Awa ndimalo omwe ali oletsedwa kupangiramo swalaat

1. Ku Manda

Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam ananena mu Hadith kuti:

لعن الله اليهود والنصارى اتخذوا قبور أنبيائهم مساجد

Allah adawatembelera Ayuda ndi Akhristu kamba koti adatenga manda azineneri awo kukhala malo opemphelera

وصف : تخريج السيوطي : (حم) عن أسامة بن زيد (حم ق ن) عن عائشة وابن عباس معا (م) عن أبي هريرة. تحقيق الألباني : (صحيح) انظر حديث رقم: 5108 في صحيح الجامع.‌
الصفحة أو الرقم : / 5108
خلاصة حكم المحدث : صـحـيـح
اسم الكتاب : صحيح وضعيف الجامع الصغير وزيادته

2. Malo omwe mzikiti wamangidwa ndiye pali manda kutsogolo kwakeko

Malo amenewo ndiwoletsedwa kupemphelera

Ummu Habeebah ndi Ummu Salamah radhia Allahu anhuma pamene anali ku Habasha anadzaona tchalitchi chomwe mkati mwake munaikidwamo zithunzi za anthu ndipo Mtumiki ananena kuti:

إن أولئك إذا كان فيهم الرجل الصالح فمات بنوا على قبره مسجدا وصوروا تيك الصور أولئك شرار الخلق عند الله يوم القيامة

Iwowo ndi anthu oti akamwalira munthu yemwe amapanga zabwino,akamwaliramo amamanga pamalopo Mzikiti (nyumba yopemphelera) ndipo amajambula zithunzi za anthuwo, ndithu amenewo(amene amapanga zimenezo) ndi anthu/zolengedwa zoipitsitsa pamaso pa Allah tsiku lomaliza.

وصف : قال الشيخ الألباني : صحيح # سند الحديث : # أخبرنا يعقوب بن إبراهيم قال حدثنا يحيى قال حدثنا هشام بن عروة قال حدثني أبي عن عائشة أن أم حبيبة وأم سلمة ذكرتا كنيسة رأتاها بالحبشة فيها تصاوير فقال رسول الله صلى الله عليه وسلم
الصفحة أو الرقم : 41 / 704
خلاصة حكم المحدث : صـحـيـح
اسم الكتاب : المجتبى من السن

Ngati kwanuko kutsogolo kwa Mzikiti kuli manda kapena mkati mwamzikiti muli manda omwe anaikidwa pambuyo poti mzikiti wamangidwa muyenera mugumule zimenezo; ndi Haraam kuswalira mzikiti umenewo.

3. Kuchimbudzi

Mtumiki salla Allah alaih wasallam ananena mu Hadith kuti:

الأَرْضُ كُلُّهَا مَسْجِدٌ إِلاَّ الْمَقْبَرَةَ وَالْحَمَّامَ

Nthaka yonse ndi Mzikiti (malo oswalira) kupatula ku Manda ndikuchimbudzi

Ibn Maajah #745
Nthaka imene mtumiki anatchula apayi ndi nthaka yake omweyi imene timaipondayi

Nthaka yomwe tikhoza kupangila tayammam. Nthaka yomweyo tikhoza kuziyeretsera ku Najisi (Mkodzo)

4. Malo omwe ngamira zimakhala ndikupumako

Malo omwe ngamira zimakhala ndi kuima kupumuliramo; malo amenewo ndiwoletsedwa kuswalira.

Pofunika tilongosole bwino apa kuti timvetsetse zomwe tikutanthauza

Mtumiki atafunsidwa za kuswalira Swalah malo omwe ngamira zimakhalamo kapena kuimamo, anati ayi osaswalira malo omwe ngamira zimaima/kukhalamo, chifukwa malowo ndiwomwe asatana amakhalamo (amakonda kukhalamo). Ndipo atafunsidwa zakuswalira Swalah malo omwe mbuzi (nkhosa) zimakhalamo/zimaima ndikumapuliramo, Mtumiki anati: Swalirani malo amenewo kamba koti malowo ndimalo a Madalitso

سئل رسول الله صلى الله عليه وسلم عن الصلاة في مبارك الإبل فقال لا تصلوا في مبارك الإبل فإنها من الشياطين وسئل عن الصلاة في مرابض الغنم فقال صلوا فيها فإنها بركة
وصف : قال الشيخ الألباني : صحيح # سند الحديث : # حدثنا عثمان بن أبي شيبة ثنا أبو معاوية ثنا الأعمش عن عبد الله بن عبد الله الرازي عن عبد الرحمن بن أبي ليلى عن البراء بن عازب قال
الصفحة أو الرقم : 133 / 493
خلاصة حكم المحدث : صـحـيـح
اسم الكتاب : سنن أبي داود

Pamenepa tinenetse kuti;
Chiweto china chirichonse chomwe chimadibwa (chomwe chili Halaal kuchidya) dziwani kuti ndowe/chimbudzi chake komanso mkodzo sumakhala najisi kwainu. Mbalame ikakubibilani mmutu mutaima osati mwaduka twahaarah ayi.
Muli ndiufulu kuswalira malo omwe mbuzi zimakhala palibe vuto.

Nanga bwanji Mtumiki akutiletsa kuswalira malo omwe ngamira zimaima ndikukhalamo kumachita kuti ngamila ndi Halaal kudya?

Yankho lake ndi ili:

Mtumiki akutiuza mu Hadith mmwambamo kuti malo amenewo ndiwomwe Shaitaan amakonda kuimamo.

Ndipo kuletsaku kunabwera kamba kazimenezo, ndipo akuti zingatheke munthu kuswali pamalowa ndiye ali mkati moswali kamba koti ngamira ingathe kuthawa Shaitaan pamalopo mwaliwilo kenako ndikukugundani mukuswali inuyo ndikupanga ngozi.
Pachifukwa chimenecho zinaletsedwa kuswalira malo amenewo., osati kamba koti ngamila ndi najisi ayi.

5. Malo omwe anthu amakonda kupangira zinthu za Haraam mmene satana amakonda kukhala

Mwachitsanzo mutchalitchi, mu bar, mu tarven (malo omweramo mowa). Malo amenewo ndi Haraam kuswaliramo.

Mtumiki anagona malo ena ake ndi maswahaba, ndipo anagonetsa kwambiri mpaka dzuwa kutuluka kummawa moti Fajir inadutsa munthawi yake. Mtumiki anawauza onse kuti akonze zokwera zawo, kenako ananena kuti malo awa anatifungatira/anabwera satana(kuti tisadzuke ife).

ليأخذ كل رجل برأس راحلته فإن هذا منزل حضرنا فيه الشيطان . ‌
وصف : تخريج السيوطي : (حم م ن) عن أبي هريرة. تحقيق الألباني : (صحيح) انظر حديث رقم: 5347 في صحيح الجامع.‌
الصفحة أو الرقم : / 5347
خلاصة حكم المحدث : صـحـيـح
اسم الكتاب : صحيح وضعيف الج

6. Malo omwe anachita kulandidwa.

Malo amenewo ukamangidwapo mzikiti ndi Haraam kuswaliramo malingana ndima Ulamaau monga Sheikh Abu Zakariyyah Yahya bun Sharaffi Annawawiyy (omwe analemba bukhu la Riyadh Swaliheen aja). Mwachidule timangoti Imaam Annawawiyy النووي

Mtumiki ananena kuti;
Asatenge munthu inch imodzi ya nthaka yamunthu wina popanda chilolezo kuchokera kwamwiniyo, koma kuti omwe angatenge nthaka yawina adziwe kuti akasenzedwa nthaka 7 mmutu mwake tsiku lomaliza.

وعن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال لا يأخذ أحد شبرا من الأرض بغير حقه إلا طوقه الله إلى سبع أرضين يوم القيامة

الصفحة أو الرقم : / 1866
خلاصة حكم المحدث : صـحـيـح
اسم الكتاب : صحيح الترغيب والترهيب

7. Mzikiti wina ulionse womwe wamangidwa chifukwa chofuna kusokoneza Asilamu kapena kumapangilamo zinthu zosemphana ndi Qur’an ndi Sunnah

Mwachitsanzo kumanga mzikiti wapadera ndikuwupanga kuti umenewu ndi mzikiti wathuwathu ife anthu a bid’ah.

Kapena kumanga mzikiti wapadera kuti ife ndiakutiakuti ndipo sitingaswali mzikiti wa akutiakuti; kudzipatsa maina. Mizikiti imeneyo Haraam kuswaliramo.

Kumanga mzikiti pofuna ziwembu kuti azipheramo anthu, ngati mmene anapangira mamunafikuna nthawi ya Mtumiki salla Allahu alaih wasallam; anamanga mzikiti ndikumuitana Mtumiki Muhammad kuti akatsegulire, monga guest of honour. Koma atapanga upo woti mmodzi akwere pamwamba pamzikiti atatenga chimwala, akangolowa Mtumiki mumzikitimo angofikira kuchiponya chimfikire Mtumiki mmutu.
Koma Allah anamutuma Jibril kuti Mtumiki asakakhale nawo pamwambowo. Surat Tauba (107):

 وَالَّذِينَ اتَّخَذُوا مَسْجِدًا ضِرَارًا وَكُفْرًا وَتَفْرِيقًا بَيْنَ الْمُؤْمِنِينَ وَإِرْصَادًا لِمَنْ حَارَبَ اللَّهَ وَرَسُولَهُ مِنْ قَبْلُ وَلَيَحْلِفُنَّ إِنْ أَرَدْنَا إِلَّا الْحُسْنَى وَاللَّهُ يَشْهَدُ إِنَّهُمْ لَكَاذِبُونَ

Ndipo (alipo amunafikina ena) amene adamanga msikiti ndi cholinga chodzetsa masautso ndi (kulimbikitsa) kusakhulupilira Allah ndi kuwagawa Asilamu (mu umodzi wawo) ndi kuupanga kukhala msasa wa omwe adam’thira nkhondo Allah ndi Mtumiki Wake kale. Ndithu, alumbira (ndikunena): “Sitidali n’cholinga china (pomanga Msikitiwo) koma ubwino.” Koma Allah akuikira umboni kuti iwo ngabodza.

8. Malo omwe Chilango/Chionongeko cha Allah chidawaonongera anthu ena kamba  kophwanya malamulo a Allah.

Mtumiki amawaletsa Asilamu kulowa mmalomo, anati ine ndikuopa kuti chilango cha Allah chingakufikireni mmenemo.. 

الصفحة أو الرقم : 403 / اسم الكتاب : الثمر المستط

9. Malo omwe Imaam waima poswalitsa akakhala wokwera, ndipo anthu a mmbuyo aima chapansi pake

Ngati pali mizikiti yomwe Imaam poswalitsa amaima malo wokwera, ndiye anthu ammbuyo mkumamuona imaam uja ali pamwamba pokwelerapo iwo mkumaoneka pansi, malo amenewo ndiwoletsedwa ndithu kuswalira ndipo musaime kumbuyo kwa Imaam ameneyo.

Mkana mumaona mma  ku Makkah, Imaam amakhala pa Ka’bah penipeni ndipo am’mbuyo amaima kumbuyo ngakhale enawo azikhala malo okwera palibe vuto.

نهى أن يقوم الإمام فوق شيء والناس خلفه ‌

Mtumiki analetsa imaam kuima pamwamba pachina chake kumachita kuti anthu ali kumbuyoku(akukuonerani mmwamba inuyo)

وصف : تخريج السيوطي : (د ك) عن حذيفة. تحقيق الألباني : (صحيح) انظر حديث رقم: 6842 في صحيح الجامع.‌
الصفحة أو الرقم : / 6842
خلاصة حكم المحدث : صـحـيـح
اسم الكتاب : صحيح وضع

10. Malo omwe pakati pake pali Zipilala

Mwachidule kutsogolo kuli chipilala komanso kumbuyo kuli chipilala, munthu akamaswali akati awerame zikupezeka kuti akupanikizika; mutu ukugunda chipilala chakutsogolo, kumbuyo thako likugunda chipilala chakumbuyo, kapena tinene kuti malo omwe ali pakati pazipilala ziwiri zoyandikana zomwe zikuwatchingira anthu, sitikuyenera kuswalirapo.

حَدَّثَنَا مُحَمَّدُ بْنُ بَشَّارٍ، حَدَّثَنَا عَبْدُ الرَّحْمَنِ، حَدَّثَنَا سُفْيَانُ، عَنْ يَحْيَى بْنِ هَانِئٍ، عَنْ عَبْدِ الْحَمِيدِ بْنِ مَحْمُودٍ، قَالَ صَلَّيْتُ مَعَ أَنَسِ بْنِ مَالِكٍ يَوْمَ الْجُمُعَةِ فَدُفِعْنَا إِلَى السَّوَارِي فَتَقَدَّمْنَا وَتَأَخَّرْنَا فَقَالَ أَنَسٌ كُنَّا نَتَّقِي هَذَا عَلَى عَهْدِ رَسُولِ اللَّهِ صلى الله عليه وسلم ‏.‏

 Hadith inachokera kwa AbdulHamid ibn Mahmud, anati: Ndinapemphera swalaat ya Lachisano pamodzi ndi Anas bin Malik. Ndipo tinali kupanikizika ndizipalala chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Choncho, tinaima kutsogolo ndi kumbuyo; Anas anati: tinali kupewa izi nthawi ya Mtumiki salla Allah alaih wasallam. Sahih (Al-Albani) Sunan Abi Dawud 673