Kusiyana kwa pakati pa Baibulo ndi  Qur’an pa malamulo okhunza mkazi, kulibe malire pa ana achikazi ongobadwa kumene, iwo akusiyanabe kwambiri. Tiyeni tifananitse Baibulo ndi Qur’an pa mwana wamkazi yemwe akufuna kuyamba kuphunzira:

Tsinde la Chiyuda ndi Torah, momwe muchokera malamulo. Komabe, malinga ndi Talmud, “akazi ndi opatulidwa pa kuphunzira Torah.” Atsogoleri ena a Chiyuda adalengeza momveka bwino kuti “Ndibwino kuti Torah  iwotchedwe kusiyana ndikuipereka kwa akazi kuti aiphunzire.”, komanso “Aliyense amene angaphunzitse mwana wake wamkazi Torah ali ngati wamuphunzitsa zonyansa.” 8

Maganizo a Paulo Woyera mu Chipangano Chatsopano sali owala pankhaniyi:

“Mofanana ndi mmipingo yonse ya oyerawo, akazi akhale chete mmipingo, pakuti sikololeka kuti iwo azilankhula, koma akhale ogonjera, monga Chilamulo chimanenera. Koma ngati akufuna kumvetsa chinachake, akafunse amuna awo kunyumba, popeza nzochititsa manyazi kuti mkazi azilankhula mumpingo. ” (1 Akorinto 14: 34-35)

Kodi mkazi angaphunzire bwanji ngati sakuloledwa kulankhula? Kodi mkazi angakule bwanji ndi nzeru ngati ali wokakamizika kukhala mu chikhalidwe cha kudzipereka nthawi zonse? Kodi angazindikire bwanji mmene dziko likuyendera ngati akukhala kunyumba ndi mwamuna wake yekha basi nthawi zonse?

Tsopano tifunse pofunafuna chilungamo: kodi Qur’an pankhaniyi ili ndi maganizo osiyana? Kankhani komwe Qur’an inafotokoza kakuyankha funso limeneli momveka:

Khawlah anali mkazi wa Chisilamu, yemwe mwamuna wake, Aws, adamuyankhula mau awa pamene anakwiya: “Iweyo kwa ine nchimodzimodzi msana wa mayi anga.” Mawu awa anali kumveka pakati pa Arabu achikunja kuti ndi mau osudzulana, omwe amamasula mwamuna kumbali iliyonse ya kukhala malo amodzi ndi mkazi wake ngati banja, koma sanali kumusiya kuti achoke kunyumba yake kapena kukwatiwa ndi mwamuna wina.

Khawla atamva mawuwa kuchokera kwa mwamuna wake, anali mmavuto. Anapita  kwa Mneneri wa Chislamu, Muhammad salla Allah alaih wasallam kuti akamulangize. Mneneri adampatsa langizo loti ayenera kupilira poti panaoneka kuti panalibenso njira ina. Khawla adalimbana ndi Mneneri pofuna kupulumutsa banja lake lomwe linayimitsidwa. Posakhalitsa, Qur’an inalowelera; Pempho la Khawla linavomerezedwa. Chigamulo chaumulungu chinathetsa chizolowezi choipachi. Surah imodzi (58) ya mu Qur’an yomwe mutu wake ndi “Almujadilah” kapena “Mkazi amene akubwezerana mau ndi Mtumiki” adatchulidwa motere:

Qur’an 58: 1: “Ndithu Mulungu wamva mawu a (amkazi) amene akubwezerana-bwezerana nawe (mawu) pa za mwamuna wake (amene adamsala); ndipo akusuma kwa Mulungu. Ndipo Mulungu akumva kukambirana kwanu; ndithu, Mulungu Ngwakumva Ngopenya (chilichonse).”

Malinga ndi Qur’an, mkazi ali ndi ufulu wokangana ngakhale ndi Mtumiki wa Mulungu mwiniwake. Palibe amene ali ndi ufulu womulangiza kuti akhale chete. Iye sali okakamizidwa kuti mwamuna wake yekhayo ndiyemwe akuyenera kukhala kochokera malamulo a mChipembedzo chake.

Kodi Mkazi ndi Wodetsedwa?