Funso: Abale anga okondedwa Mchipembedzo ndifunse nawo; kodi mwana ndibwino kumpatsa dzina lakuti “Mashaallah”? Ena akuti ndi zotheka chifukwa pali monga “Shukuran”, kuchokera ku Shukru-Llaah”, choncho “Mashaa-Allah” sangatengere gender-male or female.

Yankho: Poyamba, “Shukraan” ndi dzina lomwe likuchokera ku liwu la Arabic “Shakara (Wathokoza)”. Ndipo likutanthauza kuti “Wothokoza”. Dzinali mu Arabic sinalumikizidwe ndi -Allah (monga kunena kuti “Shukru-llah” monga mmene munamvera, komanso maina omwe alumikizidwa ndi -Allah ali ndi malamulo ake pofuna kumutchulira munthu.

*MAA SHAA ALLAH*

“Maa Shaa Allah ndi mawu omwe timayenera kunena pamene zatisangalatsa zomwe tili nazo monga chuma kapena ulemelero uliwonse, mu Surah Al Kahf aayah 39 tikumvamo kuti

وَلَوْلا إِذْ دَخَلْتَ جَنَّتَكَ قُلْتَ مَا شَاءَ اللَّهُ لا قُوَّةَ إِلَّا بِاللَّهِ

“Ndipo pamene umalowa m’munda wako ukadanena kuti “maa shaa Allah (izi ndi zimene wandifunira Allah), laa quwwata illaa billaah (mphamvu sizikadapezeka koma kupyolera mwa Allah)” (zikadakhala zabwino kwa iwe)”…

Komanso kuchokera mu athar iyi:

إذا رأى الإنسان شيئًا يعجبه فليبرك

“Akaona mmodzi wa inu zomwe zamusangalatsa, anene mau a madalitso” (kunena kuti “Maa shaa Allah (Izi nzomwe wafuna Allah)” kapena “Baaraka Allah (Allah wadalitsa)” podziteteza ku nsanje la ena pa zabwino zomwe mwaonazo.
{Source Liqaaul Baabil Maftooh Sheikh Ibn Uthaimeen Rahimahu-Allah لقاء الباب المفتوح – 19/235}

Choncho “Maa sha Allah” silingakhale dzina la munthu. Pali mau ofanana ndi “Maa shaa Allah” omwe sakuyenera kuperekedwa ngati maina monga:
“In sha-Allah” “Baaraka-Allah” “Subhaana-Allah” “Alhmaduli-Allah” “Astaghfiru-Allah”, chifukwa ndi ma Adhkaar, mau ofunika kumawayankhula pofuna chitetezo, madalitso komanso chifundo cha Allah Ta’la, osati kuitanira anthu ngati maina awo.

Allah ndiye Odziwa Zonse – Tipempha Iye ationjezere kuzindikira