Kusiyana kwa Manhaj ndi Aqeedah
Timamva ma Sheikh akamalalikira akunena kuti “Mahnaj Ahli Sunnah wal Jamaa”, ndipo nthawi zina timamva akunena kuti “Aqeedatu Ahli Sunnah wal Jamaa”. Kodi mau awiriwa “Manhaj ndi Aqeedah” ndi amodzi, kapena ndi osiyana?
Manhaj ndi liwu la general lomwe likutanthauza method (kachitidwe ka zinthu) komanso ikunyamula Aqeeda. Kutanthauza kuti Aqeedah ili Mmanhaj.
Pomwe Aqeedah ndiye pamene pakuchokera Imaan; tanthauzo la ma Shahaadah awiri (Laa ilaaha illa Allah Muhammadun Rasulu Allah), komanso zonse zomwe zikupezeka pansi pawo, imeneyo ndi Aqeedah.
الأجوبة المفيدة عن أسئلة المناهج الجديدة ص123 س44
Ndiye tidziwe kuti ngati Manhaj a munthu ali olondola, akamulowetsa ku Jannah, ndipo ngati Manhaj ili yolakwika, akalowa ku moto.
الأجوبة المفيدة عن أسئلة المناهج الجديدة ص125 س47