsedwa ndikomwe kumachitika pamakhonzedwe a chovalacho (kuthina, kuonekera mkati ndi zina zotero). Choncho Msilamu avale zoyera koma asatyengere masokedwe a chikhristu.

Kudzivunukula Tsiku la Walimah

Pomaliza mwa chidule kwambiri, kuchotsa mpango kumutu ndikudzivunukula tsiku la walima pakati pa azimayi okhaokha ndi kumacheza ngati chikhalidwe pokondwerera kwawo, sindikupeza umboni woletsa zimenezo.

Timvetsetsane kuti veil kapena popanda veil, mzimayi okwatiwa ndi azimayi onse asapezeke ku chigulu cha azibambo! Ndipo kamba kakuti akhala kugulu la azimayi okha okha, mtsikana okwatiwa ali omasuka kuvala zina zili zonse pakati pa azimayi, zosaonetsa maliseche. Komanso omwe amalimbikitsana zokonza mavalidwe amkazi okwatiwa pa Nikaah ndi walima, akungofuna azimayi azisakanikirana ndi azibambo.

Tikulangizeni kuti palibe ضرورة (kufunikira) kulikonse komwe kukupangitsa kuti azimayi ndi azibambo asakanikirane pa nikah kapena pa Walimah.

Azimai aziwuzidwa za kavalidwe popita ku mzikiti kapena kukamvera ma ulaliki a Allah ndi kunja kwina kuli konse komwe iwo afuna kupita komwe atha kukumana ndi azibambo.

Kuphunzitsa mavalidwe a mzimayi pa nikaah kapena pa walimah, kumeneko ndikutuma azimayi kuti azisakanikirana ndi azibambo, zomwe mu Chisilamu ndi zoletsedwa. Chisilamu chinaphunzitsa kale mavalidwe a mzimai malo aliwonse, ndipo palibe kuvala kwaspecial pa nikaah koposa komwe Chisilamu chinaphunzitsa. Ngati mukuphunzitsa mavalidwe a special pa nikaah, ndi zomwe mukubweretsa ma fitnazi.

Akhristu okwatirana amavulana veil pakati pa okwatira ndi okwatiwa pa chigulu cha amuna ndi akazi komanso ana, ndikuvekana ma ring komanso kupsopsonana mowakhumbidza anthu ndi kumawaombera mmanja. Zonsezo sangapange Msilamu otsatira malamulo tanena aja. Anthu oti sanasakanikirane sangapeze nthawi yovulana veil pagulu, kuvekana ring kapena kupsopsonana ngati mwambo wapadera pakati pa gulu la anthu, chifukwa ingasowe nthawi ndi malo opezerana.

Kuvulana veil, kuvekana ring, kupsopsonana komanso ku hagana kwa pagulu ndizolakwika mu Chisilamu.

Malinga ndi maganizidwe a anthu ena pa nkhaniyi, ndikufuna ndichenjeze kuti masiku athu ano bodza likakhanzikika limasanduka choonadi. Ndipo

حين سكت أهل الحق عن الباطل توهم أهل الباطل أنهم على حق

“Pamene ozindikira za Haqq (zoona, ma Sheikh, akakhala chete pamene zoipa zikuchitika), ochita zoipa amaganiza (ndipo amakhulupilira) kuti ali mu choonadi, (amaganiza kuti akulondola ndithu, ndipo akuchita malinga ndi Shariah).

Choncho ma Sheikh akuyenera kuletsa zinthu zolakwika pamene zikuchitika pakati pa Ummah, ndipo asamudandaule munthu aliyense kapena kusamala ubale wapakati pawo, koma asamale ubale wapakati pa iwon (Sheikhwo) ndi Allah Ta’la, chifukwa Iye ndiyemwe adzafinse Tsiku la Qiyamah ndikuwalipira ntchito zawozo, osati anthu.