Mapata Atatu Omwe Munthu Akuyenera Kuwadziwa

Buku Lotanthauziridwa Mchichewa, kuchokera mu Buku la 

Thalaathatul Usool wa Adillatuhaa,

lolembedwa ndi

Muhammad bun Abdul Wahab bun Sulaymaan Al Tamimiy

Zindikira – akumvere chisoni Allah – kuti tikuyenera kuphunzira zinthu zinayi izi:

  1. Kuzindikira: Kumeneku ndi kumudziwa Allah Ta’ala, kumudziwa Mtumiki wake, kuchidziwa Chipembedzo cha Chisilamu kudzera mmaumboni.
  2. Kugwiritsa ntchito zimene tazidziwazo
  3. Kuwaitanira ena ku zimene tazidziwazo
  4. Kupilira ndi zowawa zomwe tingakumane nazo pa kuitanira

Allah Ta’ala akunena:

بسم الله الرحمن الرحيم

َالْعَصْرِ –  إِنَّ الْإِنسَانَ لَفِي خُسْرٍ –  إِلَّا الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ وَتَوَاصَوْا بِالْحَقِّ وَتَوَاصَوْا بِالصَّبْرِ

Ndikuilumbirira nthawi –

Ndithu, munthu aliyense ndi wotaika (chifukwa chakugonjetsedwa ndi zilakolako zake), –

Kupatula amene akhulupirira (mwa Allah) ndi kumachita zabwino, ndikumalangizana kutsatira choona ndiponso ndi kumalangizana za kupirira (potsatira malamulo a Allah ndi zina zovuta za mdziko).

Surah Al Asr 1-3 

Imaam Al Shafi’i (Allah amumvere chisoni) anati: Zikanakhala kuti kuti Allah Ta’ala sanavumbulutse umboni kwa zolengedwa zake kupatula Surahyi, ikanakwanira kwa inu 

Al Bukhari (Allah amumvere chisoni) anayankhula pa Khomo la Kuzindikira kusanayambe kulankhula kapena kugwira ntchito: “ndipo umboni wake Allah Ta’ala akunena kuti:

فَاعْلَمْ أَنَّهُ لَا إِلَهَ إِلَّا اللَّهُ وَاسْتَغْفِرْ لِذَنبِكَ

“Dziwa kuti palibe wompembedza m’choonadi koma Allah, ndipo pempha chikhululuko pa zolakwa zako ndi zolakwa za okhulupirira achimuna ndi achikazi; Surah Muhammad 19

Mu aayah imeneyi tikutha kuona kuti Allah Ta’ala anayamba kutchula ‘ilm kenako kuyankhula ndi kugwira ntchito.

M’bale wanga wolemekezeka, dziwa kuti Msilamu aliyense wamwamuna ngakhale wamkazi, akuyenera kuzindikira zinthu zitatu izi ndikudzigwiritsa ntchito:

Choyamba:

Allah Ta’ala anatilenga ife ndipo anatipatsa zoyenereka mmoyo mwathu (rizq); ndipotu sanangotisiya choncho koma anatitumizira Mthenga, yemwe angamutsatire akalowa ku Jannah ndipo yemwe angamukane akalowa ku Moto.

Izi Allah Ta’ala akunena mu Surah Al Muzammil aayah 15-16 kuti:

إِنَّا أَرْسَلْنَا إِلَيْكُمْ رَسُولًا شَاهِدًا عَلَيْكُمْ كَمَا أَرْسَلْنَا إِلَى فِرْعَوْنَ رَسُولًا فَعَصَى فِرْعَوْنُ الرَّسُولَ فَأَخَذْنَاهُ أَخْذًا وَبِيلًا

“Ndithu, ife takutumizirani Mthenga amene adzakhala mboni yanu (tsiku la Chimaliziro; monga momwe tidamtumizira (Musa) kukhala Mtumiki kwa Fir’aun. Koma Fi’raun adamnyoza Mtumikiyo; ndipo tidamulanga chilango chokhwima.”

Chachiwiri:

Allah Ta’ala samasangalatsidwa ndikumuphatikiza ndi zina zake mu mapemphero ake (shirk), ngakhale ophatikizidwayo atakhala Mneneri otumidwa, kapena Mngelo woyandikira kwa Allah, ngakhale ena onse. Allah Ta’ala akunena mu Surah Al Jinn aayah 18 kuti:

وَأَنَّ الْمَسَاجِدَ لِلَّهِ فَلَا تَدْعُوا مَعَ اللَّهِ أَحَداً

“Ndithu, misikiti ndi ya Allah yekha! Choncho, musapembedze aliyense pamodzi ndi Allah.”

Chachitatu:

Yemwe wamtsatira Mtumiki komanso wakhulupilira umodzi wa Allah, sakuloledwa kukhala pa ubwenzi ndi omwe akumuda Allah ndi Mtumiki wake; ngakhale atakhala abale ake oyandikira kwambiri kwa iye. Izi ndi monga momwe Allah Ta’ala akunenera mu Surah Al Mujaadalah aayah 22:

لَا تَجِدُ قَوْماً يُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ يُوَادُّونَ مَنْ حَادَّ اللَّهَ وَرَسُولَهُ وَلَوْ كَانُوا آبَاءهُمْ أَوْ أَبْنَاءهُمْ أَوْ إِخْوَانَهُمْ أَوْ عَشِيرَتَهُمْ أُوْلَئِكَ كَتَبَ فِي قُلُوبِهِمُ الْإِيمَانَ وَأَيَّدَهُم بِرُوحٍ مِّنْهُ وَيُدْخِلُهُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا رَضِيَ اللَّهُ عَنْهُمْ وَرَضُوا عَنْهُ أُوْلَئِكَ حِزْبُ اللَّهِ أَلَا إِنَّ حِزْبَ اللَّهِ هُمُ الْمُفْلِحُونَ

“Supeza anthu okhulupirira mwa Allah ndi tsiku lomaliza akukonda amene akuda Allah ndi Mthenga wake, ngakhale atakhala atate awo, ana awo abale awo ndi akumtundu wawo; kwa iwo (Allah) wazika chikhulupiriro (champhamvu) m’mitima mwawo, ndipo wawalimbikitsa ndi mphamvu zochokera kwa Iye. Ndipo adzawalowetsa m’minda yomwe pansi pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo muyaya. Allah adzakondwera nawo ndipo (iwonso) adzakondwera naye. Iwowa ndi gulu la Allah. Dziwani kuti gulu la Allah ndilopambana.”

M’bale wanga wolemekezeka, dziwa kuti Chipembedzo chowona ndipo chowongoka chomwe ndi njira ya Ibrahim (alaih salaam); ndi kumupembedza Allah Yekha moyeretsa mapemphero. Ntchito imeneyo ndi yomwe Allah Ta’ala anawalamula anthu onse ndipo nchifukwa chomwe anaalengera anthu ndi ziwanda. Iye akunena mu Surah Al Dhaariyaati aayah 56 kuti:

وَمَا خَلَقْتُ الْجِنَّ وَالْإِنْسَ إِلَّا لِيَعْبُدُونِ

“Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti azindipembedza.”

Mau oti “adzindipembedza” akutanthauza kuti “adzimpanga Iye kukhala Mmodzi muntchito zonse komanso kuyankhula”

Dziwani kuti chinthu chachikulu mu zonse zomwe Allah Ta’ala analamula ndi “Tawheed” kumeneku ndi kumpanga Allah Ta’ala kukhala Mmodzi pa Ibaada (pa mapemphero).

Ndipo chinthu chachikulu mu zonse zomwe analetsa ndi “kumuphatikiza Allah ndi zolengedwa zake (Shirk)” kumenekutu ndi kupempha zina zake zosakhala Allah Ta’ala.

Umboni wa kulamula ndi kuletsa kwa zikuluzikulu zimenezi ndi monga ananenera Allah Ta’ala pa Surah Al Nisaai aayah 36:]

وَاعْبُدُ وا اللَّهَ وَلَا تُشْرِكُوا بِهِ شَيْئًا

“Ndipo mpembedzeni Allah, ndipo musamphatikize ndi chilichonse*

Kuchokera mu zonse zomwe ndalongosolazi, mukafunsidwa kuti 

Kodi Mapata atatu omwe munthu akuyenera kuwadziwa ndi ati?

Muyankhe kuti: Kapolo amudziwe Mbuye wake – Chipembedzo chake – Mtumiki wake Muhammad salla Allah alaih wasallam

Amenewatu ndiye mapata atatu omwe mukuli likufotokoza.


PHATA LOYAMBA

(Kumudziwa Allah Tabaraaka wa Ta’ala)

Ngati mungafunsidwe kuti: Mbuye wanuyo ndi ndani?

Muyankhe kuti: Mbuye wanga ndi Allah yemwe amandilera, komanso amalera (amayang’anira) zolengedwa zonse kuzera mu Mtendere wake. Iye ndi yemwe ndimampembedza ndipo ndilibe opembedzedwa wina mwachoonadi posakhala Iye.

Zimenezitu umboni wake ndi mau a Allah Ta’ala ochokera mu Surah Al Fatihah aayah 2:

الْحَمْدُ لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ

“Kutamandidwa konse nkwa Mulungu Mbuye wa zolengedwa zonse.”

China chirichonse kupatula Allah Ta’ala ndi cholengedwa, ndipo ine ndili mu gulu la zolengedwazo

 Ndipo ngati mungafunsidwe kuti: “Munamudziwa bwanji kuti ameneyo ndi Mbuye wanu?

Muyankhe kuti: “Kuzera mu zizindikiro zake komanso zolengedwa zake; mu zizindikiro zake ndi monga usiku ndi usana, komanso  dzuwa ndi mwezi. Mu zolengedwa zake ndi monga mitambo 7 ndi zonse zomwe zikupezeka mmenemo, nthaka 7 ndi zonse zomwe zikupezeka mmenemo komanso zonse zomwe zikupezeka pakati pa ntha ndi mitambo.”

Umboni wake ndi mau a Allah Ta’ala omwe akuchokera mu Surah Ghaafir aayah 57:

لَخَلْقُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ أَكْبَرُ مِنْ خَلْقِ النَّاسِ

Ndithu, kulenga kwa thambo ndi nthaka nkwakukulu kuposa kulenga kwa anthu.”

Komanso akunena mu Surat Fusswilat aayah 37 kuti:

 وَمِنْ آيَاتِهِ اللَّيْلُ وَالنَّهَارُ وَالشَّمْسُ وَالْقَمَرُ لَا تَسْجُدُوا لِلشَّمْسِ وَلَا لِلْقَمَرِ وَاسْجُدُوا لِلَّهِ الَّذِي خَلَقَهُنَّ إِنْ كُنْتُمْ إِيَّاهُ تَعْبُدُونَ

 “Ndipo zina mwa zisonyezo zake, ndi usiku, usana, dzuwa ndi mwezi. Musalambire dzuwa ngakhale mwezi, koma lambirani Mulungu (Mmodzi), amene adazilenga ngati inu mumpembedza moona.”

Al Rabb (Mbuye) nduye Opembedzedwayo.

Umboni wake ndi mau a Allah Ta’ala pa surah Al Baqarah 21-22:

يَا أَيُّهَا النَّاسُ اعْبُدُوا رَبَّكُمُ الَّذِي خَلَقَكُمْ وَالَّذِينَ مِنْ قَبْلِكُمْ لَعَلَّكُمْ تَتَّقُونَ – الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ الْأَرْضَ فِرَاشًا وَالسَّمَاءَ بِنَاءً وَأَنْزَلَ مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَأَخْرَجَ بِهِ مِنَ الثَّمَرَاتِ رِزْقًا لَكُمْ فَلَا تَجْعَلُوا لِلَّهِ أَنْدَادًا وَأَنْتُمْ تَعْلَمُونَ

E inu anthu! Pembedzani Mbuye wanu yemwe adakulengani inu ndi omwe adalipo kale, kuti mudzichinjirize (ku chilango cha Allah). (Allah) yemwe adakupangirani nthaka kukhala ngati mphasa, ndi thambo kukhala ngati denga; ndipo adatsitsa madzi kuchokera kumitambo natulutsa ndi madziwo, zipatso zosiyanasiyana kuti chikhale chakudya chanu. Choncho Allah musampangire anzake uku inu mukudziwa (kuti alibe wothandizana naye).”

Ibn Kathir rahimahuAllah Ta’ala anati: “Olenga zinthu zonsezi ndi yemwe ali oyenera kumupembedza”

Mitundu ya ibaada (mapemphero) amene Allah analamula ndi monga A Islaam (Kugonjera mu Chifuniro cha Allah) – Al Imaan (chikhulupiliro) – Al Ihsaan (Kuchita zabwino), monga kupanga dua (kupempha Allah, kuopa, kukhala ndi chiyembekezo mwa Allah, kuyezamira mwa iye, kukhala ndi khumbo mwa Allah, kukhala ndi mantha, kupereka mantha onse kwa Allah, kudziyandikitsa kwa Allah, kupempha chithandizo cha nthawi zonse  kwa Allah, kudzitchinjiriza ndi Allah kuchokera ku zoipa, kupempha chithandizo cha nthawi yomweyo kwa Allah, kuzinga, kupereka lonjezo ndi zina zambiri zomwe ndi mapemphero omwe Allah analamula. Zonsezo ndi zomuchitira Allah Ta’ala yekha basi.

Zimenezitu akakufunsani maumboni ake osonyeza kuti ndi ibaada, awuzeni kuti:

Umboni wa zimenezi ndi mau omwe Allah Ta’ala akunena mu Surah Al Jinn aayah 18 ija:

وَأَنَّ الْمَسَاجِدَ لِلَّهِ فَلَا تَدْعُوا مَعَ اللَّهِ أَحَداً

“Ndithu, misikiti ndi ya Mulungu yekha! Choncho, musapembedze aliyense pamodzi ndi Mulungu.”

Ndiye yemwe angachitire wina chirichonse chomwe choyenera kumuchitira Allah Ta’ala yekha; ameneyo ndi mushrik komanso kaafir.

Izi Allah Ta’ala akunena mu Surah Al Mu’minun aayah 117;

وَمَنْ يَدْعُ مَعَ اللَّهِ إِلَهًا آخَرَ لَا بُرْهَانَ لَهُ بِهِ فَإِنَّمَا حِسَابُهُ عِنْدَ رَبِّهِ إِنَّهُ لَا يُفْلِحُ الْكَافِرُونَ

Ndipo amene apembedza mulungu wina pomphatikiza ndi Allah (weniweni), chikhalirecho iye alibe umboni pazimenezo; basi chiwerengero chake chili kwa Mbuye wake. Ndithu, osakhulupirira sangapambane.”

Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Dua (kupempha) ndi ibaada (pemphero)”

Izi zikuchokera Mmawu a Allah Ta’la opti:

وَقَالَ رَبُّكُمُ ادْعُونِي أَسْتَجِبْ لَكُمْ إِنَّ الَّذِينَ يَسْتَكْبِرُونَ عَنْ عِبَادَتِي سَيَدْخُلُونَ جَهَنَّمَ دَاخِرِينَ

Ndipo Mbuye wanu wanena: “Ndipempheni, ndikuyankhani; koma amene akudzikweza ndi mmapemphero anga (posiya kundipembedza), adzalowa ku Jahannam ali oyaluka.”

Umboni wa kuopa ndi momwe akunenera Allah Ta’ala mu Surat Aali Imraan aayah 175:

إِنَّمَا ذَلِكُمُ الشَّيْطَانُ يُخَوِّفُ أَوْلِيَاءَهُ فَلَا تَخَافُوهُمْ وَخَافُونِ إِنْ كُنْتُمْ مُؤْمِنِينَ

Ndithudiuyo (anakuopsezani) ndi Satana yemwe amaopseza anzake. Choncho musawaope, ndiopeni Ine ngati inu mulidi okhulupirira.”

Ndipo umboni wa kukhala ndi Chiyembekezo mwa Allah ndi monga akunenera mu Surah Al Kahaf aayah 110:

فَمَنْ كَانَ يَرْجُو لِقَاءَ رَبِّهِ فَلْيَعْمَلْ عَمَلًا صَالِحًا وَلَا يُشْرِكْ بِعِبَادَةِ رَبِّهِ أَحَدًا

Ndipo amene afuna kukumana ndi Mbuye wake, achite zochita zabwino ndipo asaphatikizepo aliyense pa mapemphero a Mbuye wake”.

Umboni wa kuyezamira mwa Allah ndi mau ake omwe akupezeka mu Surah Al Maaidah aayah 23:

وَعَلَى اللَّهِ فَتَوَكَّلُوا إِنْ كُنْتُمْ مُؤْمِنِينَ

Ndipo kwa Allah yekha yadzamirani ngati inu mulidi okhulupirira (Allah).”

Komanso mu Surah Al Talaaq aayah 3:

وَمَنْ يَتَوَكَّلْ عَلَى اللَّهِ فَهُوَ حَسْبُهُ

Ndipo amene akutsamira kwa Allah (pa zinthu zake zonse), ndiye kuti Allah ali wokwana kwa iye (kumkonzera chilichonse)”

Umboni wa kukhala ndi khumbo, kudzichepetsa komanso kukhala ndi mantha, ndi mau a Allah Ta’ala mu Surah Al An’biyaa 90:

إِنَّهُمْ كَانُوا يُسَارِعُونَ فِي الْخَيْرَاتِ وَيَدْعُونَنَا رَغَبًا وَرَهَبًا وَكَانُوا لَنَا خَاشِعِينَ

Ndithu iwo adali achangu pochita zabwino; ankatipempha mwakhumbo ndi mwamantha, ndipo adali odzichepetsa kwa Ife.”

Umboni wa kuopa ndimonga akunenera mu Surah Al Baqarah aayah 150:

فَلَا تَخْشَوْهُمْ وَاخْشَوْنِي

Tero musawaope, koma opani Ine…”

Umboni wa kutembenukira kwa Allah ndi mau ake mu Surah Al Zumar aayah 54:

وَأَنِيبُوا إِلَى رَبِّكُمْ وَأَسْلِمُوا لَهُ

Ndipo tembenukirani kwa Mbuye wanu, ndipo m’gonjereni”

Umboni wa kupempha chithandizo ndi monga akunenera Allah Ta’ala mu Surah Al Fatiha aayah 5:

إِيَّاكَ نَعْبُدُ وَإِيَّاكَ نَسْتَعِينُ

Inu nokha tikukupembedzani, ndiponso Inu nokha tikukupemphani chithandizo.”

Umboni wa kudzitchinjiriza ndi monga akunenera Allah Ta’ala mu Surah Al Naas aayah 1:

قُلْ أَعُوذُ بِرَبِّ النَّاسِ

Nena: Ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye (Mleri) wa anthu (yemwe akulinganiza zinthu zawo).”

Umboni wa kupempha chithandizo cha nthawi yomweyo ndi monga akunenera Allah Ta’ala mu Surah Al Anfaal aayah 9:

إِذْ تَسْتَغِيثُونَ رَبَّكُمْ فَاسْتَجَابَ لَكُمْ

“(Kumbukirani) pamene mudali kupempha Mbuye wanu chithandizo…”

Umboni wa kuzinga ndi mawu a Allah Ta’ala mu surah Al An’aam aayah 162-163:

قُلْ إِنَّ صَلَاتِي وَنُسُكِي وَمَحْيَايَ وَمَمَاتِي لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ – لَا شَرِيكَ لَهُ وَبِذَلِكَ أُمِرْتُ وَأَنَا أَوَّلُ الْمُسْلِمِينَ

“Nena: “Ndithudi, Swala yanga, Mapemphero anga onse, moyo wanga, ndi imfa yanga, (zonse) nza Allah, Mbuye wazolengedwa zonse: Iye alibe wothandizana naye. Izi ndi zomwe ndalamulidwa, ndipo ine ndine woyamba mwaogonjera.”

Kuchokera mu Sunnah za Mtumiki salla Allah alaih wasallam, anati:

لعن الله من ذبح لغير الله

 Allah anatembelera yemwe angazinge posakhala mu (Dzina la) Allah

Umboni wa *kulonjeza (nadhr)*, ndi mawu a Allah Ta’ala mu surah Al Insaan aayah 7:

يُوفُونَ بِالنَّذْرِ وَيَخَافُونَ يَوْمًا كَانَ شَرُّهُ مُسْتَطِيرًا

“(Amene) akukwaniritsa zimene adalonjeza (okha kwa Allah), ndiponso akuopa tsiku (lalikulu) limene zoipa zake zidzakhala zofalikira ponseponse.”

Phata Lachiwiri