Malingana ndi Baibulo, munthu ayenera kukwaniritsa malonjezo omwe angapange kwa Mulungu. Iye sayenera kutswa liwu lake. Koma lumbiro la mkazi silikhala lokakamizidwa pa iye; iye akuyenera kuloledwa ndi bambo ake, ngati ali osakwatiwa; kapena ndi mwamuna wake, ngati ali okwatiwa. Ngati bambo / mwamuna savomereza malonjezo a mwana/mkazi wake, malonjezo onse opangidwa ndi iye amakhala opanda pake. Malemba akuti:

Munthu akalonjeza kwa Yehova, kapena akachita lumbiro lodzimana, asalephere kukwaniritsa mawu ake. Achite malinga ndi mawu onse otuluka pakamwa pake. “Mtsikana amene akanali m’nyumba ya bambo ake akalonjeza zinazake kwa Yehova, kapena akachita lonjezo lodzimana, bambo ake nkumumva ndithu akulonjeza kapena akuchita lonjezo lodzimanalo, koma osanenapo kanthu, malonjezo ake onsewo akhale momwemo. Zikatero, lonjezo lake lililonse lodzimana likhale momwemo. Koma ngati bambo ake amkaniza pa tsiku limene amva malonjezo ake onse, malonjezo ake odzimana amene walumbirira moyo wake, akhale opanda ntchito. Yehova adzamkhululukira chifukwa bambo ake anamkaniza. “Koma ngati mkaziyo ali wokwatiwa, ndipo akuchita lonjezo mwa kulumbirira moyo wake, kapena kulonjeza ndi pakamwa pake mosaganizira bwino, mwamuna wake n’kumva koma osanena kanthu kwa iye pa tsiku limene wamva mawu a lonjezolo, malonjezo ake a kudzimana amene walumbirira moyo wake akhale momwemo. Mwamunayo akamkaniza pa tsiku limene wamva kulonjezako, ndiye kuti wafafaniza lonjezo la mkaziyo, kapena lonjezo lake limene anachita mosaganizira bwino, limene analumbirira moyo wake ndi pakamwa pake. Yehova adzam’khululukira mkaziyo. “Koma mkazi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati akachita lonjezo, lonjezo lililonse limene walumbirira moyo wake likhale momwemo. “Komabe, ngati mkazi walonjeza ali mnyumba ya mwamuna wake, kapena ngati wachita lonjezo lodzimana mwa kulumbirira moyo wake, mwamuna wake nkumva koma osanenapo kanthu, osamkaniza, malonjezo ake onse akhale momwemo, ndipo lonjezo lililonse lodzimana limene walumbirira moyo wake likhale momwemo. Koma mwamuna wake akafafaniza malonjezowo pa tsiku limene wamva mawu alionse otuluka pakamwa pa mkaziyo, mawu olonjezerawo kapena malonjezo ake odzimana amene walumbirira moyo wake, malonjezo a mkaziyo akhale opanda ntchito. Mwamuna wake wawafafaniza, ndipo Yehova adzamkhululukira mkaziyo. Mwamuna wake ali ndi mphamvu zokhazikitsa kapena kufafaniza lonjezo lililonse la mkazi wake, kapenanso lumbiro la mkaziyo lodzimana, losautsa moyo wake. Koma ngati mwamunayo sananenepo kanthu kwa mkazi wake, masiku nkumapita, ndiye kuti mwamunayo wakhazikitsa malonjezo onse a mkaziyo, kapena malonjezo onse odzimana amene mkaziyo walumbirira moyo wake. Iye wawakhazikitsa chifukwa sananenepo kanthu kwa mkaziyo pa tsiku limene anamumva akulonjeza. Ndipo ngati mwamunayo afafaniza malonjezowo patapita nthawi pambuyo poti wawamva kale, cholakwa chizikhala pa iyeyo m’malo mwa mkazi wake.” (Numeri 30: 2-15)

Nanga ndi chifukwa chiyani malumbiro a mkazi samangika payekha? Yankho lake ndi losavuta: chifukwa iyeyo ndi wa bambo ake, asanalowe m’banja, kapena ndi mwamuna wake pambuyo pa ukwati. Udindo wa bambo pa mwana wawo wamkazi unali wamphamvu kotero kuti ngakhale atafuna akhonza kumugulitsa! Zimenezitu zinalembedwa ndi ma Rabbi kuti: “Mwamuna akhoza kugulitsa mwana wake wamkazi, koma mkazi sangagulitse mwana wake wamkazi, mwamuna akhoza kukwatitsa mwana wake wamkazi, koma mkazi sangakwatitse mwana wake wamkazi.” 17

Mabuku a ma Rabbi amanenanso kuti  ukwati umatanthauza kusamutsa udindo kuchokera kwa bambo kupita kwa mwamuna: “kumukwatitsa, kumupangitsa mkazi kukhala cholowa choyera – asanduka kukhala katundu woyenera wa mwamuna …” Mwachiwonekere, ngati mkazi ali katundu wa mwamuna, sangathe kupanga malonjezo omwe mwamuna wake savomereza.

Tikuyenera kudziwa kuti malangizo a m’Baibulo oterewa pa malumbiro a mkazi, akhala ndi zotsatira zoipa kwa akazi a Chiyuda ndi Chikhristu nthawi zonse kufikira posachedwapa. Mkazi wokwatiwa ku maiko a Kumadzulo analibe ulemelero uliwonse ngakhale udindo pa malamulo. Chochita chake chirichonse chimakhala chotsika mtengo, chosalemekezeka. Mwamuna wake amakhoza kukana mfundo iriyonse yomwe angabweretse. Akazi a maiko a Kumadzulo (komwe kuli ulemelero waukulu wa Chiyuda ndi Chikhristu) sanali kuloledwa kupanga mgwirizano uliwonse chifukwa anali pansi pa amuna awo. Iwo akhala akuzunzika kwa zaka pafupifupi zikwi ziwiri  (2000) chifukwa cha malingaliro a Baibulo pa udindo wa amayi kwa abambo ndi amuna awo. 18

Mu Chisilamu, lonjezo la Msilamu aliyense, mwamuna kapena mkazi, limamangika ndi iye mwini. Palibe amene ali ndi mphamvu zotsutsa malumbiro a wina aliyense. Kulephera kusunga lumbiro lodziwika, lopangidwa ndi mwamuna kapena mkazi, ndikoletsedwa monga momwe Qur’an yakambira:

Qur’an 5:89: “…koma akulangani kamba ka malumbiro omwe mwalumbira motsimikiza. Choncho dipo lake ndikuwadyetsa osauka khumi ndi chakudya cha mlingo wapakatikati chomwe mumawadyetsa anthu anu; kapena kuwaveka, kapena kumpatsa ufulu kapolo. Koma amene sangapeze zimenezo, asale masiku atatu. Ili ndi dipo lakulumbira kwanu pamene mukulumbira. Ndipo sungani malumbilo anu, (musaswe chomwe mudalumbirira)…”

Anzake a Mneneri Muhammad, amuna ndi akazi, ankakonda kupereka lumbiro lawo lomumvera iye. Akazi, komanso amuna, amadza kwa iye paokha ndikulumbira:

Qur’an 60:12: “E, iwe Mtumiki! Akakudzera akazi okhulupirira kudzakulonjeza kuti samphatikiza Mulungu ndi chilichonse ndi kuti saziba,sazichita chiwerewere, sazipha ana awo ndi kuti sazinena bodza lamkunkhuniza, lomwe akulipeka pakati pa manja awo ndi miyendo yawo (pompachika mwana kwa wina amene sali tate wake), ndi kutinso sadzakunyoza pachinthu chabwino (chimene ukuwaitanira), landira lonjezo lawolo, ndipo apemphere chikhululuko kwa Mulungu. Ndithu Mulungu Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni.

Mwamuna sanali kulumbira mmalo mwa mwana wake wamkazi kapena mkazi wake. Munthu sanali kukana lumbiro lopangidwa ndi wachibale wake wamkazi.

Chuma cha Mkazi