Pambuyo pa kuwerenga zolembedwa zoyambilira zokhunza amayi, anthu omwe sali Asilamu akhonza kukhala ndi funso lofanana loti: Kodi akazi a Chisilamu lero lino akutengedwa malinga momwe zalembedwera mu bukumu? Yankho lake ndiloti: Ayi. Kopa popeza funso ili sililephera kufunsidwa pa zokambirana za amayi mu Chisilamu, tiyenera kufotokoza momveka bwinobwino.

Choyamba, ziyenera kumveka bwino kuti kusiyana kwakukulu komwe kuli pakati pa Asilamu kumapangitsa kuti zambiri zikhale zophweka. Masiku ano kuli malingaliro osiyanasiyana padziko lapansi, okhunza amayi, malinga ndi kusiyana
kwa maiko, omwe amasiyana pakati pa gulu lina ndi linzake. Komabe, zizoloŵezi zina zonse ndizodziwika. Pafupifupi mafuko onse a Asilamu padziko, ali ndi mbali yomwe adapatukira ku ziphunzitso za Chisilamu zokhunza akazi. Kupatuka kumeneku kumakhala kolowera ku imodzi mwa njira ziwiri zosemphana; njira yoyamba imakhala yosakanikirana ndikupendekera kwambiri pa chikhalidwe cha makolo, pomwe njira yachiwiri imakhala yosakanikirana ndikupendekera
kwambiri ku zikhalidwe za Kumadzulo.

Anthu omwe amakopeka ndi njira yoyamba ija, amawatenga akazi motsatira chikhalidwe komanso miyambo yomwe amatengera kuchokera kwa azigogo awo. Myambo ndi zikhalidwe zimenezi kawirikawiri zimaletsa akazi maufulu awo ochuluka omwe Chisilamu chinawapatsa. Kuphatikizanso pamenepo, akazi amatengedwa mosiyana kwambiri kuyerekeza ndi amuna. Tsankho limeneli limapita kwa mkazi wina aliyense:

  • amalandiridwa ndi chisangalalo chochepa akamabadwa, kusiyana ndi mwana wamwamuna;
  • zimakhala zovuta kuti apite ku sukulu;
  • akhonza kumanidwa ufulu wopata cholowa kuchokera kwa makolo ake;
  • amakhala akuyang’aniridwa mosamalitsa kwambiri kuti asachite chinthu choipa, pomwe zochita zoipa za mchimwene wake zimalekeleredwa;
  • akhonzanso kuphedwa chifukwa chochita choipa chomwe mwana wa’mbanja lomwelo amachita modzitama nacho;
  • alibe ufulu wokamba pa zochitika za pabanja kapena zochitika za m’deralo;
  • iye sangakhale ndi ulamuliro wonse pa chuma chake ngakhale mphatso zake za ukwati;
  • ndipo potsiriza, monga mayi, nayenso angakonde kubala anyamata okhaokha kuti athe kukhala ndi ulemelero m’deralo.

Komatu pali magulu ena a Chisilamu omwe asunthidwa ndi chikhalidwe cha Kumadzulo komanso makhalidwe a moyo wawo. Izi zimachitika chifukwa choti magulu a Chisilamu oterewa amakhala akungotengera chirichonse chomwe angalandire kuchokera Kumadzulo, ndipo nthawi zambiri amatengera zotsatira zoipa za chitukuko cha Kumadzulo, nkumati akukhala motukuka. M’madera amenewa tipeza kuti chinthu chomwe “mkazi” wa Chisilamu “wamakono” amachiona kufunikira mmoyo mwake ndiko kutukuka pa kukongoletsa thupi lake basi. Choncho, nthawi zambiri amakhala otangwanika ndi mawonekedwe a thupi lake, kukula ndi kulemera kwake.
Nthawi zonse amakhala akusamalira kwambiri thupi lake kuposa maganizidwe,
komanso amakhala akusamalira kukongola kwake kuposa nzeru zake, amakwanitsa kuzikongoletsa, kudzipanga kukhala wachikoka pakati pa anthu ngakhale atakhala opanda nzeru zilizonse mmutu, osaphunzira. Alibe malingaliro a phindu pa maphunziro kapena tsogolo. Pokhala mayi wa Chisilamu, simungapeze Qur’an mkati mwa chikwama chake cha mmanja, poti nthawi zonse chimakhala chodzadza ndi zodzoladzola zomwe amayendana nazo kulikonse komwe akupita. Umoyo wake wauzimu ulibe malo pakati pa anthu chifukwa cha kutangwanika ndi kukongola kwake. Nchifukwa chake, amatha kugwiritsa ntchito nthawi ya moyo wake wonse pa kusamalira ukazi wake, kuposa kukwaniritsa umunthu wake.

Nchifukwa chiyani Asilamu ena adasemphana ndi ziphunzitso za Chisilamu? Yankho lake ndilovutirapo; Kusanthula kwakukulu kwa zifukwa zomwe Asilamu sanatsatire chiphunzitso cha Qur’an chokhudza akazi, kukhala kwakukulu kuposa phunziro lathuli. Tikuyenera kudziwa kuti Asilamu ena anasokonekera pa malamulo a Chisilamu okhudza mbali zambiri za moyo wawo kwa nthawi yayitali, ndipo pali kusiyana kwakukulu pakati pa zomwe Asilamu akuyenera kukhulupilira ndi zomwe akuchita. Kusiyana kumeneku sikunachitike posachedwapa, koma kunayamba kalekale ndipo kwakhala kukunka nakufutukuka tsiku ndi tsiku. Zotsatira za kufutukuka kumeneku ndi zoopsa kwambiri Mchisilamu, poti zakhala zikuwonetsedwa fupifupi mbali zonse za moyo wa Msilamu monga: kuponderezana pa ndale ndi kugawidwa, kubwelera mbuyo pa zachuma, kupanda chilungamo pakati pa anthu, kusokonezeka kwa maphunziro, kuwonongeka kwa nzeru, ndi zina zotero. Chikhalidwe cha chikunja chomwe chili pakati pa amayi a Chisilamu lero lino ndi chizindikiro chabe cha matenda aakulu. Ndipo kusintha kulikonse komwe kukufunikira pakati pa amayi a Chisilamu sikungakhale kwaphindu kupatula ngati sipapezeka kusintha kokwanira munjira zonse za umoyo wawo. Chisilamu chikusowekera kusintha kwamphamvu komwe kungadzawandikitse anthu ku chiphunzitso cha Chisilamu. Maganizo oti kunyozeka kwa amayi a Chisilamu ndi chifukwa cha malamulo a Chisilamu, ndi maganizo olakwika kwambiri. Dziwani kuti palibe vuto lomwe Asilamu akukumana nalo chifukwa cha kugwiritsa kwambiri malamulo a Chisilamu, koma kuti ndi zotsatira za kusatsatira malamulowo.

Zikuyenera kumvekanso bwino kuti cholinga cha kafukufuku ameneyu si kunyoza Chiyuda kapena Chikhristu. Malo a amayi mu Chiyuda ndi Chikhristu akhoza kukhala owopsya tikayerekeza ndi kumapeto kwa zaka za 20th century. Ngakhale zili choncho, ziyenera kuwonedwa m’mbiri yoyenera. Mukuyankhula kwina, kafukufuku aliyense yemwe angachitike wa amayi mu chikhalidwe cha Chiyuda ndi  Chikhristu, akuyenera kulingalira zambiri yakale yomwe mwambo umenewu unayambira. Sitikukayikira kuti maganizo a ma Rabbi ndi Abambo a Tchalitchi okhudzana ndi amayi, atengedwa kuchokera mmalingaliro omwe anafala m’madera awo. Tikaonesetsa Baibulo lenilenilo, tipeza kuti linalembedwa
ndi alembi osiyanasiyana mu nthawi zosiyanasiyana. Alembi amenewotu, zolemba zawo zinali kuchokera mu chidwi chawo pa makhalidwe ndi njira za moyo wa anthu oyandikana nawo. Mwachitsanzo, malamulo a chigololo Mchipangano Chakale anapondereza amayi kwambiri kotero kuti ndi osatheka kuwalongosola momveka malinga ndi nzeru zathuzi. Komabe, tikaonesetsa, tipezanso kuti mafuko oyambilira a Chiyuda anali otengeka kwambiri ndi mabadwidwe awo, komanso anali kufunisitsa kukhala odziwika kuposa mafuko ena oyandikana nawo, ndipo, chikhalidwe choipa cha kugonana chomwe chingachitike ndi amayi okwatiwa, chinali chiopsezo ku zikhumbo zawo zosangalatsazo;  ndiye tikutha kumvesetsa zifukwa zomwe zimachititsa kusokonezeka kwa malamuloku. Komanso, nkhanza ya Abambo a Tchalitchi kwa amayi sikuyenera kuchotsedwa mu chikhalidwe cha Chigiriki ndi Chiroma kumene amakhala. Sichikhala chilungamo kuyesa mbiri ya Chiyuda ndi Chikhristu popanda kutenga zochitika zonse za mbiri yomwe ikulumikizana ndi iwo.

Ndipotu, kumvetsetsa bwino pa zochitika za Chiyuda ndi Chikhristu ndikofunikira  kwambiri, chifukwa zitipangitsa kudziwa kufunikira kwa Chisilamu pa mbiri yakale ya dziko ndi chitukuko cha anthu. Chikhalidwe cha Chiyuda ndi Chikhristu chinatengedwa kuchokera mu zochitika ndi zikhalidwe zomwe zinalipo kale. Pofika m’zaka za mma 7th century, zimenezi zinasokoneza uthenga waumulungu wa pachiyambi womwe unavumbulutsidwa kwa Mose ndi Yesu. Kunyozeka kwa amayi mu Chiyuda ndi mu Chikhristu mu 7th century, ndi chimodzi mwa zomwe zinasokonezedwa mu uthengwawu. Nchifukwa chake padadza uthenga wina waumulungu, wawukulu, womwe udadza kudzawongolera anthu kubwelera mu njira yolungama.

Qur’an ikufotokoza ntchito ya Mtumiki watsopano monga kumasulidwa kwa

Ayuda ndi Akhristu ku zolemetsa zawo zomwe adazichitira:

Qur’an 7:157: “Omwe akutsata Mtumiki, Mneneri wosatha kuwerenga ndi kulemba. (Ngakhale ali choncho, akuphunzitsa zophunzitsa zodabwitsa); yemwe
akumpeza atalembedwa kwa iwo m’Buku la Taurat ndi Injili, akuwalamula zabwino ndi kuwaletsa zoipa, ndi kuwaloleza zabwino ndi kuwaletsa zodetsedwa (zoipa); ndi kuwatula mitolo yawo ndi magoli omwe adali paiwo (malamulo ovuta kuwatsata)…”

Choncho, Chisilamu sichiyenera kuwonedwa ngati chikhalidwe chotsutsana ndi Chiyuda kapena Chikhristu. Chiyenera kuonedwa ngati chipembedzo chomwe chikutsirizitsa, kukwaniritsa, ndi kubweretsa ungwiro wa mauthenga auzimu omwe adavumbulutsidwa kale.

Pamapeto pa phunziroli, ndikufuna kupereka malangizowa ku mtundu wonse wa Chisilamu: Amayi ambiri a Chisilamu akhala akumanidwa ufulu wawo wa Chisilamu kwa nthawi yayitali.

Zolakwitsa zakale ziyenera kukonzedwa. Kuchita zimenezo sikuti kukondera, koma ndi udindo waukulu kwa Asilamu onse.

Maiko onse a Chisilamu akuyenera kuika malamulo a ufulu wa amayi a Chisilamu kupyolera mmalangizo a Qur’an ndi chiphunzitso cha Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam.

Malamulo amenewa ayenera kubwezera amayi a Chisilamu ufulu wonse womwe adapatsidwa ndi Mlengi wawo. Kenako, njira zonse zofunikira ziyenera kukonzedwa kuti zitsimikizidwe kuti ntchitoyi ikhazikitsidwa bwino. Chikhanzikitso chimenechi ndi chakale ndipo chikuchitika mochedwa, komabe ndibwino mochedwa momwemo kusiyana ndi kusachita. Ngati Asilamu padziko lapansi sadzatsimikiziranso ufulu wa amayi awo, akazi awo, alongo awo ndi ana awo aakazi, kodi pali ena omwe adzapange zimenezo?

Kuwonjezera apo, tiyenera kukhala olimba mitima pothetsa zakale ndikukana miyambo ndi zikhalidwe za makolo athu akale, zomwe zimatsutsana ndi malamulo a Chisilamu. Kodi Qur’an sinadzudzule ma Arabu achikunja chifukwa
chotsatira miyambo ya makolo awo mwakhungu? Mbali ina, tikuyenera kukhala olimba pa chilichonse chimene timalandira kuchokera Kumadzulo, kapena ku chikhalidwe china chilichonse. Kuyanjana komanso kuphunzira kuchokera mzikhalidwe zina ndizofunika kwambiri.

Qur’an yatsimikizira kuti kugwirizana uku ndi chimodzi mwa zolinga za chilengedwe:

Qur’an 49:13: “E, inu anthu! Tidakulengani (nonse) kuchokera kwa mwamuna (m’modzi; Adamu) ndi mkazi (m’modzi; Hawaa), ndipo tidakuchitani kukhala a mitundu ndi mafuko (osiyanasiyana) kuti mudziwane (basi).” (49:13). Komabe, kutsatira kwaumbuli kwa ena omwe amatsatira, ndi chizindikiro chodziwikiratu kuti akusowekera kudzidalira kwathunthu.

Mau omalizawa, akupita kwa Atsogoleri achikunja omwe sali Asilamu, kaya Achiyuda, Achickhristu kapena ena onse. Ndizododometsa kuti nchifukwa chani chipembedzo chomwe chinasintha kakhalidwe ka amayi lero lino chikusankhidwa kuti ndi chopondereza amayi? Maganizo amenewa ndi chimodzi mwa ziphunzitso zowonjezera zabodza kwambiri zomwe zafala lero lino. Komanso, bodza limeneli likupitilizidwa mopanda malire kudzera mmabuku olembedwa mochititsa chidwi, zolemba zachidule, zithunzi komanso mafilimu a Hollywood. Zotsatira zosavomerezeka za zithunzi zosayenerazi zakhala zikubweretsa kusamvetsetsana kwathunthu ndi mantha pa chirichonse chokhudzana ndi Chisilamu. Ngati tikufuna kukhala padziko lopanda tsankho, ndikusamvesetsana; kupereka chithunzithunzi cholakwika cha Chisilamu
komanso kufalitsa nkhani zabodza, ziyenera kutha. Omwe sali Asilamu ayenera
kuzindikira kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa zikhulupiliro ndi zikhalidwe
za Asilamu, komanso kuti zochita za Asilamu sizikuimira Chisilamu. Kuchipanga
chikhalidwe cha akazi a Chisilamu lero lino kuti ndi “Chisilamu”, ndi kutalitali ndi Chisilamu monga mmene ziliri kuwapanga  akazi a Kumadzulo kuti akupanga za “Chiyuda kapena Chikhristu”. Kuchokera pa kumvesetsa kumeneku, Asilamu ndi omwe sali Asilamu akuyenera kuyamba kugwirizana pokambirana kuti achotse kumvetsetsa kolakwika, kukaikira komanso kuopa komwe kulipo pakati pa Asilamu, Ayuda ndi Akhristu. Tsogolo lamtendere laumunthu ndi lomwe lingapangitse kuti kukambirana koteroko kutheke.

Chisilamu chiyenera kuonedwa kuti ndi chipembedzo chomwe chinasintha kwambiri chikhalidwe cha amayi ndipo chinawapatsa ufulu wochuluka womwe dziko la lero lino lazindikira posachedwapa. Chisilamu chili ndi zambiri zomwe
chikuyenera kupereka kwa mayi wa lero; ulemu, ndi chitetezo kumbali zonse
komanso mmagawo onse a moyo wake, kuchokera pa kubadwa mpaka imfa, kuphatikizapo kuzindikira kufunika kwake, kufananitsa kufunika kwa ufulu wake ndi ena onse, ndi njira zomukwaniritsira uzimu wake, luntha, zosowa zakuthupi ndi nzeru. Sizodabwitsa kuwona kuti ambiri mwa omwe amasankha kubwelera ku Chisilamu m’dziko la Britain ndi amayi.  Komanso amayi ku U.S. amabwelera
Chisilamu ochuluka kupoa amuna, moti amapezeka amayi 4 olowa Chisilamu pomwe mwamuna ndi mmodzi (4:1). 85

Chisilamu chili ndi zambiri zomwe chingapereke ku dziko lathu, koma likusawukira kwambiri chikhalidwe ndi utsogoleri. Anayankhula Ambassador Herman Eilts, pamene anali kuikira umboni pamaso pa komiti yowona zakunja, ku Nyumba ya Oimira a United States Congress (Foreign Affairs of the House of
Representatives of the United States Congress),
pa June 24, 1985, adati,
“Asilamu padziko lonse lapansi ali pafupifupi 1 bilioni. Ndi chiwelengero
chochititsa chidwi kwambiri. Komatu chomwe chikundichitisa chidwi kuwonjezera pamenepo ndi choti Chisilamu lero lino ndi Chipembedzo cha Umodzi wa Mulungu chomwe chikukula mofulumira. Zimenezi ndizofunika kuziganizira. Pali china chake ndithu chomwe ndicholondola Mchisilmu.”

Zoonadi, chinachake ndi cholondola Mchisilamu ndipo ndi nthawi yoti mufufuze. Ndili ndi chiyembekezo kuti phunziro ili ndi gawo loyamba pakufufuza kwanu.

Tsamba Loyamba