“Kodi ‘Uthman Radhia Allah Anhu Atamwalira Anaikidwa Kuti?”

‘Uthman radhia Allah anhu atamwalira anasambitsidwa ndi kuvekedwa, ndipo kenako ananyamulidwa ndigulu la antchito ake, ndipo anapempheretsa janaza yake Swahaba Jubayru bun Mut’im, ma report ena amati Al Zubayr bun Al Awaaam, kapena Hakim bun Hizaam, kapena Marwaan bun Al Hakam, kapena Miswar bun Mukhramah.

Ma Khawaarij omwe anamupha ‘Uthman radhia Allah anhu, ankafunitsitsabe kupitiriza chipongwe chawo pa ‘Uthman ndipo anafuna kuwaletsa ma swahaba kusambitsa, kuswalira – ankafuna kuti amugende ali wakufa, ndikumukwilira mmanda a Ayuda (akale) ku Dayri Sal’i ngati kaafir,,, poti paja ma Khawaarij ankawapanga ma Swahaba akuluakulu ngati ‘Uthmaan kuti ndi ma Kafir ,,,, koma nkhani itamufika Aliy radhia Allah anhu, anatumiza anthu omwe anakaletsa zimenezo ndipo janaaza yake inanyamulidwa ndi Hakim bun Hizaam, Abu Jahmi bun Hudhaifa, Niyaaru bun Mukram ndi Jubayr bun Mut’am…

Limenelo ndi riwaayah limodzi chabe, kuchokera kwa Ibn Kathir mu Al-Bidaayah wa Nnihaaya, koma pali ma report ena ochokera mu Attabari vol.4/412 ndi ena ambiri, ena ofunika tahqeeq (kafukufuku).

Choncho ma Khawaarij pamodzi ndi ma Shia, mpaka lero lino amafalitsa zosemphana ndizomwe zinachitika. Tikamapanda kuwerenga basi timangokhulupilira zomwezo.

– ‘Uthman bun Affaan anaikidwa ku Hassh Kawkab, malo omwe analumikizana ndi Baqeei (Manda aakulu ku Madina).

Pachiyambi panali malo otchedwa Hassh Kawkab omwe anawandikana kwambiri ndi Baqeei, ndipo Uthmaan anagula malowa ndikuwakulitsa n’kugundana ndi Baqeei. Atamwalira anaikidwa malo amenewo.

Apa ma Khawaarij ndi ma Shia amanena kuti anaikidwa mmanda a Ayuda poti (amati) Hassh Kawkab anali manda a Ayuda, koma ili ndibodza lalikulu, poti ndizomwe ankafunitsitsa zitachitika koma zinalephereka.

Ayuda anatulutsidwa mumzinda wa Madina nthawi ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam, ndipo otsalawo anatulutsidwa nthawi ya Abu Bakr ndi Umar. Mmene imafika nthawi ya ‘Uthman m’Madina munalibe Ayuda oti mpaka kupanga manda awo.

Choncho Hassh Kawkab sanali manda a Ayuda, koma munda womwe ‘Uthman anagula ndi ndalama zake kuchokera kwa ma Answaar (Asilamu a ku Madina).
Ibn Abdul Barr rahimahu-Allah ananena kuti: Kawkab ndidzina la munthu wa ku Madina, ndipo Hassh ndiliwu lomwe likutanthauza Munda (bustaan), choncho Hassh Kawkab kutanthauza kuti Munda wa Kawkab; ‘Uthman anagula munda kuchokera kwa Kawkab ndikuwonjezera ku manda a Baqeei, ndipo ‘Uthman anali woyambilira kuikidwa mmenemo (mu Hassh Kawkab).
Al Mu’jamul Kabir vol.1/78, Al Isti’aab fi Ma’rifatil As’haab vol.3/1048 – Al Bidaayah wa Nnihaayah vol.10/324

Tisamale pankhani ya imfa ya ‘Uthman, kuikidwa mmanda kwake ndi zina zotero, chifukwa izi zinachitika munthawi ya fitna zikuluzikulu, fitna yomwe Hudhaifa anayankhula kuti “fitna yoyambilira pakuopsa, ndipo yomaliza ndiya Dajjaal”. Ndipo anthu odana ndi ‘Uthmaan radhia Allah anhu monga ma Khawaarij ndi ma Shia, amakhala akufalitsa tinkhani tabodzati tomuipitsa Swahaba,,, inde amawerenga mabuku awo omwe tikuwadziwanso.

‘Uthman anaphedwa ndi ma Khawaarij aku Egypt ndi Iraq, ma Khawaarij. Ndipo kuti azifika pophedwa kunachitika ndale yoopsa yachiwembu, kotero kuti ma Swahaba sanali kuganiza kuti iwo angafike pomupha Khalifa… Al Bidaayah wa Nnihaayah vol.10/324
Zakusambitsidwa kwake, swalaat janaaza yake,,, tikhale ndi chikhulupiliro choti anachitiridwa monga mmene Msilamu amayenera kuchitidwa malinga ndi mmene wafera. Pali mafedwe ena oti sangasambitsidwe, sangaswaliridwe, koma zimenezo sizikupungula kalikonse mu Usilamu wake.

Uyu anali Khalifa wolemekezeka ndipo nkhani ya imfa yake tisatangwanike nayo kuposa kudziwa za moyo wake ndi ntchito zake komanso maphuzniro omwe tingatenge mu ulamuliro wake monga Mtsogoleri wa Asilamu wachitatu pambuyo pa Mtumiki salla Allah alaih wasallam.
Allah Ndiye mwini kudziwa Konse