Ndi chifukwa chani timayenera kutsuka ndi mchenga kamodzi?

“Kuyeretsa kwa chiwiya chanu chomwe wanyambitamo galu ndi kutsuka ka 7, kamodzi kakeko ndi mchenga”.

Tonse tikudziwa kuti Mtumiki anatiuza kuti tidzitsuka chiwiya chomwe galu wanyambita ka seven, kamodzi ndi mchenga.

Posachedwapa ma dokotala atsimikiza kuti izi ndi zoona, chifukwa malovu agalu amakhala ndi ma germs oopsa oti madzi okha sangachotse ngakhale titatsuka kambirimbiri, koma kugwiritsa ntchito mchenga … kodi mu mchengamo anapezamo zotani?

Choyamba tione kaye kuti Mtumiki anatiphunzitsa chani:

Zinthu zomwe zimachititsa kuti galu akhale najs (uve) ndi chinyezi chirichonse chomwe chimapezeka mu galu, malinga ndi hadith ya Abu Huraira radhia Allah anhu yemwe anamumva Mtumiki salla Allah alaih wasallam:

“Kuyeretsa kwa chiwiya chanu chomwe wanyambitamo galu ndi kutsuka ka 7, kamodzi kakeko ndi mchenga”.

Najsi ilipo yambiri mwa galu, yomwe ikuyenera kutsukidwa chimodzimodzi, koma Hadith inakamba za malovu chifukwa cha zomwe malovuwo amanyamula, zoipa kuthupi la munthu.

MAYERETSEDWE A CHIWIYA CHOMWE PAGWERAPO NAJS YA GALU:

Kutsuka koyamba ndi mchenga kuti kutsuka ka 6 kuja kukhale kuti kukuyeretsa malo a mchengawo. Komanso kutsuka ndi mchengaku kukhonza kuchitika nthawi iliyonse kaya pa number 3, 4, 5 etc, koma ndi zabwino kwambiri musanafike ka chi 7 kuti kenako mukhale ngati mukutsuka malo odetsedwa ndi mchenga aja.

KUTSUKA NDI MCHENGA KUNGACHITIKE BWANJI NDONDOMEKO YAKE?
CHITANI IMODZI MWA NJIRA IZI:

1. Mutsuke ndi madzi kenako muthire mchenga ndikuyeretsa
2. Muthire mchenga kenako mutsuke ndi madzi
3. Musakanize mchenga ndi madzi kenako mutsukuluze chiwiyacho.

KODI ZINGATHEKE KUGWIRITSA NTCHITO SOPO MMALO MWA MCHENGA?

Pali kusiyana ma ulamaa pankhani imeneyi malinga ndi kuzindikira kwawo:
1. Ena anati palibe chomwe chingalowe mmalo mwa mchenga chifukwa Hadith sinakambe, yangoti mchenga.
2. Pomwe ena anati china chilichonse chikhonza kulowa mmalo mwa mchenga monga sopo ndi zina zotero.

Kusiyana kwa ma ulamaa kumeneku kukupezeka chifukwa cha kutchulidwa kwa dothi mu hadith; kodi dothi latchulidwa chifukwa choti ndi chimodzi mwa zinthu ziwiri zomwe ndi zokhazo zimagwiritsidwa ntchito podziyeretsera, monga wudhu (madzi), tayammam (mchenga)? Kapena chifukwa choti madzi paokha sangathe kuchotsa uve woonekerawo paokha?

MFUNDO YOGWIRIZANITSA KUSIYANA KUMENEKU NDI IYI

Mtumiki salla Allah alaih wasallam samangoyankhula za mmutu. Tikulangizidwa kwambiri kugwiritsa ntchito mchenga pochotsa najs ya galu, ndipo ngati palibe mchega papezekedi kuti palibe (ngakhale zili zovuta kuti usapezeke), tikhonza kugwiritsa ntchito sopo kapena mankhwala ena alionse omwe “tikuganiza” kuti angachotse zimenezi … makamakanso ngati najsiyo ili pa chovala ndiye tikuopa kuti tithimbiriza nsalu.

KODI MAU A MTUMIKIWA AKUGWIRIZANA BWANJI NDI ZA CHIPATALA (SCIENCE)?

Mu Hadith ya Abu Huraira Mtumiki salla Allah alaih wasallam anati: “Kuyeretsedwa kwa chiwiya chomwe wanyambitamo galu ndi kutsuka kasanu ndi kawiri, kamodzi mwa iko ndi mchenga”
——-
Hadith imeneyi ikulangiza zinthu ziwiri:
1. Kufunika kwa kusamala chiwiya chomwe galu wanyambitamo kapena kudyeramo/kumweramo.
2. Kutsuka chiwiyacho kangapo komanso kugwiritsa ntchito mchenga kamodzi mwa iko kukusonyeza kupezeka kwa mphamvu ya kuopsa kwa malovu agalu ku umoyo wa munthu.

Ulangizi wa za umoyo umenewutu unaperekedwa ndi Mtumiki salla Allah alaih wasallam zaka zoposa 1400 zapitazo. Ndipo nthawi imeneyo kunalibe microscope kapena goniometer, kunalibe.

Posachedwapa mpamene ma dokotala apanga kafukufuku wao pofuna kumva kuti kodi Asilamu amamupewa galu mu zinthu zambiri chifukwa chani. Ataitsata nkhani anapeza kuti kuseliko kuli mau a Mtumiki wao Muhammad salla Allah alaih wasallam olangidza kuti pamene panyambita galu adzitsukapo kangapo.

Kuyambira pamenepo anayamba kufufuza kuti mkulu ameneyu anadzitenga kuti zimenezi…anagwiritsa ntchito zida zawo nkupeza kuti ndi zoona.

Ndipo anatsimikiza kuti ndi zofunikira kwambiri kutsuka kambirimbiri pogwiritsa ntchito mchenga umene ndi chida chokhacho chomwe chingakwanitse kukokota ma bacteria ndi uve wonse womwe umakhala mmalovu a galu.

Ma dokotala analongosola kuti chinsinsi chake chotsukira kambirimbiri ndikugwiritsa ntchito mchenga ndi choti, ma germs a galu ndi an’gonoang’ono kwambiri, komanso amachulukana, choncho ma germs akakhala ang’onoang’ono, chiwelengero chawo chimakhala chochuluka ndipo amakhala amphamvu zochuluka, komanso amakhala ndi mphamvu yokanilira mu chiwiya.

Malovu a galu amene amakhala ndi ma germs woopsa chonchi amakhala otelera komanso oyendelera…choncho mchenga pamenepa umagwira ntchito yoyamwa ma microbacteria amene amakamira pansi komanso mbali mwa chiwiyacho.

Ma dokotala apeza kuti mchenga uli ndi ma antibiotics awiri (Tetracycline ndi TriLyte) amene amalimbana ndi ma bacteria. Popanga analyse dothi, ma doctor anali ndi chiyembekezo choti akhonza kupezamo kuti mwadzadza ma bacteria chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zimene zimaferamo. Komatu ai, mmalo mwake anapeza kuti mchenga ndi element yokhayo yamphamvu imene imapanga absorb ma bacteriawo ndipo siimapangidwa affect.

Zimenezitu analengedza ma doctor akuluakulu pambuyo pakupanga analyse dothi la mmanda kuti adziwe mitundu ya ma bacteria amene akupezekamo, ndipo ankayembekeza kuti apeza mulu wa ma bacteria oopsa chifukwa choti anthu ambiri amafa ndi ma bacteria osiyanasiyana. Komatu sanapeze chizindikiro cha bacteria wina aliyense. Mpameneno amabwera ndi conclusion yoti mchenga ndi chida chokhacho chimene chingayeretse ziwiya ku ma bacteria oopsa.

Mtumiki salla Allah alaih wasallam anawaphunzitsa kalekale Asilamu, kuti galu akanyambita chiwiya adzitsuka ka 7 kamodzi ndi mchenga, chifukwa anaona kale zimenezi.

Azungu adzitulukira tsopano kuti ma atom a mchenga amalowana ndi ma bacteriawo motero kuti amachokera limodzi mosavuta.
Iwo anakambaponso malinga ndi kafukufuku wawo; chifukwa chogwiritsira ntchito mchenga kuti lithandizire madzi pa nkhani imeneyi ndi choti madzi paokha sangakwanitse. Iwo anati:

“Tsopano nchifukwa chani munthu akuyenera kugwiritsanso ntchito mchenga?…chifukwa choti timabacteria timene timayambitsa matendato ndi tating’onoting’ono kotheratu, choncho tikakhala ting’onoting’ono kwambiri nkuchulukananso, timakhala tamphamvu komanso timatha kukanilira mmakoma ndi pansi pa chiwiya motero kuti kutsuka ndi mchenga ndi njira yokhayo imene ili yamphamvu kuposa madzi okha chifukwa choti mchenga umakankha malovuwo pamodzi ndi ma virus onse omwe akupezeka mmenemo mwamphamvu kwambiri kuposa kudusitsamo madzi kapena dzanja, chifukwa chotinso mchenga umakhala kuti ukukokota podutsa pomwe dzanja ndi madzi zimangotelereka. Komanso mu mchenga muli ma substance amene amalowa mma bacteriamo nkusokoneza mgwirizano wawo”

Tikamati tiyeni tidzitsatira Sunnah za Mtumiki, kumakhala ngati kukhwimitsirana umoyo. Komatu tikafufuza zonse zomwe Mtumiki anatiphunzitsa, tipeza kuti zimatiteteza tokha.
Ndiye wina adziti Mtumiki wanu Muhammad alibe ma miracles? Pomwe zomwe akuchita iyeyo tsiku nditsiku mu umoyo wake anadzikamba kale!!!